Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 11/8 tsamba 19-20
  • Pamene Mawu Akhala Zida

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Mawu Akhala Zida
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zilonda za Mawu
  • Kodi Mungapewe Bwanji Kulankhula Mawu Achipongwe?
    Galamukani!—2013
  • Sonyezani Chikondi ndi Ulemu mwa Kulamulira Lilime Lanu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kuleka Mawu Opweteka ndi Kunena Mawu Olamitsa
    Galamukani!—1996
  • Kuvumbula Mizu ya Mwano
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 11/8 tsamba 19-20

Pamene Mawu Akhala Zida

“Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga.”—MIYAMBO 12:18.

“ZINAYAMBA patatha masabata oŵerengeka titachita ukwati,” akutero Elaine.a “Mawu ankhanza, mawu onyoza, ndi kuyesayesa kundisambula. Sindinali kutha kuyang’anizana ndi mwamuna wanga. Kuganiza kwake msanga ndi lilime lake lofulumira zinali kupotoza zinthu zonse zimene ndinanena.”

Mu ukwati wake wonse Elaine anali atayang’anizana ndi chiukiro chobisika chimene sichimasiya zipsera zooneka ndi chimene sichimamvetsa anthu chisoni. Mwachisoni, mkhalidwe wake sunawongokere pamene nthaŵi yakhala ikupyola. “Takhala okwatirana kwa zaka zoposa 12 tsopano,” iye akutero. “Palibe tsiku limene limapyola popanda kundisuliza ndi kundichitira chipongwe, akumagwiritsira ntchito mawu okakala, onyansa.”

Baibulo silimanena monkitsa pamene limati lilime lingakhale “choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.” (Yakobo 3:8; yerekezerani ndi Salmo 140:3.) Makamaka zimenezi zili choncho mu ukwati. “Amene ananena kuti ‘ndodo ndi miyala zingathyole mafupa anga koma mawu sangandivulaze’ analakwa kotheratu,” akutero mkazi wina wotchedwa Lisa.—Miyambo 15:4.

Nawonso amuna angakhale oukiridwa ndi mawu. “Kodi mukudziŵa mmene kulili kukhala ndi mkazi amene nthaŵi zonse amangokutcha wonama, chitsiru chenicheni kapena zinthu zina zoipa?” akufunsa motero Mike, amene ukwati wake wa zaka zinayi ndi Tracy ukumka ku chisudzulo. “Sindingathe kubwereza kunena zinthu zimene amatchula kwa ine pakati pa anzanga olemekezeka. Nchifukwa chake sindimalankhula naye ndiponso nchifukwa chake ndimakhala nthaŵi yaitali kuntchito. Ndimapezako mtendere wambiri kuposa kumka kunyumba.”—Miyambo 27:15.

Ndi chifukwa chabwino, mtumwi Paulo analangiza Akristu kuti: “Chiwawa [“kulalata,” NW], ndi mwano zichotsedwe kwa inu.” (Aefeso 4:31) Koma kodi “mwano” nchiyani? Paulo akuusiyanitsa ndi “kulalata” (Chigiriki krau·geʹ), kumene kumatanthauza kukweza mawu. “Mwano” (Chigiriki, bla·sphe·miʹa) makamaka umatchula za mtundu wake wa uthenga. Ngati uli wankhanza, wanjiru, wonyoza, kapena wotukwana, pamenepo ndiwo mwano—kaya ukhale wofuula kapena wonong’ona.

Zilonda za Mawu

Chizoloŵezi cha kunena mawu okakala chingafooketse ukwati, monga momwe mafunde a nyanja angakokololere thanthwe lolimba. “Pamene kukula ndi kupitiriza,” akulemba motero Dr. Daniel Goleman, “mpamenenso ngozi yake imakulirapo. . . . Kuzoloŵera kusuliza ndi kunyoza kapena kunyansidwa kuli zizindikiro zangozi chifukwa kumasonyeza kuti mwamuna kapena mkazi wagamula kale zoipa mumtima ponena za mnzakeyo.” Pamene chikondi chitha, mwamuna ndi mkazi amakhala, monga momwe buku lina likunenera, “okwatirana mwalamulo, koma osati mumtima.” M’kupita kwa nthaŵi, sadzakhalanso okwatirana.

Komabe, mwano ungayambukire zambiri kuposa ukwati weniweniwo. Mwambi wa Baibulo umati: “Moyo umasweka ndi zoŵaŵa za m’mtima.” (Miyambo 15:13) Chipsinjo chimene chimadza chifukwa cha mawu ochuluka opweteka osalekeza chingawononge kwambiri thanzi la munthu. Mwachitsanzo, kufufuza kumene kunachitidwa ndi Yunivesite ya Washington (U.S.A.) kunasonyeza kuti mkazi amene amaneneredwa zachipongwe nthaŵi zonse angamagwidwe ndi chimfine, kudwala chikhodzodzo, matenda a yeast, kusokonezeka kwa m’mimba ndi m’matumbo.

Akazi ambiri amene apirira ndi mawu amwano ndiponso kumenyedwa amanena kuti mawu amakhala opweteka kwambiri kuposa nkhonya. “Kutupa ndi mapama ake kumapola ndi kuzimiririka,” akutero Beverly, “koma sindidzaiŵala konse zinthu zoipa zimene ananena ponena za mmene ndimaonekera, mmene ndimaphikira chakudya, mmene ndimasamalirira ana.” Julia akulingalira mofananamo. “Ndikudziŵa kuti zikumveka ngati misala,” iye akutero, “koma ndingakonde kuti andimenye ndi kuiŵala m’malo mwa kuzunzika ndi maganizo kosatha.”

Koma kodi nchifukwa ninji anthu ena amaukira ndi kunyodola munthu amene ananena kuti anamkonda? Nkhani yotsatira ikuyankha funsoli.

[Mawu a M’munsi]

a Maina ena mu mpambo wa nkhanizi asinthidwa.

[Mawu Otsindika patsamba 20]

“Ndingakonde kuti andimenye ndi kuiŵala m’malo mwa kuzunzika ndi maganizo kosatha”

[Mawu Otsindika patsamba 20]

“Kodi mukudziŵa mmene kulili kukhala ndi mkazi amene nthaŵi zonse amangokutcha wonama, chitsiru chenicheni, kapena zinthu zina zoipa?”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena