Mungathe Kudalira Mulungu
MUNGATHE kudalira Mulungu ndi Mawu ake, Baibulo, kotheratu. Pambuyo pa nyengo ya moyo wake wonse ya kudalira Mulungu, mwamuna wina, wopitirira zaka 100, anapereka chifukwa ichi chokhalira ndi chidaliro chake: “Taonani,” iye anatero, ‘lerolino ndilikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziŵa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasoŵapo mawu amodzi.’—Yoswa 23:14.
Mwamuna ameneyu, Yoswa, mtsogoleri wa Israyeli wakale, anaona kudalirika konse kwa Mulungu ndi Mawu ake. Zonse zimene Mulungu analonjeza Israyeli zinachitikadi. Ngati mudziŵa zambiri ponena za Mlengiyo ndi Mawu ake, mungakulitse chidaliro chimodzimodzicho. Wolambira Mulungu wina wa pambuyo pake, Mfumu Davide, anafotokoza motere: “Iwo akudziŵa dzina lanu adzakhulupirira inu; pakuti, inu Yehova, simunawasiya iwo akufuna inu.”—Salmo 9:10.
Mulungu Sadzakugwiritsani Mwala Konse
Pamene ‘mudziŵa [zambiri ponena za] dzina la Mulungu’ ndi tanthauzo la dzinalo—zifuno zake, ntchito zake, ndi mikhalidwe yake—mpamenenso mudzamdalira kwambiri. Iye ndi Bwenzi lodalirika limene silidzakugwiritsani mwala kapena kuswa pangano lake. Ndipo musalefulidwe ndi chinyengo cha awo amene amanena kuti ali omuimira ake koma amene amachita mwachinyengo kwa ena. Anthu onga amenewo amadziŵikitsidwa m’Baibulo kukhala osadalirika. Achipembedzo achinyengo amanena zinthu ndi kuchita mosiyana nazo. Monga momwe mtumwi Petro anachenjezera, amalima pamsana magulu awo. Petro analemba kuti: “Chifukwa cha iwo njira ya choonadi idzanenedwa zamwano. Ndipo m’chisiriro adzakuyesani malonda ndi mawu onyenga.”—2 Petro 2:2, 3.
Anthu otero samaimira Mulungu. Amanyoza Mawu ake. Bwanji osapenda nokha mbiri ya Mulungu mwiniyo ndi umboni monga momwe wasonyezedwera m’Baibulo? ‘Koma kodi nchifukwa ninji ndiyenera kudalira Baibulo kuposa buku lina lililonse?’ inu mungafunse choncho. Nzoonadi kuti pakhala zinyengo zambiri zachipembedzo m’mbiri yonse, koma Baibulo lili losiyana ndi zimenezo. Lingalirani za zifukwa zotsatirapozi zodalirira Baibulo.
Zifukwa Zodalirira Baibulo
Mungathe kudalira Baibulo chifukwa chakuti malonjezo ake ndi maulosi amakwaniritsidwa nthaŵi zonse. Nachi chitsanzo chimodzi chokha. Ngakhale kuti zinali ngati zosakhulupirika kwa Israyeli wogwidwa ukapolo, Yehova Mulungu, mlembi wa Baibulo, anali atalonjeza kuti adzawamasula mu ukapolo wa Babulo wamphamvu ndi kuwabwezeretsa ku Yerusalemu. Chiyembekezo chimenechi chinakhala ngati chosatheka kukwaniritsidwa chifukwa chakuti Babulo anali ufumu wamphamvu wa dziko lonse panthaŵiyo ndipo unali utawonongeratu Yerusalemu. Koma Yehova anali atatchuliratu wolamulira wachiperisi, Koresi, zaka mazana aŵiri pasadakhale, kuti adzakhala munthu amene adzagwetsa Babulo ndi kumasula anthu Ake ndipo ananeneratu za mmene chitetezero cha mtsinje wa Babulo chidzalepherera. Mungathe kuŵerenga nkhaniyi pa Yesaya 44:24–45:4.
Buku la Kukambitsirana za m’Malemba limafotokoza mmene lonjezolo linakwaniritsidwira kuti: “Koresi anali asanabadwe pamene ulosiwu unalembedwa. . . . Ulosiwo unakwaniritsidwa mokwanira kuyambira mu 539 B.C.E. Koresi anapatutsa madzi mu Mtsinje wa Firate kukhala nyanja yokumba, zipata za kumtsinje wa Babulo zinasiyidwa zotseguka mosasamala mkati mwa nthaŵi yamadyerero mumzindawo, motero Babulo anagwa kwa Amedi ndi Aperisi pansi pa Koresi. Pambuyo pa nthaŵiyo, Koresi anamasula andende Achiyuda nawabwezera ku Yerusalemu limodzi ndi malangizo a kumanganso kachisi wa Yehova kumeneko.”a Lonjezo lililonse longa limeneli lopangidwa ndi Mulungu, ulosi uliwonse umene uli m’Baibulo, wakwaniritsidwa mosaphonya.
Chitsanzo china cha ulosi umene wakwaniritsidwa nchakuti chidaliro chenichenicho chazirala m’zaka za zana lathu. Baibulo linaneneratu za zimenezi kukhala mkhalidwe wa nthaŵi imene tikukhalamo ndi moyo, pakuti limatcha nyengo imene inayamba pa Nkhondo Yadziko I mu 1914 kuti “masiku otsiriza” ndipo limanena kuti adzabweretsa “nthaŵi zoŵaŵitsa.” Linadziŵikitsa kuti m’tsiku lathu anthu adzakhala “odzikonda okha, . . . odzitamandira, odzikuza, . . . osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, . . . achiŵembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima.” (2 Timoteo 3:1-4) Ndipo linaneneratunso kuti: “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire.” (2 Timoteo 3:1-4, 13) Zimenezo nzimene taona kumene mu nthaŵi yathu.
Mungathe kudalira Baibulo chifukwa chakuti lili lodalirika. Palibe munthu amene anatsutsa momveka za kudalirika kwa Baibulo. Wasayansi wina wotchuka Bwana Isaac Newton anati: “Ndimapeza umboni wotsimikizirika wa kudalirika m’Baibulo kuposa m’mbiri wamba za m’dziko.” Mmenemo mulibe chinyengo chonga cha “madayale” a Hitler! Ndipo kodi Baibulo limasiyana motani ndi zolembedwa zina zakale? The Bible From the Beginning limati: “Pakati pa ma MSS. ambiri [malembo apamanja] odziŵika, ndi zaka zambiri zimene zapyola pakati pa kukhalapo kwa ma MSS. oyambirira ndi odziŵikawo, Baibulo limapambana malembo akale ameneŵa [aja a Homer, Plato, ndi ena]. . . . Ma MSS. olembedwa mwaluso akale ameneŵa ataikidwa pamodzi amangokhala ochepa poyerekezera ndi a Baibulo. Palibe buku lina limene lili lochitiridwa umboni monga Baibulo.” Kuchitiridwa umboni konse kwa Baibulo kumasonyeza kuona kwake kwakukulu.
Mungathe kudalira Baibulo chifukwa chakuti lili lolondola kotheratu m’mawu ake onse. Baibulo limanena kuti Mulungu “ayala kumpoto popanda kanthu, nalenjeka dziko pachabe.” (Yobu 26:7) M’malo mwa kubwereza kunena nthanthi zoyerekezera za panthaŵiyo, zonga yakuti dziko lapansi linachirikizidwa ndi njovu, Baibulo linanena zimene zinadzadziŵidwa kukhala choonadi cha sayansi yoona—kuti dziko lapansi lili ‘lolenjekeka’ mu mlengalenga. Kuwonjezera pa zimenezo, zaka zoposa zikwi ziŵiri Columbus asanabadwe, Baibulo linafotokoza bwino lomwe kuti dziko lapansi nlobulungika.—Yesaya 40:22, NW.
Mungathe kudalira Baibulo chifukwa cha kuona kwake ndi kusabisa zinthu kwake. Alembi a Baibulo sanachite chinyengo chilichonse. Ngakhale pamene zimene ananena zinavumbula kanthu kena koipa ka iwo, ka anzawo, ndi ka olamulira awo, iwo anasimba zenizeni moona mtima. Mwachitsanzo, mu uthenga wake wabwino, mtumwi Mateyu anavomereza mosabisa kuti atumwi a Yesu Kristu nthaŵi zina anali ndi chikhulupiriro chaching’ono, analimbana chifukwa cha kufuna malo, ndipo ngakhale kusiya Yesu pamene anagwidwa.—Mateyu 17:18-20; 20:20-28; 26:56.
Chifukwa china chapadera chodalirira Baibulo nchakuti uphungu wa Baibulo wathandizadi ndi kupindulitsa nthaŵi zonse pamene anthu audalira mwa kuugwiritsira ntchito. (Miyambo 2:1-9) Chilangizo cha Baibulo chimasiyana kwambiri ndi chilangizo cha “akatswiri” chimene kaŵirikaŵiri chimasinthasintha ponena za mavuto a moyo. Ponena za alangizi ena a m’nyuzipepala amene amapereka malangizo otero m’manyuzipepala ambiri a m’maiko, The Sunday Times ya ku London ikufunsa kuti: “Kodi anthu zikwi zambiriwo chaka chilichonse adzangoululirabe zakukhosi kwawo alangizi ameneŵa amene amangopereka malangizo mosaganizira?” Alembi a Baibulo sanangolemba wamba pamene anachita ntchitoyo. Analemba malangizo odalirika, ouziridwa ndi Mulungu amene akhaladi oona kwa nthaŵi yaitali.—2 Timoteo 3:16, 17.
“Malangizo a Baibulo ananditetezera kuloŵa panjira imene ikanawononga moyo wanga,” akutero Ellen, amene tsopano ali m’zaka zake za ma 30 ndiponso wokwatiwa. “Makolo anga, amene anasudzulana, sanasonyeze chidwi pa makonzedwe a ukwati, ndipo anandilimbikitsa kungokhala ndi mwamuna wongotolana naye m’malo mwa kukwatiwa naye. Pamene ndiganiza za bata limene kulondola mapulinsipulo a Baibulo kwabweretsa m’moyo wanga, ndimakondwera kuti ndinadalira Baibulo kuposa malangizo a makolo anga.”—Onani Aefeso 5:22-31; Ahebri 13:4.
“Ndinali ndi zaka 14 zokha pamene ndinayamba kuphunzira zimene Baibulo limanena pa zinthu zosiyanasiyana,” akutero Florence. “Tsopano pamene ndiganiza za kumbuyoku m’ma 1960 ndi mavuto amene anzanga anadzipatsa chifukwa cha kutsatira mikhalidwe ndi mayendedwe a m’nthaŵiyo, ndimathokoza kwambiri chitetezero chimene ndinapeza m’malangizo a Baibulo pamene ndinali msungwana wachichepere wosadziŵa zinthu kwambiri.”—Onani 1 Akorinto 6:9-11.
“Ponena za ine,” akutero James, “ndinakodwa ndi juga, kusuta fodya, ndi kumwa.” Akupitiriza kuti: “Ndikudziŵa mmene zimenezi zavulazira anthu ambiri ndi mabanja awo. Poyamba sindinadziŵe kuyenera kwa Baibulo pa mavuto anga. Koma tsopano ndikuona bwino kwambiri mmene layambukirira bwino kuganiza kwanga ndi mmene landithandizira kulondola moyo wabwinopo.”—Onani 2 Akorinto 7:1.
Mary Anne analingalira zodzipha chifukwa cha zitsenderezo za moyo ndi mavuto amalingaliro ochititsidwa ndi mmene anakulira. “Ndinaona kudzipha kukhala njira yokha yothetsera mavuto panthaŵiyo,” iye akutero. “Koma Baibulo linasintha kuganiza kwanga. Sindinadziphe chifukwa cha zimene ndinaŵerenga m’Baibulo.”—Onani Afilipi 4:4-8.
Kodi nchiyani chimene chinathandiza anthu onsewa? Anakulitsa chidaliro chachikulu mwa Mulungu ndi Mawu ake, Baibulo. Mulungu anakhala ngati bwenzi lokondedwa, lodalirika limene linawaluma khutu panthaŵi zovuta. (Yerekezerani ndi Yesaya 30:21.) Anaphunzira mapulinsipulo a Baibulo amene anawathandiza kulimbana ndi zitsenderezo ndi mavuto a moyo. Ndipo anaphunzira kudalira malonjezo odabwitsa ochokera kwa Mulungu amene sanama—monga ngati lonjezo la “dziko latsopano” lokongola lopanda chinyengo, mabodza, ndi kulimana pamsana, ndiponso lopanda chisoni, matenda, ndi imfa yomwe!—2 Petro 3:13; Salmo 37:11, 29; Chivumbulutso 21:4, 5.
Mungakulitse chidaliro chofananacho. Lerolino dziko lingakulimeni pamsana chifukwa cha kudalirika kwanu, koma khulupirirani kuti kudalira kwanu Mulungu ndi Mawu ake sizidzawonongedwa. Afalitsi a magazini ano angasangalale kwambiri kukupezerani munthu amene angakuthandizeni kudziŵa bwino kwambiri Mulungu ndi Mawu ake, Baibulo.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 8]
Mneneri wa Mulungu ananeneratu zaka 200 pasadakhale, za mmene Babulo adzagwetsedwera
[Chithunzi patsamba 9]
Bwana Isaac Newton anaona Baibulo kukhala lodalirika