Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 11/8 tsamba 10-11
  • Mtsogolo Mwabwino mwa Ana Athu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtsogolo Mwabwino mwa Ana Athu
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Omwe Amasamala
  • Lonjezo la Mulungu la Mtsogolo Mwabwino
  • Nkhondo
    Galamukani!—2017
  • Nkhondo Yothetsa Ndhondo
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Dziko Lopanda Nkhondo Posachedwa
    Galamukani!—1996
  • Nkhondo Idzatha
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 11/8 tsamba 10-11

Mtsogolo Mwabwino mwa Ana Athu

KUYAMBIRA pamene Nkhondo Yadziko II inatha, maboma alemba ndi kusaina mapangano ambiri osiyanasiyana otetezera anthu wamba pa nkhondo. Ena mwa mapangano amenewo amalola zovala ndiponso mankhwala ndi chakudya kuti zizipita kwa ana. Mapangano a maiko osiyanasiyana amalonjeza kuti adzatetezera ana kuti asamawagwire nkumagona nawo, kuwazunza, ndi kuwachita chiwawa. Mapangano amaletsanso kulemba usilikali aliyense wazaka zosakwana 15.

Lipoti la bungwe loona za ana la United Nations Children’s Fund la The State of the World’s Children 1996, limathokoza malamulo ameneŵa kuti ali “mfundo zenizeni zimene zidzasintha zinthu” ndipo limawonjezera kuti: “Andale amene amazindikira kuti pali malamulo amene iwo angawaweruzirepo atawaswa amalingalirapo kaŵirikaŵiri za malamulowo polinganiza zochita zawo.”

Ndithudi, andale amazindikiranso kuti maiko osiyanasiyana kaŵirikaŵiri alibe mphamvu ndi chifuno chomwe zosungitsa malamulo. Motero lipotilo likuvomereza kuti “poona mmene malamulo ameneŵa anyalanyazidwira, nkwapafupi kusalabadira malamulo omwe alipo a maiko.”

Ndiye pali vuto la ndalama. Mu 1993 munali nkhondo m’maiko 79. Maiko 65 a ameneŵa anali osauka. Kodi nkuti kumene maiko ameneŵa anapeza zida zomenyera nkhondo? Anazipeza makamaka kumaiko olemera. Ndipo kodi ndi maiko asanu ati omwe ali patsogolo pogulitsa zida ku maiko omatukuka kumene? Ndiwo mamembala okhazikika asanu a bungwe la zachitetezo la United Nations Security Council!

Omwe Amasamala

Komabe, pali awo amene amasamala kwambiri za mavuto a ana kumalo ankhondo. Anthu paokha ndiponso mabungwe amathandiza mwachikondi ana ovutika ndi nkhondo. Mwachitsanzo, Mboni za Yehova, zomwe sizimenya nawo m’nkhondo, zimachita zimenezo. Koma kuti tithetse kuvutika kwa ana mu nkhondo ndithudi pafunikira kuthetseratu nkhondo yeniyeniyo, chinthu chomwe chingaoneke chosatheka. Chifukwa choona mbiri yaitali ya anthu ya kukangana ndi kumenyana, ambiri afika ponena kuti anthu sadzatha kubweretsa mtendere wa dziko lonse. Pamfundo imeneyi, akunena zoona!

Anthu afikanso ponena kuti Mulungu sadzaloŵererapo pankhani za maiko kapena kubweretsa mtendere wosatha padzikoli. Pamfundo imeneyi, sakunena zoona.

Mlengi wathu, Yehova Mulungu, amalingalirapo kwambiri pa zinthu zochitika padziko lapansi pano. M’mawu ake, Baibulo, Yehova amafunsa kuti: “Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? . . . sindiko kuti abwerere kuleka njira yake, ndi kukhala ndi moyo?” Kenaka Mulungu akuyankha motsimikizira kuti: “Sindikodwera nayo imfa ya wakufayo.”—Ezekieli 18:23, 32.

Talingaliramponi: Ngati Mlengi wathu wachikondiyo amafuna kuti ngakhale akuluakulu ochimwa alape ndi kusangalala ndi moyo, ndithudi iye akufunanso kuti ana akhale ndi moyo ndi kusangalala! Komabe, sikuti Mulungu wathu wachikondi adzalekererabe kuipaku kosatha. “Ochita zoipa adzadulidwa,” amalonjeza motero Mawu a Mulungu. “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti.”—Salmo 37:9, 10.

Yesu Kristu, yemwe anasonyeza mwangwiro umunthu wa Atate wake wakumwamba, anakonda ana ndipo anati “Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.” (Mateyu 19:14) Kupereka nsembe ana kwa mulungu wa nkhondo nkonyansa kwa Yehova Mulungu ndi kwa mwana wake yemwe, Yesu Kristu.—Yerekezerani ndi Deuteronomo 18:10, 12.

Lonjezo la Mulungu la Mtsogolo Mwabwino

Mulungu walolera nkhondo ndi kuvutika kwazaka mazana ncholinga chakuti choonadi chonenedwa ndi mneneri Yeremiya chitsimikizirike kwa umuyaya wonse m’tsogolo: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Baibulo limalonjeza kuti, posachedwa, Yehova adzatsimikiza uchifumu wake pa chilengedwe chonse mwa ‘kuletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.’ (Salmo 46:9) Chinanso chomwe chinanenedweratu m’Baibulo ndi nthaŵi pamene “[anthu] adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.

Nanga zidzakhala bwanji kwa amene anaphedwa pankhondo? Kodi pali chiyembekezo chilichonse kwa iwo? Yesu analonjeza kuti akufa adzauka padziko lapansi lopanda nkhondo, akumati: ‘Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda . . . adzatuluka.’ (Yohane 5:28, 29) Mofananamo, mtumwi Paulo ananena motsimikizira kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”—Machitidwe 24:15.

Malonjezo a Mulungu adzachitikadi. Iye ali nazo zonse mphamvu ndi cholinga chofuna kuchita zonse zimene afuna. (Yesaya 55:11) Yehova akati adzathetsa nkhondo, adzachitadi. Pamene alonjeza kudzaukitsa akufa kuti akhale ndi moyo, adzachitadi. Monga momwe mngelo Gabrieli ananenera, “palibe mawu amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.”—Luka 1:37.

[Chithunzi patsamba 10]

Pakadzakhala popanda nkhondo, ana onse adzasangalala ndi moyo wabwino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena