Chaola Sichinali Mapeto
MU October wa 1347, zombo za amalonda a Kummaŵa zinakocheza padoko la Messina ku Sicily. Amalinyero opalasa ngalaŵa anali kudwala ndi kumafa. Pa matupi awo panali zotupa zakuda, kukula kwake ngati mazira zomwe zimakha mwazi ndi mafinya. Amalinyerowo anavutika ndi kupweteka kwakukulu ndipo anamwalira mkati mwa masiku oŵerengeka kuchokera pomwe zizindikiro za matendawo zinaoneka.
Makoswe ochokera m’zombozo anafalikira ndi kusakanikirana ndi mbeŵa zina m’deralo. Makoswewo anali ndi nthata zokhala ndi bakiteriya yotchedwa bacillus ya kupha anthu. Motero anafalitsa mliri wotchedwa Chaola, mliri waukulu kwambiri m’mbiri ya Ulaya kufikira panthaŵiyo.
Mliriwo unali wamitundu iŵiri. Mtundu umodzi, unkayambukira munthu akalumidwa ndi nthata yokhala ndi bakiteriyayo, umene umayenda m’mwazi ndi kukapangitsa zotupa ndi kukha mwazi kwa mkati. Wina, umayambukira ena mwa kutsokomola kapena kuyetsemula, ndi kukagwira mapapo. Popeza mitundu yonseyi inalipo, nthendayi inafala mwamsanga kwambiri. M’zaka zitatu chabe, inawononga chigawo chimodzi mwa zinayi za anthu ku Ulaya; mwinamwake anthu 25 miliyoni anafa.
Panthaŵiyo panalibe aliyense amene anadziŵa mmene nthendayo inkafalikira kuchokera kwa wina kupita kwa wina. Ena ankakhulupirira kuti mpweya unaipitsidwa, mwina chifukwa cha chivomezi kapena kundanda kwachilendo kwa mapulaneti. Ena ankaganiza kuti anthu anayamba kudwala chabe chifukwa chongoona munthu wodwala matendawo. Ngakhale kuti panali malingaliro osiyanasiyana, mwachionekere matendawo sanali kuchedwa kuyambukira. Dokotala wa ku France anati zioneka ngati kuti munthu mmodzi wodwala “akanatha kupatsa dziko lonse matendawo.”
Anthu sanadziŵa kuteteza kwake ndiponso mankhwala ake. Ambiri analingalira za maulosi a m’Baibulo monga uja wolembedwa pa Luka 21:11, umene umaneneratu za miliri m’nthaŵi zamapeto. Ngakhale kuti anapereka ndalama zochuluka m’matchalitchi, mliriwo unapitirizabe. Mtaliyana wina panthaŵiyo analemba kuti: “Mabelu sankalizidwanso ndipo palibe amene anali kulira mosasamala kanthu kuti wafedwa motani chifukwa pafupifupi aliyense ankayembekezera imfa . . . anthu anali kunena ndi kukhulupirira kuti, ‘Awa ndiwo mapeto a dziko.’”
Komabe, sanali mapeto. Pofika kumapeto kwa zaka za zana la 14, mliriwo unaleka. Dziko linapitirizabe.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Archive Photos