Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 5/8 tsamba 12-15
  • Ulendo Wanga Wautali Kuchokera pa Moyo Wangozi m’Cambodia

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulendo Wanga Wautali Kuchokera pa Moyo Wangozi m’Cambodia
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Ndinayambira Chibudha
  • Nkhondo ndi Kusintha m’Cambodia
  • Pol Pot Apha Odana Nawo
  • Moyo Watsopano mu United States
  • Kuopa Wodzandichezera
  • Kuphunzira Chingelezi Ndiponso Baibulo
  • Ndinathawa Nkhondo Ndipo Ndinapeza Moyo
    Galamukani!—2009
  • Zimene Ndinasankha Ndili Mwana
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kodi Mavuto Adzatha?
    Galamukani!—2011
  • Kodi Zinthu Zingayambe Kuyenda Bwino Padzikoli Patakhala Kuti Palibe Zipembedzo?
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 5/8 tsamba 12-15

Ulendo Wanga Wautali Kuchokera pa Moyo Wangozi m’Cambodia

YOSIMBIDWA NDI WATHANA MEAS

MUNALI mu 1974, ndipo tinkamenyana ndi gulu la Khmer Rouge m’Cambodia. Ndinali ofesala m’gulu la asilikali ankhondo a dziko la Cambodia. Pa kumenyana kwina tinagwira msilikali wa Khmer Rouge. Zimene anandiuza za zimene Pol Pota ankafuna kudzachita m’tsogolo zinasintha moyo wanga ndipo zinandipangitsa kuyamba ulendo wautali, ponse paŵiri, ulendo weniweni komanso mwauzimu.

Koma ndiloleni kuti ndiyambe ndakuuzani za chiyambi cha ulendo wanga. Ndinabadwa m’chaka cha 1945, mu Phnom Penh, m’dziko limene limadziŵika monga Kampuchea (Cambodia) m’chilankhulo cha Khmer. Amayi anapatsidwa udindo waukulu m’gulu la apolisi achinsinsi. Anali msilikali wapadera wa Prince Norodom Sihanouk, wolamulira wa dzikolo. Popeza ankandilera okha ndipo anali otangwanika kuntchito, anakakamizika kukandisiya ku kachisi wachibudha kuti ndikaphunzire.

Mmene Ndinayambira Chibudha

Ndinali ndi zaka zisanu ndi zitatu pamene ndinapita kukakhala ndi monke wamkulu wachibudha. Kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka 1969, ndinkathera nthaŵi yanga kukachisi ndi kunyumba. Mmonke ndinkatumikira anali Chuon Nat, mbusa wamkulu koposa onse wachibudha mu Cambodia panthaŵiyo. Ndinali kugwira ntchito monga mlembi wake kwa kanthaŵi, ndipo ndinamthandiza kutembenuzira Buku lopatulika la Budha lotchedwa “Mitanga Itatu” (Tipitaka, kapena Sanskrit Tripitaka), kuchokera m’chilankhulo chakale cha ku India kupita m’chilankhulo cha ku Cambodia.

Ndinaikidwa kukhala mmonke m’chaka cha 1964 ndipo ndinatumikira pa udindo umenewo mpaka 1969. Panthaŵiyi panali mafunso ambiri amene ankandivuta, monga, Nchifukwa ninji anthu ambiri amavutika chonchi, ndipo kunayamba bwanji? Ndinkaona anthu akuyesayesa m’njira zambiri kuti akondweretse milungu yawo, koma sankadziŵa kuti milingu yawoyo idzathetsa motani mavuto awo. Ine sindinapeze yankho logwira mtima m’mabuku a Chibudha, ndipo amonke enawonso analephera. Ndinakhumudwa motero ndinalingalira zochoka kukachisi, ndiponso kuleka umonke.

Potsiriza, ndinaloŵa usilikali m’gulu la Asilikali ankhondo a dziko la Cambodia mu 1971. M’chaka chomwecho cha 1971, ananditumiza ku Vietnam, ndipo chifukwa cha maphunziro anga, anandikweza kukhala second lieutenant ndipo anandisankha kukhala m’kagulu kapadera komenya nkhondo zakabisira. Tinali kumenyana ndi gulu lachikomyunizimu la Khmer Rouge ndiponso gulu la Vietcong.

Nkhondo ndi Kusintha m’Cambodia

Ndinakhala wankhanza chifukwa cha nkhondo. Ndinazoloŵera kumaona munthu akufa tsiku lililonse. Ndinamenya nawo nkhondo 157. Nthaŵi ina tili mkati mwa nkhalango, a gulu la Khmer Rouge anatizungulira kwa mwezi umodzi. Asilikali oposa 700 anafa. Anapulumukapo anthu 15 okha—ndinali mmodzi wa iwo, ndinavulazidwa. Koma ndinatulukapobe wamoyo.

Panthaŵi ina mu 1974, tinagwira msilikali wa Khmer Rouge. Pamene ndinkamfunsa mafunso, anandiuza kuti Pol Pot ankalingalira zakupha anthu onse amene ankagwira ntchito m’boma, kuphatikizapo ogwira ntchito yausilikali. Anandiuza kuti ndisiye chilichonse ndipo ndithaŵe. Iye anati: “Uzingosinthasintha maina ako nthaŵi zonse. Osalola aliyense akudziŵe kuti ndiwe ndani. Uzichita zinthu monga wosadziŵa ndi wosaphunzira. Osauza aliyense za mmene umakhalira kale.” Nditamsiya kuti apite kwawo, chenjezo lake linakhalabe m’malingaliro anga.

Asilikalife tinauzidwa kuti tinali kumenyera dziko lathu, pomwe tinkaphanso anthu a m’dziko la Cambodia. A gulu la Khmer Rouge, gulu lachikomyunizimu lomwe linkafuna kulanda ulamuliro, linali la anthu a m’dziko lathu momwemo. Ambiri mwa anthu 9 miliyoni a ku Cambodia ndi a Khmer, ngakhale kuti ambiri mwa iwo sali m’gulu la Khmer Rouge. Ndinaziona kukhala zopanda pake. Tinkapha alimi osalakwa amene analibe mfuti ndiponso nkhondo sankaifuna.

Ndikamabwera paulendo wanga wochokera kunkhondo ndinkakumana ndi zokhumudwitsa. Akazi ndi ana ankabwera, kudikirira mtima uli mmwamba kuti aone ngati amuna awo kapena abambo awo abwera. Ndinkauza ambiri a iwo kuti abale awo anaphedwa. Pa zonsezi, zomwe ndimadziŵa za Chibudha sizinkanditonthoza.

Tsopano ndimalingalirabe za mmbuyo mmene zinthu zinasinthira m’Cambodia. Isanakwane 1970, munali mtendere ndi chisungiko. Anthu ambiri analibe mfuti; kunali kuphwanya lamulo pokhapokha utakhala ndi chilolezo. Umbala sunkachitika kwenikweni. Koma itatha nkhondo yapachiŵeniŵeni yoyambika ndi Pol Pot ndi asilikali ake, zonse zinasintha. Mfuti zinali paliponse. Ngakhale ana a zaka 12 ndi 13 ankaphunzitsidwa usilikali, kuphunzira kuombera ndi kupha. Anthu a Pol Pot anapangitsa ana ena kupha makolo awo. Asilikali ankauza ana kuti, “Ngati mumakonda dziko lanu, muyenera kudana ndi adani anu. Ngati makolo anu akutumikira boma, ndi adani athu ndipo muyenera kuwapha—apo ayi inuyo mudzaphedwa.”

Pol Pot Apha Odana Nawo

Mu 1975, Pol Pot anapambana nkhondo ndipo dziko la Cambodia linakhala lachikomyunizimu. Pol Pot anayamba kupha ana asukulu onse, aphunzitsi, akuluakulu a m’boma, ndiponso aliyense amene anali wophunzira. Ngati uvala magalasi, ukanaphedwa chifukwa akanalingalira kuti ndiwe wophunzira! Boma la Pol Pot linathamangitsira anthu ambiri kunja kwa mzinda ndikukawaika kumidzi kuti azigwira ntchito yaulimi. Anthu onse ankafunikira kumavala mofanana. Tinkagwira ntchito kwa maola 15 patsiku, popanda chakudya chokwanira, mankhwala, zovala ndipo tinkagona maola aŵiri kapena atatu. Ndinalingalira zoti ndichoke m’dziko lathu mwamsanga.

Ndinakumbukira malangizo anandipatsa msilikali wa Khmer Rouge. Ndinataya zithunzi zanga zonse, mapepala, ndi china chilichonse chimene chikanandigwiritsa. Ndinakumba dzenje ndi kufotsera ena a makalata ofunika. Ndiye ndinanyamuka ulendo kuloŵera chakumadzulo kupita ku Thailand. Unali ulendo woopsa. Ndinkazemba mageti ndipo ndimayenera kukhala wochenjera nthaŵi imene amaletsa kuyenda, popeza ndi asilikali a Khmer Rouge okha amene ankaloledwa ndi boma kumayenda.

Ndinapita ku dera lina kukakhala ndi mnzanga wina kwa kanthaŵi. Ndiye a Khmer Rouge anasamutsa anthu onse ku dera limenelo kupita nawo kwina. Anayamba kupha aphunzitsi ndi madokotala. Ndinathaŵa ndi anzanga atatu. Tinabisala m’nkhalango ndipo tinkadya zipatso zilizonse zomwe tinkapeza m’mitengo. Kenaka, ndinapita kukamudzi kakang’ono m’chigawo cha Battambang, kumene mnzanga ankakhala. Mwadzidzidzi, kumeneko ndinakumana ndi munthu yemwe anali msilikali uja amene anandiuza za mmene ndithaŵire yemwe tsopano anali atapuma pa usilikali! Popeza ndinammasula, anandibisa m’dzenje kwa miyezi itatu. Anauza mwana kuti azikaponyamo chakudya koma osamayang’ane m’dzenjemo.

Patapita nthaŵi ndinali ndi mwayi wothaŵa, ndipo ndinapeza amayi, azakhali, ndi mlongo wanga, amene nawonso ankathaŵira kumalire a dziko la Thailand. Inali nthaŵi yachisoni kwa ine. Amayi ankadwala, ndipo kenaka anamwalira ndi matenda ndiponso kusoŵeka kwa chakudya mumsasa wa othaŵa kwawo. Komabe, ndinayamba kukhala ndi chiyembekezo mmoyo wanga. Ndinakumana ndi Sopheap Um, mkazi amene pambuyo pake anadzakhala mkazi wanga. Tinathaŵa pamodzi ndi azakhali ndi mlongo wanga kudutsa malire a Thailand kupita kumsasa wa othaŵa kwawo wa United Nations. Banja lathu linavutika kwambiri pankhondo yapachiŵeniŵeni ya ku Cambodia. Abale athu 18, kuphatikizapo mbale wanga ndi mlamu wanga anafa.

Moyo Watsopano mu United States

Pa msasa wa othaŵa kwawo, anafufuza za moyo wathu wapoyamba ndipo UN inayesetsa kupeza munthu woti nkutithandiza kuti tipite ku United States. Pomaliza anapezeka! Mu 1980, tinafika ku St. Paul, Minnesota. Ndinazindikira kuti ndinafunikira kuphunzira Chingelezi mwamsanga kwambiri kuti zinthu zindiyendere bwino m’dziko limeneli. Wondithandizayo anangonditumiza kusukulu kwa miyezi yochepa, ngakhale kuti ndinafunikira kuphunzira kwa miyezi yambiri. M’malo mwake anandipezera ntchito yosesa m’hotelo. Koma popeza ndinkangodziŵa Chingelezi pang’ono chabe, ndinkangolakwitsalakwitsa. Mwini wake akandiuza kuti ndibweretse makwerero, ndinkabweretsa chitini chotayamo zinyalala!

Kuopa Wodzandichezera

Mu 1984, ndinkagwira ntchito usiku ndipo masana ndinkagona. Tinkakhala kudera limene kunalibe kugwirizana pakati pa amwenye ndi anthu akuda. Chiwawa ndiponso mankhwala osokoneza bongo anali ponseponse. Tsiku lina m’maŵa, mkazi wanga anandidzutsa nthaŵi ya 10 koloko nkundiuza kuti pakhomo panali patabwera munthu wakuda. Ankaopa chifukwa ankaganiza kuti wabwera kudzatibera. Ndinasuzumira pakhomo, zoonadi panali pataimadi munthu wakuda atavala bwino ali ndi bulifikesi, ndipo anali ndi mzungu. Ndinaona kuti panalibe chovuta.

Ndinamfunsa chomwe ankagulitsa. Anandisonyeza magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Palibe chomwe ndinamvetsetsa. Ndinayesera kuwakana chifukwa miyezi iŵiri yapitayo, wogulitsa mabuku wachiprotesitanti anandinyenga kuti ndilipire $165 kugula mabuku asanu. Komabe, munthu wakudayo anandisonyeza zithunzi m’magaziniwo. Zithunzizo zinali zosangalatsa ndi zokongola! Ndipo munthuyo anali kumwetulira kwambiri. Motero ndinapereka $1 ndi kuŵatenga.

Patapita masabata aŵiri pambuyo pake, anabweranso ndi kundifunsa ngati ndinali ndi Baibulo la m’Chikambodia. Ndinali nalodi limene ndinalandira ku tchalitchi la Nazarene, ngakhale kuti sindinkalimvetsa. Koma ndinachita chidwi kuti anthu aŵiri osiyana mitundu anabwera kunyumba kwanga. Ndiye anandifunsa kuti, “Kodi ukufuna kuphunzira Chingelezi?” Ndinkafunadi, koma ndinalongosola kuti ndinalibe ndalama zoti nkulipirira maphunzirowo. Anandiuza kuti adzandiphunzitsa kwaulele, mwakugwiritsira ntchito mabuku onena za m’Baibulo. Ngakhale kuti sindinkadziŵa kuti amaimira chipembedzo chanji, ndinalingalira kuti, ‘sindizilipira, koma ndiphunzira kuŵerenga ndi kulemba Chingelezi.’

Kuphunzira Chingelezi Ndiponso Baibulo

Ndinkaphunzira pang’onopang’ono. Ankati akandionetsa buku loyamba la m’Baibulo, Genesis, ndiye ine ndinkanena m’Chikambodia kuti, “Lo ca bat.” Iye akati, “Baibulo,” ine ndimanena kuti, “Compee.” Ndinayamba kuzindikira, choncho ndinalimbikitsidwa. Popita kuntchito ndinkatenga dikishonale yanga yotanthauzira Chingelezi m’Chikambodia, magazini ya Nsanja ya Olonda, Baibulo la New World Translation, ndi Baibulo langa la Chikambodia. Panthaŵi yabuleki, ndinkaphunzira Chingelezi, liwu ndi liwu, mwakuyerekezera m’mabukuwo. Kuphunzira pang’onopang’ono kumeneku, pamodzi ndi maphunziro a mlungu ndi mlungu, kunatenga zaka zoposa zitatu. Koma, pomaliza, ndinayamba kuŵerenga Chingelezi!

Mkazi wanga ankapitabe ku kachisi wachibudha ndipo ankasiyira chakudya makolo akale. Koma zimene zinkapindula ndi ntchentche basi! Ndinali ndi zizoloŵezi zina zoipa zimene zinazika mizu mwa ine zomwe zinayambika pamene ndinali msilikali ndiponso ndili Mbudha. Pamene ndinali mmonke, anthu ankabweretsa nsembe, kuphatikizapo ndudu za fodya. Ankakhulupirira kuti ngati mmonke asuta nduduzo, zimakhala ngati makolo awo akale akusuta. Motero ndinali kusuta kwambiri. Ndiye kenaka kuusilikali ndinkamwa moŵa kwambiri ndi kusuta mankhwala osokoneza bongo kuti ndisamachite mantha kunkhondo. Choncho pamene ndinayamba kuphunzira Baibulo ndinafunikira kusintha zinthu zambiri. Apa mpamene ndinazindikirira kuti pemphero nlothandiza kwambiri. M’miyezi yochepa chabe, ndinasiya zizoloŵezi zanga zoipazo. Izi zinasangalatsa kwambiri banja lonse!

Ndinabatizidwa monga mboni m’chaka cha 1989, ku Minnesota. Panthaŵi imeneyo ndinamva kuti kuli mpingo wa Mboni wolankhula Chikambodia ndiponso panali anthu ambiri a ku Cambodia ku Long Beach, ku California. Titakambitsirana ndi mkazi wanga, tinalingalira zosamukira ku Long Beach. Kusamuka kumeneku kunapangitsa zinthu zambiri kusintha! Choyamba mlongo wanga anabatizidwa, kenaka azakhali anga (amene tsopano ali ndi zaka 85) ndiponso mkazi wanga. Otsatira anali ana anga atatu. Pambuyo pake mlongo wanga anakwatiwa ndi Mboni, imene tsopano ikutumikira monga mkulu mumpingo.

Ku United States kuno, takumana ndi ziyeso zambiri. Takumana ndi mavuto azachuma ndiponso matenda, koma mwa kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo, takhalabe okhulupirika kwa Yehova. Iye wadalitsa kuyesayesa kwanga pazauzimu. Mu 1992, ndinasankhidwa kukhala mtumiki wotumikira mumpingo, ndipo mu 1995, ndinakhala mkulu kuno ku Long Beach.

Tsopano, ulendo umene unayambira pamene ndinali mmonke wachibudha ndi ofesala ku bwalo lankhondo m’Cambodia wosakazika ndi nkhondo wathera pa ufulu ndi chimwemwe panyumba yathu m’dziko lachilendo. Tili ndi chikhulupiriro chatsopano chomwe tinangochipeza kumene mwa Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu. Zimandiwawa kuona kuti anthu adakali kuphana m’Cambodia. Ichi nchifukwa chabwino chakuti ine ndi banja langa tidikire ndi kulengeza za dziko latsopano lolonjezedwa, mmene nkhondo zonse zidzatha ndipo anthu onse azidzakondadi anansi awo monga mmene adzikondera iwo okha!—Yesaya 2:2-4; Mateyu 22:37-39; Chivumbulutso 21:1-4.

[Mawu a M’munsi]

a Pol Pot anali mtsogoleri wachikomyunizimu wa gulu la asilikali ankhondo la Khmer Rouge limene linapambana nkhondo ndi kulanda boma la Cambodia.

[Mapu/Chithunzi patsamba 12]

VIETNAM

LAOS

THAILAND

CAMBODIA

Battambang

Phnom Penh

Zaka zomwe ndinali mmonke wa Chibudha

[Mawu a Chithunzi]

Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.

[Chithunzi patsamba 14]

Ndi banja langa, pa Nyumba ya Ufumu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena