Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 2/8 tsamba 20-24
  • Konzekerani Kudzawalola Kupita

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Konzekerani Kudzawalola Kupita
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuphunzitsa Ana Kukhala Osamala Zinthu
  • Kuwongolera Kwachikondi
  • Maphunziro Opatsa Moyo
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Phunzitsani Ana Anu kukonda Yehova
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 2/8 tsamba 20-24

Konzekerani Kudzawalola Kupita

“ANA a ubwana wake wa munthu akunga mivi m’dzanja lake la chiphona,” analemba choncho m’Baibulo wamasalmo. (Salmo 127:4) Muvi sumakalasa chandamale mwangozi. Umafunikira kuulozetsa mosamalitsa ndi kuuponya molunjika. Mofananamo, ana sangafikire chandamale cha kukula nakhala anthu anzeru popanda chithandizo cha makolo. Baibulo limalangiza kuti: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”—Miyambo 22:6.

Kusintha kwa mwana kuti aleke kudalira makolo nayambe kudziimira payekha sikungachitike tsiku limodzi. Choncho, kodi makolo angayambe liti kuphunzitsa ana awo kudziimira paokha? Mtumwi Paulo anakumbutsa mnyamatayo Timoteo kuti: “Kuyambira ukhanda wako wadziŵa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Kristu Yesu.” (2 Timoteo 3:15) Tangolingalirani, amayi wa Timoteo anayamba kumphunzitsa zauzimu ali khanda lenileni!

Choncho, ngati makanda angathe kupindula mwa kuwaphunzitsa zauzimu, kodi si chanzeru kuyambirira kuphunzitsa ana za moyo wamtsogolo? Njira imodzi yochitira zimenezo ndiyo mwa kuwaphunzitsa kukhala osamala zinthu, okhoza kudzipangira zosankha.

Kuphunzitsa Ana Kukhala Osamala Zinthu

Kodi ana anu mungawathandize motani kukhala osamala zinthu? Mwamuna wina Jack, ndi mkazi wake Nora, anakumbukira izi ponena za mwana wawo wamkazi: “Asanayambe nkomwe kuyenda, anaphunzira kunyamula sokosi zake kapena tinthu tina ndi kukaika kuchipinda kwake, natiika bwinobwino m’madirowa ake. Anaphunziranso kuika zidole ndi mabuku ake m’malo ake oyenera.” Zimenezi ndi zinthu zazing’ono, komabe tikuona kuti mwanayo anali atayamba kale kuganiza mwanzeru.

Mwana akamakula, nthaŵi zina angapatsidwe maudindo okulirapo. Abra ndi Anita analola mwana wawo wamkazi kukhala ndi galu wakewake. Mwanayo anali ndi udindo wakusamalira galuyo ndipo mpaka kumapatulapo pa ndalama zake kuti azimsamalira. Kuphunzitsa ana kusamalira maudindo awo kumafuna kuleza mtima. Koma kumapindula ndipo kumawathandiza kukula m’maganizo.

Ntchito zapanyumba zimapereka mpata wina wophunzitsirapo ana kukhala osamala zinthu. Makolo ena samafuna ana awo kugwira ntchito iliyonse panyumba, chifukwa amaona ngati amangowavutitsa m’malo mowathandiza. Ena amaganiza kuti ana awo sayenera ‘kukhala ndi moyo wovutitsidwa umene iwo anali nawo paubwana.’ Maganizo ameneŵa ali olakwika. Malemba amati: “Ngati munthu angolekerera kapolo wake kuyambira paunyamata, akakula adzakhala wosayamika.” (Miyambo 29:21, NW) Mfundo ya lembali imagwiranso ntchito kwa ananso. Zimakhala zachisoni pamene wachinyamata akula nakhala “wosayamika” komanso wosatha kugwira ngakhale ntchito zosavuta zapanyumba.

M’nthaŵi za m’Baibulo, anyamata ndi atsikana ankapatsidwa ntchito zapanyumba. Mwachitsanzo, ali ndi zaka 17, Yosefe anathandizira paudindo wosamalira ziŵeto za banja lawo. (Genesis 37:2) Imeneyo siinali ntchito yopepuka, pakuti atate wake anali ndi nkhosa zochuluka kwambiri. (Genesis 32:13-15) Mutaganizira mfundo yakuti Yosefe anakula nakhala mtsogoleri wamphamvu, nkosavuta kukhulupirira kuti chiphunzitso cha paubwana wake chinaumba umunthu wake m’njira yabwino. Davidenso, mfumu yamtsogolo ya Israyeli anapatsidwa udindo wosamalira nkhosa za banja lawo.—1 Samueli 16:11.

Kodi pali phunziro lotani kwa makolo a masiku ano? Gaŵirani ana anu ntchito zapanyumba zothandiza. M’kupita kwa nthaŵi, mwa khama, ndi kuleza mtima, mutha kuphunzitsa ana kuyeretsa, kuphika, kusamala payadi, ndi kukonza nyumba ndi galimoto. Ndithudi, zambiri zimadalira pa msinkhu ndi nzeru za mwanayo. Koma ngakhale ana aang’ono akhozabe ‘kuthandiza adadi kukonza galimoto’ kapena ‘amami kuphika chakudya.’

Kuphunzitsa ana ntchito zapanyumba kumafunanso kuti makolo apatse anawo mphatso yamtengo wapatali kwambiri—nthaŵi yawo. Makolo ena omwe anali ndi ana aŵiri, anafunsidwa kuti chinsinsi chake nchiyani cholelera mwana kuti akule bwino. Iwo poyankha anati: “Nthaŵi, nthaŵi, nthaŵi!”

Kuwongolera Kwachikondi

Pamene ana agwira bwino ntchito yawo, kapena pamene achita khama kuti aigwire bwino, athokozeni ndi kuwatamanda moona mtima! (Yerekezerani ndi Mateyu 25:21.) Ndithudi, ana samagwira ntchito mwaluso lofanana ndi la munthu wamkulu. Ndipo pamene ana aloledwa kudzisankhira zochita, kaŵirikaŵiri amalakwitsa. Koma samalani kuti musawasulize monyanyitsa! Kodi inunso simunalakwitsepo zinthu pauchikulire wanu? Nangano bwanji osaleza mtima pamene mwana wanu alakwa? (Yerekezerani ndi Salmo 103:13.) Lolerani zolakwa zina. Zioneni kukhala mbali ya kakulidwe ka ana.

Olemba mabuku ena Michael Schulman ndi Eva Melkler anati: “Ana amene makolo awo amachita nawo mwaubwenzi samaopa kuti adzalangidwa pamene adzichitira okha chinthu china.” Komabe, “ana a makolo amphwayi kapena aukali amaopa kuchita okha china chilichonse, ngakhale zinthu zothandiza, chifukwa amaopa kuti makolo awo adzawapeza ndi cholakwa china pazimene achitazo ndipo adzawadzudzula kapena kuwalanga.” Mawu ameneŵa amagwirizana ndi chenjezo la Baibulo kwa makolo lakuti: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.” (Akolose 3:21) Choncho, pamene mwana alephera kuchita zimene munali kuyembekezera, bwanji osamthokozabe pakuyesera kwakeko? Mlimbikitseni kuti ulendo wina akachite bwino koposa. Mdziŵitseni kuti kupita kwake patsogolo kumakusangalatsani kwambiri. Msonyezeni kuti mumamkonda.

Ndithudi, nthaŵi zina kuwongolera kumakhala kofunikira. Zimenezi zingakhale zoonekera kwambiri m’zaka zakutha msinkhu, pamene anyamata ndi asungwana amakhala akumenyera nkhondo kuti adziŵike, pofuna kuonetsa ufulu wawo. Choncho makolo angachite bwino kuwamvetsa anawo pamene akuyesetsa kupata ufulu wawo m’malo mwa kuwayesa opanduka nthaŵi zonse.

Zoona, achinyamata ali ndi chikhoterero cha kuchita zinthu mwaphuma kapena kugonja pa “zilakolako za unyamata.” (2 Timoteo 2:22) Choncho kulephera kuikira malire wachinyamata pakhalidwe lake kungawononge maganizo ake; adzalephera kukhala wodziletsa ndi woleza mtima. Baibulo limachenjeza kuti: “Mwana womlekerera achititsa amake manyazi.” (Miyambo 29:15) Koma chilango choyenera, choperekedwa mwachikondi, chimapindula ndipo chimakonzekeretsa wachinyamata mmene angadzachitire ndi zofunika ndi zovuta akadzakula. Baibulo limalangiza kuti: “Wolekerera mwanake osammenya amuda; koma womkonda amyambize kumlanga.” (Miyambo 13:24) Komabe, kumbukirani kuti cholinga cha chilango ndicho kulangiza ndi kuphunzitsa—osati kukhaulitsa. ‘Kumenya’ kotchulidwa panopa mwachionekere kumaimira ndodo imene abusa ankakusira nayo nkhosa. (Salmo 23:4) Kumatanthauza chitsogozo chachikondi—osati kumenya kwankhanza.

Maphunziro Opatsa Moyo

Chitsogozo cha makolo chimakhala chofunika kwambiri makamaka pamaphunziro a mwana. Khalani ndi chidwi pamaphunziro a mwana wanu. Mthandizeni kusankha maphunziro oyenera akusukulu ndi kuti asankhe mosamala kaya ngati maphunziro owonjezera ali ofunika kapena ayi.a

Ndithudi, maphunziro ofunika kopambana ndiwo maphunziro auzimu. (Yesaya 54:13) Ana afunikira kukhala ndi makhalidwe aumulungu kuti akakhale bwino atakula. Ayenera kuphunzitsidwa ‘kuzindikira’ bwino. (Ahebri 5:14) Makolo angawathandize kwambiri pambali imeneyi. Mabanja pakati pa Mboni za Yehova amalimbikitsidwa kumaphunzira Baibulo nthaŵi zonse ndi ana awo. Mwa kutsatira chitsanzo cha amayi ake a Timoteo, amene anaphunzitsa mwanayo Malembo kuyambira ukhanda wake, makolonso omwe ndi Mboni amaphunzitsa ana awo aang’ono.

Barbara, kholo lopanda mwamuna, amachititsa phunziro la Baibulo la banja lake kukhala nthaŵi yosangalatsa kwambiri kwa ana ake. “Madzulowo ndimaonetsetsa kuti ana anga ndawapatsa chakudya chabwino kwambiri chimene amakonda. Ndimaikapo matepi a nyimbo za Ufumu za Kingdom Melodies kuti ndiwakonzekeretse maganizo. Ndiyeno, titayamba ndi pemphero, kaŵirikaŵiri timaphunzira magazini a Nsanja ya Olonda. Koma ngati pali kanthu kena kofunikira, nditha kugwiritsira ntchito mabuku monga lija lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza”b Malinga ndi kunena kwa Barbara, kuphunzira Baibulo kumathandiza ana ake “kuona zinthu mmene Yehova amazionera.”

Inde, palibe mphatso ina iliyonse imene mwana angapatsidwe yoposa chidziŵitso ndi kuzindikira Mawu a Mulungu, Baibulo. Likhoza “kuchenjeza achibwana, kuphunzitsa mnyamata kudziŵa ndi kulingalira.” (Miyambo 1:4) Ngati ali wokonzekera motero, mnyamata kapena msungwana amayamba kukhala wodzidalira ali wokhoza kuthana ndi mavuto ndi mikhalidwe yatsopano.

Ngakhale ndi choncho, kuchoka kwa ana kumasinthabe kwambiri moyo wa makolo ambiri. Mmene iwo angachitire ndi mkhalidwe wa kumsoŵa mwanayo ndiyo nkhani yathu yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani za mutu wakuti “Makolo—Muli ndi Ntchito ya Kunyumba Nanunso!” m’magazini ya Galamukani! ya September 8, 1988.

b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mawu Otsindika patsamba 22]

“Ana a makolo amphwayi kapena aukali amaopa kuchita okha china chilichonse, ngakhale zinthu zothandiza, chifukwa amaopa kuti makolo awo adzawapeza ndi cholakwa china pazimene achitazo ndipo adzawadzudzula kapena kuwalanga.”—Bringing Up a Moral Child, lolembedwa ndi Michael Schulman ndi Eva Mekler

[Bokosi patsamba 22]

Nkovuta Kuti Makolo Opanda Mnzawo wa m’Banja Alole Mwana Achoke

Rabecca, kholo lopanda mnzake wa m’banja anati: “Nkovuta kwambiri kwa makolo opanda mnzawo wa m’banja kulola ana awo apite. Tikapanda kusamala, timachita monyanyitsa powateteza ndi powasonyeza chikondi chathu.” Buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja,c pamasamba 106-7, limapereka maganizo othandiza awa:

“Nkwachibadwa kwa makolo opanda mnzawo wa m’banja kukhala okondana kwambiri ndi ana awo, komabe ndi bwino kusamala kuti tisalumphe malire oikidwa ndi Mulungu pakati pa makolo ndi ana. Mwachitsanzo, pangabuke mavuto aakulu ngati kholo lopanda mnzake wa m’banja liyembekeza kuti mwana wake wamwamuna achite monga ndiye mwamuna m’nyumbamo kapena ngati litenga mwana wake wamkazi kukhala woululirana naye zinsinsi, likumalemetsa msungwanayo ndi mavuto a zinsinsi zake. Kuteroko nkulakwa, kumavutitsa mwanayo maganizo, ndipo mwinanso kumamsokoneza.

“Sonyezani ana anu kuti inuyo, monga kholo, mudzawasamalira—osati kuti iwo asamalire inuyo. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 12:14.) Nthaŵi zina, mungafune wina woti akupangeni nzeru kapena kukulimbikitsani. Pitani kwa akulu achikristu kapena mlongo wina wachikulire, osati kwa ana anu aang’onowo.—Tito 2:3.” Pamene makolo opanda anzawo a m’banja aika malire oyenera ndi kusunga unansi wabwino pakati pa iwo ndi ana awo, kaŵirikaŵiri kumakhala kopepukirapo kuti iwo alole anawo kuchoka panyumba.

[Mawu a M’munsi]

c Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 23]

Kuphunzitsa ana ntchito kungawathandize kukhala osamala zinthu akadzakula

[Chithunzi patsamba 24]

Phunziro la Baibulo la banja lingapatse ana nzeru yofunikira kuti akadzisunge akadzakula

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena