Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 10/8 tsamba 14-15
  • Kodi Miyezo ya Mulungu ndi Yosafikirika?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Miyezo ya Mulungu ndi Yosafikirika?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Amalolera
  • Musaleke
  • Tumikirani Yehova Mogwirizana ndi Mfundo Zake Zabwino Kwambiri
    Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
  • Ndi Udindo Wanu Kusankha Pakati pa Choyenera ndi Chosayenera
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2024
  • Anthu a Yehova Amakonda Chilungamo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Malamulo a Mulungu Amatipindulitsa
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 10/8 tsamba 14-15

Lingaliro la Baibulo

Kodi Miyezo ya Mulungu ndi Yosafikirika?

“MULUNGU SAMAPIMA ANTHU NDI MA INCHI.”—MWAMBI WAKALE WA KU SCOTLAND.

MAYESO a kusukulu, mafunso oyambira ntchito, ndi kupimidwa kwa thanzi zili chabe zina za nthaŵi zosinthirapo zinthu m’moyo pamene munthu amayesedwa. Koma ponena za kukhala ndi moyo tsiku ndi tsiku molingana ndi miyezo ya Mulungu, anthu ambiri amalingalira kuti sangaifikire. Kodi inunso ndi zimene mumakhulupirira? Kodi Mungaifikire miyezo ya Mulungu?

Kuti tiyankhe, tiyeni tiyambe taona miyezo imene Mulungu waikira alambiri ake. Baibulo limamveketsa bwino mmene tiyenera kukhalira ndi moyo. (Salmo 119:105) Wolemba Baibulo Mfumu Solomo yanzeru anapeza kuti “choyenera” anthu onse ndicho ‘kuwopa Mulungu, kusunga malamulo ake.’ (Mlaliki 12:13) Mneneri Mika ananena kuti: “Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?”—Mika 6:8.

Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu iyemwini, analengeza kuti palibe malamulo oposa ‘kukonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse’ ndi ‘kukonda mnzako monga udzikonda mwini.’ (Marko 12:30, 31) Ndiponso, timasonyeza kuti timamkonda Mulungu mwa kulabadira malamulo ake onse.—1 Yohane 5:3.

Kunena mosavuta, anthu ayenera kumukonda ndi kumulemekeza Mulungu, kulabadira malamulo ake, kuchita mopanda tsankhu, kukhala achifundo kwa onse, ndi kupeŵa kunyada. Kodi miyezo imeneyi sitingaifikire?

Mulungu Amalolera

Mulungu moyenerera amayembekezera anthu kufikira miyezo yake. Komabe, ndi kuona mtima konse, kodi pali munthu wina aliyense amene amalabadira miyezo imeneyi mosaphonya nthaŵi zonse? Mosakayikira ayi, pakuti tinalandira choloŵa cha kupanda ungwiro chochokera kwa kholo lathu Adamu. (Aroma 5:12) Motero, ndife okhoterera pa kulakwa. Komabe zimenezo sizimatiletsa kutumikira Mulungu movomerezeka.

Mwachitsanzo, talingalirani za kuvuta kwa kuphunzira kuyendetsa galimoto. Pamafunika nthaŵi ndi tcheru nthaŵi zonse kuti muphunzire kuyendetsa bwino lomwe kwakuti nkukhoza mayeso a kuyendetsa galimoto. Zoonadi, tidzafunikabe kuphunzira kuyendetsa bwino ngakhale pambuyo potenga laisensi. Pamene chidziŵitso chikula, timaonjezera maluso. Koma kulibe oyendetsa galimoto osaphonya!

Mokondweretsa, Mulungu amalolera zochititsa kulephera kwathu. Saali wokhwimitsa zinthu, wofuna zimene sitingathe kuchita, ndipo samatifufuza zolakwa nthaŵi zonse. Iye amadziŵa zifooko zathu. Mfumu David amene anachita tchimo lalikulu anachitira umboni kuti: “Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.” Chifukwa ninji? “Pakuti monga m’mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo [cha Mulungu] chikulira iwo akumuwopa iye.” Ngakhale kuti Yehova amadziŵa kuti timachimwa, ali wokonzeka kuika zolakwa zathu kutali “monga kummaŵa kutanimpha ndi kumadzulo.”—Salmo 103:10-14.

Musaleke

“Pamene ndachita tondovi,” akufotokoza motero mlambiri wina woona mtima wa Mulungu, “nthaŵi zina ndimalingalira kuti sindidzapambana konse pa kukhala ndi moyo molingana ndi miyezo ya Mulungu. Koma pamene ndimalingalira bwinopo, ndimaona kuti ndingathe kukhala ndi moyo monga mmene Mulungu amafunira. Koma sikuli kopepuka!” Musalefulidwe ngati mulingalira motero. Sindinu woyamba, kapena simudzakhala womaliza kukhala ndi malingaliro onga ameneŵa.

Mtumwi Wachikristu Paulo mosabisa anavomera kuti: “Pamene ndifuna chabwino, choipa chiriko. Pakuti monga mwa munthu wa mkati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lili kulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo. . . Munthu wosauka ine.” Komabe sanalingalire kuti zimene Mulungu anafuna zinali zolimba kwambiri, pakuti iye anawonjezera kuti: “Adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi? Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu. Ndipo chotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la uchimo.” (Aroma 7:21-25) Motero anadzimvabe kukhala wokhoza kukondweretsa Mulungu ngakhale anali wochimwa.

Yehova, Mlengi wathu wachikondi, amakhululukira zolakwa zathu ndi kulephera kwathu kupyolera mwa dipo la nsembe ya Mwana wake wokondedwa, Yesu. “Ndipo akachimwa wina,” analemba motero mtumwi Yohane, “nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama ndipo iye ndiye chiwombolo cha machimo athu.” (1 Yohane 2:1, 2) Chopinga chimene uchimo umaikapo ndi chimene chimatiletsa kufikira miyezo ya Mulungu ya ubwenzi chimachotsedwapo kapena kuswedwa ndi mphamvu ya nsembe ya Kristu. Motero unansi ndi Mulungu umabwezeretsedwa.

Kuvomereza makonzedwe ameneŵa modzichepetsa kumadzetsa chikhululukiro, pakuti Mulungu akhala “pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa.” (Yesaya 57:15) Tingadalire Iye kudzutsa mzimu wathu. Iye amalonjeza ‘kuutsa wosauka kumchotsa kufumbi.’ Sitifunikiranso kuchita tondovi pamene tilephera kumvera Mulungu mosaphonya. M’malo mwake, tingakhale otsimikiza kuti Mulungu samanyalanyaza konse kuyesayesa kwathu kuti tifikire miyezo yake.—Salmo 113:7; Ahebri 6:10-12.

Ngakhale kuti ndi kovuta, mudzaona kuti mudzakhala okondwa kuchita zimene zimakondweretsa Mulungu. Kudzipereka kwa Mulungu kumachititsa moyo kukhala wopepuka kwa inu ndi kwa okuzungulirani. Ndiponso ganizirani ponena za mtsogolo. Kulimbikira kukhala molingana ndi miyezo ya Mulungu tsopano kumadzetsa chiyembekezo cha moyo wosatha m’mikhalidwe ya paradaiso.—Yesaya 48:17; Aroma 6:23; 1 Timoteo 4:8.

Akatswiri okwera mapiri amadziŵa kuti atafika pansonga ya phiri, angofika pakatikati pa ulendo. Iwo afunikabe kutsika motetezereka. Mofananamo, awo owopa Mulungu ayenera ponse paŵiri kufikira miyezo ya Mulungu ndi kulimbikira kuisunga.—Luka 21:19; Yakobo 1:4.

Pezani chitonthozo mwa kudziŵa kuti miyezo ya Mulungu ndi yofikirika. Pamene mulephera nthaŵi zina kuisunga bwino lomwe, pemphani chikhululukiro chake. Dalirani chichirikizo chake cha chikondi. (Salmo 86:5) Motero, pokhala ndi Yehova ndi Mwana wake monga Athandizi anu, mungafikire miyezo ya Mulungu ndi kupeza chiyanjo chake.—Miyambo 12:2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena