Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 9/8 tsamba 10-13
  • Malangizo Ofunika a Kuyamwitsa Bere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malangizo Ofunika a Kuyamwitsa Bere
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Khanda Lisanafike
  • Masiku Oyambirira
  • Pamene Muyenera Kumletsa Kuyamwa
  • Umboni wa Mlengi Wachikondi
  • Zimene Mungachite Mwana Akabadwa
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Zimene Makanda Amafunikira Ndiponso Zimene Amafuna
    Galamukani!—2004
  • Kodi Zinthu Zimasintha Bwanji M’banja Mukabadwa Mwana?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Pagona Vutoli Mpati, Nanga Kuipa Kwake N’kotani?
    Galamukani!—2003
Galamukani!—1994
g94 9/8 tsamba 10-13

Malangizo Ofunika a Kuyamwitsa Bere

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! MU NIGERIA

Ngati inu, mofanana ndi amayi ambiri, mwasankha kuyamwitsa bere khanda lanu, ndiye kuti mwasankha kugwiritsira ntchito kakonzedwe koperekedwa mwachikondi ndi Mlengi wa mtundu wa anthu. Mkaka umene thupi lanu limatulutsa udzapereka zakudya zonse zofunikira kwa khanda lanu, zochirikiza thanzi labwino ndi kakulidwe kake. Udzathandizanso kutetezera khanda lanu ku matenda ofala. Pokhala ndi chifukwa chabwino,

WHO (World Health Organization) ikunena kuti: “[Mkaka wa kubere] ndiwo chakudya chabwino koposa zonse zimene mwana angapeze. Zoloŵa m’malo zina zonse, kuphatikizapo mkaka wa ng’ombe, mkaka waufa wosungunula, ndi mitundu ya phala la makanda, zimaposedwa.”

Kuyamwitsa bere kumadzetsa mapindu kwa inunso. Sipamakhala kutsuka mabotolo kapena kupha tizilombo m’botolo ndipo sipamakhala maulendo opita ku khichini pakati pausiku kukakonzera khanda lanu chakudya. Kuyamwitsa bere kudzakupindulitsaninso mwakuthupi, popeza kuti kudzakuthandizani kutaya kulemera kumene munakhala nako m’nthaŵi ya pathupi ndipo kudzathandiza chibaliro chanu kubwerera paukulu wake wa nthaŵi zonse. Ndipo kufufuza kumasonyeza kuti akazi amene amayamwitsa bere ana awo sali othekera kwambiri kudwala kansa ya maŵere.

“Pafupifupi mayi aliyense akhoza kuyamwitsa bere khanda lake,” ikutsimikizira motero United Nations Children’s Fund. Chotero, mwachionekere inunso mukhoza kutero. Komabe, mungapeze kuti kuyamwitsa bere sikuli kopepuka monga momwe munaganizira, makamaka ngati mukuyesa kukuchita kwanthaŵi yoyamba. Zili choncho chifukwa chakuti kuyamwitsa bere, ngakhale kuti kuli kwachibadwa, sikumangochitika mwachibadwa; ndiko luso limene mufunikira kuphunzira. Mungapeze kuti kumakutengerani masiku angapo kapena ngakhale milungu ingapo kuti inu ndi khanda lanu mukhazikitse njira yatsiku ndi tsiku yabwino ndi yosangalatsa yochitira zimenezo.

Khanda Lisanafike

Ngati simunayamwitsepo mwana mwachipambano, lankhulani ndi amayi amene atero. Iwo angakuthandizeni kupeŵa kapena kuthetsa zovuta. Angathandizenso kukulitsa chidaliro chanu cha luso lanu la kuyamwitsa khanda lanu bwino lomwe.

Panthaŵi ya kukhala ndi pathupi ndi pambuyo pake, kuli kofunika kuti muzipumula mokwanira. Ndiponso, tsimikizirani kuti mumadya chakudya chokwanira. Breastfeeding, chofalitsidwa cha WHO, chikunena kuti: “Kudya mosakwanira pathupi pasanakhale kapena m’nthaŵi yapathupi kungachititse khandalo kusakula bwino m’chibaliro. Kungachititsenso mayiyo kusakhoza kusunga mafuta okwanira m’thupi odzapangira mkaka wokwanira pambuyo pake. Chotero, m’nthaŵi yonseyo ya pathupi ndi yoyamwitsa, mayi amafunikira kudya zakudya zopatsa thanzi za mitundu yosiyanasiyana.”

Kusamalira maŵere kulinso kofunika. Mkati mwa miyezi yotsirizira ya pathupi, tsukani maŵere anu posamba, koma musaikeko sopo. Maselo a mu areola (mbali yakuda m’mphepete mwa nkhumbu) amatulutsa mafuta akupha tizilombo amene amachititsa nkhumbu kukhala zonyoŵa ndipo amazitetezera ku matenda. Sopo ikhoza kuumika nkhumbu ndi kuchotsa kapena kusukulutsa mafutawo. Ngati maŵere anu auma kapena anyerenyetsa, mungaikeko mafuta ofeŵetsa kapena lotion. Koma samalani kuti musawapake kunkhumbu kapena m’mbali yakuda m’mphepete mwake.

Kale madokotala analimbikitsa kuti amayi “azilimbitsa” nkhumbu zawo m’nthaŵi ya pathupi mwa kusisita mwamphamvu. Ngakhale kuti zimenezi zinali zofunikira kaamba ka kuletsa zilonda za kunkhumbu panthaŵi ya kuyamwitsa, kufufuza kumasonyeza kuti machitidwewo sali othandiza kwenikweni. Zilondazo kaŵirikaŵiri zimachititsidwa ndi kusaika khandalo pamalo abwino poyamwitsa bere.

Ukulu wa maŵere ndi mpangidwe wake sindizo zimakhozetsa kuyamwitsa kwabwino, koma khandalo silingathe kuvumata bwino nkhumbu yobwerera mkati kapena yophwatalala. Mungadziyese nokha mwa kutsinya pang’onopang’ono kumbuyo pang’ono kwa nkhumbu iliyonse ndi chala chanu chamanthu ndi chamkombaphala kuchititsa kuti nkhumbuzo zituluke kunja. Ngati sizituluka, onanani ndi dokotala wanu. Mwinamwake angakuuzeni kumavala breast shell, chovala kumaŵere panthaŵi ya pathupi kapena pambuyo poyamwitsa. Zovala kumaŵere zimenezi kaŵirikaŵiri zimawongolera mpangidwe wa nkhumbu zophwatalala kapena zobwerera mkati.

Masiku Oyambirira

Kuli bwino kwa inu kuyamba kuyamwitsa bere khanda lanu mkati mwa ola limodzi litabadwa. Ena angalingalire kuti pasanapite nthaŵi pambuyo pa ntchito yonseyo ya kuona mwana, onse aŵiri mayi ndi khanda amakhala otopa kwambiri moti sangakhoze kuyamba kugwirana. Koma kaŵirikaŵiri mayi amatsitsimulidwa ndi chochitikacho, ndipo khanda, pambuyo pa mphindi zingapo za kuzoloŵera moyo wa kunja kwa mimba, limafuna kusangalala ndi bere.

Amayi atsopano angayamwitse ana awo obadwa kumene mkaka wachikasu kapena woonekera monga madzi wotchedwa colostrum. “Golidi wamadzi” ameneyu ngwaphindu kwambiri kwa khanda. Uwo uli ndi zinthu zimene zimalimbana ndi tizilombo ta bacteria. Ulinso ndi maprotini ochuluka ndi mlingo waung’ono wa shuga ndi mafuta, zimene zimaukhalitsa chakudya choyenera m’masiku oŵerengeka oyambirira a moyo. Pokhapo ngati pali vuto la matenda, khandalo silidzafunikiranso chakudya kapena chakumwa china chilichonse. Kuwonjezerapo kuyamwitsa botolo kungachititse khanda kumakana kuyamwa bere, popeza kuti kumakhala kosavuta kuyamwa botolo.

Amayi ambiri amayamba kutulutsa mkaka wopanda colostrum pambuyo pa masiku aŵiri kufikira asanu mwana atabadwa. Mwazi wowonjezereka wopita kumaŵere panthaŵi imeneyi ungakulitse maŵere anu ndi kuwachititsa kukhala ofeŵa. Zimenezi nzachibadwa. Kaŵirikaŵiri kuyamwitsa bere kudzathetsa vutolo. Komabe, nthaŵi zina maŵere otupa amachititsa nkhumbu kuphwatalala. Popeza kuti zimenezi zimakukhalitsa kovuta kwa khanda kuyamwa, mungafunikire kutulutsa mkaka mwa kugwiritsira ntchito manja. Mungachite zimenezi mwa kusisita bere lililonse ndi manja onse aŵiri, kuyambira mmunsi mwake kupita kunkhumbu.

Simukhoza kudziŵa kuchuluka kwa mkaka umene khanda lanu limayamwa kubere lanu, koma musade nkhaŵa—thupi lanu lili lokhoza kupereka zonse zimene khanda lanu limafunikira, ngakhale ngati ali amapasa! Pamene muyamwitsa kwambiri, ndi pamenenso mudzatulutsa mkaka wochuluka. Ichi ndi chimodzi cha zifukwa zimene simuyenera kuwonjezera pa mkaka wa bere zakumwa zina za m’botolo, zonga ngati mkaka waufa wosungunula kapena mkaka wa ng’ombe. Ngati mutero, khanda lanu silidzayamwa kwambiri kwa inu. Zimenezo zidzakuchititsaninso kusatulutsa mkaka wokwanira.

“Makanda obadwa m’miyezi yokwanira sali kwenikweni osakhoza kuchita kanthu monga momwe kwalingaliridwira ndipo akhoza kulinganiza chakudya chawo choyenerera iwo ndi matupi a amayi awo, malinga ngati anthu ena awalola kuchita zimenezo,” akulemba motero Gabrielle Palmer mu The Politics of Breastfeeding. Lamulo lotsogolera ndilo la kugaŵira malinga ndi kufunidwa kwa chinthu—pamene khanda lanu lifuna chakudya (kaŵirikaŵiri mwa kulira), inu mumachigaŵira. Poyambirira, kufunako kudzakhalapo pambuyo pa maola aŵiri kapena atatu alionse. Muyenera kulola khanda lanu kuyamwa maŵere onse aŵiri panthaŵi iliyonse pamene liyamwa. Makanda ochuluka amatenga mphindi 20 kufikira 40 kuti amalize kudya, ngakhale kuti makanda ena amakonda kudya mwapang’onopang’ono, molekezalekeza. Odya pang’onopang’ono oterowo angatenge mphindi 60 kuti amalize chakudya chawo. Kaŵirikaŵiri, mwana wanu amadya zokwanira ngati amayamwa kwanthaŵi zosachepera pa zisanu ndi zitatu m’maola 24, ngati mungamumve kuti akumeza, ndipo ngati amanyoŵetsa mateŵera asanu ndi atatu kapena kuposerapo patsiku pambuyo pa tsiku lachisanu.

Luso lofunika koposa limene muyenera kuphunzira poyamwitsa bere ndilo kagwiridwe koyenera ka mwana wanu pamene ali kubere. Kumuika pamalo osayenera kungachititse khanda lanu kusayamwa mkaka wokwanira. Makanda ena amakana ngakhale kuyamwa.

Kuika mwana pamalo osayenera kungachititse vuto lina lofala: nkhumbu zong’ambika kapena zochita zilonda. Breastfeeding Source Book limati: “Zilonda za kunkhumbu zimachititsidwa ndi zinthu zingapo, koma chachikulu ndicho mmene khandalo ‘limagwirira kubere,’ ndipo zimenezonso zimadalira kwambiri pa malo amene mutu wake uli kulinga ku berelo. Kuti likhale pamalo abwino, khanda lanu liyenera kukhala pafupi, mutu wake utakhala pakati mpakati (osapenya kumwamba, pansi kapena kumbali), ndipo akumayang’anizana mwachindunji ndi nkhumbu kotero kuti asaikokere kumbali imodzi.”

Chofunikira nchakuti milomo ya mwana ivumate bwino bere, nkhumbu italoŵa m’kamwa mwake kwa masentimita pafupifupi atatu. Mudzadziŵa kuti malowo alibwino ngati thupi lonse la khanda lanu lipenya kwa inu, ngati akoka mkaka motalikirapo, ngati ali womasuka ndi wosangalala, ndipo ngati simumva nkhumbu kupweteka.

Pamene Muyenera Kumletsa Kuyamwa

Pambuyo pa milungu yoŵerengeka yoyambirira, nonse aŵiri inuyo ndi khanda lanu mudzakhala mutadziŵana ndipo mwinamwake mutakhazikitsa njira yabwino ndi yosangalatsa yochitira zinthu. Kwa miyezi inayi mpaka isanu ndi umodzi yotsatira, khanda lanu silidzafunikira chakudya kapena chakumwa china kuwonjezera pa mkaka wa kubere. Pambuyo pa nthaŵi imeneyo muyenera mwapang’onopang’ono kumpatsa zakudya zina, zonga ndiwo zamasamba zopotedwa, zakudya za dzinthu, kapena zipatso. Komabe, kufikira khanda lanu litafika pamsinkhu wa miyezi isanu ndi inayi kapena khumi, chakudya chake chachikulu chidzakhalabe mkaka wochokera kwa inu; motero ndibwino nthaŵi zonse kuyamwitsa bere mwana wanu musanampatse chakudya cholimba.

Kodi muyenera kupitiriza kuyamwitsa bere kwa utali wotani? Kwa utali uliwonse wothekera, imatero WHO. Amayi ambiri amapitiriza kuyamwitsa kufikira mkati kwambiri mwa chaka chachiŵiri, akumasamalira za ana awo osati masiku. Buku lakuti Mothering Your Nursing Toddler limanena kuti: “Sikovuta kuona kufunika kwa kupitiriza kuyamwitsa ana athu—chisangalalo chawo poyamwa ndi kuvutika kwawo pamene amanidwa. Chifukwa chapafupi koma chofunika kwambiri chopitirizira kuyamwitsa ndicho kukondweretsa mwana.”

Umboni wa Mlengi Wachikondi

Pamene muyamwitsa bere khanda lanu, mwinamwake pakati pausiku pamene ena onse m’banja ali mtulo, lingalirani za Mlengi wa kakonzedwe kameneka. Ngakhale ngati simumvetsetsa choloŵane wa kachitidwe amene amachitheketsa, chozizwitsa cha kuyamwitsa bere chidzakuthandizani kuona nzeru ndi chikondi cha Mlengi wathu.

Talingalirani ponena za icho—palibe chakudya chabwinopo kwa makanda choposa mkaka wa amayi. Uwo umapereka zakudya ndi zakumwa zonse zofunikira za khanda mkati mwa miyezi yoyambirira ya moyo. Panthaŵi imodzimodziyo, uwo uli mankhwala odabwitsa amene amatetezera ku matenda. Uli wachisungiko, waukhondo, wosafuna kuphika kulikonse, ndipo wosawonongetsa ndalama iliyonse. Uwo umapezeka kwa mayi aliyense, ndipo umatuluka wochulukirapo pamene mwanayo akukula.

Ndipo talingalirani za mfundo yakuti kuyamwitsa bere kuli chochitika chosangalatsa kwa onse aŵiri mayi ndi mwana. Kupatsa chakudya, kukhudzana kwa kamwa ndi thupi, ndi kufunditsana ndi matupi poyamwitsa bere zonsezo zimathandiza kulimbitsa chomangira cha chikondi ndi kuyandikana pakati pa mayi ndi mwana.

Ndithudi, Mlengi wa kakonzedwe kodabwitsa kameneka ayenera kutamandidwa koposa. Mosakayikira konse, inu mudzabwereza mawu a wamasalmo Davide, yemwe analemba kuti: “Ndikuyamikani [Yehova] chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwiza; ntchito zanu nzodabwiza; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.”—Salmo 139:14.

[Bokosi patsamba 12]

Amuna, Khalani Ochirikiza

• Lolani mkazi wanu kudziŵa kuti mukuvomereza kuyamwitsa bere kwake. Mlimbikitseni ndi kumchirikiza mwachikondi.

• Thandizani mkazi wanu kuti azidya zakudya zonse zopatsa thanzi m’nthaŵi ya pathupi ndi pamene khanda likuyamwa.

• Onani kuti akupumula mokwanira. Mkazi wotopa angakhale ndi vuto la kusatulutsa mkaka wokwanira. Kodi mungathandize kuchepetsa ntchito zake mwa kusamalira ana ena kapena kuthandiza ntchito zapanyumba?

• Ngati mkazi wanu amapumula ndi kusangalala, mkaka wake udzatuluka bwino. Mchititseni kukhala wosangalala monga momwe mungakhozere. Tcherani khutu ku mavuto ake, ndipo thandizani kuwathetsa.

[Bokosi patsamba 13]

Kuyerekezera Bere ndi Botolo

“Mkaka wa kubere uli wopatsa thanzi kwambiri, waukhondo kwambiri, umatetezera makanda ku matenda ofala, ndipo umachepetsa upandu wa mayi wa kudwala kansa ya maŵere ndi ya chimake cha dzira. Mkaka wogula wa ana, kuwonjezera pa kukwera mtengo, kaŵirikaŵiri umasukulutsidwa mopambanitsa ndi madzi oipa ndipo umamwetsedwa kwa ana m’mabotolo oyamwitsira osaphedwamo tizilombo. M’zitaganya zosauka, kusiyana kuli kwakukulu kwambiri kwakuti pafupifupi miyoyo ya ana 1 miliyoni ikhoza kupulumutsidwa chaka chilichonse ngati amayi a dziko lonse angabwerere ku kuyamwitsa bere lokhalokha kwa miyezi inayi mpaka isanu ndi umodzi yoyambirira.”—The State of the World’s Children 1993, chofalitsidwa cha United Nations Children’s Fund.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena