Paradaiso Wopanda Mavuto—Kodi ndi Maloto Chabe?
“KUNOTU nkwabata!” Nyanja ya Redfish m’chigawo cha Idaho, U.S.A., imaonekadi yabata mutakhala pamwamba m’nkhalango ya mitengo ya pine. “Ndiganiza kuti ndi mmenedi paradaiso adzakhalira,” anatero mlendo wina wodzacheza.
Dzuŵa linaŵala bwino pagombe la kummwera pachisumbu cha Cyprus m’nyanja ya Mediterranean. Mafunde anali kukapiza pagombepo mwapang’onopang’ono. Mlendo wina wodzacheza ali mu resitiranti yokhala pamwamba pa phiri anati: “Uyu ndi paradaiso!”
Ambiri a ife timasangalala tikamakumbukira zinthu ngati zimenezi. Koma okhala kumalo ngati amenewo amazindikira kuti maonekedwe onga paradaiso amenewo amabisa zovuta za tsiku ndi tsiku: moto m’nkhalango za mmunsi mwa mapiri a Rocky Mountains, kuipitsa nyanja komwe kumakhudza nsomba ndiye kenaka anthu—kuwonjezera pa mikangano ya maiko ndi ya mafuko.
Paradaiso—Nchiyani?
Kodi inu mumalingalira paradaiso kukhala wotani? The New Shorter Oxford English Dictionary inapereka malongoseledwe oyamba awa: “Munda wa Edene wonenedwa mu Gen[esis] 2, 3.” Izi zimasonya ku malongosoledwe a m’buku loyamba la Baibulo a dera limene Mulungu anaikako munthu woyamba, Adamu. M’Paradaiso woyamba ameneyu, munamera “mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya” yambiri.—Genesis 2:9.
Malongosoledwe achiŵiri a dikishonaleyo amagwirizanitsa “paradaiso” ndi “Kumwamba, malinga ndi ziphunzitso za Akristu ndi Asilamu” koma imawonjezera kuti: “Masiku ano kwenikweni ndi nthano chabe.” Komabe, kwa apaulendo ndi odzacheza athu aja, paradaiso anali “malo okongola kwambiri kapena opatsa chimwemwe,” malongosoledwe achitatu a dikishonaleyo.
Nduna yaikulu ya dziko la Britain ya m’zaka za zana la 16 Bwana Thomas More inalemba buku lotchedwa Utopia mmene inalemba za dziko longopeka kumene malamulo, boma, ndiponso chikhalidwe zinali zangwiro. Zinaoneka kukhala zosatheka kwakuti lerolino Webster’s New Collegiate Dictionary imalongosola kuti “Utopia” ndi “cholinga chosatheka chakutukula chikhalidwe cha anthu.”
Kwa otsatira Jim Jones, mkulu wa kagulu kachipembedzo ka People’s Temple, Utopia inali kulambula m’nkhalango ya ku Guyana. Nzachisoni kuti, mu 1978 paradaiso amene anali kumfunayo anakhala malo kumene ena mwa iwo oposa 900 anafera—zoopsa kwambiri! Chifukwa cha zimenezo anthu nthaŵi zina amagwirizanitsa lingaliro la paradaiso ndi magulu achipembedzo achilendo amene zochita zawo nzoopsa ndi zosautsa.
M’dziko la upandu ndi chiwawa, mmene matenda amagwira akulu ndi ana chimodzimodzi, kumene udani ndi kusamvana zipembedzo kumagaŵa anthu, malo okongola kaŵirikaŵiri amangokhala achiphamaso chabe. Nzosadabwitsa kuti anthu amalingalira za paradaiso kuti sangakhale chinanso koma maloto chabe! Komabe izi sizinawaletse anthu ena kuyesayesa kupeza paradaiso kapena kupanga wawo. Kodi amutha?