Njira Zisanu ndi Imodzi Zotetezera Thanzi Lanu
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU NIGERIA
MALINGA ndi bungwe la World Health Organization (WHO), pafupifupi 25 peresenti ya anthu okhala m’maiko omatukuka alibe madzi abwino. Oposa 66 peresenti—pafupifupi anthu 2,500,000,000—alibe kotayira zinyalala ndiponso zam’suweji. Kwa ambiri zotsatira zake ndi matenda ndi imfa.
Zikakhala motero, kusunga ukhondo kumakhala kovuta. Komabe, ngati mukhala aukhondo, mudzadzitetezera nokha ku matenda ambiri. Nazi zinthu zisanu ndi chimodzi zomwe mungachite kudzitetezera nokha ndi banja lanu ku tizilombo toyambitsa matenda tomwe tingaloŵe m’thupi mwanu ndi kupangitsa matenda.
1. Sambani m’manja mwanu ndi sopo ndi madzi mukakhudza tubzi ndipo musanagwire chakudya.
Chinthu chofunika poteteza matenda ndicho kukhala ndi sopo ndi madzi nthaŵi zonse kuti aliyense m’banja lanu azikhoza kusamba m’manja. Sopo ndi madzi zimachotsa tizilombo m’manja toyambitsa matenda—tizilombo tomwe mwina tikhoza kubwera pachakudya kapena mkamwa. Popeza ana aang’ono amaika zala mkamwa kaŵirikaŵiri, nkoyenera kuwasambitsa m’manja kaŵirikaŵiri, makamaka mukafuna kuwapatsa chakudya.
Nkofunika kwambiri kusamba m’manja ndi sopo mutachokera kuchimbudzi, musanagwire chakudya, ndiponso mutasambitsa mwana kumatako kapena mwana amene wachita chimbudzi kumene.
2. Gwiritsirani ntchito chimbudzi.
Popewa kufalikira kwa tizilombo toyambitsa matenda, nkofunika kuti muzitaya bwino tubzi. Matenda ambiri, makamaka kutseguka m’mimba, amachititsidwa ndi tizilombo tokhala mu tubzi ta munthu. Tizilombo timeneti timatheka kuloŵa m’madzi akumwa kapena m’chakudya, kumanja, kapenanso m’ziŵiya ndi pamagome ogwiritsidwa ntchito pokonza chakudya kapena pakudya. Zikatero, anthu akhoza kudya tizilomboto ndi kudwala.
Kuti mupewe zimenezi, gwiritsirani ntchito chimbudzi. Ndoŵe za nyama ziyenera kutayidwa kutali ndi nyumba ndi pamene mumatunga madzi. Mudzadabwa kuzindikira kuti tubzi ta makanda ndi ana aang’ono ntoopsa kwambiri kuposa ta akulu. Choncho ngakhale ana ayenera kuphunzitsidwa kugwiritsira ntchito chimbudzi. Ana akamachitira chimbudzi kwina, tubzito tiyenera kuchotsedwa mwamsanga ndi kutayidwa m’chimbudzi kapena kukwiriridwa.
Zimbudzi ziyenera zizikhala zaukhondo ndi zovindikira.
3. Gwiritsirani ntchito madzi abwino.
Mabanja omwe ali ndi madzi abwino okwanira, amumpopi, sadwala kaŵirikaŵiri kuyerekezera ndi omwe alibe. Omwe alibe madzi amumpopi akhoza kuteteza thanzi lawo mwa kuvundikira zitsime zawo ndi kutaya madzi oipa kutali ndi madzi akumwa, osamba, kapena ochapira. Nkoyeneranso kusasunga ziŵeto m’nyumba ndiponso zizikhala kutali ndi madzi akumwa.
Njira ina yodzitetezera ku matenda ndiyo kusunga zibekete, zingwe, ndi mitsuko zosungira madzi zili zoyera monga momwe kungathekere. Mwachitsanzo, kuli bwino kupachika chibekete koposa kuchisiya pansi.
Madzi akumwa omwe amasungidwa m’nyumba ayenera kusungidwa m’mtsuko woyera wovundikira. Potungamo madzi mu mtsuko muyenera kugwiritsira ntchito chikho kapena kapu yotsuka. Osalola anthu kupisamo manja m’madzi akumwawo kapena kumwera mu mtsuko chomwecho ndi mlomo.
4. Ŵiritsani madzi akumwa kusiyapo ngati achoka mumpopi wabwino.
Madzi abwino kwambiri akumwa amachokera mumpopi. Madzi omwe mungatunge kwina kulikonse ngosakayikitsa kuti ali ndi tizilombo toyambitsa matenda, ngakhale angamaoneke oyera.
Kuŵiritsa madzi kumapha tizilombo toyambitsa matenda. Motero ngati mutunga madzi kudziŵe, mumtsinje, kapena m’mathanki, nkwanzeru kuwaphitsa ndiye kenaka nkuwaleka kuti azizire musanayambe kumwa. Madzi akumwa opanda tizilombo toyambitsa matenda ndi ofunika kwambiri kwa makanda ndi ana aang’ono, chifukwa matupi awo ali ndi mphamvu zochepa zolimbana ndi tizilombo toyambitsa matenda kusiyana ndi akulu.
Ngati nzosatheka kuŵiritsa madzi akumwa, asungeni m’chosungira chapulasitiki choonekera mkati kapena chagalasi chovundikira. Ndiye siyani chotengeracho padzuŵa kwa masiku aŵiri musanayambe kugwiritsira ntchito madziŵo.
5. Sungani chakudya chanu mwaukhondo.
Chakudya chomwe mudye chosaphika muyenera kuchitsuka bwino. Zakudya zina ziyenera kuphikidwa kwambiri, makamaka nyama ndi nkhuku.
Nkoyenera kudya chakudya mwamsanga chitangophikidwa; mwanjira imeneyi sipangakhale mpata wakuti chivunde. Ngati musunga chakudya kwa maola oposa asanu, muyenera kuchisunga chotentha kapena m’firiji. Musanayambe kudya, muyenera kuchitenthetsa kaye.
Nyama yaiŵisi nthaŵi zonse imakhala ndi tizilombo toyambitsa matenda, motero musalekerere kuti ikhudze chakudya chimene mwaphika. Mutatha kukonza nyama yaiŵisi, tsukani zipangizo ndiponso chinthu chilichonse chimene inakhudza.
Zinthu zogwiritsidwa ntchito kukonza chakudya ziyenera kusungidwa zaukhondo. Chakudya chiyenera kuvundikiridwa ndi kuchiika poti ntchentche, makoswe, mbeŵa ndi zinyama zina sizingafike.
6. Tenthani kapena kwirirani zinyalala zonse zapanyumba.
Ntchentche, zomwe zimafalitsa tizilombo toyambitsa matenda zimakonda kuswerana m’zakudya zomwe mwataya. Motero zinyalala zapanyumba siziyenera kutayidwa panja. Tsiku ndi tsiku muyenera kukwirira, kutentha, kapena kuzitaya mwanjira ina.
Mwa kugwiritsira ntchito njira izi, mukhoza kudziteteza inu eni ndiponso banja lanu ku kutseguka m’mimba, kolera, typhoid, njoka zam’mimba, matenda obwera mukadya chakudya chovunda, ndiponso matenda ena ambiri.
[Mawu a Chithunzi]
Magwero a nkhani: Facts for Life, lofalitsidwa ndi United Nations Children’s Fund, United Nations Educational, Scientific, and Cultural Organization, ndi WHO mogwirizana.