Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 7/8 tsamba 29
  • Khalani Okonzeka kaamba ka Mtsogolo Mwabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Okonzeka kaamba ka Mtsogolo Mwabwino
  • Galamukani!—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Konzekerani Kaamba ka Chipulumutso Kuloŵa M’dziko Latsopano
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Limbani Mtima pamene Chilanditso Chikuyandikira
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kodi Mwakonzekera Tsiku la Yehova?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Chipulumutso Kudzera mu Ufumu wa Mulungu Chayandikira!
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 7/8 tsamba 29

Khalani Okonzeka kaamba ka Mtsogolo Mwabwino

“KHALANI okonzeka,” Yesu analimbikitsa motero. (Luka 12:40) Tikatero, pamene Kristu adza “ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu,” tidzakhoza kulabadira mwachimwemwe lamulo lake lakuti: “Ŵeramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.”—Luka 21:27, 28.

Chiwomboledwe chotani? Eya, chonga chija chimene Nowa ndi banja lake anakhala nacho—inde, kupulumuka mapeto a dziko ili! “Dziko lapansi lipita,” analemba motero mtumwi Yohane, “koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.”—1 Yohane 2:17.

M’dziko latsopano la Yehova, nzika za pa dziko lapansi za Mfumu, Yesu Kristu, zidzakhala ndi moyo wosatha. “Olungama adzalandira dziko lapansi,” limatero Baibulo, “nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Mulungu walonjeza mtsogolo mwabwino kwambiri chotani nanga kwa anthu ake! “Mulungu yekha adzakhala nawo,” Mawu ake amatero. “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.” Umenewu ndi ulosi woona!—Chivumbulutso 21:3, 4.

Komabe, kuti mukapeze mtsogolo motere, muyenera kuchitapo kanthu. Chofunika choyamba ndicho kupeza chidziŵitso. Baibulo limafotokoza kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—Yohane 17:3.

Mufunikiranso kusonkhana nthaŵi zonse ndi ena amene akufunafuna chidziŵitso chimenechi, monga momwe mtumwi analimbikitsira: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi . . . ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:24, 25) Inde, anthu a Yehova akuona tsiku la chiwomboledwe kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu lilikuyandika nthaŵi zonse, tero adziŵika chifukwa cha kusonkhana kwawo pamodzi.

Ponena za msonkhano wina m’sitediyamu ina yaikulu, Sunday Telegraph ya ku London inasimba kuti: “Palibe kupanda chiyembekezo kumene kumapezeka nthaŵi zonse ndi aja amene amalengeza kuti ‘Mapeto Ayandikira.’ Iwo angakhale atayandikiradi. Komabe, pakali pano aliyense akuoneka kuti akukondwa ndi mkhalidwe wabwino, woongoka, Wopembedza koma wosangalatsa.” Ndiyeno pepalalo linawonjezera: “Ngati dongosolo la dziko lilipoli lilidi pafupi kuwonongeka, Mboni ku Twickenham zikuoneka kukhala zokonzeka kupanga lina.”

Kukhala okonzeka kumatanthauza kukhala otanganitsidwa, kuchita ntchito yonga ija yochitidwa ndi Nowa, yemwe anatumikira monga “mlaliki wa chilungamo” m’masikuwo Chigumula chisanachitike. (2 Petro 2:5) Kukhala okonzeka kumatanthauzanso kusonyeza ‘mayendedwe opatulika ndi chipembedzo.’ Mukuitanidwa, inde, kulimbikitsidwa, kugwirizana ndi anthu a Yehova pa “kuyembekezera ndi kufulumira kwa [kukhalapo, NW ] kwake kwa tsiku la [Yehova, NW ].”—2 Petro 3:11, 12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena