Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 2/8 tsamba 10-13
  • Kodi Tsokalo Lidzatha Liti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tsokalo Lidzatha Liti?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chochititsa Chachikulu
  • Tsokalo Lidzatha Posachedwa
  • Kupindula Tsopano Lino
  • Thandizo Lochokera Kumwamba
  • Makolo Khalani Chitsanzo Chabwino kwa Ana Anu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Chitetezo m’Nyumba
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 2/8 tsamba 10-13

Kodi Tsokalo Lidzatha Liti?

KODI ndiliti pamene ana adzaleka kukhala anthu obedwa, ochitiridwa nkhanza, olimidwa pamsana, ndipo kaŵirikaŵiri oyambukiridwa moipa ndi ausinkhu wawo? Kodi kuperekedwa kwa lamulo ndi zilango zokakala kaamba ka upandu wochitidwa kwa ana zidzawatetezera? Kodi mautumiki a kupereka chakudya, nyumba, ndi maphunziro kwa anthu osauka angaletse nkhanza ndi kuthaŵa panyumbako? Kodi kuphunzitsa makolo amene amasamala ana awo maluso a kulankhulana kwabwinopo kudzathandiza makolowo kulimbana ndi zinyengo za chikondwerero zimene zimanyengerera ana awo kuloŵa m’mikhalidwe yowononga?

Ngakhale kuti njira zotero zingakhale zothandiza, anawo adzangokhalabe pamavuto ochuluka kufikira pamene chochititsa cha matsoka amenewo chichotsedwa. Malinga ndi kunena kwa wachichepere wina, kuyesayesa kulikonse m’kulimbana ndi vuto la ana othaŵa panyumba kumene sikumaletsa nkhanza kapena kusiyidwa panyumba mwachionekere sikungakhale kogwira mtima, popeza kuti chivulazo chachitidwa kale.

Chochititsa Chachikulu

Kodi nchiyani chimene chili choputira chachikulu cha mavuto onsewa? Kodi adzathetsedwa motani? Baibulo limafotokoza kuti banja likuukiridwa ndi zolengedwa zauzimu zosaoneka, Satana ndi ziwanda zake, amene amakondwera ndi nkhanza, kulimidwa pamsana mwa kugonedwa, ndi chilakolako choipa. (Genesis 6:1-6; Aefeso 6:12) Pamene Yesu anali padziko lapansi, ana anaukiridwa ndi ziwanda zimenezi. Mnyamata wina anazunzidwa mwa kumvimviniziridwa pansi ndi kuchita thovu ndi kugwetseredwa pamoto.—Marko 9:20-22.

Ngakhale kwa zaka mazana ambiri Yesu asanafike padziko lapansi, ziwanda zinasangalatsidwa ndi kuzunzidwa ndi kutenthedwa kwa ana aang’ono mpaka imfa operekedwa nsembe kwa milungu yonyansa yachikunja, yonga Baala, Kemosi, ndi Moleki. (1 Mafumu 11:7; 2 Mafumu 3:26, 27; Salmo 106:37, 38; Yeremiya 19:5; 32:35) Chotero, lerolino, m’dziko limene likukhala loluluzika mowonjezereka kwambiri, sikuyenera kukhala kodabwitsa kuti ziwanda zimalunjikitsa chiukiro pa ana kuti avutitsidwe ndi nthumwi zaumunthu zofuna kutero zimene zimanyazitsa, kuvulaza, ndi kupha ana. Ochita maupandu ankhanza otero kaŵirikaŵiri amadzaza m’maganizo mwawo ndi zithunzithunzi zaumaliseche, zimene zimasonkhezera zilakolako zawo zoipa.

Zitsenderezo zimene ziwanda zimapereka pa mtundu wa anthu zawonjezereka m’nthaŵi yathu, pakuti Baibulo limatcha nyengo ino ya mbiri kuti “masiku otsiriza” a dongosolo la zinthu loipa limene lilipoli. Linaneneratu kuti zimenezi zikakhala “nthaŵi zoŵaŵitsa.” Tsopano kuposa ndi kale lonse, chisonkhezero cha ziwanda chimachititsa anthu kusonyeza kululuzika kwa zolengedwa zauzimu zoipa zimenezi. Baibulo linaneneratu kuti anthu m’tsiku lathu akakhala aukali, osadziletsa, opanda chikondi chachibadwidwe, osakonda ubwino.—2 Timoteo 3:1-5, 13.

Zimenezo zimafotokoza bwino kwambiri za anthu aumbombo amene amapanga mafilimu, malekodi, magazini, ndi mabuku amene amatamanda chigololo, anamgoneka, kudzipha, mbanda, kugwirira chigololo, kugonana pachibale, ukapolo, ndi kuzunza. Kupyolera m’njira zimenezi ndi zina, ziwanda zachirikiza mkhalidwe, umene, monga mpweya woipa, waipitsa maganizo ndi mitima ya achichepere ndi achikulire omwe, ukumasukuluza makhalidwe abwino abanja ndi khalidwe labwino laumulungu.

Kuwonjezereka kwa kubedwa kwa ana, nkhanza, ndi kupha kuli mbali ya chizindikiro cha masiku otsiriza. Ndiponso, Baibulo linati ‘anthu adzakhala odzikonda okha, osayanjanitsika, osayera mtima, achiwembu.’ Chifukwa chake lerolino kaŵirikaŵiri zomangira zaukwati zimaduka mofulumira zitangopangidwa. Pamene zisudzulo zikuwonjezeka, mpamenenso kufwamba ana kochitidwa ndi kholo kukuwonjezeka. Ndipo pamene kumenya mwankhanza ndi kupha mnzawo wa muukwati yemwe ali naye kapena wakale kuwonjezeka, unyinji wa ochitiridwa nkhanza ake umakhala akazi. Motero, tikuona mbadwo wa ana amene makolo awo amawakakamiza kuthaŵa panyumba mwa kuwasiya ndi kuwachitira nkhanza. Ndiponso, nthaŵi yathu njodzazidwa ndi ana amene ali “osamvera akuwabala,” amene ali “aliuma,” ndi amene amasankha zothaŵa panyumba limodzi ndi ausinkhu wawo m’malo mwa kulemekeza makhalidwe aumulungu.—2 Timoteo 3:2-4.

Tsokalo Lidzatha Posachedwa

Komabe, chisonkhezero cha Satana ndi ziwanda zake chidzatha posachedwa. (Chivumbulutso 12:12) Ulosi wa Chivumbulutso 20:1-3 umanena kuti Mulungu adzachotsa Satana ndi ziwanda zake. Pambuyo pa zimenezo, Ufumu wakumwamba wa Mulungu, motsogoleredwa ndi Yesu Kristu, udzalamulira dziko lapansili m’chilungamo, ukumalamulira molungama ndi kupereka chisungiko kwa onse. (Salmo 72:7, 8; Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Madongosolo azamalonda aumbombo amene amatsendereza osauka ndi kulima pamsana anthu kaamba ka phindu adzakhala atapita, pakuti “dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake.” (1 Yohane 2:17) Awo onse amene amachita zoipa adzachotsedwa, monga momwe Miyambo 2:22 inaneneratu kuti: “Oipa adzalikhidwa m’dziko.”

Mika 4:4 amafotokoza kuti m’dziko latsopano la Mulungu mudzakhala chisungiko ndi mtendere kwa onse: “Sipadzakhala wakuwawopsa.” Kodi zimenezo nzotheka motani? Kupyolera mu lamulo lachifumu la chikondi. Lamulo lalikulu limenelo lidzalamulira maganizo ndi zochita zonse. Awo amene adzakhala ndi moyo panthaŵiyo adzakhala ataphunzira kusonyeza umunthu wa Yesu ndi wa Atate wake, Yehova Mulungu, popeza kuti ngati satero, sadzaloledwa kupitiriza kukhala ndi moyo. Mwa kudziveka iwo eni ndi ‘chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso,’ dyera lidzakhala litazulidwa m’khalidwe la anthu. (Akolose 3:12) Moyo udzakhala wodzala ndi chimwemwe; mabanja adzakhala odzazidwa ndi chikondi padziko lonse.

Yesaya 65:21-23 akulonjeza za chakudya chochuluka ndi nyumba zabwino kwa aliyense: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. . . . Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka.” Sipadzakhalanso nkhanza. Sipadzakhalanso kuvutika kwa ana kapena kwa makolo.

Kupindula Tsopano Lino

Ngakhale tsopano lino, m’nyengo yomaliza ya dongosolo ili loipa, kudziŵa Yehova ndi za chifuno chake cha kubwezeretsa dzikoli ku paradaiso kumadzetsa mapindu. Kwapereka chiyembekezo ndi chifukwa cha kukhala achimwemwe kwa achichepere ambiri ndi makolo, ngakhale ngati akhala ochitiridwa nkhanza a m’nthaŵi yathu. Mwachitsanzo, Tamara, wotchulidwa m’nkhani yathu yapitayo, akufotokoza zimene zinachitika m’moyo wake.

“Pamene ndinali ndi zaka 18, ndinakwatiwa ndipo ndinalekana ndi gulu la ‘mabwenzi,’ amene ena a iwo potsiriza pake anatsekeredwa m’ndende, kumwerekera mu anamgoneka, kapena mu uhule. Koma ndinali ndikali ndi mkhalidwe umodzimodziwo, chotero tinayamba kukangana ndi mwamuna wanga. Komabe, mwana wathu wamwamuna atangobadwa, kanthu kena kamene kanasinthiratu moyo wanga kanachitika. Ndinapeza Baibulo ndi kuyamba kuliŵerenga. Usiku wina ndinaŵerenga chaputala cha Miyambo chimene chimati ‘kupeza luntha kuli ngati kupeza chuma chobisika.’ (Miyambo 2:1-6) Ndisanakagone usiku umenewo, ndinapempherera luntha limenelo. Mmaŵa wotsatira, Mboni za Yehova zinaliza belu pakhomo panga. Ndinayamba kuphunzira nazo Baibulo, komano kugwiritsira ntchito zimene ndinali kuphunzira m’Baibulo kunanditengera nthaŵi. Potsirizira pake, ndinatsimikiza mtima kutsatira njira ya moyo Wachikristu ndipo ndinabatizidwa. Tsopano, pamodzi ndi mwamuna wanga, ndimathandiza ena kupeza mpumulo umene Mulungu amapereka.”

Inde, Tamara anapeza Magwero a mpumulo wonse, Yehova Mulungu. Iye ndiye Atate wakumwamba amene sadzasiya konse amene amammamatira. Salmo 27:10 limatiuza kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.”

Domingos, wotchulidwa pachiyambiyo, nayenso anapeza banja lenileni limene lampatsa chitonthozo, chilimbikitso, ndi chichirikizo. Iye akusimba kuti: “Tsiku lina ndinalandira kope la buku la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuruyo ndipo ndinadabwa kudziŵa kuti Mulungu anali ndi dzina, Yehova.a Ndinafika pa umodzi wa misonkhano ya Mboni za Yehova ndipo ndinazizwa kuona kuti kumeneko kunalibe kusankhana. Mbonizo zinayamba kuphunzira nane Baibulo mosasamala kanthu za kusavala bwino kwanga, mkhalidwe wosasamala, ndi kunyumwira aliyense. Pang’ono ndi pang’ono anandithandiza kuleka moyo wanga wakale. Anandithandiza kupeza ntchito. Potsirizira pake ndinathandizidwa kupita patsogolo kulinga ku ubatizo.”

Mipingo ya Mboni za Yehova ili ngati malo opulumukira kwa achichepere. Mbonizo nzachimwemwe kuthandiza aliyense amene akufuna kudziŵa za chiyembekezo chabwino kwambiri chimene chili mtsogolo. Chitonthozo chimene chimadza kwa awo amene amafuna unansi ndi Atate wawo wakumwamba nchachikulu, popeza kuti Mbonizo zimaphunzitsidwa kupereka chilangizo ndi njira zochokera m’Mawu a Mulungu Baibulo. Mboni ina ikufotokoza kuti achichepere afunikira kusonyezedwa kuti mkhalidwe wonyansa umene angakhale alimo ngwonyansanso kwa Yehova. Mboniyo ikuti: “Yehova safuna kuti ana achitiridwe nkhanza. Safuna kuti akhale achisoni. Komanso safuna kuti asinthanitse mtundu umodzi wankhanza ndi wina—nkhanza imene amapeza m’misewu. Iwo angathe kufikira anthu achikulire m’gulu la Yehova kuti awafotokozere za mavuto awo ndi kusonyezedwa mmene angawathetsere.”

Kwa ana amene mitima yawo ili yolabadira, Mawu a Mulungu amapereka chisonkhezero champhamvu cha kupeŵa msampha wa chitsenderezo cha ausinkhu wawo. Frances, msungwana wa zaka 17, anasonkhezeredwa ndi mnzake wa kusukulu kujomba kusukulu nthaŵi zambiri popanda kuuza makolo ake. Potsirizira pake, anathaŵa panyumba. Atavutitsa mitima ya makolo ake kwa maola ambiri, anabwerera. Pambuyo pake, Mboni ziŵiri za mumpingo wake zinafika. Izo zinatulukira kuti mkhalidwe wa pabanjapo sunali chochititsa vutolo, ndipo mwachikondi izo zinapereka uphungu. Zinafotokoza thayo Lachikristu la achichepere la kulemekeza makolo awo (Aefeso 6:1, 2); kufunika kwa kupeŵa kusaona mtima, popeza anajomba kusukulu popanda kuuza makolo ake (Aefeso 4:25); ndi kufunika kwa kupeŵa mayanjano oipa. (1 Akorinto 15:33) Iye anamvera uphunguwo.

Thandizo Lochokera Kumwamba

Nayenso Cheryl anapeza thandizo la Yehova polimbana ndi kufwambidwa kwa ana ake kochitidwa ndi yemwe kale anali mnzake wa muukwati.b Pamene anafunsidwa za chimene chinamthandiza kulimbana ndi mkhalidwe wochititsa mantha umenewu, iye anati: “Chinthu choyamba chimene ndinachita chinali kuŵerenga Masalmo, makamaka Salmo 35. Kunali kotonthoza kudziŵa kuti Yehova anali kuona chisalungamo chimene ndinakumana nacho.” Salmo 35:22, 23 limati: “Yehova, mudachipenya; musakhale chete: Ambuye, musakhale kutali ndi ine. Galamukani, ndipo khalani maso kundiweruzira mlandu wanga.”

Pambuyo pa zaka ziŵiri, limodzi ndi chichirikizo cha Yehova ndi thandizo la Mboni, Cheryl anayang’anizana ndi yemwe kale anali mwamuna wake, ndipo anakaona ana ake. Iye anali wokhoza kupereka mayankho otonthoza ponena za chifukwa chake zimenezi zinawachitikira ndi kuwatsimikizira kuti sanawataye. Chifukwa chakuti Cheryl anaphunzitsa ana ake kulemekeza Yehova, iye anali wokhoza kuwauza chidaliro chimene anali nacho mwa iwo. Iye anafotokoza kuti: “Ndidziŵa kuti ana anga amakonda Yehova, ndipo iye sadzalola chivulazo chanthaŵi yaitali kudza pa iwo.”

Ndimo mmenedi zinayendera. Ndi kuyesayesa kwakhama kwa Cheryl kuonana ndi akuluakulu a dipatimenti ya alendo oloŵa m’dziko ndi kudalira kwake Yehova kupyolera m’pemphero lakhama, anabwezeredwa ana ake. Cheryl anati: “Ndiyenera kunenadi kuti kunali mwa dzanja la Yehova lokha kuti abwezeredwe kwa ine.”

Nkofunika chotani nanga kuphunzitsa ana athu tsopano lino kudziŵa Yehova ndi kumlambira! Baibulo pa 1 Petro 3:12 limati maso a Yehova “ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo.” Yehova alidi pothaŵirapo pa ana athu. Dzina lake ndilo “linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.”—Miyambo 18:10.

Ngakhale kuti tikukhala m’nthaŵi zangozi kwambiri ndipo nthaŵi zonse sitimadziŵa zimene zidzagwera ana athu, makolo amene amalambira Yehova amadziŵa kuti palibe chivulazo chanthaŵi yonse chimene chidzadza pa ana awo amene ali okhulupirika. Iye walonjezadi kuukitsa akufa amene afa mu nthaŵi yathu ndi kuchotseratu zoŵaŵa ndi mavuto amene akanthidwa nawo.—Yesaya 65:17, 18; Yohane 5:28, 29.

Chiyembekezo cha dziko latsopano la Mulungu nchabwino kwambiri. Chabwinonso ndicho kudziŵa kuti posachedwapa Mulungu adzachotsa Satana ndi dongosolo lake loipa padziko lapansi. Chiwopsezo chilichonse kwa ana athu chidzakhala chitapita. Imodzi ya nyimbo zimene Mboni za Yehova zimaimba pa misonkhano yawo yampingo imafotokoza za dongosolo latsopano limenelo motere: “Pomveka nyimbo za ana,/padzakhalatu mtendere,/ndi akufa adzauka,/poyang’anabe pamphotho”!

Panthaŵi ina pamene mudzakumana ndi Mboni za Yehova, zipempheni kukusonyezani mmene nanunso mungadziŵire zambiri ponena za zisangalalo zimene zili patsogolopa m’dziko latsopano la Mulungu lolungama limene likudzalo. Zidzakhala zachimwemwe kukuthandizani kuona mmene Mawu a Mulungu angadzetsere chitonthozo chochuluka tsopano lino ndiponso pambuyo pake moyo wosatha.—Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:4, 5.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Onani nkhani ya patsamba 6.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

“Yehova safuna kuti ana achitiridwe nkhanza”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena