Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nchifukwa Ninji Sindimatha Kuphunzira?
“Sindinafune kupita kunyumba,” akukumbukira motero Jessica, “ndi kuyang’anizana ndi makolo anga. Ndinali nditalepheranso maphunziro angapo.”a Pausinkhu wa zaka 15, Jessica ngwanzeru ndi wokongola. Koma monga achichepere ambiri, amavutika kwambiri ndi magiredi ake.
KUSACHITA bwino kusukulu kaŵirikaŵiri kumakhalapo chifukwa cha mphwayi kulinga ku maphunziro kapena kulinga ku mphunzitsi wa munthu mwini. Koma si mmene zilili ndi Jessica. Iye amangoona kudziŵa zinthu zocholoŵana kukhala kovuta kwambiri. Motero, zimenezi zinachititsa Jessica kulephera kuchita bwino m’masamu. Ndiponso kuvutika kuŵerenga kunamchititsanso kukhala kovuta kuti achite bwino m’maphunziro enanso.
Kumbali ina, Maria, samatha kulemba zilembo molondola. Nthaŵi zonse amabisa manotsi amene amalemba kumisonkhano yachikristu chifukwa chakuti amachita manyazi ndi zilembo zake zolakwika. Komabe, sindiye kuti Jessica kapena Maria alibe nzeru. Jessica ngwabwino kwambiri kwa anthu kwakuti amatumikira monga wogwirizanitsa woikidwa ndi sukulu kapena wothetsa mavuto pamene mavutowo abuka pakati pa anzake a kusukulu. Ndipo ku zamaphunziro Maria ndi mmodzi wa amene ali pakati pa 10 peresenti ya ochita bwino koposa m’kalasi yake.
Vuto lake: Jessica ndi Maria ali ndi vuto la kuphunzira. Akatswiri amanena kuti pafupifupi 3 mpaka 10 peresenti ya ana onse angakhale ndi mavuto amodzimodziwo pa kuphunzira. Tania, amene tsopano ali ndi zaka za kuchiyambi kwa 20, akuvutika ndi zimene zimadziŵika kuti Attention Deficit Hyperactivity Disorder (ADHD).b Iye akunena kuti: Ndimavutika kwambiri pamisonkhano yachikristu, pa phunziro laumwini, ndi pemphero chifukwa cha kusakhoza kutchera khutu kwanga kapena ngakhale kukhazikika. Utumiki wanga umayambukiridwa chifukwa chakuti ndimalumpha kuchoka pankhani iyi kumka pa ina mwamsanga kwambiri kwakuti wina sangatsatire.”
Pamene matendawo sali ophatikizidwa ndi hyperactivity [kusakhazikika] amatchedwa Attention Deficit Disorder (ADD). Anthu amene amadwala matenda ameneŵa kaŵirikaŵiri amanenedwa kukhala olota masana. Ponena za awo amene ali ndi ADD, katswiri wa minyewa Dr. Bruce Roseman anati: “Amakhala atatsegula buku, ndipo kwa mphindi 45, palibe chimene amachita.” Mulimonse mmene zingakhalire iwo amavutika kwambiri kusumika maganizo.
Ofufuza za mankhwala akuti posachedwapa ayamba kumvetsa zimene zimachititsa mavutowa. Komabe, zambiri sizikudziŵikabe. Ndipo kusiyana pakati pa matenda osiyanasiyana ndi kusakhoza kuchita zinthu kumene kumadodometsa kuphunzira sikumadziŵika bwino. Mosasamala kanthu za chochititsa chenicheni kapena dzina lopatsidwa ku nthenda yakutiyakuti—kaya ndi vuto la kuŵerenga, kukumbukira, kutchera khutu, kapena kukhala wosakhazikika—nthendayo ingadodometse maphunziro a munthu ndipo ingachititse kuvutika kwambiri. Ngati muli ndi vuto la kuphunzira, kodi mungalimbane nalo motani?
Chitokoso cha Kulimbana Nalo
Talingalirani za Jessica, amene watchulidwa m’mawu oyamba. Atatsimikizira kuti angagonjetse vuto lake la kuŵerenga, anapitiriza kuyesa kuŵerenga mabuku osiyanasiyana. Kusintha kwakukulu kunachitika pamene anapeza buku la ndakatulo limene linamsangalatsa kwambiri. Anapezanso buku lofanana nalo, limenenso anasangalala kuliŵerenga. Pambuyo pake anakondweretsedwa ndi mpambo wa mabuku a nthano, ndipo pang’onopang’ono vuto la kuŵerenga linayamba kuchepa. Phunziro limene lilipo ndilo lakuti kulimbikira kumafupa. Inunso mungagonjetse vuto la kuphunzira kapena mungapange kupita patsogolo kwabwino kwambiri mwa kusaleka.—Yerekezerani ndi Agalatiya 6:9.
Bwanji za kulimbana ndi vuto la kuiŵala zinthu msanga? Mfungulo yofunika yothetsera vutoli ili m’mawu akuti: “Kubwereza nkumene kumachititsa kusunga zinthu.” Nicky anaona kuti kubwereza mwapakamwa zimene anamva ndi kuŵerenga kunamthandiza kukumbukira zinthu. Yesani zimenezo. Zingathandize inunso. Momvekera bwino, m’nthaŵi za Baibulo anthu ankatchula mawu momveka ngakhale pamene anali kudziŵerengera okha. Chotero, Yehova analamula wolemba Baibulo Yoswa kuti: ‘Uŵerenge [Chilamulo cha Mulungu] chamunsi usana ndi usiku.’ (Yoswa 1:8, NW; Salmo 1:2, NW) Kodi nchifukwa ninji kutchula mawu momveka kunali kofunika kwambiri? Chifukwa chakuti kuchita motero kunali kugwiritsira ntchito mphamvu ziŵiri—ya kumva ndi ya kuona—ndipo kunali kuthandiza kusiya chikumbuko chachikulu m’maganizo a woŵerenga.
Kwa Jessica, kuphunzira masamu kunalinso ntchito yaikulu kwambiri. Komabe, anayesa kuphunzira njira za masamu mwa kuzibwereza—nthaŵi zina akumathera theka lonse la ola panjira imodzi. M’kupita kwa nthaŵi kuyesayesa kwakeko kunafupidwa. Chotero bwerezani, bwerezani, bwerezani! Kachitidwe kabwino ndiko kukhala ndi pepala ndi cholembera pafupi pamene mukumvetsera m’kalasi kapena kuŵerenga kotero kuti mulembe manotsi.
Nkofunika kwambiri kuti mudzipereke pa kuphunzira. Pangani kutsalira pambuyo pa kuŵeruka ndi kulankhula ndi aphunzitsi anu kukhala chizoloŵezi. Adziŵeni. Auzeni kuti muli ndi vuto la kuphunzira koma kuti muli wotsimikizira kuligonjetsa. Aphunzitsi ambiri adzakhala ofunitsitsa kukuthandizani. Chotero pemphani thandizo lawo. Jessica anachita zimenezo ndipo analandira thandizo lofunika kwambirilo kuchokera kwa mphunzitsi wachifundo.
Phunzirani Kusumika Maganizo
Kudziikira chonulirapo ndi mphotho kumathandizanso. Kuika chonulirapo chenicheni—tinene kuti monga kutsiriza homuweki ina—musanatsegule wailesi yakanema kapena nyimbo zanu zokondedwa kwambiri kungakusonkhezereni kusumika maganizo. Tsimikizirani kuti zonulirapo zimene mukuikazo nzofikika.—Yerekezerani ndi Afilipi 4:5, NW.
Nthaŵi zina kupanga masinthidwe enieni pamalo anu kungathandize. Nicky analinganiza kukhala kutsogolo kwenikweni kwa kalasi pafupi ndi aphunzitsi kuti azisumika bwino maganizo. Jessica anaona kuti kunali kopindulitsa kuchita homuweki ndi bwenzi lakhama. Mungaone kuti kungopanga chipinda chanu kuoneka bwino kungakhale kothandiza.
Kuchepetsa Kusakhazikika
Ngati simumakhazikika, kuphunzira kungakhale chinthu chopweteka. Komabe, akatswiri ena akunena kuti kusakhazikika kungasinthidwe kukhala maseŵero olimbitsa thupi. “Umboni ukuwonjezereka,” ikutero U.S.News & World Report, “wakuti kukhoza kwa kudziŵa ndi kukumbukira zinthu zakale kwa munthu aliyense kumawongoleredwa ndi kusintha kwa zinthu za m’thupi muubongo zimene zimachititsidwa ndi maseŵero.” Chotero, kuchita moyenerera maseŵero olimbitsa thupi—kusambira, kuthamanga, kuseŵera mpira, kutchova njinga, kuchita skating, ndi zina zotero—kungakhale bwino kaamba ka thupi ndi maganizo omwe.—1 Timoteo 4:8.
Mankhwala amaperekedwa nthaŵi zonse kwa okhala ndi vuto la kuphunzira. Kwanenedwa kuti pafupifupi 70 peresenti ya achichepere odwala ADHD amene apatsidwa mankhwala otsitsimula asonyeza kusintha. Kaya mudzalandira machiritso a mankhwalawo chili chosankha cha inu ndi makolo anu mutaganizira za ukulu wa vutolo, ziyambukiro zoipa za machiritsowo zomwe zingakhalepo, ndi zinthu zina zofunika.
Sungani Kudzilemekeza Kwanu
Pamene kuli kwakuti vuto la kuphunzira silimaonedwa kukhala vuto la mumtima, ilo lingakhale ndi zotulukapo zokhudza mtima. Msanganizo wa kusayanjidwa nthaŵi zonse ndi kusulizidwa ndi makolo ndi aphunzitsi nthaŵi zonse, kulephera kapena kungoyesa m’maphunziro a kusukulu, ndi kusoŵa mabwenzi apafupi kungachititse mosavuta kusadzidalira. Achichepere ena amabisa malingaliro ameneŵa mwa kukhala aukali ndi owopseza.
Koma simuyenera kutaya kudzidalira kwanu chifukwa cha mavuto a kuphunzira.c “Chonulirapo changa,” akutero katswiri wina amene amathandiza achichepere okhala ndi mavuto a kuphunzira, “ndicho kusintha kaonedwe kawo ka moyo—kuchokera pa kunena kuti ‘Ndine wopusa, ndipo palibe cholongosoka chimene ndingachite’ . . . kufika pa kunena kuti ‘ndikugonjetsa vutoli, ndipo ndingachite zambiri zowonjezereka kuposa ndi mmene ndinali kuganizirira.’”
Ngakhale kuti simungachite zambiri pa kaonedwe ka zinthu ka ena, mungasonkhezere ka inu mwini. Jessica anachita zimenezo. Iye akuti: “Pamene ndinadziweruza malinga ndi zimene anzanga kusukulu ankanena ndi kunditcha kwawo maina otonza, ndinafuna kuthaŵa pa sukulu. Koma tsopano ndimayesa kunyalanyaza zimene amanena ndipo ndimayesetsabe kuchita zomwe ndingathe. Nzovuta, ndipo ndimadzikumbutsabe, koma zimathandiza.”
Jessica anafunikira kulimbana ndi chinthu china. Mlongo wake wamkulu ankachita bwino kwambiri m’maphunziro onse. “Zimenezo zinali kuwononga kudzidalira kwanga,” akutero Jessica, “mpaka pamene ndinaleka kudziyerekezera naye.” Chotero musamadziyerekezera ndi abale anu.—Yerekezerani ndi Agalatiya 6:4.
Kulankhula ndi bwenzi lodalirika kudzakuthandizaninso kuika zinthu m’malo ake. Bwenzi loona lidzamamatira kwa inu mokhulupirika pamene mukuyesa kuwongolera. (Miyambo 17:17) Komabe, bwenzi lonyenga mwina lidzakulefulani kotheratu kapena mosayenerera kukuchititsani kudziona monga ngati kuti ndinu wapamwamba. Chotero sankhani mosamala mabwenzi anu.
Ngati muli ndi vuto la kuphunzira, ndiye kuti mumawongoleredwa nthaŵi zambiri kuposa achichepere ena. Koma musalole zimenezo kukuchititsani kudziona moipa. Onani chilangizo m’njira yaumulungu, monga chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Kumbukirani, chilangizo chopatsidwa ndi makolo anu chili umboni wakuti amakukondani ndipo amakufunirani zabwino koposa.—Miyambo 1:8, 9; 3:11, 12; Ahebri 12:5-9.
Ayi, mavuto anu a kuphunzira sayenera kukulefulani. Mungachitepo kanthu ponena za iwo ndi kukhala ndi moyo wopindulitsa. Koma palinso chifukwa chachikulu cha kukhalira ndi chiyembekezo. Mulungu walonjeza kubweretsa dziko latsopano lachilungamo mmene chidziŵitso chidzachuluka ndipo mmene mavuto alionse a maganizo ndi thupi adzachotsedwa. (Yesaya 11:9; Chivumbulutso 21:1-4) Chotero khalani wotsimikiza mtima kuphunzira zowonjezereka ponena za Yehova Mulungu ndi zifuno zake, ndipo chitani zinthu mogwirizana ndi chidziŵitso chimenecho.—Yohane 17:3.
[Mawu a M’munsi]
a Maina ena asinthidwa.
b Chonde onani mpambo wakuti “Chifukwa Chake Ana Ena Ali Ovuta Kwambiri” mu kope la Galamukani! wa December 8, 1994, ndi nkhani yakuti “Kodi Mwana Wanu Ali Ndi Mavuto a Kuphunzira?” mu kope la February 8, 1983.
c Onani nkhani yakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi ndi Motani Mmene Ndingakulitsire Ulemu Waumwini?” m’kope la Galamukani! wa October 8, 1983.
[Chithunzi patsamba 30]
Dziperekeni pa kuphunzira