Mmene Nyengo Idzakhalira Mtsogolo
KUIPITSA mlengalenga nlimodzi la mavuto achilengedwe amene anthu apangitsa. Ena ndi kudula mitengo yochuluka, kupha nyama mowononga, ndiponso kuipitsa mitsinje, nyanja zing’onozing’ono ndi nyanja za mchere. Lililonse la mavuto ameneŵa linafufuzidwa bwino, ndipo papangidwa njira zothetsera mavutowo. Popeza mavuto amakhudza dziko lonse, amalira njira zothetsera zapadziko lonse. Ambiri akugwirizana ponena za mavutowo ndiponso zimene ayenera kuchita kuti awathetse. Chaka ndi chaka, timamva zakuti pafunikira kuchitapo kanthu. Chaka ndi chaka, pamangochitika zochepa chabe. Nthaŵi zonse okhazikitsa malamulo amadandaula chifukwa cha mavuto ndipo amagwirizana kuti payenera kuchitika kanthu koma amawonjezerapo kuti, “tisachite ndife, kasachitike tsopano.”
Mu 1970 pa tsiku la Earth Day, ochita zionetsero ku New York City anatenga chikwangwani chachikulu. Chikwangwanicho chinkasonyeza Dziko Lapansi likufuula kuti “Thandizeni!!” Kodi alipo amene adzamva dandaulo limenelo? Mawu a Mulungu amapereka yankho: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Salmo 146:3, 4) Kenaka wamasalmoyo akusonya Mlengi, pakuti Iye yekha ndiye ali ndi mphamvu, nzeru, ndiponso amafuna kuthetsa mavuto ovuta onse amene mtundu wa anthu ukukumana nawo. Timaŵerenga kuti: “Wodala munthu amene . . . chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake. Amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili mmwemo.”—Salmo 146:5, 6.
Lonjezo la Mulungu Wachikondi
Dziko lapansi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Iye analilenga ilo, pamodzi ndi zinthu zonse zodabwitsa zomwe zimapangitsa nyengo ya padziko lapansi pano kukhala yokondweretsa. (Salmo 115:15, 16) Baibulo limati: “[Mulungu] analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yake, nayala thambo ndi kuzindikira kwake; polankhula Iye, pali unyinji wa madzi m’mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, alenga mphezi idzetse mvula, natulutsa mphepo m’zosungira zake.”—Yeremiya 10:12, 13.
Chikondi cha Mlengi kwa anthu chinalongosoledwa ndi Mtumwi Paulo kwa anthu a mu mzinda wakale wa Lustra. Iye anati: “[Mulungu] sanadzisiyira Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.”—Machitidwe 14:17.
Tsogolo la pulaneti lathuli silidalira pa zoyesayesa ndi mapangano a anthu. Ponena za nyengo, Yemwe ali ndi mphamvu za kulamulira adalonjeza anthu ake akale kuti: “Ndidzakupatsani mvula m’nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m’minda idzabala zipatso zake.” (Levitiko 26:4) Posachedwapa anthu adzasangalala ndi kakhalidwe kameneko padziko lonse. Sizidzachitikanso kuti anthu omvera azidzaopa mkuntho, kukwera kwa mafunde, kusefukira kwa madzi, chilala, kapena masoka achilengedwe ena alionse.
Mafunde, mphepo, ndi nyengo zidzakhala zosangalatsa. Anthu akhoza kupitirizabe kunena za nyengo, koma sadzachitapo kanthu. Mtsogolomu, malinga ndi chifuniro cha Mulungu, moyo udzakhala wosangalatsa mwakuti sipadzafunikira kuchita chilichonse kuti tiwongolere nyengo.