Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 3/8 tsamba 9-11
  • Chimasuko pa Ulova Motani Ndipo Liti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chimasuko pa Ulova Motani Ndipo Liti?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kufunafuna Ntchito
  • Kufunika kwa Chichirikizo cha Malingaliro
  • Chimasuko pa Kuwopa Ulova
  • Musamafune Zambiri Pamoyo Wanu
    Galamukani!—2010
  • Mliri wa Ulova
    Galamukani!—1996
  • Ulova—Chifukwa Ninji Ulipo?
    Galamukani!—1996
  • Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 3/8 tsamba 9-11

Chimasuko pa Ulova Motani Ndipo Liti?

MONGA momwe alili Mlengi wake, munthu angapeze chimwemwe pantchito, imene imafotokozedwa molondola kukhala “mtulo wa Mulungu.” (Mlaliki 3:12, 13; Yohane 5:17) Ntchito yokondweretsa ingatipatse chimwemwe ndi kutichititsa kumva kukhala othandiza ndi ofunidwa. Palibe munthu amene amafuna kuti ntchito imthere, mosasala kanthu kuti imabweretsa chimwemwe chaching’ono motani. Kuwonjezera pa malipiro, ntchito yolipidwa imachititsa zinthu kulongosoka, kukhala ndi chifuno, ndi umunthu wake. Mposadabwitsa kuti kaŵirikaŵiri “malova amafuna ntchito kuposa chinthu china chilichonse.”

Kufunafuna Ntchito

Monga momwe taonera kale, mkhalidwewo pakati pa anthu ofunafuna ntchito ngocholoŵana kwambiri. Chifukwa chake, pali njira zambiri zovomerezeka zofunira ntchito. Aliyense amene ali woliyenerera akhoza kugwiritsira ntchito thandizo la boma kwa malova kumene lili lopezeka; ndipo ngati kuli kofunika, akhoza kulembetsa kumaofesi a anthu apaulova ndi kulandira thandizo lake. Ena amapeza ntchito mwa kudzipangira ntchito. Koma muyenera kusamala. Kaŵirikaŵiri ntchito yodzilemba imadya ndalama zambiri zoiyambitsira zimene zimakhala zovuta kuzilipirira. Kulinso kofunika kudziŵa ndi kulipirira msonkho ndi kulemekeza malamulo amsonkho—chinthu chovuta kuchita m’maiko ena!—Aroma 13:1-7; Aefeso 4:28.

Kuti apeze ntchito, ena adzipatsa ntchito ya kufunafuna ntchito, akumadzipereka pa zimenezi mwa njira zina ndi khama. Ena alembera makampani amene akufuna antchito, kapena aika chilengezo m’nyuzipepala zakumaloko—zina zimene zimasindikiza mwaulere zilengezo za kufunafuna ntchito. Kaŵirikaŵiri Galamukani! wapereka malangizo ogwira ntchito pankhaniyi—kwa achichepere ndi achikulirenso.a—Onani mabokosi, patsamba 11.

Muyenera kukhala wokhoza kusintha—wololera kuchita ntchito ya mtundu uliwonse, kuphatikizapo ntchito zimene simumakonda kwenikweni. Akatswiri amanena kuti pakati pa zinthu zoyambirira zimene munthu amafunsidwa pofunsira ntchito ndizo kudziŵa kwake ntchitoyo ndi utali wa kukhala kwake pa ulova. Kukhala paulova kwanthaŵi yaitali kuli chizindikiro choipa kwa woyembekezera kulemba munthu ntchito.

Munthu amene anathera nthaŵi yake mwanzeru kusukulu kuti aphunzire maluso amakhala ndi mwaŵi wabwino kwambiri wa kupeza ntchito yake yoyamba. “Ulova,” akutero Alberto Majocchi, mphunzitsi wa maphunziro azachuma, “umayambukira makamaka antchito opanda maluso.”

Kufunika kwa Chichirikizo cha Malingaliro

Chinthu chimodzi chochititsa ndicho kukhala ndi kaonedwe ka zinthu kabwino. Zimenezi zingathandizire kwambiri pakati pa kupeza ntchito ndi kusapeza ntchito. Malova amayamikira kwambiri chichirikizo cha malingaliro, chimene chimawathandiza kupeŵa kudzipatula kapena kuloŵa mu mkhalidwe wa kuchita mphwayi. Chimathandiziranso kugonjetsa kusadzilemekeza kumene kungakhalepo chifukwa cha kudziyerekezera ndi ena amene akali pantchito.

Kukhalira moyo pa ndalama zochepa kungakhale kovuta. “Pokhala wovutika maganizo, kugwiritsira ntchito bwino nthaŵi imene ndinali nayo kunali kondivuta,” akutero Stefano. “Mkhalidwewo unandiumitsa thupi kwambiri,” Francesco akukumbukira motero, “kwakuti ndinayamba kufunafuna zifukwa kwa anzanga ena okondedwa.” Apa mpamene chichirikizo cha banja chimafunika kwambiri. Kusoŵa kwa ndalama kumafuna kuti anthu onse a m’banjamo asinthe kuti agwirizane ndi mkhalidwe wosinira zinthu. Franco, amene anachotsedwa ntchito pausinkhu wa zaka 43 atagwira ntchito pakampani imodzimodziyo kwa zaka 23, akuti: “Kuyambira panthaŵi imene ndinachotsedwa ntchito, mkazi wanga anali ndi chidaliro chamtsogolo ndi wolimbikitsa kwambiri.” Armando akuthokoza kwambiri mkazi wake chifukwa cha “kuchenjera kwake pogula zinthu.”—Miyambo 31:10-31; Mateyu 6:19-22; Yohane 6:12; 1 Timoteo 6:8-10.

Mapulinsipulo a Baibulo angatithandize kukhala ndi mzimu wachiyembekezo ndi kusaiŵala zinthu zofunika koposa. Aja amene anafunsidwa ndi Galamukani!, otchulidwawo, apeza chitsimikiziro chotonthoza m’Baibulo. Chimenechi chinawapangitsa kumva kuti ali pafupi ndi Mulungu. (Salmo 34:10; 37:25; 55:22; Afilipi 4:6, 7) Kukhala ndi unansi wapafupi ndi Yehova Mulungu ndiko kofunika koposa, pakuti iyeyo akulonjeza kuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.”—Ahebri 13:5.

Kaya munthu ali paulova kapena ayi, Mawu a Mulungu amalimbikitsa aliyense kukulitsa mikhalidwe yothandiza paumoyo watsiku ndi tsiku. Sikuti zimangochitika mwamwaŵi kuti nthaŵi zina Mboni za Yehova amazifuna ndi kuziyamikira kukhala antchito oona mtima. Zimatsatira uphungu wa Baibulo wakukhala akhama ndi odalirika, osati aulesi.—Miyambo 13:4; 22:29; 1 Atesalonika 4:10-12; 2 Atesalonika 3:10-12.

Chimasuko pa Kuwopa Ulova

Kuseri kwa kusoŵa ntchito kuli chochititsa chake—dyera ndi umbombo wa anthu. Monga momwe Baibulo limanenera, “wina apweteka mnzake pomlamulira.”—Mlaliki 8:9.

Vuto la ulova—ndi mavuto enanso—lidzathetsedwa ndi kuchotsedwa kwa ulamuliro wa munthu, umene tsopano uli ‘m’masiku ake otsiriza.’ (2 Timoteo 3:1-3) Dziko limene lilidi latsopano lili lofunika. Inde, dziko mmene anthu olungama angakhalemo ndi kugwiramo ntchito pansi pa ulamuliro wolungama ndi woyenera, mmene simudzakhalanso umbombo. (1 Akorinto 6:9, 10; 2 Petro 3:13) Nchifukwa chake Yesu anaphunzitsa anthu kupemphera kuti Ufumu wa Mulungu udze ndi kuti chifuniro Chake chichitidwe padziko lapansi.—Mateyu 6:10.

Pofotokoza mwaulosi za kuchotsedwa kwa mavuto ena aakulu a anthu, Mawu a Mulungu amasonyeza zimene Ufumuwo udzachititsa: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; . . . osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka.” (Yesaya 65:21-23) Kuwopa ulova kudzatheratu posachedwa. Ngati mukufuna kudziŵa zambiri ponena za chothetsera mavuto cha Mulungu, chonde onanani ndi Mboni za Yehova m’dera lanu.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Galamukani! wa November 8, 1994, masamba 12-14; August 8, 1991, masamba 6-10; January 22, 1983, masamba 17-19 (Chingelezi); ndi June 8, 1982, masamba 3-8 (Chingelezi).

[Bokosi patsamba 11]

Kudzipangira Ntchito Panyumba

• Kuyang’anira khanda, kusamalira mwana

• Kugulitsa ndiwo zamasamba zapanyumba kapena maluŵa

• Kusoka, kuchepetsa kapena kukulitsa zovala, kusoka zigamba

• Kuloŵa ntchito zaganyu m’makampani

• Kuphika makeke ndi zakudya zina

• Kupetera, kuluka madoilo, kuluka majuzi; kupendera, kuumba miphika; ndi umisiri wina

• Kusoka mipando

• Kusamalira zolembedwa, kutayipa, kutumikira ndi kompyuta panyumba

• Utumiki wa kuyankha matelefoni

• Kuluka tsitsi

• Kulandira ofuna pogona ndi chakudya

• Kulemba makeyala ndi kuika makalata a osatsa malonda m’maemvulopu

• Kutsuka ndi kupolisha galimoto (kasitomala amabweretsa galimoto kwanu)

• Kuŵeta chiŵeto ndi kuchiphunzitsa

• Kukonza maloko ndi kupanga makiyi (malo ake panyumba)

• Zambiri za ntchito zimenezi zingalengezedwe mwaulere kapena pamtengo wotsika m’manyuzipepala akwanu

[Bokosi patsamba 11]

Kudzipangira Ntchito Kumalo Ena

• Kutsala pa nyumba (pamene anthu apita kutchuthi ndipo afuna kuti nyumba yawo iyang’aniridwe)

• Kuyeretsa: masitolo; maofesi; nyumba ndi zipinda zalendi pambuyo pa kumangidwa, pambuyo pa kuzima moto, anthu atachokamo; ntchito ya m’nyumba (m’nyumba za ena); mazenera (amakampani ndi a nyumba za anthu)

• Kukonza zinthu zowonongeka: ziŵiya zamtundu uliwonse (malaibulale amakhala ndi mabuku a kukonza zowonongeka osavuta kuwamva)

• Ntchito ya zogwiragwira zambiri: kupanga nyumba zamatabwa; kupanga makabati, zitseko, mabalanda; kupaka utoto; kupanga mpanda; kufolera denga

• Ntchito ya pafamu: kubzala kapena kukolola mbewu, kutchera zipatso

• Kukongoletsa mkati ndi kusamalira zomera: m’maofesi, m’mabanki, m’mabwalo amasitolo ndi mochezera, malo ofikira alendo

• Kuyang’anira malo: osamalira malo, mkulu wamalo (nthaŵi zina zimenezi zimaphatikizapo malo okhala aulere)

• Insuwalansi, ya chuma ndi nyumba

• Kuika makalapeti, kuchapa

• Kupereka nyuzipepala (achikulire ndi ana), mautumiki ena a kupereka zinthu: zosatsa malonda, makalata a konsolo

• Kusamutsa zinthu, kusunga zinthu

• Kukonza malo kukhala okongola, kudulira mitengo, kusamalira kapinga, kudula nkhuni

• Woyendetsa basi ya sukulu

• Kujambula ndi kamera (zithunzithunzi ndi zochitika za anthu)

• Nyambo za asodzi

• Kuchitirana ntchito: kukonzeredwa galimoto mosinthana ndi kukonza zamagetsi, kusoka mosinthana ndi kukonza mipope, ndi zina zotero

[Chithunzi patsamba 10]

“Osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo.”—Yesaya 65:22

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena