Mamiliyoni Ambiri Akhala Akapolo
PANTHAŴI imene Olaudah Equiano anabadwa, zombo za ku Ulaya zinali zitanyamula akapolo a ku Afirika kudutsa Atlantic Ocean kwa zaka mazana aŵiri ndi theka. Koma ukapolo unali wakale kuposa pamenepo. Kugwira anthu ukapolo, makamaka chifukwa cha nkhondo, kunali kuchitika kwambiri padziko lonse kuyambira nthaŵi zamakedzana.
Namonso mu Afirika, ukapolo unali wofala kale kwambiri zombo za ku Ulaya zisanafike. The New Encyclopædia Britannica imati: “Anthu akhala ndi akapolo mu Afirika wa akuda m’mbiri yonse yolembedwa. . . . Ukapolo unali kuchitika kulikonse ngakhale Chisilamu chisanayambe, ndipo akapolo akuda ogulidwa ku Afirika anagulitsidwa kwambiri m’dera lonse la Asilamu.”
Zimene zinasiyanitsa malonda a akapolo odutsa Atlantic ndi ena zinali kukula kwake ndi nthaŵi imene anatenga. Malinga ndi kuyerekezera kolondola kwambiri, chiŵerengero cha akapolo amene anadutsa Atlantic Ocean kuyambira m’zaka za zana la 16 mpaka la 19 chinali pakati pa 10 miliyoni ndi 12 miliyoni.
Njira Yambali Zitatu
Mwamsanga pambuyo pa ulendo wapanyanja wa Christopher Columbus mu 1492, atsamunda Achizungu anakhazikitsa migodi ndi minda ya nzimbe ku America. Kuwonjezera pa kugwira eni dzikolo ukapolo, Azunguwo anayamba kuitanitsa akapolo kuchokera ku Afirika.a Kunyamula akapolo pazombo kudutsa Atlantic kunayamba pang’onopang’ono chapakati pa ma 1500, koma pofika m’tsiku la Equiano, chapakati pa ma 1700, kunakhala kowopsa—andende pafupifupi 60,000 chaka chilichonse.
Zombo zochokera ku Ulaya zinatsatira njira yambali zitatu. Choyamba zinkanyamuka ku Ulaya kupita kummwera ku Afirika. Ndiyeno zinayenda panjira yapakati (yolunzanitsa ziŵirizo) kupita ku America. Potsiriza zinabwerera ku Ulaya.
Pamalo onse atatu a njirayo, akulu a amalinyero anachita malonda. Zombo zinachoka pamadoko a ku Ulaya zili zodzala katundu—nsalu, zitsulo, mfuti, ndi zakumwa zaukali. Zitafika kugombe lakumadzulo kwa Afirika, akulu a amalinyero anasinthanitsa malonda ameneŵa ndi akapolo operekedwa ndi eni malonda a ku Afirika. Akapolowo anapakiridwa m’zombo, zimenenso zinapita ku America. Ku America, akulu a amalinyerowo anagulitsa akapolowo nalongedza katundu wotulutsidwa ndi akapolo—shuga, kachasu, manyuchi, fodya, mpunga, ndipo, kuyambira m’ma 1780, thonje. Ndiyeno zombozo zinabwerera ku Ulaya, mbali yomaliza ya njira ya ulendowo.
Kwa eni malonda Achizungu ndi Achiafirika, limodzinso ndi atsamunda a ku America, malonda a amene anatcha katundu wamoyo anali opindula kwambiri, njira yopangira ndalama. Kwa aja amene anagwidwa ukapolo—amuna ndi akazi awo, atate ndi amayi, ana aamuna ndi aakazi—malondawo anali ankhanza ndi owopsa.
Kodi akapolowo anachokera kuti? Ena anafwambidwa, monga momwe zinachitikira kwa Olaudah Equiano, koma ambiri anagwidwa m’nkhondo zapakati pa maufumu a mu Afirika. Omwe anali kuwapereka anali Aafirika. Wolemba mbiri Philip Curtin, katswiri wa malonda a akapolo, akulemba kuti: “Azungu anadzadziŵa posapita nthaŵi kuti Afirika anali woipa kwambiri pa thanzi lawo kwakuti iwo sakanakhoza kuukira paokha kuti agwire akapolo. Kugwira akapolo kunakhala ntchito yochitidwa ndi Aafirika chabe . . . Unyinji wa anthu ogulitsidwa ukapolo panthaŵi yake yoyamba anali makamaka andende a kunkhondo.”
Njira Yapakati
Ulendo wopita ku America unali wowopsa. Poyenda ulendo kumka kugombe ali omangidwa maunyolo m’timagulumagulu, Aafirika anazunzika kwambiri, nthaŵi zina miyezi yambiri, m’malinga amiyala kapena m’zithando zamatabwa. Pamene zombo za akapolo zopita ku America zinafika, andendewo anali kale ndi thanzi loipa chifukwa cha nkhanza imene inachitidwa pa iwo. Komanso zoipa kwambiri zinali kudza.
Ataguguzidwira m’chombo, kuvulidwa zovala, ndi kupimidwa ndi dokotala wa m’chombocho kapena mkulu wa amalinyero, amuna anaikidwa m’matangadza napititsidwa kuchipinda chapansi. Akulu a zombo analonga akapolo ambirimbiri m’chipinda cha katundu kuti akapeze ndalama zambiri. Akazi ndi ana anali ndi ufulu wokulirapo wa kuyendayenda, ngakhale kuti zimenezi nazonso zinawaika pangozi ya kugonedwa ndi amalinyero.
Mpweya m’chipindacho unali kununkha monyansa. Equiano akufotokoza zimene akukumbukira: “Kuchepa kwa malowo ndi kutentha kwa kunja, kuwonjezerapo kuchuluka kwa anthu m’chombo, chimene chinali chodzala kwambiri kwakuti panalibe malo amene munthu akanakhoza kutembenukira, kunatsala pang’ono kutikomola. Zimenezi zinachititsa thukuta lambiri, kwakuti posapita nthaŵi mpweya unakhala wosayenera kupuma chifukwa cha kununkha kosiyanasiyana konyansa kwambiri, ndipo zinachititsa nthenda mwa akapolowo, zimene ambiri anafa nazo . . . Kukuwa kwa akazi ndi kubuula kwa amene anali kufa kunachititsa malowo kukhala owopsa mosalingalirika.” Andendewo sakanachitira mwina kusiyapo kupirira mikhalidwe imeneyo paulendo wonsewo wodutsa nyanja, umene unatenga pafupifupi miyezi iŵiri, nthaŵi zina kuposapo.
M’mikhalidwe imeneyo yauve wosaneneka, nthenda zinachuluka. Miliri ya kamwazi ndi nthomba inali yowanda. Imfa zinachuluka. Zolembedwa zimasonyeza kuti kufikira m’ma 1750, Mwafirika 1 mwa 5 m’chombo anafa. Akufawo anaponyedwa panyanja.
Kufika ku America
Pamene zombozo zinayandikira ku America, amalinyerowo anakonzekeretsa Aafirika kuti awagulitse. Anamasula andendewo maunyolo awo, kuwanenepetsa ndi zakudya, ndi kuwadzola mafuta a mngole kuti aoneke ngati athanzi ndi kuti zilonda ndi mabala zibisike.
Nthaŵi zambiri akulu a amalinyero ankachita selo pogulitsa andende awo, koma nthaŵi zina ankakonza “kulimbirana,” kumene kunafuna kuti ogulawo alipiriretu mtengo woikika. Equiano akulemba kuti: “Chizindikiro chitangoperekedwa, (mwachitsanzo ng’oma itaombedwa) ogulawo amagudukira kubwalo kumene akapolo ali, namasankha katundu amene akonda koposa. Phokoso ndi kukuwa kumene kumakhalapo ndi kufunitsitsa koonekeratu pankhope za ogulawo zimawonjezera kwambiri mantha a Aafirika owopsedwawo.”
Equiano akuwonjezera: “Mwanjira imeneyi, popanda chifundo, achibale ndi mabwenzi amalekanitsidwa, unyinji wawo osadzaonananso.” Kwa mabanja amene mwanjira ina anakhoza kukhalira pamodzi m’miyezi yapitayo akumapirira mikhalidwe yowopsayo, limeneli linali tsoka lopweteka kwenikweni.
Ntchito ndi Chikoti
Akapolo Achiafirika anagwira ntchito m’minda kulima khofi, mpunga, fodya, thonje, ndipo makamaka nzimbe. Ena anagwira ntchito zolimba m’migodi. Ena anali akalipentala, apachipala, opanga mawatchi, opanga mfuti, ndi amalinyero. Ndiponso ena anali antchito zapanyumba—oyeretsa m’nyumba, alezi, osoka zovala, ndi ophika. Akapolo anali kulambula malo, kupanga misewu ndi kumanga nyumba, ndi kupanga mifuleni yokumba.
Komabe, ngakhale kuti anachita ntchito zonsezo, akapolowo anayesedwa chuma cha munthu, ndipo mwalamulo mbuye wawo ndiye anali ndi mphamvu zonse pa chuma chake. Komabe, ukapolo unapitiriza kukhalako osati chifukwa chabe cha kumanidwa mphamvu ndi ufulu. Komanso unapitiriza kukhalako chifukwa cha chikoti. Ulamuliro wa ambuye wawo ndi akapitawo awo unadalira pa kukhoza kwawo kuvulaza. Ndipotu anavulazadi kwambiri.
Kuti aletse chipanduko ndi kuti athe kuyang’anira akapolo awo, ambuye wawo anali kupereka chilango choipa chowononga thupi ngakhale pa zolakwa zazing’ono. Equiano akulemba kuti: “Kunali kofala [ku West Indies] kwa akapolo kusindikizidwa pathupi zilembo zoyamba za dzina la mbuye wawo, ndi magoli olemera achitsulo okoloweka m’makosi mwawo. Ndipotu panthaŵi zambiri zowasereula ankamangidwa maunyolo ambiri, ndipo kaŵirikaŵiri zida zozunzira zinali kuwonjezedwa. Nthaŵi zina chopunamitsa chachitsulo, zida zotsinira chala chamanthu, ndi zina zotero. . . . zinagwiritsiridwa ntchito pa zolakwa zazing’onong’ono. Ndaonapo munthu wakuda akumenyedwa kufikira mafupa ake ena atathyoka ngakhale chifukwa cholekerera mphika kufwafwamira madzi pamoto.”
Nthaŵi zina akapolowo anasankha kupanduka. Komabe, zipanduko zochuluka sizinapambane ndipo iwo analangidwa mwauchiŵanda.
[Mawu a M’munsi]
a Maiko a ku Ulaya amene mwachindunji anachita malonda odutsa Atlantic anali makamaka Britain, Denmark, France, Netherlands, Portugal, ndi Spain.
[Chithunzi patsamba 5]
Akufawo anaponyedwa panyanja
[Mawu a Chithunzi]
Culver Pictures
[Chithunzi patsamba 5]
Akapolo ambirimbiri anapakiridwa m’chipinda cha katundu
[Mawu a Chithunzi]
Schomburg Center for Research in Black Culture / The New York Public Library / Astor, Lenox and Tilden Foundations