Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 7/8 tsamba 12-15
  • Kodi Mungachitenji ndi Fungo Loipa la m’Kamwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungachitenji ndi Fungo Loipa la m’Kamwa?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Zodziŵika Ponena za Fungo Loipa la m’Kamwa Nzotani?
  • “Mwadzuka Bwanji! Kodi Fungo la m’Kamwa Mwanu Lili Bwanji?”
  • Mmene Mungaletsere Fungo Loipa la m’Kamwa
  • N’chifukwa Chiyani Muyenera Kumakaonana ndi Dokotala wa Mano?
    Galamukani!—2007
  • Zimene Mungachite Kuti Mupewe Chiseyeye
    Galamukani!—2014
  • Mmene Majeremusi Olimbanazoŵa Amadzukiriranso
    Galamukani!—2003
Galamukani!—1995
g95 7/8 tsamba 12-15

Kodi Mungachitenji ndi Fungo Loipa la m’Kamwa?

Limanenedwa kukhala chimodzi cha zinthu zimene ochuluka amadandaula nazo padziko, likumasautsa oposa 80 peresenti ya anthu achikulire panthaŵi zosiyanasiyana. Limachititsa munthu manyazi, kukhumudwa, ndi kuvutika mtima.

KWA madokotala, limadziŵika kwambiri monga halitosis, wotengedwa ku liwu la Chilatini lakuti halitus, lotanthauza “mpweya,” ndi mphatikira mtsogolo -osis, amene amatanthauza mkhalidwe woipa. Ndiponso ena amalitcha kununkha m’kamwa. Koma anthu ochuluka amangoti fungo loipa la m’kamwa!

Kodi muli ndi fungo loipa la m’kamwa? Pamene kuli kwakuti sikungakuvuteni kuzindikira fungo loipa la m’kamwa mwa anthu ena, kungakhale kosatheka kwa inu kuzindikira lanu. Magazini a American Dental Association, JADA, amafotokoza kuti timazoloŵera fungo lathu loipa la m’kamwa ndi kuti ngakhale anthu “okhala ndi fungo loipitsitsa la m’kamwa angakhale osazindikira vutolo.” Chifukwa chake, ife ambiri timazindikira za fungo lathu loipa la m’kamwa kokha pamene munthu wina watiuza. Nzochititsa manyazi chotani nanga!

Choonadi chakuti vutolo nlofala sichimatonthoza. Ambiri amaona fungo loipa la m’kamwa kukhala lonyansa ndi losakondweretsa. Nthaŵi zina, lingachititse kusweka mtima koipa. Dr. Mel Rosenberg, mkulu wa Laboratory of Oral Microbiology pa Tel Aviv University ku Israel akuti: “Kununkha m’kamwa, kwenikweni kapena kongoganizira, kungachititse wina kudzilekanitsa ndi anthu ena, milandu ya chisudzulo, ndipo ngakhale kulingalira zodzipha.”

Kodi Zodziŵika Ponena za Fungo Loipa la m’Kamwa Nzotani?

Akatswiri a zaumoyo azindikira kwanthaŵi yaitali kuti fungo loipa la m’kamwa ndilo umboni wa thanzi loipa limene lingakhalepo. Pachifukwa chimenecho, chiyambire nthaŵi zakale, madokotala apenda mafungo a m’kamwa mwa munthu.

Pafupifupi zaka mazana aŵiri zapitazo, katsŵiri wa chemistry Wachifrenchi wotchuka Antoine-Laurent Lavoisier anapanga chopimira mpweya chopendera mbali za mpweya wa munthu. Chiyambire pamenepo, asayansi apanga mitundu ina yabwinopo. Lerolino, malaboletale ku Canada, Israel, Japan, ndi Netherlands akugwiritsira ntchito halimeter, imene imapima mphamvu ya mafungo onyansa a m’kamwa. Ku New Zealand, asayansi apanga malo omerako plaque, otchedwanso makamwa opanga. Zimenezi zili ndi mkhalidwe wonga wa m’kamwa mwenimweni mwa munthu, ndi mate, plaque, mabakiteriya, ndipo ngakhale fungo loipa.a

Mothandizidwa ndi sayansi yamakono yopanga zinthu, asayansi aphunzira zambiri ponena za fungo lathu la m’kamwa. Mwachitsanzo, malinga ndi kunena kwa magazini a Scientific American, “ofufuza tsopano apeza misanganizo ya mipweya pafupifupi 400 mumpweya wa fungo labwino la m’kamwa mwa munthu.” Komabe, si misanganizo yonseyi imene imatulutsa fungo loipa. Zimene makamaka zimachititsa fungo loipa la m’kamwa ndi hydrogen sulfide ndi methyl mercaptan. Kwanenedwa kuti mipweya imeneyi imachititsa m’kamwa mwathu kukhala ndi fungo lofanana kwambiri ndi la skunk.

M’kamwa mwa munthu mumakhala mabakiteriya amitundu yoposa 300. Tufts University Diet & Nutrition Letter ikuti: “Pokhala mwakuda, mofunda, ndi mwachinyontho, m’kamwa ndimo m’malo abwino koposa okuliramo mabakiteriya ochititsa fungolo.” Koma ndi mitundu inayi yokha imene makamaka imachititsa fungo loipa la m’kamwa. Iwo amakhala m’kamwa mwanu, koma mwinamwake simunawadziŵebe maina awo. Ndiwo Veillonella alcalescens, Fusobacterium nucleatum, Bacteroides melaninogenicus, ndi Klebsiella pneumoniae. Iwo amadya nyenyeswa za chakudya, maselo akufa, ndi zinthu zina m’kamwa. Ntchito imeneyi ya mabakiteriya imatulutsa mpweya wonunkha pambuyo pake. Mchitidwewo ngwofanana ndi zimene zimachitika zinyalala zikawola. Moyenerera, magazini a mano akuti J Periodontol akufotokoza kuti: “Nthaŵi zambiri, halitosis imayambira m’kamwa mwenimwenimo, chifukwa cha kuvunda kochititsidwa ndi ma microbe [kuwola kwa zinthu].” Ngati mchitidwewu ulekereredwa, ungachititse mano kuwola ndi chiseyeye.

“Mwadzuka Bwanji! Kodi Fungo la m’Kamwa Mwanu Lili Bwanji?”

Mchitidwe umenewu wakuwola m’kamwa umafulumira kuchitika kutulo. Chifukwa ninji? Masana, m’kamwa mumatsukidwa ndi mate odzala oxygen ndi okhala ndi asidi pang’ono, akumachotsa mabakiteriya. Komabe, kutuluka kwa mate kwa kutulo paola lililonse kumachepa kufika pa 1/50 kuposa kwanthaŵi zonse. Malinga ndi kunena kwa magazini ena, m’kamwa mouma “mumakhala ngati chithaphwi cha mabakiteriya oposa 1,600 biliyoni,” akumapanga “mpweya wa mmaŵa” ndi kununkha kwake.

Kutuluka kochepa kwa mate kungachititsidwenso ndi kupsinjika pamene muli maso. Mwachitsanzo, mlankhuli wapoyera wamantha angaume m’kamwa pokamba nkhani yake ndipo chifukwa cha zimenezo angakhale ndi halitosis yoipa kwambiri. Kuuma m’kamwa kulinso zotulukapo kapena zizindikiro za matenda ambiri.

Si nthaŵi zonse pamene fungo loipa limachititsidwa ndi ntchito ya mabakiteriya m’kamwa. Kwenikweni, kununkha m’kamwa kaŵirikaŵiri kuli chizindikiro cha mikhalidwe ndi matenda osiyanasiyana. (Onani bokosi patsamba 13.) Pachifukwa chimenechi, ngati muli ndi fungo loipa la m’kamwa losadziŵika bwino ndipo losatha, ndi bwino kukaonana ndi dokotala.

Ndiponso fungo loipa lingachokere m’mimba. Komabe, mosiyana ndi zimene ambiri amakhulupirira, zimenezi sizimachitikachitika. Kaŵirikaŵiri, mafungo ena oipa amafika m’kamwa mwanu kuchokera m’mapapu. Motani? Zakudya zina, zonga adyo kapena anyenzi, zitapukusika, zimaloŵa m’mwazi ndi kupita ku mapapu. Ndiyeno mafungo ake amapumidwa kudzera pakholingo kuloŵa m’kamwa ndi mu mphuno mwanu kutulukira kunja. Malinga ndi kunena kwa magazini akuti Health, “kufufuza kwasonyeza kuti anthu amakhala ndi fungo la adyo ngakhale pamene angotikitira kachidutswa kake kuphazi kwawo kapena kukameza kosatafuna.”

Kumwa moŵa nakonso kumaloŵetsa m’mwazi wanu ndi mapapu fungo la moŵa. Zimenezi zikachitika, palibe zimene mungachite kuti muwongolere mkhalidwewo kusiyapo kungoyembekeza. Mafungo a zakudya zina amakhalabe m’thupi mwanu kwa maola okwanira 72.

Mmene Mungaletsere Fungo Loipa la m’Kamwa

Fungo loipa la m’kamwa silingaletsedwe mwa kungotafuna zonunkhira zofanana ndi maswiti. Kumbukirani kuti kaŵirikaŵiri fungo loipa limakhalapo chifukwa cha ntchito ya mabakiteriya m’kamwa. Munthu ayenera kukumbukira nthaŵi zonse kuti nyenyeswa za chakudya zotsalira m’kamwa zimakhala chakudya cha mabakiteriya ambirimbiri. Chifukwa chake, njira ina yofunika yogonjetsera fungo loipa ndi ya kutsuka m’kamwa mwanu nthaŵi zonse, motero mukumachepetsa chiŵerengero cha mabakiteriya. Mungachite zimenezi mwa kuchotsa nthaŵi zonse nyenyeswa za chakudya ndi plaque m’mano mwanu. Motani? Kukwecha mano anu ndi mswachi mutadya chakudya ndi pokagona nkofunika. Koma kukwecha manoko kwangokhala imodzi ya njirazo.

Pali mbali zina za mano zimene mswachi sumafikako. Chotero kuyeretsa mano kamodzi patsiku ndi kachingwe koyeretsera nkofunika kwambiri. Akatswiri amalangizanso kukwecha lilime lanu mosamala ndi mswachi, limene lili malo amene mabakiteriya amakonda kubisalamo ndi kusweranamo. Kupima mano nthaŵi ndi nthaŵi ndi kuchotsa zoumirira za m’mano kochitidwa ndi dokotala wa mano ndi wotsuka mano nakonso nkofunika. Kunyalanyaza njira iliyonse ya zimenezi kungachititse fungo loipa la m’kamwa ndipo, m’kupita kwa nthaŵi, matenda oipa a m’mano ndi a nkhama.

Palinso njira zina zakanthaŵi zimene zingatsatiridwe kusintha fungo lanu la m’kamwa. Imwani madzi, tafunani chingamu chopanda shuga—chitani kanthu kena kamene kadzawonjezera kutuluka kwa mate anu. Kumbukirani kuti mate amachita ngati mankhwala achibadwa otsukira m’kamwa amene amachotsa mabakiteriya ndi kuchititsa malowo kukhala osawayenera.

Mankhwala otsukira m’kamwa ogula angathandize, koma kufufuza kwaposachedwapa kumasonyeza kuti simuyenera kuwadalira kotheratu polimbana ndi fungo loipalo. Kwenikweni, kuchukucha kaŵirikaŵiri ndi mankhwala otsukira m’kamwa okhala ndi alcohol kungachititse kuuma m’kamwa. Ena a mankhwala otsukira m’kamwa omwe munthu angagule othandiza koposa amachepetsa plaque ndi 28 peresenti chabe. Chotero mutatsuka m’kamwa ndi mankhwala anu amene mumakonda, mungakhalebe ndi mabakiteriya oyambirira oposa 70 peresenti. Magazini akuti Consumer Reports akufotokoza kuti pa kuyesa kosiyanasiyana, “fungo loipa loyamba linabwerera patapita mphindi 10 kufika ku ola limodzi pambuyo potsuka” m’kamwa ndi mankhwala. Ngakhale mankhwala otsukira m’kamwa amphamvu koposa, amene m’maiko ambiri amangoperekedwa ndi madokotala, amachepetsa plaque ndi 55 peresenti yokha. Patangopita maola angapo, mabakiteriya amabwerera pa unyinji wawo woyamba.

Mwachionekere, ponena za kuletsa fungo loipa la m’kamwa, muyenera kupeŵa mzimu wa kuchita zinthu mwawamba. M’malo mwake, muyenera kuona m’kamwa mwanu ndi mano monga zipangizo zamtengo wapatali zimene zimafuna kukonza nthaŵi zonse. Akalipentala ndi amakanika osamala amatetezera zipangizo zawo ku dzimbiri, ndi zowononga zina mwa kutsatira malangizo olunjika ozisamalirira atamaliza ntchito iliyonse. Mano anu ndi m’kamwa zili zamtengo wapatali kuposa zipangizo zilizonse zopangidwa ndi anthu. Chotero zikonzeni ndi kuzisamalira malinga ndi mmene zimafunira. Mwa kuchita zimenezi, mudzachepetsa fungo loipa la m’kamwa, limodzi ndi kukhumudwitsa ndi kunyazitsa kwake. Chofunika koposa, m’kamwa mwanu mudzakhala moyera ndi mwabwino kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

a Plaque ndi zinthu zonanda zimene zimakuta mano. Kwakukulukulu zimapangidwa ndi mabakiteriya amene angawononge mano anu ndi nkhama.

[Bokosi patsamba 13]

Kodi Chimachititsa Fungo Loipa la m’Kamwa Nchiyani?

Zotsatirazi ndi zina za mikhalidwe, matenda, ndi zizoloŵezi zambiri zimene zingachititse fungo loipa la m’kamwa:

Chifuwa

Gastritis yosatha

Nthenda ya shuga

Kumwa moŵa

Kuuma m’kamwa

Empyema

Kugeya

Chiseyeye

Ndumu ya Hiatal

Impso kulephera kugwira ntchito

Matenda a chiŵindi

Kusamba

Zilonda m’kamwa

Kutulutsa mazira

Kusasamalira m’kamwa

Sinusitis

Kusuta fodya

Mitundu ina ya kansa

Mitundu ina ya mankhwala

Kuwola mano

TB

Zilonda za paopaleshoni ya m’nkhama

[Bokosi patsamba 14]

Lilime Lanu Nalonso Limafuna Kusamalira

Pitani pa kalirole pafupi kwambiri, ndi kuyang’ana bwino lilime lanu. Kodi lili ndi timing’alu tambirimbiri? Zimenezi nzachibadwa. Koma timing’alu timeneto ta palilime lanu tingakhale mapanga a mabakiteriya ambirimbiri. Atalekereredwa, mabakiteriya angachititse vuto losatha la fungo loipa la m’kamwa ndi mikhalidwe yoipa. Komabe, anthu kaŵirikaŵiri amanyalanyaza lilime lawo potsuka m’kamwa.

Madokotala a mano amanena kuti kukwecha pamwamba pa lilime nthaŵi zonse ndi mswachi wofeŵa ndiko mankhwala a halitosis. Akatswiri ena amalimbikitsa kugwiritsira ntchito chopalira lilime. Ku India, anthu agwiritsira ntchito zopalira lilime ku mibadwomibadwo monga njira yothetsera fungo loipa la m’kamwa. Zaka zapitazo izo zinali kupangidwa ndi chitsulo, koma lerolino zopalira zapulasitiki nzofala kwambiri. Kumadera ena, mungafunikire kukaonana ndi dokotala wa mano kuti mupeze chopalira.

[Zithunzi patsamba 15]

Kusamalira m’kamwa kwabwino kumaphatikizapo kuyeretsa mano ndi kachingwe limodzinso ndi kukwecha mano ndi lilime

[Mawu a Chithunzi patsamba 12]

Life

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena