Lingaliro la Baibulo
Kodi Nkulakwa Kudya Nyama?
“TAONANI, NDAKUPATSANI INU THERERE LONSE LAKUBALA MBEWU LILI PADZIKO LAPANSI, NDI MITENGO YONSE MMENE MULI CHIPATSO CHA MTENGO WAKUBALA MBEWU; CHIDZAKHALA CHAKUDYA CHA INU.”—Genesis 1:29.
SUJATA wazaka 18 zakubadwa, wochokera m’banja lachihindu losadya nyama, anavomereza lamulo la Mulungu la zakudya lopatsidwa kwa munthu woyamba, Adamu. Koma kenaka anafunsa kuti: “Nchifukwa ninji nanga anthu amapha nyama ndi kudya pamene kuli kwakuti pali zinthu zina zambiri zakudya?”
Anthu ambiri padziko lonse lapansi amapereka malingaliro ofananawo. Anthu mamiliyoni mazana ambiri m’maiko a Kummaŵa safuna nyama m’zakudya zawo. Ndiponso, chiŵerengero cha anthu osadya nyama m’maiko a Kumadzulo chikukwera. Ku United States kokha, anthu pafupifupi 12.4 miliyoni amanena kuti sakudya nyama, kuposerapo ndi mamiliyoni atatu m’zaka khumi zapitazo.
Kodi nchifukwa ninji anthu ambiri safuna nyama m’zakudya zawo? Nanga moyo wa nyama kwenikweni tiyenera kuuona motani? Kodi kudya nyama kumasonyeza kusalemekeza moyo? Malinga nzimene zikunenedwa pa Genesis 1:29, kodi tingati nkulakwa kudya nyama? Choyamba, tiyeni tione chifukwa chimene ena sadyera nyama.
Kodi Nchifukwa Ninji Ena Sakudya Nyama?
Kwa Sujata, zakudya zake zimagwirizana ndi zikhulupiriro za chipembedzo chake. “Ndinakula monga Mhindu, wokhulupirira chiphunzitso cha kubadwanso kwa munthu,” iye akufotokoza motero. “Popeza kuti mzimu wa munthu ungabwerenso mumpangidwe wa nyama, ndimaona kuti nyama ndi ine ndife amodzi. Choncho sibwino kuzipha monga chakudya.” Zipembedzo zina zimavomerezanso kusadya nyama.
Kuwonjezera pa zikhulupiriro za chipembedzo, pali zifukwa zina zimene zimasonkhezera anthu kusankha zakudya. Mwachitsanzo, Dr. Neal Barnard, akutsimikiza kotheratu kuti: “Zifukwa zenizeni zodyera nyama ndizo chizoloŵezi kapena umbuli.” Iye akutero chifukwa chakuti akulingalira mavuto a thanzi amene amabwera chifukwa chakudya nyama, monga matenda a mtima ndi kansa.a
Ku United States, kwanenedwa kuti achinyamata osadya nyama akuwonjezereka kwambiri. Chifukwa chimodzi chochitira izi ndicho kuchitira nyama chifundo. “Ana ang’onoang’ono amakonda nyama,” akutero Tracy Reiman wa m’bungwe la People for the Ethical Treatment of Animals [Bungwe Lowonetsetsa Kuti Nyama Zikukhala Mwaufulu]. “Atayamba kuphunzira za zimene zimachitikira nyama asanaziphe kuti zikhale chakudya, izi zimakulitsa chifundo chawo.”
Anthu ambiri ozindikira kufunika kwa zinthu za chilengedwe nawonso akunena kuti kuŵeta nyama kaamba ka chakudya kumawonongetsa kwambiri zinthu za chilengedwe. Mwachitsanzo, pamafunika malita 3,300 a madzi kuti atulutse kilogalamu imodzi ya nyama ya ng’ombe, ndiponso malita 3,100 kuti atulutse kilogalamu imodzi ya nkhuku. Izi zimapangitsa anthu ena kuti asamadye nyama.
Nanga inuyo mukuti bwanji? Kodi muyenera kusala nyama? Musanayankhe funso limenelo, talingalirani kaye za mfundo ina. Monga momwe timaŵerengera pa Salmo 50:10, 11, Yehova Mulungu, Mlengi wa zinthu zonse, akuti: “Zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga, ndi ng’ombe za pa mapiri zikwi. Ndidziŵa mbalame zonse za m’mapiri: Ndipo nyama za kuthengo zili ndi Ine.” Popeza kuti nyama zonse ndi za Mulungu, ndi bwino kudziŵa mmene Mlengiyo amaonera moyo wa nyama ndi mmene munthu angaipangire kukhala chakudya.
Kodi Kupha Nyama Nkulakwa?
Anthu ena, monga Sujata, amene amaganiza kuti nyama nzofanana ndi anthu, amakhulupirira kuti kupha nyama kaamba ka cholinga chilichonse nkulakwa—makamaka kuzipha kaamba ka chakudya. Komabe, Malemba amasonyeza kuti Mulungu amasiyanitsa pakati pa moyo wa nyama ndi moyo wa munthu, ndipo amavomereza kupha nyama kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, Aisrayeli anali kupha nyama ngati iyo ipereka chiopsezo ku moyo wa munthu kapena ku ziŵeto za wina.—Eksodo 21:28, 29; 1 Samueli 17:34-36.
Kalekale, Mulungu anavomereza kupereka nsembe za nyama monga mbali ya kulambira. (Genesis 4:2-5; 8:20, 21) Analamulanso Aisrayeli kuti azichita chikumbutso cha Ulendo wawo kuchoka ku Igupto pokondwerera Paskha chaka ndi chaka, zimene zinaphatikizapo kupereka nsembe mwana wa nkhosa kapena wa mbuzi ndi kudya nyama yake. (Eksodo 12:3-9) Ndipo malinga ndi Chilamulo cha Mose, panalinso nthaŵi zina pamene amapereka nsembe za nyama.
Ataŵerenga Baibulo kwa nthaŵi yoyamba, mayi wina wachihindu wazaka 70 zakubadwa anaona kuti lingaliro lopereka nsembe za nyama linali loipa. Koma pamene chidziŵitso chake cha Malemba chinakula, anazindikira kuti Mulungu anali ndi cholinga pamene analamulira anthu kupereka nsembe. Izo zinalozera ku nsembe ya Yesu Kristu, imene inali kudzakwaniritsa chofunika cha lamulo kaamba ka chikhululukiro cha machimo. (Ahebri 8:3-5; 10:1-10; 1 Yohane 2:1, 2) Nthaŵi zambiri, ansembe anali kudya nyama zoperekedwa nsembe ndipo nthaŵi zina alambiri enawo amadya nawo. (Levitiko 7:11-21; 19:5-8) Mulungu, amene ali mwini zamoyo zonse, kwenikweni anali ndi cholinga pamene anayambitsa makonzedwe ameneŵa. Zoonadi, pamene Yesu anafa, nsembe za nyama zinali zosafunikanso m’kulambira.—Akolose 2:13-17; Ahebri 10:1-12.
Kudya Nyama
Nanga bwanji ponena za kupha nyama kuti zikhale chakudya? Nzoonadi kuti chakudya choyambirira cha munthu sichinali nyama. Koma pambuyo pake Yehova analola kuti chakudyacho chiphatikizepo nyama. Zaka 4,000 zapitazo—m’masiku a Nowa wolungamayo—Yehova anadzetsa chigumula cha dziko lonse ndipo anathetsa kuipa konse pa nthaŵiyo. Nowa, banja lake, ndi zamoyo zimene anaziloŵetsa m’chingalawa zinapulumuka Chigumula. Iwo atatuluka m’chingalawa, Yehova kwa nthaŵi yoyamba anati: “Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.” (Genesis 9:3) Komabe, panthaŵi imodzimodziyo, Mulungu anapereka lamulo lakuti: “Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m’chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.” (Genesis 9:6) Mwachionekere, Mulungu anasiyanitsa pakati pa nyama ndi anthu.
Kwenikweni, lingaliro la Sujata ponena za nyama linachokera ku chikhulupiriro chake cha chiphunzitso cha kubadwanso kwa munthu. Ponena za nkhaniyi, Baibulo limanena kuti ngakhale kuti anthu ndi nyama nzamoyo, moyo umafa. (Genesis 2:7; Ezekieli 18:4, 20; Machitidwe 3:23; Chivumbulutso 16:3) Monga miyoyo, anthu ndi nyama zonse zimafa ndipo zimaleka kukhalapo. (Mlaliki 3:19,20) Komabe, anthu ali ndi chiyembekezo cha chiukiriro m’dziko latsopano la Mulungu.b (Luka 23:43; Machitidwe 24:15) Zimenezi zikusonyeza kuti nyama ndi anthu ndi osiyana.
“Komabe, nchifukwa ninji chakudya chinasintha?” Sujata anafuna kudziŵa. Chifukwa cha Chigumula chija, mphepo ya dziko lapansi inasintha. Kaya Yehova analamulira anthu kuti azidya nyama chifukwa chakuti anadziŵiratu kuti mibadwo yamtsogolo idzakhala m’madera mmene zomera zidzakhala zosoŵa, Baibulo silinena zimenezo. Koma Sujata anavomereza kuti Mwini wa zamoyo zonse anali wokhoza kusintha zinthu.
Kulemekeza Moyo wa Nyama
Koma Sujata anazizwabe, ‘Kodi sitiyenera kulemekeza moyo wa nyama mpang’ono pomwe?’ Inde, tiyenera kutero. Ndipo Mlengi wa zinthu zonse watiuza mmene tingachitire zimenezo. “Koma nyama, mmene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye,” likufotokoza motero lamulo lake pa Genesis 9:4. Kodi nchifukwa ninji amaletsa kudya mwazi? “Pakuti moyo wa nyama ukhala m’mwazi,” limatero Baibulo. (Levitiko 17:10, 11) Yehova wapereka lamulo ili: ‘Mutapha nyama, mwazi wake muziuthira panthaka ngati madzi.’—Deuteronomo 12:16, 24.
Pamene anati tizidya nyama, sanapereke chilolezo chokhetsa mwazi wa nyama mosafunikira pongosangalatsidwa ndi kusaka kapena kufuna kuonetsa chamuna. Mwachionekere, Nimrode anachita zimenezi. Baibulo limamudziŵikitsa monga “mpalu wamphamvu wotsutsana ndi Yehova.” (Genesis 10:9, NW) Ngakhale lerolino, mkhalidwe wosaka ndi kupha nyama pongofuna kusangalatsidwa ungayambe kumera mizu mwa anthu ena. Koma mzimu umenewo umasonyeza kusalemekeza moyo wa nyama kwankhalwe, ndipo Mulungu savomereza zimenezo.c
Kuchitira Nyama Chifundo
Lerolino, anthu osadya nyama ena amachita chisoni kwambiri ndi mmene maindasitale ogulitsa nyama amachitira ndi nyamazo. “Ogulitsa zapafamu sakhudzidwa kwenikweni ndi mmene nyama zimazunzikira,” ikuthirira ndemanga motero The Vegetarian Handbook. “Mwachisoni, popeza kuti nyama zimaŵetedwera pafupi komanso m’malo ochita kukonza,” likutero bukulo, “nyama zamakono zikuzunzidwa kwambiri kusiyana ndi kalelonse.”
Ngakhale kuti kudya nyama sikumasemphana ndi chifuno cha Mulungu, kuzichitira nkhanza kumasemphana nacho. “Wolungama asamalira moyo wa choŵeta chake,” limatero Baibulo pa Miyambo 12:10. Ndipo Chilamulo cha Mose chinalamulira kuti azisamalira ziŵeto.—Eksodo 23:4, 5; Deuteronomo 22:10; 25:4.
Kodi Mkristu Ayenera Kusala Nyama?
Monga momwe taonera kale, nkhani yosadya nyama—kapena kukhalabe wakudya nyama—kwenikweni ili nkhani yaumwini. Munthu angasankhe kusala nyama mogwirizana ndi thanzi lake, mkhalidwe wake wa zachuma, kufuna kusamalira za chilengedwe, kapena chifundo chake kaamba ka nyama. Koma ayenera kuzindikira kuti yangokhala njira imene wadzisankhira ya kadyedwe. Sayenera kusuliza amene amadya nyama, inde ngakhale amene amadya nyama sayenera kusuliza amene amasala nyama. Kudya nyama kapena kusala nyama sikupangitsa wina kukhala woposa mnzake. (Aroma 14:1-17) Ndipo kadyedwe sikayenera kukhala chinthu chachikulu kopambana pamoyo wa munthu. “Munthu sadzakhala ndi moyo,” anatero Yesu, “ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.”—Mateyu 4:4.
Ponena zochitira nkhanza nyama ndi kusasamala zinthu za chilengedwe za dzikoli, Yehova walonjeza kuti adzathetsa dongosolo loipa ndi ladyera lilipoli ndipo m’malo mwake adzapanga dziko lapansi latsopano. (Salmo 37:10, 11; Mateyu 6:9, 10; 2 Petro 3:13) M’dziko latsopano limenelo, anthu ndi nyama zidzakhala pamtendere, ndipo Yehova ‘adzasamalira zosoŵa za chamoyo chilichonse.’—Salmo 145:16; Yesaya 65:25.
Ngati mungafune kudziŵa zambiri kapena ngati mungakonde kuti wina azibwera kudzachita nanu phunziro la Baibulo laulere la panyumba, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka, 10101, Zambia, kapena kukeyala yoyenera ili patsamba 5.
[Mawu a M’munsi]
b Onani Nsanja ya Olonda ya May 15, 1997, masamba 3-8, yofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
[Mawu a Chithunzi patsamba 30]
Punch