Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 1/8 tsamba 16-20
  • M’khichini Mungakhale Mosangalatsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • M’khichini Mungakhale Mosangalatsa
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuphunzira “m’Kalasi” ya m’Khichini
  • Kuphika Nkosangalatsa!
  • Umodzi wa m’Banja
  • 2. Muziyesetsa Kukhala Aukhondo
    Galamukani!—2012
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Mmene Mungatetezere Ana Anu
    Galamukani!—2007
  • Udindo Wanu Monga Kholo
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 1/8 tsamba 16-20

M’khichini Mungakhale Mosangalatsa

“TATULUKA m’khichini muno!” Ana ambiri anjala adzudzulidwa choncho pofuna kuti alaŵiretu chakudya chamadzulo. Komabe, makolo ayenera kuitanira ana awo m’khichini, m’malo mwa kuwaingitsira kunja. Chifukwa nchiyani? Chifukwa nchakuti khichini ndi kalasi yosangalatsa.

M’khichini ndi malo amene ana angaphunziremo maluso a kupangapanga zinthu ndi njira zothetsera mavuto, malo amene angaphunziremo kutumikira ena ndi kugwira ntchito monga mbali ya gulu, malo amene makambitsirano aphindu ogwira mtima angachitike mwachibadwa, malo ophunzitsira mikhalidwe yofunika mwakachetechete. Inde, m’makabati odzaza zinthu, madulowa, ndi m’mashelefu a khichini iliyonse muli maphunziro amtengo wapatali—ongoyembekezera kuperekedwa pokonza chakudya chotsatira.

M’nyengo ino ya zasayansi ndi chidziŵitso, nkugwiritsiranji ntchito khichini monga malo ophunzitsira ana? Yankho ndilo nthaŵi. Makolo ambiri amazindikira kuti palibiretu chimene chingaloŵe m’malo nthaŵi imene amacheza ndi ana awo—njochuluka!a Koipeza ndilo vuto. Akatswiri ena amalimbikitsa makolo kulingalira ntchito imene amagwira masiku onse pakhomo monga mwaŵi wochita zinthu limodzi ndi ana awo ndi kumawaphunzitsa. Izi zikugwirizana ndi lamulo limene Mulungu anapatsa makolo m’mtundu wa Israyeli wakale: “Ndipo mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.”—Deuteronomo 6:6, 7.

Popeza kuti kaŵirikaŵiri timathera nthaŵi m’khichini, akuoneka kukhala malo oyenera ogwiriramo ntchito pamodzi monga banja. Mosiyana ndi maulendo apadera okacheza, amene kaŵirikaŵiri amafunikira kudikira mpaka titapeza nthaŵi, nyonga, kapena ndalama kuti tiwalinganize, chikhumbo cha chakudya sichinganyalanyazidwe. Kuonjezera pa izo, khichini ili ndi chikoka chachibadwa kwa ana. Ndiiko komwe, ndi kuti kwinanso kumene iwo angaphunzitsidwe kugwiritsira ntchito mipeni mosamala ndi ziŵiya zina? Ana poseŵera angaonongenso zinthu nthaŵi zina! Komabe, kodi ndi maphunziro otani amene angaperekedwe m’khichini?

Kuphunzira “m’Kalasi” ya m’Khichini

Louise Smith—wodziŵidwa ndi ophunzira ake a zaka zinayi zakubadwa monga Mayi wamakeke—ananena mawu otsatiraŵa mwa chidziŵitso chake cha zaka 17 za kuphunzitsa ana kuphika: “Chakudya ndi chiŵiya chachikulu chophunzitsira chifukwa ana onse amachidziŵa. Mphamvu zawo zonunkhizira, zolaŵira, ndi zokhudzira nzakuthwa kwambiri pausinkhu waubwana kwakuti amakhala atcheru ndithu. Ndipo mungaphunzitse kuŵerenga, masamu, ndi maluso othetsera mavuto kupyolera m’chakudya.” Kutsanula, kusinja, kusenda, kupepeta, kutakasa, ndi kupiringa zimathandiza ana kukulitsa luso lamanja ndi kugwirira limodzi kwa maso ndi manja. Kusankha (kupatula sawawa ndi mtedza) ndi kupima (ndi makapu opimira) kumaphunzitsa malingaliro amene amachita monga njerwa zomangira pophunzira masamu. Kutsatira malangizo a kaphikidwe ndiko njira yogwiritsirira ntchito manambala, milingo, kusunga nthaŵi, luntha ndi chinenero. Ndipo wina sangangoloŵa ntchito ya m’khichini yovuta ndi yangozi zochuluka imeneyi popanda kuphunzira kanthu kena ponena za kusamala, thayo, kulinganizika kwaumwini, ndi kugwira ntchito ndi ena.

Chosayenera kunyalanyizidwa ndicho kuphunzira kuphika. Si zachilendo kuti ana amene amayamba mwa kuthandiza m’khichini akhale okhoza kukonza zakudya pamene afika m’zaka zawo zaunyamata. Ndi kholo lotanganitsidwa lotani limene silingamayamikire zimenezo nthaŵi ndi nthaŵi? Ndiponso, kuphika kumathandiza achichepere kukulitsa chidaliro ndi kukhala odzichirikiza—mikhalidwe imene idzawapindulitsa pamene asenza mathayo auchikulire pambuyo pake, kaya adzakwatira kapena kukhalabe mbeta.—1 Timoteo 6:6.

Lee, yemwe anakhalabe mbeta mpaka kupyola pa zaka 30, amakumbukira kuti: “Mayi wanga anayamba kundiphunzitsa ntchito zamasiku onse za m’khichini pamene ndinali pafupifupi ndi zaka zisanu ndi chimodzi zakubadwa. Poyamba ndinakonda kupanga mabisiketi, makeke, ndi maswiti ena. Koma pofika zaka zisanu ndi zinayi, ndinali wokhoza kukonza chakudya cha banja lathu, ndipo ndinali kumatero kaŵirikaŵiri. Pambuyo pake, monga mbeta yachikulire, ndinaona kuti kudziŵa kuchita ntchito zosiyanasiyana zapanyumba, kuphatikizapo kuphika, kunapangitsa moyo kukhala wosavuta. Ndipo ndingaterodi kuti zimenezi zawonjezera chisangalalo changa muukwati wachipambano.”

Kuphika Nkosangalatsa!

Kodi kholo lingapeze motani nthaŵi yophunzitsa ana m’khichini? Nakubala wina analimbikitsa kulinganiza ndandanda ya nthaŵi yokhala ndi zododometsa zochepa. Ngati muli ndi ana angapo, mungafune kugwira ntchito ndi mwana mmodzi pa nthaŵi imodzi ngati iwo akungoyamba kumene. Kuti muchite zimenezi, sankhani nthaŵi pamene ana ena akupuma chogona kapena pamene ali kusukulu. Konzekerani kutayirapo nthaŵi yochulukirapo kuposa imene mumataya ngati mukuphika nokha. Ndipo konzekerani kukhala ndi chisangalalo m’khichini!

Paphunziro lanu loyamba, mungamlole mwana wanu kusankha kanthu kena kamene amakonda kudya. Sankhani njira ya kaphikidwe yosavuta imene ili ndi zotulukapo zamwamsanga. Tsimikizirani kuti ili ndi zochita zimene angakhoze kutsiriza. Kuti musampangitse mwana wanu kujijirika ndi kunyong’onyeka, mloleni kuti apezeretu pasadakhale zofuna kuphikidwazo ndi miphika. Mwinamwake pasadakhale mungakonzeretu pang’ono zina za zinthu zofuna kuphikazo kuti nthaŵi yophikayo isatalike kwambiri kapena kukhala yotopetsa.

Ŵerengani pamodzi ndi mwana wanu malangizo akaphikidwewo, mukumamsonyeza mmene angachitire ntchito iliyonse. Mpatseni mwananu malo akeake m’khichinimo—kapena dulowa yokhala ndi mabeseni angapo ndi ziŵiya zoŵerengeka—ndipo mpatseni apuloni. M’malo mwakuti mnyamata avale apuloni ya mkazi, mpatseni ina yopangidwira khukhi wachimuna. Kungochokera kuchiyambi, gogomezerani kufunika kwa kusamala ndipo ikani malamulo oyenera a m’khichini.—Onani bokosi lakuti “Phunziro Loyamba—Kusamala,” tsamba 18.

Koposa zonse, yesani kukupangitsa kukhala kosangalatsa. Musati mwananu azingokuyang’anani iyayi; nasambe m’manja, ndipo akhale ndi chochita pa ntchitoyo yokonza chakudya. Mpatseni mpata woti atulukire zatsopano mwa kuyesa ndi kufunsa mafunso. Ndipo ngati chakudyacho sichinaphikike bwino, musadandaule iyayi. Ngati mwananu wachiphika yekha, adzafunabe kuchidya!

Umodzi wa m’Banja

Mosakayikira, mapindu aakulu amene angachokere m’khichini amaphatikizapo kugwirizana ndi makhalidwe abwino abanja. Mungakhale mutazindikira kuti m’mabanja ena lero, ziŵalo za banja zimatanganitsidwa ndi zochita zapaokha, popanda kwenikweni kuchitira pamodzi zinthu. M’mikhalidwe yoteroyo, panyumba pamangokhala ngati malo opumira, pongodyera chakudya. Mosiyana ndi zimenezo, banja limene limaphikira pamodzi limadyeranso pamodzi ndi kutsuka mbale limodzi. Zochita zimenezi zimawapatsa mipata yakaŵirikaŵiri yolankhulana, kusamalana, ndi kuyandikana wina ndi mnzake. “Ndinali ndi makambitsirano abwino koposa ndi anyamata anga pasinki m’khichini,” nakubala wina anakumbukira choncho. Ndipo Hermann, atate wachikristu anawonjezera kuti: “Tinachita dala kusakhala ndi makina otsuka mbale kwa zaka zingapo, kotero kuti mbale zinayenera kumatsukidwa ndi kupukutidwa pamanja. Ana athu tinawapatsa ntchito yomapukuta, akumasinthana. Panalibe nthaŵi yabwino kuposa imeneyo yolankhulana momasuka.”

Inde, nthaŵi imene mumathera m’khichini ndi ana anu—mlungu ndi mlungu, chaka ndi chaka—imapereka maziko okulitsirapo makhalidwe abwino auzimu ndi mikhalidwe yaumulungu. Ndi mkati mwa mphindi zomasuka zoterozo zaumodzi mmene makambitsirano ochokera mumtima angachitike mwachibadwa pakati pa kholo ndi mwana ndipo chisonkhezero cha chitsanzo cha kholo chingakhudze mtima wa mwanayo. Kuphunzitsa koteroko kungampindulitse mwana kwa moyo wake wonse, pakuti Miyambo 22:6 imati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”—Miyambo 22:6.

Chotero, monga kholo ngati mukufunafuna njira yothera nthaŵi yochuluka ndi ana anu, bwanji osawapempha akuthandizeni kukonza keke kapena chakudya? Mudzaona kuti kugwira ntchito limodzi nawo m’khichini ndiyo njira yodyetsera ndiponso yosamalira banja lanu.

[Mawu a M’munsi]

a Onani mafotokozedwe ankhaniyi pamutu wakuti: “‘Quality Time’ Doled Out in Limited Quantities,” m’kope la Galamukani! wachingelezi wa May 22, 1993, masamba 16-17.

[Bokosi patsamba 18]

Phunziro Loyamba—Kusamala

Khalani Wosamala

• Mwamphamvu komabe osati moopseza, fotokozani ngozi zakugwira ntchito m’khichini, monga mmene mukanafotokozera ngozi zapamsewu wochuluka magalimoto. Sonyezani chitsanzo chabwino inu mwininu.

• Yang’anirani ana pamene akugwira ntchito m’khichini. Musalole mwana kugwiritsira ntchito chotengera kapena chiŵiya, makamaka chamagetsi, kufikira pamene angathe kuchigwiritsira ntchito mosamala.

• Sungani khichini yanu ili yaudongo. Pukutani madzi ndi kusesa nyenyeswa mwamsanga. Zifuyo ndi zododometsa zina ziyenera kukhala panja pamene mukuphika.

Samalani Zala

• Makina amagetsi osakanizira (mixers, kapena blenders, ndiponso foodprocessors) angagwiritsiridwe ntchito kokha ngati wachikulire akuyang’anira. Tsimikizirani kuti makinawo azimitsidwa mwana wanu asanatakase zili m’mbale yamakinawo.

• Mipeni ikhale yakuthwa, popeza kuti mpeni wobuntha umafunikira mphamvu choncho ungangoterezuka.

• Ngati mwananu akuphunzira kugwiritsira ntchito mpeni, onani kuti akutsatira masitepe awa: (1) atenge mpeni mwa kugwira chigwiriro chake, (2) akhazike mpeni pa chakudya, (3) aike dzanja linalo pamsana pa mpeni, ndipo (4) asindikize kuti adule chakudyacho.

• Gwiritsirani ntchito thabwa lodulirapo. Kuti kabichi, anyenzi, ndi matomato zisakunkhunizike mmene mwana wanu akuyesa kudula, zitemeni pakati ndi kukhazika mbali yadeteyo pa thabwa lodulirapo.

Samalani Musapse

• Nthaŵi zonse zimitsani chitofu ndi uvuni pamene sizikugwira ntchito. Chotsani mathaulo, ndi nsalu zina pafupi ndi chitofu.

• Lozetsani zigwiriro zamiphika chapakatikati pa chitofu, pamene siingagundidwe mokhweka nkukhutuka.

• Ngati mulola mwana wanu kugwira ntchito pa chitofu, tsimikizirani kuti waimirira pachopondapo chokhazikika bwino.

• Musanyamule chinthu chotentha musanadziŵe kale pamene mudzachikhazika. Tsimikizirani kuti enanso m’khichinimo adziŵa kuti mwanyamula chinthu chotentha, makamaka ngati muti mudzere chakumbuyo kwawo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena