Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nchifukwa Ninji Ndili Wonenepa Kwambiri?
“Ndimadzimva kukhala wonenepa ndithu, ngakhale kuti pamene ndiyang’ana pa matchati amene amasonyeza kunenepa koyenera kwa munthu, sindili wonenepa kwambiri.”—Patti.
“Kukhala wonenepa . . . kumachotsa ulemu wako kwambiri. Ndakhala wonenepa kwambiri kuyambira pamene ndinali mu giredi lachinayi . . . Pamenepo mpamene anayamba kunditcha maina onyoza.”—Judd.
KUNENEPA. Iko kuli chinthu chovutitsa maganizo kwambiri pakati pa achichepere ena, makamaka atsikana. Pamene kagulu kena ka atsikana a msinkhu wopita kusukulu kanafunsidwa, 58 peresenti ya iwo anadziona kukhala onenepa.
Malinga ndi kufufuza kwina kwa ku United States, 34 peresenti ya atsikana achichepere onenepa kwambiri anayamba amwapo mibulu yochepetsa thupi. Pafupifupi 1 mwa 4 amadzisanzitsa dala! Posimba za kufufuza kwinanso, The New Teenage Body Book likunena kuti: “Mochititsa mantha, pafupifupi theka la a zaka zisanu ndi zinayi ndi pafupifupi 80 peresenti ya a zaka khumi ndi a khumi ndi chimodzi anali kuchepetsa kudya. Pafupifupi 70 peresenti ya atsikana a zaka khumi ndi ziŵiri mpaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi anali kuyesayesa kuchepetsa thupi—ndipo 90 peresenti ya a zaka khumi ndi zisanu ndi ziŵiri anali kuchepetsa kudya kuti achepetse thupi.”
Mzimu Wakufuna Kuwonda
Kwa zaka mazana ambiri, thupi lonenepa bwino linalingaliridwa kukhala lokongola kwa amuna ndi akazi omwe. Koma mkati mwa ma 1920, indasitale yopanga zovala zamakono ya ku United States inapanga masinthidwe ena ake. Mwadzidzidzi thupi lowonda linakhala lokhumbirika. Zaka makumi ambiri pambuyo pake, kuwonda kukupitirizabe kukhala kwamakono. TV ndi magazini zathandizira kuchirikiza lingaliro limeneli ndi unyinji wa zosatsa malonda zawo zamachenjera zimene zimasonyeza amuna ndi akazi ochepa thupi. Zilibe kanthu kuti anthu ambiri owonda ameneŵa amadzipha ndi njala kuti akhale owonda! Mamiliyoni a achichepere (ndi achikulire) aphunzitsidwa mwamachenjera kukhulupirira kuti kukongola ndiko kuwonda. Pamenepo, nzosadabwitsa kuti achichepere ambiri omwe sali owonda amadzilingalira mofala kukhala onenepa ndi osakongola.
Chitsenderezo chochokera kwa ausinkhu wawo chimaipitsirapo mkhalidwewo. Achichepere onenepa kwambiri kaŵirikaŵiri amasekedwa nthaŵi zonse, kunyodoledwa, ndi kudedwa, zimene zinachititsa wolemba wina kuzitcha “kupweteka kwakukulu kwa maganizo”—kupweteka kumene kungakhalepobe mpaka mu uchikulire.
Kodi Ndani Amene Amati Ndinu Wonenepa?
Mwamwaŵi, funso lakuti kaya ndinu wonenepadi kwambiri kapena ayi silimapimidwa chabe ndi mmene mumaonekera mukavala zovala zanu—malinga ndi lingaliro la odziŵa zamankhwala. Kaŵirikaŵiri madokotala amafotokoza munthu kukhala wonenepetsa ngati alemera ndi 20 peresenti kuposa kulemera kwake koyenera. Komabe, matchati ovomerezedwa a msinkhu ndi kulemera ali ozikidwa pa maavareji, ndipo angangopereka lingaliro lachisawawa la mmene munthu wathanzi ayenera kulemerera. Chotero madokotala ena amakonda kupima kunenepetsa osati ndi kulemera kokha komanso ndi mafuta a thupi opambanitsa. Malinga ndi kunena kwa A Parent’s Guide to Eating Disorders and Obesity, “mafuta ayenera kupanga 20 mpaka 27 peresenti ya mnofu wa thupi mwa akazi ndi 15 mpaka 22 peresenti ya mnofu wa thupi mwa amuna.”
Ofufuza ena amakhulupirira kuti pali achichepere ochepa kwambiri omwe alidi onenepa kwambiri. Malinga ndi lingaliro la azaumoyo, pangakhale popanda chifukwa chenicheni choti muchepetse thupi. M’kufufuza kotchulidwa poyambirirapo, loposa theka la atsikana amene anafunsidwa anadzilingalira kukhala onenepa kwambiri, koma 15 peresenti yokha inalidi yotero.
Kodi Nchifukwa Ninji Ndimaoneka Chonchi?
Zimenezi sizingakutonthozeni kwenikweni pamene mudziyang’ana pa kalilole; mwinamwake mungakhale mulibiretu thupi limene mumalilingalira kukhala lokongola. Mtsikana wina wachichepere anadandaula kuti: “Ndingakonde kuchepetsa thupi, kutalikirapo, ndi kukhala ndi thupi loumbika bwino kwambiri.”
Komabe, kumbukirani kuti pokhala wachichepere, thupi lanu likusintha mofulumira. “Anyamata ndi atsikana omwe amanenepa pa unamwali,” akulongosola motero Dr. Iris Litt. “Koma pamene kuli kwakuti anyamata amawonjezera kwambiri minyewa ya mnofu, atsikana amawonjezera minyewa ya mafuta. Pa unamwali, mtsikana amachoka pa kukhala ndi pafupifupi maperesenti asanu ndi atatu a mafuta—amene amakhala ndi amuna ndi akazi omwe—kufika pa 22 peresenti ya mafuta a thupi. Panthaŵi imodzimodziyo, masinthidwe a mafupa amawonjezera kunenepa mwa atsikana. Anyamata amakhala ndi mapeŵa aakulu, pamene atsikana amakhala ndi ziuno zazikulu.” Masinthidwe ameneŵa amatenga nthaŵi. Koma mtsikana wonenepa wa zaka 11 kapena 12 angakhale wachichepere wa thupi loumbika bwino atafika pa unamwali. Nthaŵi zina sangatero.
Ngati zimenezi zinakuchitikirani, mwapang’ono zingakhale chifukwa cha majini amene munalandira kwa makolo anu. Madokotala ena amakhulupirira kuti, limodzi ndi mtundu wa khungu lanu, maonekedwe a tsitsi, ndi msinkhu, kaumbidwe ka thupi lanu ‘kanalembedwa’ m’majini pa kutenga pathupi, monga momwe analembera wamasalmo. (Salmo 139:16) Dr. Lawrence Lamb, akumapereka mfundo imodzimodziyo imene wamasalmo anauziridwa kulemba akunena m’buku lake lakuti The Weighting Game, kuti: “Munabadwa ndi cholembedwa cha moyo chimene chimasankha kuti muyenera kulemera makilogalamu angati, ndi kuti muyenera kukhala ndi mafuta ochuluka motani, pa nthaŵi zosiyanasiyana za moyo wanu.”
Zofufuza zatsimikizira chiyambukiro chimene majini ali nacho pa maumbidwe a thupi. Ana olera amakhala ndi matupi ofanana ndi makolo awo owabala, mosasamala kanthu za maumbidwe a thupi a makolo awo owalera. Ndipo popeza kuti ana amapasa amakhala ndi majini ofanana, siziyenera kutidabwitsa kuti amapasa kaŵirikaŵiri amakhal olemera mofanana.
Kodi zimenezi zikutanthauzanji kwa inu? Mwachitsanzo, tangolingalirani kuti makolo anu onse aŵiri ngonenepetsa. Pamenepo muli ndi kuthekera kwa 80 peresenti kwakuti nanunso mudzakhala wonenepetsa. Kuthekerako kumatsika ndi theka ngati kholo limodzi lokha lili lonenepetsa. Maseŵera ndi kadyedwe zingathandize pang’ono. Koma kwakukulukulu, timakhala ndi maumbidwe enieni a thupi lathu. Ngati muli ndi thupi la ectomorph, ndiye kuti mwachibadwa ndinu wowonda ndi wokhala ndi mafupa oonekera. Koma ngati majini anu akuchititsani kukhala wa endomorph—munthu wokhala ndi thupi lobulungika ndi mafuta ambiri athupi—ndiye kuti simunapangidwe kukhala wowonda. Ngakhale pa kulemera kwanu kovomerezedwa m’zamankhwala, mudzaoneka wamkulu kuposa mmene mumafunira.
Kukhutira ndi Maonekedwe a Thupi Lanu
Kodi nzokhumudwitsa? Mwinamwake. Koma mbiri yabwino njakuti Yehova Mulungu analenga anthu aŵiri oyambirira, Adamu ndi Hava, angwiro m’kaumbidwe ka thupi. Ngakhale kuti anakhala opanda ungwiro ndi kupatsira kupanda ungwiro kwa ana awo, Mulungu adzatsimikizira kuti zophophonya zilizonse za choloŵa zakuthupi zidzawongoleredwa m’dziko lake latsopano lolungama.—Yobu 14:4; Aroma 5:12; 2 Petro 3:13.
Kumbukirani kuti, miyezo ya kukongola ingakhale chotulukapo cha kusintha malingaliro a anthu ndi zokonda za munthu mwini. Motero, zimene zimalingaliridwa kukhala zokongola zimasiyanasiyana m’dziko lonse ndipo zingasinthe ndi kupita kwa nthaŵi. Chotero kodi nkuloleranji “dziko lokuzingani kukukanikizirani m’chikombole chake”? (Aroma 12:2, Phillips) Kodi nkugonjereranji ku miyezo ndi malingaliro amene kaŵirikaŵiri amakhala opotozedwa?
Palibe chifukwa chenicheni chakuti mudzinyazitse kapena kukhala wovutika maganizo kokha chifukwa chakuti sindinu wowonda. Mulungu samatiweruza mwa maonekedwe akuthupi a msinkhu kapena maumbidwe a thupi lathu. “Munthu ayang’ana chooneka ndi maso,” Baibulo limatero, “koma Yehova ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:7) Inde, ali “munthu wobisika wamtima” amene ali ndi kanthu kwa Mulungu—osati ukulu wa matako anu kapena chuuno chanu. (1 Petro 3:4) Ndipo ngati muli wachimwemwe, woleza mtima, wopatsa, ndi wodera nkhaŵa za ena, anthu adzakopeka nanu.
Izi sizikutanthauza kuti palibe chimene mungachite kuti muwongolere maonekedwe anu. Koma ngati simuli wachimwemwe konse chifukwa cha kaonekedwe ka thupi lanu, simufunikira kulanga thupi lanu ndi chakudya. Mwinamwake mungangofunikira kukhala wosamala ndi mitundu ndi maonekedwe a zimene mumavala, kusankha zovala ndi mitundu imene imabisa zimene mumazilingalira kukhala zolakwika ndi kuonetsera maonekedwe anu abwino.
Chikhalirechobe, mungalingalire kuti kudzakhala kopindulitsa kuchepetsako thupi pang’ono. Kapena mungakhale ndi vuto lenileni la kunenepetsa ndipo muyenera kuchepetsa thupi osati kuti muoneke bwino chabe koma kaamba ka thanzi. Nkhani yathu yotsatira ikulongosola mmene mungachitire zimenezo mwa chisungiko.
[Bokosi patsamba 26]
“Ndine Wowonda Kwambiri”
Si achichepere onse amene amavomereza kuti kukhala wowonda nkwabwino. “Ndine mnyamata wa zaka 15 wowonda kwambiri amene ndimasekedwa nthaŵi zonse,” akudandaula motero Mark wachichepere. Kaŵirikaŵiri kuwonda kuli chiyambukiro choipa cha unamwali. Thupi lomakula limadya unyinji waukulu wa macalorie. Wachichepere sangayambe kubwezeretsa unyinji umenewu kufikira ataleka kukula. Majini alinso ndi thayo. Ndithudi, matenda kapena kusalinganizika bwino kwa mahomoni kungachititsenso kuwonda kopambanitsa, ndipo chisamaliro cha dokotala chili chofunika m’mikhalidwe yoteroyo. Chithandizo cha akatswiri chingakhalenso chofunika kwa achichepere amene amaleka kudya chifukwa cha kuvutika maganizo kapena chifukwa cha matenda owopsa a kadyedwe, monga ngati anorexia nervosa.
Mulimonse mmene zingakhalire, ngati muganiza kuti ndinu wowonda kwambiri, funsani dokotala. Mwinamwake mungangofunikira kuvomereza maonekedwe anu—ndipo mwinamwake ngakhale kuphunzira kukonda—maonekedwe anu.
[Chithunzi patsamba 25]
Ambiri amaganiza kuti ngonenepa kwambiri chifukwa sali ndi maonekedwe a thupi ofanana ndi a anthu amene amasonyezedwa posatsa malonda m’magazini