Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Amalola Zinthu Zoipa Kuchitika?
LIDIJA anali wachichepere pamene nkhondo inaulika m’dziko lakwawo—dziko limene kale linkadziŵika kuti Yugoslavia. “Ndinathera masiku ambiri m’chinyumba chamdima,” akukumbukira motero. “Kaŵirikaŵiri ndinali kufuna kuthaŵira kunja, ngakhale ngati zimenezo zikanandiphetsa! Nkhondoyo isanayambe, unali ndi zinthu zonse zimene ungafune, koma tsopano unali wokondwa kungokhala ndi moyo.”
Posapita nthaŵi kupsinjika maganizo ndi mavuto ochititsidwa ndi nkhondo zinayambukira Lidija moipa mwauzimu. Akunena kuti: “Kwa milungu yambiri sitinali kupita kuntchito ya kulalikira kapena kumisonkhano. Ndinalingaliradi kuti Yehova anali kutinyalanyaza. Ndinali kudzifunsa kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji sakutithandiza tsopano lino?’”
Nkhondo, upandu, chiwawa, matenda, masoka, ngozi—zinthu zoipa zonga zimenezi zingachitikire ngakhale achichepere. Ndipo pamene tsoka likukanthani, mwachibadwa mungadabwe kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji Mulungu amalola zinthu zoipa zimenezi kuchitika?’
Anthu a Mulungu m’nthaŵi zakale anafunsa mafunso onga amenewo. Mwachitsanzo, pamene mneneri Habakuku anaona mkhalidwe woluluzika umene unali pakati pa anthu a Mulungu, analira kuti: “Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva inu? Ndifuulira kwa inu za chiwawa, koma simupulumutsa. Mundionetseranji zopanda pake, ndi kundionetsa zovuta?” (Habakuku 1:2, 3) Achichepere ena achikristu lerolino amavutika mtima mofananamo.
Talingalirani za mmene Mkristu wina wachichepere anamvera atate wake atamwalira mwadzidzidzi. Iye akuti: “Ndinapenga ndipo ndinali kukuwira kunja pazenera, kukuwira Yehova Mulungu. . . . Ndinampatsa mlandu wa zonse. Zachitika motani zimenezi? Bambo wanga anali atate wabwino kwambiri ndipo anali mwamuna wachikondi, koma tsopano izi zachitika—kodi Yehova sasamala?” Mumkhalidwe wonga umenewu, kusokonezeka, kupwetekedwa maganizo, kapena ngakhale kukwiya nkwachibadwa. Kumbukirani kuti, mneneri wokhulupirikayo Habakuku nayenso anavutika poona kuti kuipa kunaloledwa kukhalapo. Komabe, ngati munthu apitiriza kusunga maganizo opweteka, pali ngozi. ‘Angakwiyire Yehova iye mwini.’—Miyambo 19:3, NW.
Chotero, kodi ndi motani mmene mungapeŵere kugonjera mkwiyo? Choyamba, muyenera kudziŵa kumene kumachokera zoipa.
Zinthu Zoipa Sizimachokera kwa Mulungu
Baibulo limanena momveka kuti Mulungu sanafune kuti tizivutika chonchi. Iye anaika okwatirana aŵiri oyamba m’mudzi wa paradaiso mmene munalibe zopweteka ndi kuvutika. (Genesis 1:28) Mosakayikira mukudziŵa bwino lomwe mmene zinthu zinalakwikira: Cholengedwa chosaoneka chauzimu, chimene chinadzadziŵika kuti ndi Mdyerekezi ndi Satana, chinasonkhezera Adamu ndi Hava kusamvera Mulungu. (Genesis, chaputala 3; Chivumbulutso 12:9) Mwa kuchita zimenezi, Adamu analoŵetsa mbadwa zake zonse mu uchimo ndi zotulukapo zake zowononga.—Aroma 5:12.
Mwachionekere, si Mulungu amene anabweretsa zoipa pa anthu, koma munthu iye mwini. (Deuteronomo 32:5; Mlaliki 7:29) Ndithudi, zinthu zonse zoipa zimene anthu amavutika nazo lerolino—kudwala, imfa, nkhondo, chisalungamo—zinachokera pa kusamvera kwadala kwa Adamu. Ndiponso, tonsefe timayambukiridwa ndi zimene Baibulo limatcha kuti “nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika.” (Mlaliki 9:11, NW) Anthu oipa ndi olungama omwe amakumana ndi ngozi ndi masoka a mwadzidzidzi.
Chilolezo cha Mulungu cha Kuipa
Pamene kuli kwakuti nkotonthoza kudziŵa kuti kuipa sikumachokera kwa Mulungu, mungadabwebe kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji amalola kuipa kupitirizabe?’ Kachiŵirinso, zimenezi zimatibweretsa ku nkhani zimene zinadzutsidwa m’Edene. Mulungu anauza Adamu kuti ngati sadzamvera, adzafa. (Genesis 2:17) Komabe, Mdyerekezi anauza Hava kuti ngati adzadya chipatso cha mtengo woletsedwa, iye sadzafa! (Genesis 3:1-5) Kwenikweni, Satana anatchadi Mulungu kukhala wabodza. Ndiponso, Satana anatanthauza kuti munthu angamapeze bwino kwambiri ngati adzipangira zosankha zake ndipo ngati sanayembekeze kuti Mulungu azimuuza zochita!
Mulungu sakananyalanyaza milandu imeneyi. Kodi munaonapo mnzanu wa m’kalasi akutsutsa ulamuliro wa aphunzitsi? Ngati aphunzitsi angomlekerera, ophunzira ena nawonso amayamba kuchita chipongwe. Mofananamo, chipwirikiti cha m’chilengedwe chonse chikanaulika ngati Yehova sanayang’anizane ndi chitokoso cha Satana mwachindunji. Yehova anachita zimenezo mwa kulola munthu kutsatira njira ya Satana yochitira zinthu. Kodi munthu wakhala ndi ufulu wonga wa Mulungu umene Satana analonjeza? Ayi. Ulamuliro wa Satana wabweretsa msokonezo waukulu ndi mavuto, zikumamsonyeza kukhala wabodza wanjiru!
Kodi Mulungu adzalola kuipa kupitirizabe kosatha? Ayi. Kuti athetse nkhani zimene Satana anadzutsa, posachedwapa Mulungu adzathetsa kuipa konse. (Salmo 37:10) Koma kodi tingapilire motani pakali pano?
Nkhani Imene Imaloŵetsamo Inu
Choyamba, zindikirani kuti nkhani imeneyi ya pakati pa Mulungu ndi Satana imaloŵetsamo inu! Motani? Talingalirani za buku la m’Baibulo lotchedwa ndi dzina la munthu wolungamayo Yobu. Pamene Mulungu anasonyeza Yobu kukhala chitsanzo cha wolambira wokhulupirika, Satana anayankha kuti: “Kodi Yobu akhoza kukulambirani ngati sapezapo kalikonse?” (Yobu 1:9, Today’s English Version) Ndithudi, Satana ananena kuti ataloledwa kutsendereza, akhoza kuchotsa munthu aliyense pa kutumikira Mulungu!—Yobu 2:4, 5.
Chotero Satana waneneza anthu onse owopa Mulungu. Wakunenezani inuyo. Komabe, Miyambo 27:11 imati: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” Inde, pamene mutumikira Mulungu mosasamala kanthu za mavuto opweteka, kwenikweni mumathandizira pa kutsimikizira Satana kukhala wabodza!
Zoona, pamene mwayang’anizana ndi zinthu zoipa, nkovuta kulingalira za nkhani zoloŵetsedwamo. Diane, amene anali ndi zaka zakubadwa khumi zokha pamene amayi wake anamwalira, akuti: “Ndinadera nkhaŵa kuti mwina ndidzakhala wokakala mtima kapena wodzala ndi chisoni chifukwa cha ziyeso za m’moyo wanga.” Komabe, kudziŵa chifukwa chimene Mulungu walolera kuipa kwamthandiza kukhala ndi lingaliro loyenera la mavuto ake. Tsopano akunena kuti: “Ngakhale kuti pali zinthu zovuta kuchita nazo m’moyo wanga, dzanja la Yehova lakhala ndi ine nthaŵi zonse.”
Diane akutikumbutsa za mfundo ina yofunika kwambiri yakuti: Yehova samayembekezera kuti tidzalimbana ndi zitsenderezo zimenezi patokha. Salmo 55:22 limatitsimikizira kuti: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo iye adzakugwiriziza: Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” Kotoyo wachichepere anapeza zimenezi kukhala zoona. Anakumana ndi tsoka pamene makolo ake anaphedwa m’chivomezi chimene chinachitika ku Kobe, Japan, mu 1995. Ponena za iyeyo ndi abale ake aang’ono, iye akuti: “Titha kupirira chifukwa chakuti amayi wanga anatiphunzitsa kudalira pa Yehova.”
Bwanji nanga za Lidija, mtsikana wachichepere wotchulidwa pachiyambiyo? M’kupita kwa nthaŵi, anazindikira kuti Yehova sanamsiye konse. Tsopano akunena kuti: “Nthaŵi zonse Yehova analipo kaamba ka ife. Anatitsogolera nawongolera mapazi athu.”
Yehova—Mulungu Wachikondi Amene Amasamala
Inunso mungakhale ndi thandizo la Mulungu pamene zinthu zoipa zikuchitikirani. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Yehova amasamala za inu! Ndipo ngakhale kuti amalola zinthu zoipa kuchitikira anthu abwino, amaperekanso chitonthozo chachikondi. (2 Akorinto 1:3, 4) Njira imodzi imene amachitiramo zimenezi ndiyo kudzera mumpingo wachikristu. Mmenemo mungapeze ‘mabwenzi opambana ndi mbale kuumirira,’ amene angakulimbikitseni pamene muloŵa m’mavuto. (Miyambo 18:24) Kotoyo akukumbukira kuti: “Kuyambira patsiku loyamba pambuyo pa chivomezi, tinapita kumalo kumene abale anakumana, ndipo tinalandira chilimbikitso ndi zinthu zofunikira. Zimenezo zinandichititsa kumva kukhala wosungika. Malinga ngati tili ndi Yehova ndi abale, ndiganiza kuti tingapirire chilichonse.”
Chifukwa chakuti Yehova amakudziŵani monga munthu panokha, akhoza kusamaliranso zofunikira zanu pamene zinthu zoipa zichitika. Daniel akukumbukira mmene wapiririra kutayikiridwa atate wake, akumati: “Yehova amakhala atate wako, ndipo gulu lake limapereka amuna auzimu oti uwatsanzire. Nthaŵi zonse Yehova amapereka mayankho pa mafunso amene ndimakhala nawo amene mwachibadwa ndikanakambitsirana ndi atate.” Diane wakhala ndi chisamaliro chofananacho chachikondi cha Yehova chiyambire imfa ya amayi wake. Iye akunena kuti: “Kudzera mwa anthu achikulire, akulu msinkhu mwauzimu amene apereka chilimbikitso, chitsogozo, ndi uphungu, iye wanditsogolera ndi kundithandiza kulimbana ndi zofooketsa zilizonse.”
Zoonadi, kukumana ndi zinthu zoipa sikumakondweretsa konse. Koma pezani chitonthozo podziŵa chifukwa chimene Mulungu amalolera zinthu zimenezi. Nthaŵi zonse dzikumbutseni kuti Mulungu adzathetsa vutolo posachedwapa. Inde, zotsalira zonse za zoipa zimene takumana nazo zidzafafanizidwa m’kupita kwa nthaŵi! (Yesaya 65:17; 1 Yohane 3:8) Mwa kugwiritsira ntchito mwaŵi wa zinthu zonse zimene Mulungu amapereka kuti zitithandizire kupirira, mungachite mbali yanu pa kusonyeza Satana kukhala wabodza. Posapita nthaŵi, ‘Mulungu adzapukuta misozi yonse kuichotsa pamaso panu.’—Chivumbulutso 21:3, 4.
[Zithunzi patsamba 17]
Posachedwapa Yehova adzathetsa zinthu zonse zoipa