Patsogolopa—Nthaŵi Yabwino Koposa!
MALINGA ndi kunena kwa Baibulo, Mulungu anafuna kuti mtundu wa anthu udzakhale ndi moyo kosatha mu paradaiso wa pa dziko lonse lapansi. (Genesis 1:28; 2:8, 9) Mwachionekere, ife tapatuka motalikirana kwambiri ndi chifuno choyambirira cha Mulungu. Kodi nchiyani chimene chinachitika?
Anthu aŵiri oyamba sanamvere Mulungu, akumabweretsa kupanda ungwiro ndi imfa pa iwo eni ndi mbadwa zawo zonse. (Genesis 2:16, 17; 3:6, 7, 17-19; Aroma 6:23) Baibulo limalongosola kuti: “Tchimo linadza m’dziko ndi munthu mmodzi, ndipo tchimo lake linadzetsa imfa. Chotero, imfa yayambukira mtundu wonse wa munthu chifukwa chakuti aliyense wachimwa.”—Aroma 5:12, Today’s English Version.
Mosasamala kanthu za mkhalidwe umenewu, chifuno cha Mulungu nchosasintha. “Mawu anga ali ngati chipale ndi mvula imene imagwa kuchokera kumwamba kudzathirira dziko lapansi. Zimachititsa mmera kukula ndi kupatsa mbewu zobzala ndi chakudya. Momwemonso mawu anga amene ndilankhula . . . Adzachita zonse zimene ndinawatuma kukachita.” (Yesaya 55:10, 11, Today’s English Version.) Kodi nchiyani chimene Mulungu akulonjeza kutichitira?
MADALITSO MU UFUMU WA MULUNGU
Moyo Wosatha
“Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
“Sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.”—Chivumbulutso 21:4.
Chisungiko
“Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe.”—Salmo 37:10.
Ntchito Yokhutiritsa
“Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo—sizidzagwiritsidwa ntchito ndi munthu wina. Adzalima minda ya mpesa ndi kusangalala ndi vinyo—sadzamwedwa ndi ena. Monga mitengo, anthu anga adzakhala ndi miyoyo yaitali. Adzakondweradi ndi zinthu zimene adzagwirira ntchito.”—Yesaya 65:21, 22, TEV.
Thanzi
“Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala mmenemo, adzakhululukidwa mphulupulu zawo.”—Yesaya 33:24.
Sikudzakhala Kupunduka
“Maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzaimba.”—Yesaya 35:5, 6.
Chakudya Chambiri
“M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.”—Salmo 72:16.
Mtendere
“Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa pa dziko lapansi. Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.”—Salmo 46:8, 9.
ZIMENE MUFUNIKIRA KUCHITA
Kodi muyenera kuchitanji kuti mulandire madalitso ameneŵa amene Mulungu walonjeza? Baibulo limayankha pa Yohane 17:3: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” Inde, mwa kuphunzira za Mulungu—dzina lake, chifuno chake, ndi malamulo ake—timapeza chitsogozo. Ndiponso, mwa kuphunzira za Yesu—moyo wake pa dziko lapansi, nsembe yake ya dipo la machimo athu, malo ake monga Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu—tingakhale ndi chidaliro chakuti chifuno cha Mulungu chidzakwaniritsidwa.
Kulekerera kuipa kwa Mulungu kwasonyeza mopanda chikayikiro chilichonse kuti munthu, monga wa paulendo amene ali m’dera losalidziŵa, sangalongosole mapazi ake. (Yeremiya 10:23) Indedi, mwa maboma onse ambirimbiri—kuyambira pa maulamuliro otsendereza kufikira pa maulamuliro aufulu—munthu wayesayesa njira iliyonse yolingaliridwa. Komabe, m’mikhalidwe yabwino, chipambano chake chakhala chochepa kwambiri.
Tikuthokoza chotani nanga kuti Ufumu wa Mulungu udzayankha pemphero loperekedwa ndi miyandamiyandalo: “Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Madalitso a Ufumu wa Mulungu adzaperekedwa ku dziko lapansi pamene uwo posachedwa uloŵa m’malo mwa maboma onse a anthu. Baibulo limalonjeza kuti: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.
Imeneyo idzakhala nthaŵi yabwino kwambiri chotani nanga! Chidziŵitso cha m’Baibulo chingatipatsedi chiyembekezo. Inde, zinozo ndi nthaŵi zovuta—ndipo zikuipiraipirabe. Koma zimenezo zikungosonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza a dongosolo lino loipa la zinthu. Posachedwapa nthaŵi zoipazi zidzaloŵedwa m’malo ndi nthaŵi zabwino koposa mu Ufumu wa Mulungu!