Tchalitchi cha Katolika mu Afirika
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU ITALY
TCHALITCHI cha Katolika chili ndi anthu mamiliyoni makumi ambiri mu Afirika, ndipo mavuto ake ngaakulu kumeneko. Kuchiyambiyambi kwa chaka chatha atsogoleri atchalitchicho oposa 300 anakumana ku Vatican ku Rome kuti akambitsirane za ena a mavuto ameneŵa mkati mwa sinodi yapadera ya mwezi umodzi.
Potsegulira magawo ake monga momwe kwasimbidwira mu L’Osservatore Romano papa anati: “Lero kwanthaŵi yoyamba Sinodi ya Tchalitchi cha mu Afirika yophatikizapo kontinenti yonseyo ikuchitika. . . . Afirika yense ali muno mu Tchalitchi cha St Peter lero. Bishopu wa Rome akulonjera Afirika ndi chimwemwe chachikulu.”
Nkhondo ya Mafuko
Monga momwe ambiri akudziŵira, mavuto a Tchalitchi cha Katolika ngaakuludi makamaka m’maiko a mu Afirika a Burundi ndi Rwanda, amene kwakukulukulu ali Achikatolika. Nkhondo ya mafuko kumeneko inakhala nkhani ya padziko lonse m’ngululu yathayi pamene zikwi mazana ambiri anaphedwa ndi anansi awo. Mboni ina yodzionera ndi maso inasimba kuti: “Tinaona akazi obereka ana aang’ono kumsana akumapha ena. Tinaona ana akumapha ana ena.”
National Catholic Reporter inasimba za kuvutika maganizo kwa atsogoleri a Katolika. Iyo inati papa “anamva ‘ululu waukulu’ ndi malipoti a kumenyana kwatsopano m’dziko laling’ono la mu Afirika [la Burundi], limene chiŵerengero cha anthu ake kwakukulukulu chili cha Akatolika.”
Kupululutsana mu Rwanda kunalidi kowononga utsogoleri wa Akatolika. “Papa Atsutsa Kuphana kwa Mafuko m’Dziko Lomwe 70% ndi Akatolika,” unalengeza motero mutu wina m’nyuzipepala imodzimodziyo. Nkhaniyo inati: “Kumenyana kwa m’dziko la mu Afirika kukuloŵetsamo ‘kupulula mtundu wonse kwenikweni kumene, mwatsoka, ngakhale Akatolika ali nako mlandu,’ anatero papa.”
Popeza kuti nkhanza za ku Rwanda zinali kuchitidwa panthaŵi yeniyeniyo ya sinodi ya Katolika yopanga mbiri yochitikira ku Rome, mwachionekere mabishopuwo anasumika maganizo pa mkhalidwe wa ku Rwanda. National Catholic Reporter inati: “Nkhondo ya ku Rwanda ikuvumbula kanthu kena kochenjeza: Chiphunzitso Chachikristu sichinazike mizu mokwanira mu Afirika kuti chithetse kusankhana mafuko.”
Poona nkhaŵa ya mabishopu osonkhanawo, National Catholic Reporter inapitiriza kunena kuti: “Nkhani imeneyi [ya kusankhana mafuko] inakhudzidwa ndi Albert Kanene Obiefuna, bishopu wa Awka, ku Nigeria, pamene anali kulankhula pa sinodipo.” M’kulankhula kwakeko, Obiefuna anafotokoza kuti: “Moyo weniweni wa munthu wa mu Afirika uli wa m’banja ndiponso moyo wake Wachikristu ngwozikidwa pa miyambo ya fuko lake.”
Ndiyeno, mosakayikira akumalingalira za Rwanda, Obiefuna anapitiriza kulankhula kwakeko pasinodi kuti: “Kulingalira kumeneku kuli kowanda kwakuti pakati pa anthu a mu Afirika pali mwambi wakuti pamene zinthu zifika povuta, lingaliro Lachikristu la Tchalitchi monga banja sindilo limene limapambana koma m’malo mwake mwambi wakuti ‘mwazi uli wochindikala kuposa madzi.’ Ndipo pano mwa kutchula madzi munthu angalingalire za madzi a Ubatizo mwa amene munthu amabadwira m’banja la Tchalitchi. Ubale wamwazi ngwofunika kwambiri kwa munthu wa mu Afirika amene wakhala Mkristu.”
Motero bishopuyo anavomereza kuti mu Afirika chipembedzo cha Katolika chalephera kupanga ubale Wachikristu umene okhulupirira ake amakondanadi monga momwe Yesu Kristu anaphunzitsira kuti ayenera kutero. (Yohane 13:35) M’malo mwake, “ubale wamwazi ngwofunika kwambiri” kwa Akatolika a mu Afirika. Zimenezi zasonkhezera udani wa mafuko pakati pawo mosalingalira chilichonse. Monga momwe papa anavomerezera, Akatolika mu Afirika ayenera kukhala ndi mlandu wa nkhanza zina zoipitsitsa zaposachedwapa.
Kukhalapo Kwake Kukunenedwa Kukhala Kuli Pachiswe
Mabishopu a ku Afirika pa sinodipo anafotokoza za mantha awo ponena za kukhalapo kwa Chikatolika mu Afirika. “Ngati tikufuna kuti Tchalitchi chipitirize kukhalabe m’dziko lakwathu,” anatero Bonifatius Haushiku, bishopu wa ku Namibia, “tiyenera kulingalira mosamalitsa kwambiri nkhani ya inculturation.”
Pofotokoza malingaliro amodzimodziwo, Adista, woimira atolankhani Achikatolika mu Italy anati: “Kulankhula za ‘inculturation’ ya Uthenga Wabwino mu Afirika kumatanthauza kulankhula za chiyembekezo chenicheni cha Tchalitchi cha Katolika mu kontinenti imeneyo, za mipata yake ya kupitiriza kukhalako kapena kusakhalako.”
Kodi mabishopuwo akutanthauzanji ndi liwulo “inculturation”?
Tchalitchi ndi “Inculturation”
John M. Waliggo anafotokoza kuti “kutengera ndilo liwu limene lakhala likugwiritsiridwa ntchito kwanthaŵi yaitali kusonyeza mkhalidwe wofananawo.” Kunena mosavuta, mawu akuti “inculturation” amatanthauza kuloŵetsa miyambo ndi zikhulupiriro za zipembedzo za mafuko m’madzoma ndi m’kulambira Kwachikatolika, zikumachititsa madzoma, zinthu, majesichala, ndi malo akale kukhala ndi dzina latsopano ndi tanthauzo latsopano.
Inculturation imalola anthu a mu Afirika kukhala Akatolika abwino komabe omamatira pamachitachita, madzoma, ndi zikhulupiriro za zipembedzo zawo za mafuko. Kodi payenera kukhala choletsa chilichonse? Mwachitsanzo, nyuzipepala ina Yachitaliyana La Repubblica, inafunsa kuti: “Kodi sizoona kuti ku Ulaya Krisimasi inagwirizanitsidwa ndi phwando la Solis Invicti, limene limachitika pa December 25?”
Ndithudi, monga momwe Josef Kadinala Tomko, kadinala wa Congregation for the Evangelization of Peoples, ananenera: “Tchalitchi cha amishonale chinayamba kuchita ntchito ya inculturation kale lomwe liwulo lisanayambe kugwiritsiridwa ntchito.” Phwando la Krisimasi limasonyeza nkhaniyo bwino lomwe, monga momwe La Repubblica inasonyezera. Poyambirira ilo linali phwando lachikunja. “Deti la December 25 silimagwirizana ndi kubadwa kwa Kristu,” ikuvomereza motero New Catholic Encyclopedia, “koma ndi phwando la Natalis Solis Invicti, phwando Lachiroma la dzuŵa panthaŵi ya solstice.”
Krisimasi yangokhala umodzi wa miyambo yambiri ya tchalitchi yogwirizanitsidwa ndi chikunja. Motero ndimo mmenenso kulili ndi ziphunzitso zonga Utatu, kusafa kwa moyo, ndi chizunzo chosatha cha miyoyo ya anthu pambuyo pa imfa. John Henry Kadinala Newman wa m’zaka za zana la 19 analemba kuti “olamulira a Tchalitchi kuyambira kalekale anali okonzekera, ngati pakabuka mkhalidwe wina, kutengera, kapena kutsanzira, kapena kuvomereza madzoma ndi miyambo yokhalako ya anthu.” Pondandalika machitachita ndi maholide ambiri, iye anati “zonsezo zinali ndi chiyambi chachikunja, ndipo zinayeretsedwa mwa kuloŵetsedwa kwake m’Tchalitchi.”
Pamene Akatolika aloŵa m’madera osakhala Achikristu, monga mbali zina za mu Afirika, kaŵirikaŵiri amapeza anthu amene ali kale ndi machitachita achipembedzo ndi zikhulupiriro zofanana ndi za tchalitchicho. Zimenezi zili chifukwa chakuti mkati mwa zaka mazana apitawo tchalitchicho chinatengera machitachita ndi ziphunzitso za anthu osakhala Akristu ndi kuziloŵetsa m’Chikatolika. Machitachita otero ndi ziphunzitso, Kadinala Newman anatero, “zinayeretsedwa mwa kuloŵetsedwa kwake m’Tchalitchi.”
Motero, pamene Papa John Paul II anachezera anthu osakhala Akristu mu Afirika chaka chatha, anagwidwa mawu mu L’Osservatore Romano kukhala akunena kuti: “Mu Cotonou [Benin, Afirika] ndinakumana ndi okhulupirira matsenga, ndipo mwa zimene analankhula kunali kwachionekere kuti mwanjira inayake iwo ali kale ndi kanthu kena m’maganizo mwawo, miyambo, zizindikiro ndi m’zikhoterero kofanana ndi zimene Tchalitchi chikufuna kuwapatsa. Akungoyembekezera nthaŵi yakuti winawake adze ndi kuwathandiza kusintha ndipo mwa Ubatizo akhale ndi moyo mogwirizana ndi chimene mwanjira inayake anali kuchidziŵa ndi kuchitsatira Ubatizo usanachitike.”
Kodi Muyenera Kuchitanji?
Kulephera kwa tchalitchi kuphunzitsa anthu a mu Afirika Chikristu choona ndi chosaipitsidwa kwakhala ndi zotulukapo zatsoka. Kusankhana mafuko kwapitiriza kukhalapo, monga momwe kukonda dziko la munthuwe kwachitira kulikonse, kukumachititsa Akatolika kuphana. Nchipongwe chotani nanga kwa Kristu! Baibulo limanena kuti kuphana kwambanda kotero kumasonyeza anthu kukhala “ana a mdyerekezi,” ndipo za oterowo Yesu anati: “Chokani kwa Ine, inu akuchita kusayeruzika.”—1 Yohane 3:10-12; Mateyu 7:23.
Pamenepa, kodi nchiyani chimene Akatolika oona mtima ayenera kuchita? Baibulo limalimbikitsa Akristu kukhala osamalitsa pa kusalolera molakwa machitachita alionse kapena zikhulupiriro zimene zingapangitse kulambira kwawo kukhala kodetsedwa m’maso mwa Mulungu. “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana,” Baibulo limatero. Kuti muyanjidwe ndi Mulungu, mufunikira ‘kupatuka pakati pawo ndi kusakhudza kanthu kosakonzeka m’maso mwa Mulungu.’—2 Akorinto 6:14-17.
[Chithunzi patsamba 20]
‘Nkhondo ya ku Rwanda ndiyo kupulula mtundu wonse kwenikweni kumene ngakhale Akatolika ali nako mlandu,’ anatero Papa
[Mawu a Chithunzi patsamba 18]
Chithunzi: Jerden Bouman/Sipa Press