Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 10/8 tsamba 16-19
  • Sukulu ya mu Afirika Kodi Inaphunzitsanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sukulu ya mu Afirika Kodi Inaphunzitsanji?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Sukulu Yapanyumba
  • Maluso a Umoyo
  • Thayo la Pamudzi
  • Maphunziro a Chipembedzo
  • Maphunziro Amwambo Lerolino
  • Miyambi ya Aakani Imasonyeza Chikhalidwe Chawo
    Galamukani!—2003
  • Kodi Mwana Wanga Azipita ku Sukulu?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Mfungulo Zopezera Maphunziro Abwino
    Galamukani!—1996
  • Kodi Baibulo Limaletsa Maphunziro Akusukulu?
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 10/8 tsamba 16-19

Sukulu ya mu Afirika Kodi Inaphunzitsanji?

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU GHANA

SUKULU ya mu Afirika? Anthu ena a kumaiko a Azungu angadabwe kumva kuti makonzedwe oterowo analikodi m’nthaŵi zakale. Nzachisoni kuti, lingaliro loperekedwa ndi mafilimu la munthu wa mu Afirika monga chigaŵenga chonyamula muvi silinachokebe m’maganizo mwa anthu. Ambiri sangaganize mpang’ono pomwe mmene munthu wa mu Afirika wa m’nthaŵi zamakedzana angaligaliridwire kukhala wophunzira.

Nzoona kuti Aafirika okulira m’midzi sanaphunzire m’kalasi. Komabe, kalekale, maphunziro Achizungu asanafike m’dziko lino, midzi yambiri mu Afirika inali ndi njira zophunzitsira zogwira ntchito kwambiri zimene zinathandiza ana kudziŵa bwino kakhalidwe ndi kukula bwino m’midzi yawo. Mwachitsanzo, talingalirani maphunziro a Aakani, anthu olankhula Chitwi a ku Ghana.

Sukulu Yapanyumba

Pakati pa Aakani, panyumba panali monga kalasi ya pulaimale. Maphunziro a mwana anayamba pamene anaphunzira kulankhula kwa makolo ake. Panthaŵi imodzimodzi, anayambanso kuphunzira makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, pamene mlendo panyumbapo anapereka moni kwa mwana, mwanayo anaphunzitsidwa mayankhidwe abwino ndi aulemu. Ndiyeno, pamene mwanayo anatumidwa kwa ena, anaphunzitsidwa njira yaulemu yofikitsira uthenga umene anamtumiza.

Motero nzeru ya kuphunzitsa ya Aakani sinali yosiyana ndi yonenedwa m’Baibulo pa Miyambo 22:6: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” Makolo, makamaka atate, anasamalira kwambiri za kulera mwana. Mwambi wina Wachiakani umati: “Ngati mwana satenga amake, amatenga atate ŵake.”

Pamene mwana anali kukula, maphunziro akenso anawonjezeredwa. Anaphunzitsidwa za moyo, osati m’mabuku, koma m’nthano zopeka, zonga zija za kangaude woyerekezera wotchedwa Kwaku Ananse. Ndipo anawo anazikonda kwabasi nthanozo! Madzulo kuli kamphepo kozizirira, kapena usiku wozizira woŵala mwezi, amakhala kumoto namamvetsera mwachisangalalo nthano zimenezi za zilakiko ndi za kulephera.

Nthano ina yotchuka kwambiri imasimba kuti Ananse anayendayenda kuzungulira dziko lonse lapansi kukasonkhanitsa nzeru zonse naziika mumphika. Atakwaniritsa chifuno chakecho, anaganiza zokamangirira mphikawo kumwamba mumtengo, kuti wina aliyense asapeze nzeru imeneyi. Anayamba kukwera kwake mtengo wautaliwo, atamangirira mphika wodzala nzeruwo kuchingwe nulenjekeka pamimba pake. Pokalakata mtengowo, mwana wake wachisamba, Ntikuma, anafika nafuula kwa Ananse kuti: “Ha, Bambo inu! Kodi amakwera mtengo mphika uli kumimba? Bwanji osauika kumsana kuti mupeze mpata wokwerera bwino?” Ananse anayang’ana pansi nakalipira mwana wake kuti: “Kodi iwe ukuphunzitsa ine?”

Koma tsopano kunali koonekeratu kuti nzeru ina inalikobe kunja kwa mphikawo! Atakwiya pozindikira zimenezi, Ananse anaponyera mphika wakewo pansi, ndipo unasweka ndi kumwazira nzeruyo ponseponse. Aja amene anayamba kufikapo anakhala anzeru koposa. Phunziro lake: Palibe munthu ali ndi nzeru zonse. Chotero Aakani ankati: “Mutu umodzi supanga upo.”—Yerekezerani ndi Miyambo 15:22; 24:6.

Maluso a Umoyo

Maphunziro a Aakani anaphatikizaponso maluso a umoyo. Anyamata ambiri anaphunzira ntchito za atate awo—kaŵirikaŵiri ya ulimi. Koma panalinso maluso ena owaphunzira, monga kusaka nyama, kufula madzi a mtengo wa ngole ophikira moŵa, ndi maluso oluka zinthu monga mitanga. Pa maluso ovuta kwambiri, monga kusema mitengo kapena kuwomba nsalu, anyamata anali kugwira ntchito ndi amisiri odziŵa. Bwanji nanga atsikana? Maphunziro awo anali makamaka a maluso apanyumba monga kuyenga mafuta a mbewu, kupanga sopo ndi mbiya, kuwomba nsalu, ndi zina zotero.

“Programu” ya maphunziro amwambo imeneyo inaphatikizaponso sayansi. Chidziŵitso cha zitsamba za mankhwala, kakonzedwe kake ndi kuzigwiritsira ntchito kwake, chinapatsiridwa ndi tate kwa mwana kapena gogo kwa mdzukulu. Mwana anaphunziranso kuŵerengera masamu, akumagwiritsira ntchito zala ndi mibulu, miyala, ndi zizindikiro patimitengo. Maseŵero onga oware ndi nsolo anakulitsa maluso awo akuŵerenga.

Mwa kufika pa mabwalo amilandu, Aakani achichepere anadziŵanso za nkhani za ndale ndi milandu. Maliro ndiponso mapwando anaperekanso mipata yophunzirira nyimbo zamaliro zakumaloko, ndakatulo, mbiri yakale, nyimbo, kuimba ng’oma, ndi kuvina.

Thayo la Pamudzi

Pakati pa Aakani, mwana sanapatulidwe payekha. Akali mwana anayenera kudziŵa za thayo lake la pamudzi. Anayamba kuphunzira zimenezi mwa kuseŵera ndi anzake. M’kupita kwa zaka anali kugwira ntchito za onse monga ntchito zapamudzi. Pamene anapulupudza, analangidwa, osati ndi makolo ake okha koma ndi mkulu aliyense wapamudzi. Ndithudi, linali thayo la mkulu aliyense kulanga mwana aliyense wopulupudza.

Chilango chotero chinalandiridwa bwino chifukwa ana anaphunzitsidwa kulemekeza kwambiri akulu. Kwenikweni, Aakani ankanena kuti: “Mkazi wokalamba sali gogo wa munthu mmodzi.” Kulemekeza achikulire ndi kuwatumikira kunali thayo. Ndipo mwana aliyense amene, popanda chifukwa chomveka, anakana kutumikira munthu wamkulu ananeneredwa kwa makolo ake.

Maphunziro a Chipembedzo

Aakani anali anthu opembedza kwambiri, ndi olemekeza chilengedwe ndi zakuthambo zosadziŵika. Zoona, iwo anakhulupirira milungu yambiri. Ngakhale ndi choncho, Aakani anakhulupirira kuti kunali munthu Wamkulukulu mmodzi yekha. (Aroma 1:20) Liwu Lachiakani lakuti “Mulungu,” mulungu aliyense, ndi onyame. Komabe, kwa Aakani liwulo linaoneka kukhala losakwanira kutchulira Mlengi. Choncho, anamutcha Onyankopɔn, kutanthauza “Mulungu Amene Iye Yekha Ndiye Wamkulu.”

Analambiranso milungu yaing’ono pokhulupirira kuti anali makonzedwe a Mulungu Wamkulu Mmodzimodziyo. Kwa iwo, zimenezi zinali monga momwe mfumu yandodo inatumikiridwa kupyolera mwa mafumu aang’ono. Mulimonse mmene zinalili, mwana Wachiakani aliyense anaphunzitsidwa chipembedzo chimenechi.

Maphunziro Amwambo Lerolino

M’zaka zaposachedwapa Aafirika mamiliyoni ambiri asamukira ku mizinda yaikulu kumene maphunziro a m’kalasi aloŵa m’malo njira zophunzitsira zamwambo. Komabe, sukulu yamwambo ya mu Afirika ikupitirizabe m’malo ena, makamaka kumidzi. Eya, Aafirika ena akhaladi ndi maphunziro onse aŵiri amwambo ndi akusukulu!

Mwachitsanzo, talingalirani za Alfred, mtumiki Wachikristu m’Ghana. Ngakhale kuti anaphunzira kusukulu, amalemekeza kwambiri njira za moyo za mwambo. Alfred akuti: “Achibale anga ambiri osaphunzira, ngakhale kuti ali chabe ndi maphunziro achikhalidwe cha mwambo, ali aphunzitsi abwino kwambiri pambali zenizeni za moyo. Kugwira ntchito ndi Akristu anzanga pakati pawo kwandiphunzitsa njira zambiri zogwira mtima zoperekera uthenga m’njira yosavuta, ndi yachibadwa. Motero ndikhoza kulankhula ndi anthu ophunzitsidwa mwambo ndi opita kusukulu. Kaŵirikaŵiri, ndimasankha mwambi kapena fanizo limene iwo amagwiritsira ntchito, ndimaukonza bwino, ndi kuugwiritsira ntchito m’nkhani zanga za Baibulo. Zimenezi kaŵirikaŵiri zimachititsa omvetserawo kukondwa ndi kuwomba m’manja! Komabe, ndimathokozadi amuna ndi akaziwo ophunzitsidwa mwambo.”

Mwachionekere, sukulu ya mu Afirika ili ndi mbali zambiri zokhumbirika ndipo iyenera kulemekezedwa, osati kunyozedwa. Nzoona kuti siikanatulutsa zopangapanga za sayansi zodabwitsa, koma inapanga mabanja olimba, kusamalana kwa anthu, ndi anthu akhama, osangalala, opatsa, ndi a mzimu wochereza. Motero, mposadabwitsa kuti Aafirika ambiri a m’tauni amafuna kukhala pafupi ndi achibale akumidzi mwa kupitako nthaŵi ndi nthaŵi. Komabe, nthaŵi zimenezo zimakhala ndi zochitika zochititsa manyazi. Kaŵirikaŵiri a kutauni samadziŵa chochita pa chikhalidwe cha mwambo. Mwachitsanzo, kaŵirikaŵiri samadziŵa kuti popereka moni wachanza kwa anthu ambiri, njira “yoyenera” ndiyo kuyambira kulamanja kupita kulamanzere. Komabe, maulendo oterowo angakhaledi olimbikitsana.

Ngakhale ndi choncho, tiyenera kuvomereza kuti ngakhale kuti sukulu ya mwambo ya mu Afirika inaphunzitsa ulemu ndi kulambira, sinapereke chidziŵitso chopatsa moyo chonena za Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu. (Yohane 17:3) Mboni za Yehova zili ndi mwaŵi wa kugwira ntchito pakati pa Aakani ndi mafuko ena Achiafirika kupereka chidziŵitso chimenechi. Izo zaphunzitsa Aafirika zikwizikwi amene sanapite kusukulu ya boma kuŵerenga ndi kulemba kuti aphunzire Mawu a Mulungu modziŵerengera okha. Kwa awo amene “amazindikira chosoŵa chawo chauzimu,” awa ndiwo maphunziro ofunika koposa amene munthu angapeze.—Mateyu 5:3, NW.

[Zithunzi patsamba 17]

Pakati pa Aakani, mwana anaphunzitsidwa thayo lake la pamudzi

[Chithunzi patsamba 18]

Pa Nyumba Zaufumu za Mboni za Yehova pamakhala makalasi ophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena