Kuti Ndilankhule ndi Mwana Wanga, Ndinaphunzira Chinenero China
KUBADWA kwa mwana wathu wamwamuna, Spencer, mu August 1982 kunali imodzi ya nthaŵi zachimwemwe koposa m’moyo wathu. Anali khanda lathanzi! Ineyo ndi mwamuna wanga tinalinganiza kukhala ndi zaka zisanu zoyembekeza tisanakhale ndi mwana wathu woyamba. Pamene miyezi inali kupita atabadwa, tinali ndi chimwemwe chotani nanga kumuona akukula! Kupimidwa kwa nthaŵi zonse mwezi ndi mwezi ku ofesi ya dokotala kunali kwabwino nthaŵi zonse. Ndinathokoza Yehova chifukwa cha dalitso labwino kwambiri limenelo.
Komabe, podzafika nthaŵi imene Spencer anali ndi miyezi isanu ndi inayi, ndinayamba kuona kuti chinachake chinali cholakwika. Sanali kulabadira mawu kapena mapokoso ena. Kuti ndione ngati anali kumva, ndinali kuima penapake poti asandione ndiyeno ndinali kumenya ziwaya kapena zinthu zina. Nthaŵi zina anali kutembenuka, koma osati nthaŵi zonse. Pa kupimidwa kwake pamene anali ndi miyezi isanu ndi inayi, ndinakambitsirana nkhaŵa zanga ndi dokotala wake, koma ananditsimikizira kuti mwana wanga anali bwinobwino ndi kuti panalibe chilichonse cholakwika chodetsa nkhaŵa. Komabe, m’kupita kwa miyezi, sanali kulabadirabe kapena kutulutsa mawu.
Pakupimidwa kwake pamene anali ndi chaka chimodzi, ndinafotokozanso nkhaŵa zanga kwa dokotala. Kachiŵirinso, sanapeze chilichonse cholakwika, koma anati tikaonane ndi dokotala wa makutu. Ndinapita ndi Spencer kumeneko kuti akamupime, koma zimene anali kupeza zinali zosiyanasiyana. Ndinabwererako nthaŵi yachiŵiri ndi yachitatu, koma anangondiuza kuti zimene anali kupeza zinali zosiyanasiyanabe. Dokotalayo anaganiza kuti pamene Spencer anali kukula, kupimidwa kwake kudzadziŵika bwino. Zaka zitatu zoyambirira za moyo wa mwana ndizo zofunika kwambiri kuti adziŵe chinenero. Ndinayamba kudera nkhaŵa kwambiri. Ndinapitiriza kufunsa dokotala wa makutu ponena za kupima kumene kungasonyeze zopezedwa zotsimikizirika. Potsirizira pake, anandiuza za kupima kumva mwa kupima ubongo kochitidwa ku Chipatala cha Maso ndi Makutu cha Massachusetts.
Ndinathedwa Mphamvu
Mlungu wotsatirapo tinapita kuchipatalacho ku Boston. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andipatse nyonga ya kuchita ndi zilizonse zimene anali kudzapeza. Mumtima mwanga ndinali kulingalira kuti Spencer anali wogontha wamba ndi kuti chothandizira kumva ndicho chokha chimene chingafunikire. Ha! mmene ndinalakwira nanga! Pambuyo pa kupimako, wopimayo anatiitana mu ofesi mwake. Zimene anapeza zinali zotsimikizirika: Spencer anali wogontha chifukwa cha vuto lalikulu la m’minyewa ya kuubongo. Pamene ndinafunsa chimene zimenezo zinatanthauza kwenikweni, iye anafotokoza kuti mwana wanga sanali wokhoza kumva zonena za munthu ndi zinthu zina zambiri. Izi si zimene ndinayembekezera kumva; ndinathedwa mphamvu.
Nthaŵi yomweyo, ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi zimenezi zinachitika motani? Kodi nchiyani chingakhale chitachititsa zimenezi?’ Ndinayamba kukumbukira pamene ndinali ndi pathupi ndi pamene ndinali kubala. Zonse zinayenda bwino. Spencer anali asanadwalepo matenda a m’makutu kapena matenda alionse aakulu ochititsidwa ndi kuzizira. Malingaliro anandichulukira! Kodi ndikanachitanji tsopano? Ndinaimbira foni a banja lakwathu ndi mabwenzi angapo ndi kuwauza zimene anapeza pakupima. Bwenzi langa lina lomwe lili Mboni linandilimbikitsa kuona zimenezi monga chitokoso; ndinayeneradi kuphunzitsa Spencer m’njira ina. Ndinayamikira Yehova kaamba ka nyonga yofunikirayo.
Kodi Nchiyani Chikanakhala Chabwino Koposa kwa Spencer?
Palibe chimene ndinali kudziŵa ponena za kulera mwana wogontha kapena chimene kugontha kunali. Kodi ndikalera motani mwana wanga ndi kulankhula naye mokwanira? M’maganizo mwanga munali malingaliro ndi nkhaŵa zambirimbiri.
Mlungu wotsatira tinabwerera kuchipatalako, ndipo tinakambitsirana zosankha zathu ndi wopimayo. Iye anafotokoza kuti njira imodzi, yogwiritsira ntchito mawu, inali yolinganizidwira kuphunzira kulankhula ndi luso la kudziŵa zimene zikunenedwa mwa kuyang’ana milomo. Njira ina inali ya kugwiritsira ntchito chinenero cholankhula ndi manja, chimene chili chinenero cha agonthi. Panali programu imene inali kudzapereka malangizo pa chinenero cholankhula ndi manja ndiyeno pambuyo pake kudzaloŵetsamo luso la kudziŵa zimene zikunenedwa mwa kuyang’ana milomo ndi maluso a kulankhula. Wopimayo ananenanso kuti kuli bwino kugwiritsira ntchito zothandizira kumva kuti zimthandizire kumva zochepa zimene mwana wanga anakhoza kumva. Ndiyeno tinapita kwa dokotala wa makutu wa kumaloko, amene anaika Spencer zomthandizira kumva. Pamene tinali kumeneko dokotala wa makutuyo ananena kuti Spencer angakhale wophunzira wabwino kwambiri wa njira yogwiritsira ntchito mawu.
Kodi nchiyani chikanakhala chabwino koposa kwa Spencer? Ndinalingalira za chimene chinalidi chofunika. Yehova amafuna kuti tizilankhulana ndi ana athu; zimenezi nzofunika kwambiri ngati tikufuna kukhala ndi moyo wa banja wachipambano. Tikanatha kulondola njira yogwiritsira ntchito mawu ndi kusumika maganizo pa kuphunzira kulankhula ndi luso la kudziŵa zimene zikunenedwa mwa kuyang’ana milomo. Zinali zotheka kuti Spencer akanaphunzira luso lake la kulankhula mpaka pamene ena akanatha kumamumva. Koma sitikanadziŵa zimenezo kwa zaka zambiri! Kodi tinafunikira kuchitanji tsopano? Tinasankha kugwiritsira ntchito chinenero cholankhula ndi manja.
Mwezi wotsatira Spencer analoŵa mu imene panthaŵiyo inkatchedwa kuti programu ya kulankhulana kokwanira. Ineyo ndi Spencer yemwe tinali kuphunzira chinenero cholankhula ndi manja choyambirira, ndipo Spencer anali kuphunzitsidwanso kulankhula Chingelezi ndi kudziŵa zimene zikunenedwa mwa kuyang’ana milomo. Anandisonyeza mmene ndingaphunzitsire mwana wanga. Panapita miyezi, ndipo Spencer anali kupita bwino patsogolo. Komabe, ndinali kukhalabe ndi nthaŵi zimene ndinali kumva kukhala wothedwa mphamvu. Ndinalefulidwa pamene ndinamva ana ena akunena kuti “Mama” kapena kuphunzira kunena kuti “Yehova.” Komano ndinali kudzifunsa kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji ndikumva chonchi? Mwana wanga ngwachimwemwe ndi wathanzi.’ Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kuyamikira mwaŵi wa kukhala ndi mwana wabwino ameneyu.
Pamene Spencer anali ndi zaka ziŵiri zakubadwa, tinapanga makonzedwe akuti tikapezeke pamsonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova umene programu yake ikatembenuzidwa mu American Sign Language (ASL) [Chinenero Cholankhula ndi Manja cha ku America]. Ndinakambitsirana za kulefulidwa kwanga ndi aŵiri ena okwatirana amene anagwirapo ntchito ndi Mboni zogontha kwa zaka zambiri. Iwo anandiuza za misonkhano ya Mboni za Yehova ya ASL ya mwezi ndi mwezi yochitidwa ku Massachusetts nandilimbikitsa kupita kumeneko.
Ndinatsatira uphungu wawo, ndipo aŵirife ine ndi Spencer tinayamba kupezekapo. Kumeneko tinali ndi mwaŵi wa kukumana ndi kuchitira zinthu pamodzi ndi ogontha achikulire. Ku mpingo wathu wachingelezi, Spencer sanapindule kwenikweni ndi misonkhano. Ankangomamatira kwa ine, popeza ndine ndekha amene ndinali wokhoza kulankhula naye. Kugwiritsidwa mwala kwake pamisonkhano imeneyi kunali kuwonjezereka pamene anali kukula, ndipo khalidwe lake linaipa. Komabe, pamene tinapita kumisonkhano yochitidwa m’chinenero cholankhula ndi manja, zimenezi sizinali choncho. Iye ankatha kuchita zinthu ndi aliyense mwaufulu popanda kudzera mwa amayi wake monga womasulira. Anakhala ndi maunansi ofunika kwambiri ndi anthu a mumpingo. Tonsefe aŵiri tinawongolera kugwiritsira kwathu ntchito chinenero cholankhula ndi manja, ndipo ndinaphunzira mmene ndingakhalire mphunzitsi wabwino kwambiri pa phunziro lathu la Baibulo lapanyumba. Zinali zabwino chotani nanga! Tsopano, kwa nthaŵi yoyamba, kumisonkhano ndinali kukhala ndi mwana wanga ndi kungokhala AMAYI wake m’malo mwa kukhala womasulira wake!
Nthaŵi ya Kusintha Kwakukulu kwa Ine
Ndi chivomerezo cha mwamuna wanga, pamene Spencer anali ndi zaka zitatu zakubadwa, ndinamloŵetsa m’programu ya ana ogontha, yochitidwa pa sukulu ina ya boma. Misonkhano ya kagulu yophunzitsa makolo inali kuchitidwa, ndipo ndinagwiritsira ntchito mwaŵiwu kuphunzira zowonjezereka. Pamsonkhano wina gulu la achikulire ndi achichepere ogontha linakambitsirana ndi omvetsera. A m’gululo anafotokoza kuti sanali kulankhulana mokwanira kapena kusalankhulana kumene ndi makolo awo kapena mabanja akwawo. Pamene ndinawafunsa chifukwa chake, anayankha kuti makolo awo sanaphunzire chinenero cholankhula ndi manja, chotero sanakhoze kulankhulana mokwanira ndi makolo awo ponena za moyo, malingaliro awo, kapena zinthu zowakondweretsa. Zinaoneka kuti sanamve kukhala mbali ya mabanja awo.
Imeneyi inali nthaŵi ya kusintha kwakukulu kwa ine. Ndinalingalira za mwana wanga. Ndinalephera kumyerekezera akukula ndi kuchoka panyumba osakhalapo ndi unansi ndi makolo ake. Ndinatsimikiza mtima kwambiri kuposa ndi kale lonse kuti ndidzapitiriza kuwongolera luso langa la chinenero cholankhula ndi manja. M’kupita kwa nthaŵi, ndinazindikira mowonjezereka kuti chosankha cha kugwiritsira ntchito chinenero cholankhula ndi manja ndicho chinali chabwino koposa kwa ife. Chinenero chake chinapitirizabe kukula, ndipo tinali kukambitsirana nkhani iliyonse, monga “Kodi tidzapita kuti patchuthi?” kapena “Kodi ukufuna kudzakhala chiyani utakula?” Ndinazindikira kuti ndikanaphonya zambiri ngati ndikanayesa kudalira pa kulankhulana ndi mawu.
Pa zaka zisanu zakubadwa, Spencer anaikidwa m’kalasi yokhazikika ya ana akumva ndi mphunzitsi wokhoza kulankhula ndi manja. Anakhala m’programu imeneyi kwa nthaŵi yaitali ya zaka zitatu. Anada sukulu, ndipo kunali kovuta kumuona akupita m’mavuto aakulu ameneŵa. Koma chabwino chinali chakuti ndinali wokhoza kulankhula naye pamene tinayesa njira zosiyanasiyana zolimbanirana ndi kugwiritsidwa mwala kwake. Komabe, potsirizira pake, ndinaona kuti programu imeneyi pasukulu ya boma sinali yabwino kaamba ka ulemu wake waumwini kapena kupita kwake patsogolo m’maphunziro.
Mu 1989 ukwati wanga unatha. Tsopano ndinali kholo losakwatiwa lokhala ndi mwana wamwamuna wa zaka zisanu ndi chimodzi amene anali kudziŵa mofulumira chinenero chake cholankhula ndi manja. Ngakhale kuti ndinali kulankhula naye, ndinadziŵa kuti ndinafunikira kuwongolera luso langa la ASL kuti ndisunge ndi kulimbitsa kulankhulana pakati pathu.
Nthaŵi ya Kusamuka
Ndinafufuza maprogramu ambiri a ana ogontha m’maboma angapo ndi kupeza sukulu ku Massachusetts kumene ASL ndi Chingelezi chomwe zinali kugwiritsiridwa ntchito mu imene amati ndi njira ya zinenero ziŵiri. Ndiponso, ndinauzidwa kuti posachedwa m’dera la Boston mudzakhala mpingo wa Mboni za Yehova wa ASL, ndipo bwenzi lina linapereka lingaliro lakuti tisamukire kumeneko. Monga kholo lokhala lokha, lingaliro losamuka kuchoka panyumba pathu ndi kusiya banja ndi mabwenzi ku midzi ya New Hampshire kupita kudera la mzinda waukulu linali lovuta kulilandira. Nayenso Spencer ankasangalala kukhala kunja kwa mzinda. Komabe, panali zinthu ziŵiri zimene ndinayenera kuzilingalira. Spencer anafunikira kukhala pasukulu pamene aphunzitsi ndi ophunzira onse anali kulankhulana mosavuta m’chinenero cholankhula ndi manja, ndipo ndinaona kuti kunali bwino kwambiri kukhala mumpingo wa Mboni zina zogontha.
Tinasamuka zaka zinayi zapitazo, pamene Spencer anali ndi zaka zisanu ndi zinayi. Posakhalitsa, Mpingo wa Chinenero Cholankhula ndi Manja ku Malden, Massachusetts, unapangidwa, ndipo kuyambira pamenepo, Spencer wapita patsogolo kwambiri. Khalidwe lake lawongokera kwambiri, ndipo amasangalala kukhala pamisonkhano. Ndimasangalala kwambiri kumuona akulankhulana ndi kupanga maunansi ndi ena. Abale ndi alongo ogontha mumpingo ali zitsanzo zabwino kwambiri zoti mwana wanga atsanzire, akumamthandiza kuona kuti iyenso angafitse zonulirapo zauzimu. Ndipo wachitadi zimenezi. Tsopano amapereka nkhani mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndipo akutumikira monga wofalitsa wosabatizidwa. Iye wanena kuti akufuna kubatizidwa.
Ndimasangalala chotani nanga mu utumiki, kumuona akufotokoza chikhulupiriro chake kwa anthu ena ogontha, m’chinenero cholankhula ndi manja! Wakulitsadi kudzilemekeza kwake. Spencer wandiuza zimene amalingalira ponena za mpingowo. Anati: “Kwathu ndi kuno. Abale ndi alongo amatha kulankhula nane.” Mwana wanga samandipemphanso kuchoka misonkhano itangotha. Tsopano ndimayenera kumuuza kuti ndi nthaŵi yoti tichoke pa Nyumba ya Ufumu!
Kusukulu imene amapitako tsopano, Spencer amalankhula mosavuta ndi ana ena ogontha. Makambitsirano ake ndi iwo athandiza kuona kusiyana pakati pa lingaliro la dziko la ana ndi lingaliro la Yehova la iwo. Ineyo ndi Spencer timalankhulana momasuka ndipo tili ndi unasi wathithithi, mogwirizana ndi mapulinsipulo a Baibulo. Pamene abwera kuchokera kusukulu masana, timachitira limodzi homuweki yake. Timapitira limodzi kumisonkhano yathu ndi ku utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Komabe, Spencer amatha kuona kuti si ana onse a kusukulu kwake amene ali ndi unansi wathithithi umenewu ndi makolo awo.—Akolose 3:20, 21.
“Timalankhula za Zilizonse”
Pafupifupi chaka chimodzi chapitacho, ndinaona Spencer akundiyang’ana monga ngati kuti anali kufuna kundiuza kenakake. Ndinamfunsa ngati panali chimene anali kufuna. “Ayi,” anayankha motero. Ndinamfunsa mafunso angapo ponena za mmene zinthu zinalili kusukulu ndi zina zotero. Ndinadziŵa kuti pali kenakake kamene anafuna kundiuza. Ndiyeno, mkati mwa phunziro lathu la banja la Nsanja ya Olonda, ananena kuti, “Kodi mukudziŵa kuti ena a makolo a ophunzira a kusukulu kwanga sadziŵa chinenero cholankhula ndi manja?” Ndinamuyang’ana modabwa. “Ndikunenetsa,” iye anatero. “Pali makolo amene sangalankhule ndi ana awo.” Anafotokoza kuti makolo ena anafika kusukuluko ndi kuti anawaona akusonyasonya ndi kuyerekezera ndi thupi lawo zimene anali kufuna kunena poyesayesa kulankhula ndi ana awo. “Ndili ndi mwaŵi kwambiri kuti munaphunzira chinenero cholankhula ndi manja. Timatha kulankhulana. Simumangosonyasonya; timalankhula za zilizonse.”
Mmene zinandikhudzira mtima nanga zimenezi! Ambiri a ife sitimayamikira zoyesayesa za makolo athu kufikira titakula. Koma pano, pamsinkhu wa zaka 12, mwana wangayu anali kundiuza mmene analili woyamikira kuti tinali ndi kulankhulana kwatanthauzo.
Monga amayi, chimodzi cha zonulirapo zanga chinali kukhala ndi unansi wabwino ndi mwana wanga ndi kukhala woyandikana naye. Mwina zimenezi sizikanachitika ngati sindinaphunzire chinenero cholankhula ndi manja. Kudzipatulira kwanga kwa Yehova kunandisonkhezera kulingalira mwamphamvu za mathayo anga monga kholo; zimenezi zinachititsa zosankha zofunika za kulankhulana kukhala zosavuta kwambiri. Tonsefe aŵiri tapindula mwauzimu chifukwa cha zosankha zimenezi. Mawu a pa Deuteronomo 6:7 ngofunika chotani nanga, pamene makolo akuuzidwa kuuza ana awo malamulo a Yehova ‘pokhala pansi m’nyumba zawo, ndi poyenda iwo panjira, ndi pogona iwo pansi, ndi pouka iwo.’ Ndilidi woyamikira kuti ineyo ndi Spencer timalankhulana momasuka ponena za “zazikulu za Mulungu.” (Machitidwe 2:11)—Yosimbidwa ndi Cindy Adams.
[Mawu Otsindika patsamba 10]
‘Ndinalephera kumyerekezera akukula popanda kukhala ndi unansi ndi makolo ake’