Nchifukwa Ninji Timakalamba ndi Kufa?
“KUSIYAPO kudziŵa kwathu kuti kusintha kwa msinkhu kumachitikira m’maselo,” Dr. Leonard Hayflick akuvomereza motero, “zimene tidziŵa lerolino ponena za chochititsa ukalamba chachikulu sizochuluka kwambiri kuposa zimene tinadziŵa zaka zana limodzi zapitazo.” Kwenikweni, iye akuti: “Sitikudziŵa chifukwa chabwino chilichonse chimene ukalamba umakhalirako.”
Kufufuza kochitidwa m’malaboletale pafupifupi zaka 30 zapitazo kunasonyeza kuti pamene maselo abwino a munthu otengedwa ku mluza anaikidwa m’malo abwino koposa kuti akule, anadzafa pambuyo podzigaŵa pafupifupi nthaŵi 50. Mosiyana ndi zimenezo, maselo otengedwa kwa munthu wokalamba anangodzigaŵa nthaŵi ziŵiri mpaka khumi asanafe. Chotero, The Incredible Machine, buku la National Geographic Society linati: “Umboni wa kufufuza umachirikiza lingaliro lakuti imfa imaikidwiratu mwa yense wa ife pakubadwa.”
Komabe, kodi nkotheka kuti maselo apitirizebe kumadzigaŵa? Inde, nkotheka. “Ndithudi,” anatero akatswiri aŵiri a zaukalamba, Profesa Robert M. Sapolsky ndi Caleb E. Finch, “zikuchita ngati kuti kusakalamba ndiko kunali mkhalidwe woyambirira wa zamoyo pa dziko lapansi.” Chodabwitsa nchakuti ngakhale maselo ena opunduka a munthu lerolino samakalamba.
Buku lakuti The Body Machine, lokonzedwa ndi Dr. Christiaan Barnard, amene anachita opaleshoni yoyamba yochotsa mtima mwa munthu wina kuuika mwa wina, linafotokoza kuti: “Kupezeka kwa ‘maselo osafa’ kunapereka vuto lalikulu kwa akatswiri a biology ofuna kudziŵa za ukalamba, kufikira atazindikira kuti maselowo ngopunduka.” Inde, mitundu ina ya maselo a kansa ingachirikizidwe mwa kusungidwa m’malo abwino koposa kuti azikula mopitiriza akumadzigaŵagaŵa kosatha! The World Book Encyclopedia inati: “Ngati asayansi angadziŵe mmene maselo opundukawo amapitirizira kukhalako, angapeze chidziŵitso cha mchitidwe wa kukalamba kwa maselo.” Chotero, lerolino maselo ena a kansa mwachionekere amadzigaŵagaŵa kosatha m’malaboletale, koma maselo abwino amakalamba ndi kufa.
Njira Yolakwika
Kodi kukalamba kwa anthu ndi kufa zimachitika chifukwa cha “kusoŵa mphamvu yakudzigaŵa kwa maselo [abwino],” malinga ndi kunena kwa The Body Machine? Ngati zili choncho, bukulo linatero, “nkofunika kupeza ndi kumvetsa njira imene imalamulira mphamvu zabwino zimenezi zobwerezabwereza kuti tiigwiritsire ntchito poyesa kuwonjezera moyo wa munthu.”
Ngati mukukumbukira za m’nkhani yapitayo, Dr. Hayflick analankhula za “zozizwitsa zochokera pa kutenga mimba mpaka kubadwa ndiyeno kufika pa kukhwima kwa mphamvu ya kugonana ndi pa uchikulire.” Ndiyeno anatchula za “njira yosavuta kwambiri yochirikiza zozizwitsa zimenezo kosatha.”
Ngakhale kuti asayansi kwa zaka zambiri ayesayesa mwakhama, iwo alephera kupeza njira imene ingachirikize moyo kosatha. “Zochititsa ukalamba zidakali chinsinsi,” likuvomereza motero buku lakuti The Incredible Machine.
Komatu, chochititsa ukalamba ndi imfa si chinsinsi ayi. Yankho lake lilipo.
Kodi Yankho Lake Nlotani?
Amene ali ndi yankho ndi uja amene anayambitsa “zozizwitsa zochokera pa kutenga mimba mpaka kubadwa,” Mlengi wathu wanzeru zonse, Yehova Mulungu. “Chitsime cha moyo chili ndi inu,” Baibulo limatero za iye. “Dziŵani kuti Yehova ndiye Mulungu; iyeyu anatilenga, ndipo [osati ife tokha, NW].”—Salmo 36:9; 100:3.
Talingalirani mmene Yehova Mulungu anakonzera modabwitsa kakulidwe kanu m’chibaliro, akumalemba, titero kunena kwake, buku la malangizo opangira inuyo, munthu wapadera! “Inu munalenga impso zanga; munandiumba [m’mimba mwa amayi wanga, NW],” analemba motero wamasalmo a Baibulo. “Thupi langa silinabisikira inu popangidwa ine mobisika . . . Maso anu [anaona ngakhale mluza wanga, ndipo m’buku lanu ziŵalo zake zonse zinalembedwamo, NW].” (Salmo 139:13, 15, 16) Ndithudi, thupi lathu lopangidwa modabwitsa silinakhaleko mwangozi!
Komabe, ngati Yehova Mulungu anatilenga angwiro kuti tikhale ndi moyo kosatha, nchifukwa ninji timakalamba ndi kufa? Chiletso choikidwa pa munthu woyamba, Adamu, amene Mulungu anaika m’mudzi wokongola pa dziko lapansi, chimapereka yankho. Mulungu anamlamula kuti: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.”—Genesis 2:16, 17.
Kodi chinachitika nchiyani? M’malo mwa kumvera Atate wake wakumwamba, Adamu sanamvere, akumagwirizana ndi mkazi wake, Hava, kudya mtengowo. Iwo mwadyera anasusukira lonjezo labodza la mngelo wopanduka. (Genesis 3:1-6; Chivumbulutso 12:9) Chotero, monga momwe Mulungu anachenjezera, iwo anafa. Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anapangidwa ndi mphamvu ya kukhala ndi moyo kosatha, zimenezi zinadalira pa kumvera kwawo Mulungu. Mwa kusamvera kwawo, anachimwa. Ndiyeno, pokhala ochimwa, anapatsira mbadwa zawo zonse chilema cha imfa m’matupi awo. “Chotero imfa inafikira anthu onse.”—Aroma 5:12; Yobu 14:4.
Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti palibe chiyembekezo chakuti ukalamba ndi imfa zidzagonjetsedwa. Sitiyenera kupeza vuto kukhulupirira kuti Mlengi wathu wanzeru zonse angachiritse chilema chilichonse cha majini ndi kupereka nyonga kuti miyoyo yathu ipitirizebe kwamuyaya. Koma kodi adzachita motani zimenezi? Ndipo tiyenera kuchitanji kuti tikapeze moyo wosatha umene iye walonjeza?