Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 10/8 tsamba 28-30
  • Kodi Ndingapeze Motani Nthaŵi ya Kukondwera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingapeze Motani Nthaŵi ya Kukondwera?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchitira Zinthu Pamodzi
  • Macheza Amene Amamangirira
  • Kusangalala kwa Banja
  • Pamene Muli Nokhanokha
  • ‘Kukondwera’ mu Utumiki wa Yehova
  • Kodi Nchifukwa Ninji Achichepere Ena Amangosangalala Mmene Amafunira?
    Galamukani!—1996
  • Zosangalatsa Zomwe Zimatsitsimula
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Chimafunika N’chiyani Kuti Phwando Likhale Losangalatsa?
    Galamukani!—2011
  • Tetezerani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 10/8 tsamba 28-30

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingapeze Motani Nthaŵi ya Kukondwera?

“Ndiganiza kuti timakhala ndi zinthu zambiri zokondweretsa. Mumpingo mwathu timayesetsadi kusonkhana kaamba ka kucheza. Timapeza chikondwerero chabwino. Ana ochuluka akudziko sanganene zimenezo.”—Jennifer.

KUSANGULUKA—aliyense amakufuna nthaŵi ndi nthaŵi. The World Book Encyclopedia imati kusanguluka kungaperekedi “mbali yofunika pathanzi la munthu la maganizo ndi lakuthupi.” Aha, Baibulo lenilenilo limanena kuti pali “mphindi yakuseka,” ndiko kuti, nthaŵi yakuti munthu asangalale!—Mlaliki 3:1, 4.a

Liwulo “kusanguluka” limatanthauza kubwezeretsa, kutsitsimulidwa mwakuthupi. Nzochititsa chisoni kunena kuti, zinthu zambiri zimene achichepere amachita kaamba ka “kukondwera”—monga ngati mapwando osalamulirika kapena kusuta chamba ndi kumwetsa moŵa kapena kuchita chisembwere—sizilidi zotsitsimula mpang’ono pomwe, koma zowononga. Motero kupeza zochita zosangulutsa zimene zili zosangalatsa ndi zabwinonso kungakhaledi kovuta. Koma monga momwe Jennifer, wogwidwa mawu poyambayo, akusonyezera zingatheke!

Kuchitira Zinthu Pamodzi

Posachedwapa Galamukani! anafunsa achichepere angapo pa nkhaniyi. Ochuluka ananena kuti amasangalala kucheza ndi achichepere anzawo. Kodi mumalingalira mofananamo—ndipo kaŵirikaŵiri simuitanidwa? Nangano bwanji osayamba ndinuyo? Mwachitsanzo, msungwana wina wa ku South Africa wotchedwa Leigh, akunena kuti: “Ngati ndikufuna kukaonerera kanema ina yake, ndimaimbira telefoni mnzanga wina, ndipo timauza mabwenzi athu ena.” Kaŵirikaŵiri amafika pa kuonetsedwa koyambirira kwa kanemayo. Pambuyo pake, makolo awo amadzawanyamula, ndipo amakadyera pamodzi chakudya ku lesitilanti ya kumaloko.

Zochita za m’maseŵero zimaperekanso mipata ya kulimbitsa thupi kwabwino ndi mayanjano okoma. (1 Timoteo 4:8) Roelien wachichepere akuti: “Choyamba ndimakambitsirana ndi a m’banja lathu za kumene ndikufuna kupita, ndiyeno timaitana kagulu kuti kagwirizane nafe.” Indedi, achichepere achikristu apeza mpambo wabwino kwambiri wa maseŵero abwino amene angatengemo mbali ndi ena: kuchita skate, kupalasa njinga, kuthamanga, kuseŵera mpira wa tenesi, baseball, mpira wa miyendo, ndi volleyball, kungotchulapo oŵerengeka.

Simufunikiratu kuthera ndalama zambiri kapena kukhala ndi ziŵiya zambambande kuti musangalale. “Ineyo, makolo anga, ndi mabwenzi anga, tathera maola ambiri osangalatsa tikumayenda m’mapiri apafupi ndi m’madera achipululu,” akutero msungwana wina wachichepere wachikristu. “Kukangoyenda kokha mu mphepo yabwino ndi mabwenzi abwino nkokondweretsa kwambiri!”

Macheza Amene Amamangirira

Komabe, kwa achichepere ambiri, kukondwera kumatanthauza kufika pamacheza. “Timakonda kukhala ndi mabwenzi kudzadya nafe ndi kudzamvetsera nyimbo,” akutero Aveda wachichepere. Macheza ali ndi malo ake pakati pa Akristu. Yesu Kristu mwiniyo anafika pamapwando apadera, maukwati, ndi pamacheza ena. (Luka 5:27-29; Yohane 2:1-10) Akristu oyambirira mofananamo anasangalala pa nthaŵi zimene anasonkhana kaamba ka chakudya ndi mayanjano omangirira.—Yerekezerani ndi Yuda 12.

Ngati makolo anu akulolani kuchita macheza panyumba panu, kodi mungachitenji kuti mupeŵe mavuto ndi kutsimikizira kuti aliyense adzasangalala? Kukonzekera kosamala ndiko mfungulo yake. (Miyambo 21:5) Mwachitsanzo: Nkwanzeru kuitana mabwenzi ofika chiŵerengero chimene mungathe kuyang’anira moyenera. Magulu ocheperapo kaŵirikaŵiri samakhala “michezo” kapena “mapwando osalamulirika.”—Agalatiya 5:21; Byington.

Akristu a m’zaka za zana loyamba anachenjezedwa kupeŵa kuyanjana ndi awo ‘oyenda dwachedwache.’ (2 Atesalonika 3:11-15) Ndipo njira yotsimikizirika yowononga macheza lerolino ndiyo kuitana achichepere amene ali odziŵika kukhala opanda khalidwe ndi osalamulirika. Pamene kuli kwakuti mukufuna kukhala wosamala za amene mudzaitana, musangoitana mabwenzi amodzimodziwo anthaŵi zonse. ‘Futukukani,’ ndipo dziŵani enanso, kuphatikizapo achikulire, mumpingo.—2 Akorinto 6:13, NW.

Kodi mudzawapatsa zakumwa zoziziritsa kukhosi? Ngati ndi choncho, izo siziyenera kukhala zambambande kapena zokwera mtengo kuti alendo anuwo asangalale. (Luka 10:38-42) “Nthaŵi zina timadya pizza usiku,” akutero Sanchia, msungwana wa ku South Africa. Kaŵirikaŵiri alendo amadzipereka kubweretsa chakudya pang’ono.

Kodi ndi zinthu zina zotani zimene mungachite pamacheza—kupatula pa kungoonerera TV, kumvetsera nyimbo, kapena kukambitsirana? “Kaŵirikaŵiri timalinganiza za madzulowo padakali nthaŵi,” akutero Sanchia. “Timaseŵera maseŵero kapena kupempha wina kuimba limba, motero tonse timaimba nyimbo pamodzi.” Wachichepere wina wa mu Afirika wotchedwa Masene akuti: “Nthaŵi zina timaseŵera makhadi, draughts, ndi chess.”

Jennifer, wogwidwa mawu poyambayo, anauza Galamukani! kuti: “Tili ndi mkulu wina mumpingo mwathu amene amatiitana kukaseŵera maseŵero a Baibulo. Ufunikira kukhala wodziŵa bwino Baibulo kuti useŵere bwino.” Woimira Galamukani! anafunsa achichepere ena kuti: “Kodi simuganiza kuti kuseŵera maseŵero a Baibulo nkwachikale?” Onsewo anayankha mofuula kuti, “Ayi!”

“Nkosonkhezera maganizo,” anatero msungwana wina wachichepere. “Nkokondweretsa!” anateronso wina. Pamene maseŵero a Baibulo aseŵeredwa kaamba ka kusangalala, ndipo pamene mzimu wa mpikisano uikidwa pamalo ake angakhale okondweretsa ndi ophunzitsa!—Onani nkhani yakuti “Making Get-Togethers Enjoyable yet Beneficial,” mu kope la Galamukani! wachingelezi wa June 22, 1972.

Kusangalala kwa Banja

M’nthaŵi za Baibulo sikunali kwachilendo kuti mabanja asangalale pamodzi ndi mitundu ina ya kusanguluka. (Luka 15:25) Komabe, olemba buku la The Kids’ Book About Parents achichepere akuti “masiku ano makolo ndi ana ngotanganitsidwa kwambiri kwakuti palibe amene amakhala ndi nthaŵi ya kulinganiza zinthu . . . Tikuganiza kuti nkofunika kwa makolo ndi ana kutsimikizira kuti akuthera nthaŵi ina pamodzi mlungu uliwonse akumachita zinthu zongowasangulutsa.”

“Lachisanu ndilo tsiku lathu la banja,” akutero wachichepere wina wa mu Afirika wotchedwa Paki. “Kaŵirikaŵiri timaseŵera maseŵero pamodzi.” Ndipo tisaiŵaletu abale anu. Bronwyn wachichepere akuti: “Ndimakonda kujambula ndi kuchita zinthu zina zaumisiri ndi mphwanga.” Kodi mungayambe kuchitapo kanthu ndi kupereka lingaliro la kusangalala kwinakwake m’banja lanu?

Pamene Muli Nokhanokha

Bwanji ngati muli nokha? Zimenezo sizikutanthauza kuti muyenera kukhala wonyong’onyeka ndi wosukidwa. Pali njira zambiri zothandiza ndi zosangalatsa za kugwiritsira ntchito nyengo zotero. Mwachitsanzo, zinthu zimene mumakonda. Chiyambire nthaŵi za Baibulo amuna ndi akazi apeza kuti kuphunzira nyimbo nkokhutiritsa. (Genesis 4:21; 1 Samueli 16:16, 18) “Ndimaimba limba,” akutero Rachel. “Ndiko kanthu kena kamene ungachite pamene unyong’onyeka.” Ngati muli wosakonda kuimba, mungasangalale ndi kusoka zovala, kulima dimba, kusunga masitampu, kapena kuphunzira chinenero chachilendo. Monga mfupo yake, mwina inu mungakulitse maluso ena amene angadzakhale othandiza m’zaka zamtsogolo.

Baibulo limatiuza kuti amuna achikhulupiriro, onga Isake, anafunafuna nthaŵi ya kusinkhasinkha ali okha. (Genesis 24:63) Mnyamata wina wa ku Austria wotchedwa Hans akuti: “Nthaŵi ndi nthaŵi, ndimapita kumalo ena andekha m’dimba ndi kukhala pansi ndi kumaonerera kuloŵa kwa dzuŵa. Zimenezi zimandibweretsa chisangalalo chachikulu kwambiri ndipo zimandithandiza kuyandikirana pafupi ndi Mulungu wanga, Yehova.”

‘Kukondwera’ mu Utumiki wa Yehova

Baibulo linalosera kuti Kristu “adzakondwera” ndi kutumikira Yehova Mulungu. (Yesaya 11:3) Ndipo pamene utumiki wopatulika kwa Mulungu suli kwenikweni kusanguluka, ungakhale wotsitsimula ndi wokhutiritsa.—Mateyu 11:28-30.

Hans, wogwidwa mawuyo, akukumbukira chochitika china chokondweretsa. Iye akuti: “Ine ndi mabwenzi anga timakonda kukumbukira kutha kwa milungu imeneyo imene tinathera tikumagwira ntchito pamalo omangapo Nyumba ya Msonkhano [yolambiriramo]. Tinaphunzira mmene tingagwirire ntchito pamodzi, ndipo tinadziŵana bwino kwambiri. Pokumbukira zimenezo, timakhala okhutira kuti tinachita kanthu kena koyenera kamene kanali kosangalatsa.”

Umboni wa achichepere achikristu ameneŵa umasonyeza bwino lomwe mfundo ina: Simufunikira kuphonya kusangalala. Tsatirani mapulinsipulo a Baibulo. Khalani woyerekezera zinthu! Tsatirani njira zabwino! Mudzapeza kuti mungathe kusangalala m’njira zimene zingakumangirireni ndipo osati kukuwonongani.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani yakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi Nchifukwa Ninji Achichepere Ena Amangosangalala Mmene Amafunira?” m’kope lathu la August 8, 1996.

[Mawu Otsindika patsamba 30]

“Kukangoyenda kokha mu mphepo yabwino ndi mabwenzi abwino nkokondweretsa kwambiri!”

[Chithunzi patsamba 29]

Simufunikira kuthera ndalama zambiri kuti musangalale ndi mabwenzi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena