Lingaliro la Baibulo
Chikondi Chimene Chimamangirira
MU 1978 mkuntho waukulu ku North Atlantic unakantha sitima yapamadzi yonyamula anthu Queen Elizabeth 2. Mafunde otalika ngati nyumba yazipinda khumi zosanja anawomba sitimayo, akumaipangitsa kupeyukapeyuka ngati kanthu kopepuka. Ziŵiya ndi mapasinjala zinamwazika mkati pamene chombocho chinali kupeyukapeyuka mowopsa. Modabwitsa, anthu anavulala pang’ono chabe pakati pa mapasinjala 1,200. Uinjiniya wabwino, ziŵiya zabwino, ndi kamangidwe ka sitimayo kabwino zinaichititsa kusasweka.
Zaka mazana ambiri zapitazo panali sitima inanso yapanyanja imene inaloŵa mu mkuntho waukulu. Mtumwi Paulo ndi ena 257 anali mkati mwake. Powopera kuti sitimayo ingasweke chifukwa cha kukula kwa mkunthowo, zikuoneka kuti amalinyero ake anaponyera pansi pa sitimayo “zothandizira”—unyolo kapena zingwe—kukulunga nazo ngalawayo kuti zigwirire pamodzi matabwa a ngalawa ya malondayo. Mapasinjala onse amene anali mkati anapulumutsidwa, ngakhale kuti ngalawayo sinatero.—Machitidwe, chaputala 27.
Nthaŵi zina ziyeso m’moyo mwathu zimatipangitsa kumva ngati tili m’ngalawa ya panyanja yoŵinduka. Mafunde a nkhaŵa, kugwiritsidwa mwala, ndi kupsinjika mtima angatikanthe, akumayesa chikondi chathu kufikira kumapeto. Kuti tipyole m’mikuntho imeneyo ndi kupeŵa kusweka, nafenso tifunikira zothandizira.
Pamene Mikuntho Ibuka
Chikhulupiriro ndi chipiriro cha mtumwi Paulo zalembedwa bwino lomwe m’Baibulo. Iye anagwiritsa ntchito kaamba ka mipingo yachikristu yoyambirira. (2 Akorinto 11:24-28) Zimene anachita mu ntchito ya Ambuye zimapereka umboni woonekera bwino wa kukonda kwake kwakukulu mnansi ndi unansi wake wamphamvu ndi Mulungu. Komabe, moyo wa Paulo nthaŵi zina unali wovuta. Mtumwiyo anapyola mikuntho yambiri, yeniyeni ndi yophiphiritsira yomwe.
M’tsiku la Paulo, pamene ngalawa inakumana ndi mkuntho waukulu, kupulumuka kwa mapasinjala ndi ngalawayo kunadalira pa luso la amalinyero ndiponso pa kulimba kwa ngalawayo. Zimenezo zinalinso choncho pamene mtumwiyo anakumana ndi mikuntho yophiphiritsira. Ngakhale kuti Paulo anali atapirira kusoŵa zinthu zakuthupi, kumangidwa, ndi kuzunzidwa, mikuntho yoipitsitsa imene inatokosa bata lake lauzimu ndi la mumtima ndi kukhoza kwake kupitiriza kukonda inachokera mumpingo wachikristu.
Mwachitsanzo, Paulo anagwira ntchito mosatopa kwa chaka ndi theka kukhazikitsa mpingo mu Korinto. Kudziŵana kwake ndi Akorinto kunamchititsa kukulitsa chikondi pa gulu la nkhosalo. Paulo ananenadi kuti iyeyo anali ngati atate kwa iwo. (1 Akorinto 4:15) Komabe, ngakhale kuti panali mbiri ya chikondi chake ndi kugwiritsa ntchito kaamba ka mpingowo, ena mu Korinto anamnenera mwachipongwe Paulo. (2 Akorinto 10:10) Polingalira zonse zimene anali atachita modzimana, ha, zinali zolefula chotani nanga zimenezo!
Kodi aja amene anali atalandira chikondi chachikulu cha Paulo akanakhala motani ankhanza kwambiri ndi osuliza? Paulo ayenera kukhala atamva monga ngati kuti anali kukhadzulidwa, monga ngalawa yogwidwa mu mkuntho. Kukanakhala kosavuta chotani nanga kwa iye kugonja, kulingalira kuti kuyesayesa kwake kwapapitapo kunali kwachabe, kapena kukhala woŵaŵidwa mtima! Kodi nchiyani chinamangirira Paulo? Kodi nchiyani chimene chinamletsa kusweka ndi zogwiritsa mwala?
Chikondi Chimene Chimatimangirira Pamodzi
Paulo sanasiye konse chikayikiro kwa oŵerenga ake ponena za kumene kunachokera nyonga ndi chisonkhezero chake chomwe. Analemba kuti: “Chikondi cha Kristu chitikakamiza.” (2 Akorinto 5:14) Paulo anasonyeza magwero aakulu a nyonga ndi chisonkhezero. Nyonga yokakamizayo ndiyo ‘chikondi cha Kristu.’ Katswiri wina wa Baibulo ananena mawu otsatirawa ponena za lembali: “Paulo samanena kuti chikondi chathu cha Kristu chimatimangirira ku utumiki wathu . . . Kumeneko kukanakhala kusamaliza mawu onse. Chikondi chathu cha Kristu chimayambitsidwa ndi kudyetsedwa nthaŵi zonse mosalekeza ndi chikondi chake kwa ife.”—akanyenyewo ngathu.
Chikondi chimene Kristu anasonyeza mwa kudzipereka ku imfa yomvetsa ululu pa mtengo wozunzirapo—motero akumapereka moyo wake wangwiro monga dipo lopulumutsira anthu onse okhulupirira—chinasonkhezera, kukakamiza, ndipo kuumiriza Paulo kupitiriza kutumikira zinthu za Kristu ndi abale onse. Chifukwa chake, chikondi cha Kristu chinalamulira Paulo, kumletsa kukhala wadyera, ndi kulunjikitsa zolinga zake pa kutumikira Mulungu ndi anthu anzake.
Indedi, magwero a chisonkhezero cha moyo wa chikhulupiriro chachikristu ndiwo chikondi cha Kristu. Pamene tiyang’anizana ndi mayeso amene angatilefule mwakuthupi, mwamalingaliro, ndi mwauzimu, mphamvu yosonkhezera ya chikondi cha Kristu imatikhozetsa kuchita zoposa zimene munthu wina wosonkhezeredwa pang’ono akanaleka kuchita. Imatipatsa nyonga ya kupirira.
Sitingadalire pa malingaliro athu opanda ungwiro kutilimbitsa ndi kutisonkhezera. Makamaka zimenezi zili choncho pamene ziyeso zathu zichitika chifukwa cha kugwiritsidwa mwala kapena nkhaŵa. Komanso, chikondi cha Kristu chili ndi mphamvu ya kutilimbitsa mu utumiki wathu, kutilimbitsa ndi kutisonkhezera, chinkana tili m’mayesero. Chikondi cha Kristu chimakhozetsa Mkristu kupirira osati kokha kuposa pa ziyembekezo za ena koma mwinamwake kuposa pa ziyembekezo za iye mwini.
Ndiponso, popeza kuti chikondi cha Kristu chili champhamvu, chisonkhezero chake sichimatha. Ndicho mphamvu yokakamiza imene simagwedezeka kapena kuzimiririka konse. “Chikondi sichitha nthaŵi zonse.” (1 Akorinto 13:8) Chimatikhozetsa kupitiriza kumtsatira mokhulupirika, zivute zitani.
Ziyeso za malingaliro zili ndi mphamvu imene ingatiswe. Chotero, nkofunika chotani nanga kuti tisinkhesinkhe pa chikondi chimene Kristu amatisonyeza. Chikondi cha Kristu chidzatimangirira. Chikondi chake chimatikhozetsa kupeŵa kutaya chikhulupiriro chathu. (1 Timoteo 1:14-19) Ndiponso, chikondi cha Kristu chimatisonkhezera kuchita zonse zimene tingathe kulemekeza uyo amene anachititsa chikondi cha Kristu kukhala chotheka, Yehova Mulungu.—Aroma 5:6-8.