Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 12/8 tsamba 30-31
  • Kodi Mulungu Amapereka Mphotho?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Amapereka Mphotho?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mphotho Zili Ntchito za Chikondi
  • Mphotho Zalero ndi Zamtsogolo
  • Khalani ndi Chithunzi cha Mphothoyo m’Maganizo
  • Yehova Amapereka Mphoto kwa Anthu Omufunafuna ndi Mtima Wonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • “Amapereka Mphoto kwa Anthu Omufunafuna Ndi Mtima Wonse”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Anthu Onse Abwino Amapita Kumwamba?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Yehova Ndi “Wobwezera Mphoto Iwo Akum’funa Iye”
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 12/8 tsamba 30-31

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mulungu Amapereka Mphotho?

INDE, amatero. Pamenepa, kodi ndi dyera kutumikira Mulungu ndi chiyembekezo cha kupatsidwa mphotho? Iyayi, pakuti iye mwiniyo amaikira atumiki ake okhulupirika mphotho. Kwenikweni, pokhala Mulungu wachilungamo ndi chikondi, Yehova amadziikira thayo la kupereka mphotho kwa amene amamtumikira. Mbali ya Mawu ake pa Ahebri 11:6 imati: “Munthu amene ayandikira kwa Mulungu ayenera kukhala ndi chikhulupiriro pa zinthu ziŵiri, choyamba kuti Mulungu aliko ndipo chachiŵiri kuti Mulungu amapereka mphotho kwa amene amamfunafuna.”—Phillips.

Kusonyeza chikhulupiriro chenicheni mwa Mulungu kumachititsa munthu kukhala naye pa ubwenzi, ndipo ubwenzi umenewu umadzetsa mphotho. Mulungu amadalitsa amene amafunafuna chiyanjo chake mwakhama.

Mphotho Zili Ntchito za Chikondi

Yehova amafuna kuti tidziŵe kuti iye ali Mulungu amene amapereka mphotho kwa iwo omkonda. Mwachitsanzo, makolo amene amasamala amafunafuna njira zoperekera mphotho kwa mwana wawo amene mofunitsitsa amachita ntchito zapanyumba chifukwa cha kukonda kwake makolo. Makolo angapereke zambiri m’malo mwa zofunika za moyo zokha, akumafupa mwana wawo ndi mphatso yapadera. Nthaŵi zina mphatsoyo ingakhale ndalama zokaika ku banki kaamba ka chithandizo cha mtsogolo cha mwanayo. Chotero, Mulungu sali ngati anthu amene samayamikira kapena kusamala awo amene amachita zinthu chifukwa cha chikondi kapena kukhulupirika. Yehova ali wokoma mtima ndipo amayandikira kwa mabwenzi ake. Ngati musungabe chikhulupiriro chanu mwa iye, ‘sadzakusiyani konse, kungakhale kukutayani.’—Ahebri 13:5.

Mulungu amayamikira ndipo amayanja onse amene amachita ngakhale utumiki wochepa kwambiri kwa iye, akumawapatsa mipata yowonjezereka ya kumdziŵa. Mawu a Yesu pa Mateyu 10:40-42 amasonyeza mfundo imeneyi motere: “Iye wakulandira inu, andilandira Ine, ndi wakulandira Ine, amlandira Iye amene ananditumiza Ine. Iye wakulandira mneneri, pa dzina la mneneri, adzalandira mphotho ya mneneri; ndipo wakulandira munthu wolungama, pa dzina la munthu wolungama, adzalandira mphotho ya munthu wolungama. Ndipo amene aliyense adzamwetsa mmodzi wa aang’ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.”

Yesu anatumizidwa ndi Atate wake, Yehova. Chifukwa chake, munthu amene alandira bwino ophunzira a Kristu—akhale aneneri, anthu olungama, kapena wamng’ono—amalandira Kristu ndi Mulungu yemwe, amene anatumiza Kristu. Ndithudi, munthuyo adzadalitsidwa; sadzakhala wopanda kulandira mphotho. Nkhokwe yake ya chuma chauzimu idzadzala kwambiri. Chifukwa? Chifukwa chakuti Yehova amakumbukira ngakhale utumiki wochepa kwambiri wochitidwa pochirikiza Ufumu wake, ndipo ntchitoyo sidzakhala yopanda mphotho.—Ahebri 6:10.

Nkosangalatsa kuti Petro, wophunzira wa Yesu, anafunsa Yesu molunjika ngati iye ndi atumwi ena akalandira mphotho: “Onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata Inu; nanga tsono tidzakhala ndi chiyani?” (Mateyu 19:27) Yesu sanaone funso limenelo kukhala losayenera koma anapereka yankho labwino, akumati: “Onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amayi, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzaloŵa moyo wosatha.”—Mateyu 19:29.

Mphotho Zalero ndi Zamtsogolo

Yankho limene Yesu anapereka limasonyeza kuti otsatira ake amalandira mphotho ponse paŵiri tsopano ndi mtsogolo. Mphotho ina yalero ndiyo kukhala kwawo mbali ya banja lomakula la mitundu yonse la abale ndi alongo auzimu. Pamene kuli kwakuti matchalitchi a Dziko Lachikristu akubuula ndi kucheperachepera kwa ziŵalo zawo ndi kusoŵa kwake chichirikizo, nyumba zosonkhanira za Mboni za Yehova zikusefukira mophiphiritsira. Mboni zatsopano zikwi mazana ambiri zikubatizidwa chaka ndi chaka.

Mphotho inanso ndiyo mtendere wamaganizo ndi chikhutiro ndi chimwemwe zimene ubwenzi ndi Mulungu ndi chidziŵitso chonena za iye zimadzetsa. Inde, “chipembedzo pamodzi ndi [kukhutira ndi zimene tili nazo, NW]” chipindulitsa kwambiri. (1 Timoteo 6:6) Munthu amasonyezadi mkhalidwe wamaganizo wachimwemwe pamene akhoza kunena monga momwe mtumwi Paulo ananenera kuti: “Ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo.”—Afilipi 4:11.

Paulo atatsala pang’ono kufa, analemba za mphotho ya mtsogolo ya “kagulu ka nkhosa” ka otsatira a Yesu odzozedwa—mphotho ya chiukiriro cha moyo wakumwamba kuti: “Chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ake.”—Luka 12:32; 2 Timoteo 4:7, 8.

Otsatira a Yesu mamiliyoni ambiri amene ali ‘nkhosa zake zina’ akuyembekezera mphotho yamtsogolo ya moyo wosatha padziko lapansi losandulizidwa kukhala paradaiso. (Yohane 10:16) Ndipo Yesu analonjeza kuti otsatira ake amene alikufa ‘adzabwezeredwa mphotho pa kuuka kwa olungama.’—Luka 14:14.

Khalani ndi Chithunzi cha Mphothoyo m’Maganizo

Kuli koyenera kuyesayesa kukhala ndi chithunzi cha madalitso otero m’maganizo, ngakhale kuti palibe amene adziŵa kwenikweni mmene madalitsowo adzakhalira. Kodi simumakondwera kumva zimene Yesaya 25:8 amanena kuti: “Iye wameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse”? Yesayesani kuona mwa maganizo zimene mawu a Yesaya 32:17 amanena: “Ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika ku nthaŵi zonse.” Inde, anthu onse adzakhala akugwira ntchito pamodzi mwaubwenzi woona. (Yesaya 65:21-25) Ngakhale lerolino, pamakhala nyumba ndi zinthu zabwino kwambiri chifukwa cha ntchito yakhama. Chifukwa chake, m’dziko latsopano la Mulungu, anthu athanzi m’mikhalidwe yangwiro adzakhoza kupanga zilizonse zofunikira kuchititsa moyo kukhala wosangalatsa.—Salmo 37:4.

Mphotho zimene Mulungu amatipatsa sizili chifukwa cha utumiki uliwonse woyenerera mphotho umene timachita koma zimakhala mphatso yosonkhezeredwa ndi chikondi chake pa ife mosasamala kanthu za mkhalidwe wathu wauchimo wa choloŵa. (Aroma 5:8-10) Komabe, pali kugwirizana pakati pa mphotho yoyembekezeredwayo ndi khalidwe lathu. Tiyenera kufunafuna Yehova mwakhama ndi chikhulupiriro cholimba ndi chipiriro. (Ahebri 10:35-39) M’mawu ena, “chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ayi; podziŵa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya choloŵa.” Inde, iye amaperekadi mphotho.—Akolose 3:23, 24.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena