Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 2/8 tsamba 28-30
  • Kodi Ndiulule Tchimo Langa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndiulule Tchimo Langa?
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Palibe Chobisika’
  • Kuulula Tchimolo
  • Kuwauza Makolo Anu
  • Kuwafikira Akulu
  • ‘Ndikuwopa Kuchotsedwa’
  • Landirani Chilango cha Yehova Nthawi Zonse
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Mulungu Amafuna Kuti Tiziulula Ndiponso Kulapa Machimo Athu?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Muyenera Kuchita chiyani Ngati Mwachita Tchimo Lalikulu?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Ndingasiye Motani Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri?
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 2/8 tsamba 28-30

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndiulule Tchimo Langa?

“Ndili ndi manyazi kwambiri, kaya ndichite bwanji kaya. Ndikufuna kupita kwa makolo anga, koma ndili ndi manyazi kwabasi.”—Lisa.a

ANALEMBA choncho mtsikana wina wovutika maganizo. Anali atapalana ubwenzi ndi wosakhulupirira kwa nyengo ya zaka zingapo pamene tsiku lina, ataledzera moŵa, anagona naye.

Mwachisoni, zinthu zoterozo zimachitika kaŵirikaŵiri, ngakhale pakati pa achichepere achikristu. Pamene tili ocheperapo ndi opanda chidziŵitso, timapanga zolakwa zambiri. Koma pamene kuli kwakuti kuchita cholakwa chaching’ono sinkhani yaikulu, kuchita tchimo lalikulu monga chisembwere, ndi nkhani yaikuludi. (1 Akorinto 6:9, 10) Pamene zimenezo zichitika, wachichepere ayenera kupeza chithandizo. Vuto ndilo lakuti sikwapafupi kuulula machimo ako.

Mtsikana wina wachikristu wosakwatiwa anachita dama. Anasankha kuulula tchimo lake kwa akulu ampingo, naika ndi deti pamene akanatero. Komano analikankhira detilo patsogolo. Pambuyo pake, nkulikankhiranso detilo patsogolo. Posakhalitsa, chaka chathunthu chinapita!

‘Palibe Chobisika’

Ngati mwagwera m’tchimo lalikulu, mufunikira kuzindikira kuti kukhala chete silingaliro labwino. Chifukwa china nchakuti choonadi chimadzavumbulukabe basi. Adakali mwana wamng’ono, Mark anaswa chokometsera chadothi chapakhoma. “Ndinayesa kuchimatiranso mosamala,” amakumbukira choncho, “koma sipanapite nthaŵi kuti makolo anga aone ming’alu yake.” Zoona, simulinso mwana. Koma makolo ambiri angaone pamene kanthu kena kalakwika mwa ana awo.

“Ndinayesa kubisa mavuto anga ndi mabodza,” akuvomereza choncho Ann wazaka 15, “koma ndinapeza kuti ndinali kungoipitsa zinthu.” Kaŵirikaŵiri, maboza amavumbulika. Ndipo pamene makolo anu aona kuti munawanamiza, angakhumudwe—kukhumudwanso kwambiri kuposa mmene akanachitira ngati mukanangowalunjika.

Chofunikanso kwambiri nchakuti Baibulo limati: “Pakuti palibe chinthu chobisika, chimene sichidzakhala choonekera; kapena chinsinsi chimene sichidzadziŵika ndi kuvumbuluka.” (Luka 8:17) Yehova amadziŵa chimene tachita ndi chimene tikuchita. Simungathe kudzibisa ngati Adamu analephera. (Genesis 3:8-11) Posakhalitsa, machimo anu angadziŵidwenso ndi ena.—1 Timoteo 5:24.

Kukhala chete kungakuvulazeni m’njira zinanso. Wamasalmo Davide analemba kuti: “Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse. Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine.” (Salmo 32:3, 4) Inde, nkhaŵa ya kuyesa kusunga chinsinsi ingasautse mtima. Nkhaŵa ndi liwongo, ndiponso kuwopa kuvumbulidwa, kungakudzetsereni chisoni. Mungayambe kumatalikirana ndi mabwenzi ndi banja. Mungamvenso ngati kuti Mulungu mwiniyo wakutayani! “Ndinali kulimbana ndi chikumbumtima chaliwongo chifukwa ndinamkwiyitsa Yehova,” analemba choncho wachichepere wotchedwa Andrew. “Chinali kundilasa mumtima.”

Kuulula Tchimolo

Kodi pali njira ina iliyonse yopezera mpumulo pa kusautsika mtima kumeneku? Inde, ilipo! Wamasalmo anati: “Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa.  . . Ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.” (Salmo 32:5; yerekezerani ndi 1 Yohane 1:9.) Mofananamo Andrew anapeza mpumulo weniweni ataulula tchimo lake. Amakumbukira kuti: “Ndi mtima wonse ndinamfikira Yehova ndi kupemphera kuti andikhululukire.”

Nanunso mungachite zofananazo. Pempherani kwa Yehova. Akudziŵa zimene mwachita, koma modzichepetsa zivomerezeni kwa iye m’pemphero. Pemphani chikhululukiro, musaleke chifukwa choganiza kuti ndinu woipa kwambiri koti nkusakhoza kuthandizidwa. Yesu anafa kuti ife tikhale ndi kaimidwe kabwino ndi Mulungu ngakhale kuti ndife opanda ungwiro. (1 Yohane 2:1, 2) Mungapemphenso nyonga yopangira masinthidwe ofunikira. Kuŵerenga Salmo 51 kungakuthandizeni kwenikweni kumfikira Mulungu.

Kuwauza Makolo Anu

Komabe, pali zambiri zofunikira koposa chabe kungoululira Mulungu. Muyeneranso kuwauza makolo anu. Analamulidwa ndi Mulungu kukulerani “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Angachite zimenezo kokha ngati akudziŵa mavuto anu. Ndiponso, kuwauza makolo anu sikungakhale kwapafupi kapena kosangalatsa. Koma pambuyo pa kukhumudwa koyamba, angabweze mtima wawo. Mwinanso angakondwere kuti munawadaliradi mpaka kuwavumbulira vuto lanu. Fanizo la Yesu la mwana woloŵerera limanena za mnyamata yemwe analoŵerera m’chisembwere. Koma potsirizira pake pamene anadzaulula, atate wake anamlandira ndi manja aŵiri! (Luka 15:11-24) Mosakayikira makolo anu angakuthandizeninso. Ndi iko komwe, adakakukondani.

Zoona, mungawope kuti mudzakhumudwitsa makolo anu. Koma sikuulula tchimoko kumene kungakhumudwitse makolo anu; koma kuchita tchimolo nkumene kudzatero! Kuulula ndiko sitepe loyamba lowatonthoza. Ann, wotchulidwa poyamba paja, anauza makolo ake ndipo pambuyo pake anapeza mpumulo waukulu.b

Koma chopinga china cha kuulula ndicho manyazi ndi kugwa nkhope. Mlembi wokhulupirikayo Ezara sanawachita machimowo iye mwini, koma pamene anaulula machimo a Ayuda anzake, anati: “Ndigwa nkhope, ndi kuchita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga.” (Ezara 9:6) Ndithudi, nkoyenera kumva manyazi pamene mwachita cholakwa. Zimasonyeza kuti chikumbumtima chanu chikugwirabe ntchito. Ndipo pambuyo pa kanthaŵi malingaliro amanyaziwo adzacheperachepera. Andrew anati: “kuulula nkovuta kwambiri ndi kogwetsa nkhope. Koma kudziŵa kuti Yehova adzakhululukira koposa nkotsitsimula.”

Kuwafikira Akulu

Ngati muli Mkristu, nkhani sidzangothera pakuwauza makolo anu. Andrew akutero kuti: “Ndinadziŵa kuti ndinayenera kuwauza akulu ampingo vuto langa. Kunali kotsitsimula chotani nanga kudziŵa kuti iwo analipo kuti andithandize!” Inde, achichepere pakati pa Mboni za Yehova angathe ndipo ayenera kupita kwa akulu ampingo kuti akapeze chithandizo ndi chilimbikitso. Koma bwanji osangopemphera kwa Yehova basi nkuzisiyira pompo? Chifukwa nchakuti Yehova waikizira akulu thayo la ‘kulindirira moyo wanu.’ (Ahebri 13:17) Angakuthandizeni kupeŵa kugweranso m’tchimo.—Yerekezerani ndi Yakobo 5:14-16.

Musadzinyenge mwa kulingalira kuti mungadzithandize nokha. Ngati munalidi wolimba ndithu, ndiye bwenzi mutagweranso m’tchimolo ngati? Mwachionekere, mufunikira chithandizo cha wina. Molimba mtima Andrew anatero. Uphungu wake? “Ndikulimbikitsa aliyense amene wachita tchimo lalikulu kapena amene analichitapo, kuti atsegulire Yehova mtima wake ndiponso mmodzi wa abusa ake.”

Koma tsopano mkulu mungamfikire motani? Sankhani mmodzi yemwe muli womasuka naye. Mungayambe mwa kunena kuti: “Ndifuna kukuuzani kanthu kena” kapena “Ndili ndi vuto” kapena ngakhale “Ndili ndi vuto ndipo ndifuna kuti mundithandize.” Kukhala kwanu woona mtima ndi womasuka kudzasonyezadi kulapa kwanu ndi chikhumbo chanu cha kusintha.

‘Ndikuwopa Kuchotsedwa’

Bwanji nanga za kuthekera kwa zimenezo? Nzoona kuti kuchita tchimo lalikulu kumampangitsa munthu kuyenera kuchotsedwa, koma sizimangochitika iyayi. Kuchotsedwa nkwa aja amene amakana kulapa—amene amakana mouma khosi kusintha. Miyambo 28:13 imati: “Wobisa machimo ake sadzaona mwaŵi; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.” Kuwafikira kwanu akulu kuti akuthandizeni ndi umboni wa chikhumbo chanu cha kusintha. Kwenikweni akulu ndi ochiritsa, osati olanga iyayi. Ali ndi thayo la kuchita ndi anthu a Mulungu mwachifundo ndi ulemu. Akufuna kukuthandizani ‘kulambula misewu yolunjika yoyendamo mapazi anu.’—Ahebri 12:13.

Zoona, pamene pali chinyengo kapena kubwerezabwereza cholakwa chachikulu, “ntchito” zokhutiritsa “zoyenera kutembenuka mtima” zikusoŵeka. (Machitidwe 26:20) Nthaŵi zina kuchotsa kumakhalapo. Ngakhale ngati wolakwayo alapa, akulu amakakamizika kupereka chilango china chake. Kodi muyenera kupsa mtima kapena kuŵaŵidwa ndi chosankha chawocho? Pa Ahebri 12:5, 6 Paulo akulangiza kuti: “Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye, kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye; pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, nakwapula mwana aliyense amlandira.” Chilango chilichonse chimene mungalandire, chioneni monga umboni wakuti Mulungu amakukondani. Kumbukirani kuti kulapa kwenikweni kudzatipangitsa kukhala ndi unansi wabwino ndi Atate wathu wachifundo, Yehova Mulungu.

Zimafuna kulimba mtima kuti uvomereze machimo ako. Koma mwakutero, mungawongole zinthu osati ndi makolo anu okha komanso ndi Yehova Mulungu mwiniyo. Musalole mantha, kunyada, kapena manyazi kukuletsani kupeza chithandizo. Kumbukirani: Yehova “adzakhululukira koposa.”—Yesaya 55:7.

[Mawu a M’munsi]

a Maina ena asinthidwa.

b Ponena za chidziŵitso cha mmene mungawafikire makolo anu, onani mutu 2 wa buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mawu Otsindika patsamba 30]

‘Ndikulimbikitsa onse amene anachimwapo kutsegulira Yehova mitima yawo.’—Andrew

[Chithunzi patsamba 29]

Kuululira makolo anu kungakuchizeni mwauzimu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena