Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 7/8 tsamba 24-27
  • Kupeza Mayankho mwa Kuyang’ana Kumwamba, Osati Pansi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupeza Mayankho mwa Kuyang’ana Kumwamba, Osati Pansi
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Tili ndi Majini a Nyama Kapena Majini Owonongeka?
  • Chifukwa Chake Sitifuna Kufa
  • Tinapangidwa Kukhala ndi Moyo Kosatha
  • Dziko Latsopano Lomwe Maziko Ake Nchikondi
  • Kodi Imfa Ndi Mapeto a Zonse?
    Galamukani!—2007
  • Kodi Moyo Wosatha Ndi Wothekadi?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Tinalengedwa Kuti Tiziphunzira Mpaka Kalekale
    Galamukani!—2004
  • Mukhoza Kudzakhala Padzikoli Kwamuyaya
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)——2018
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 7/8 tsamba 24-27

Kupeza Mayankho mwa Kuyang’ana Kumwamba, Osati Pansi

CHIPHUNZITSO cha chisinthiko chimati panali kusintha mosiyanasiyana koma pang’onopang’ono kumene kunatipangitsa kukhala nyama zapamwamba. Kumbali ina, Baibulo limati tinayamba tili angwiro, m’chifanizo cha Mulungu, koma kuti patapita nthaŵi pang’ono pambuyo pake, anthu anakhala opanda ungwiro ndipo pang’ono ndi pang’ono tinayamba kubwerera m’mbuyo.

Makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anadziika okha pangozi imeneyi pamene anafuna kumadzisankhira okha zochita ndipo anawononga chikumbumtima chawo mwa kusamvera Mulungu mwadala. Anachita ngati akuyendetsa galimoto ndiye mwadala nkuwomba zitsulo zotetezera m’mphepete mwa msewu wa malamulo a Mulungu, nkukagwera kumene tili tsopano komwe kuli kuvutika ndi matenda, ukalamba, ndi imfa, kuphatikizapo kusankhana mitundu, kudana kwa zipembedzo, ndi nkhondo zoopsa.—Genesis 2:17; 3:6, 7.

Tili ndi Majini a Nyama Kapena Majini Owonongeka?

Zoonadi, Baibulo silinena mwa usayansi zimene zinachitikira matupi a Adamu ndi Hava angwirowo pamene anachimwa. Baibulo si buku la sayansi, monga mmene buku la malangizo a galimoto si buku lophunzitsa kukonza galimoto. Koma monga buku la malangizo oyendetsera galimoto, Baibulo ndi lolondola; si nthanthi.

Pamene Adamu ndi Hava anawomba chowatetezera chomwe ndi malamulo a Mulungu, matupi awo anawonongeka. Pambuyo pake anayamba kufooka kupita ku imfa. Potsatira lamulo lakuti ana azitenga zomwe makolo anasiya, ana awo, anthu onse, anatenga kupanda ungwiro. Motero, nawonso amafa.—Yobu 14:4; Salmo 51:5; Aroma 5:12.

Mwachisoni, zomwe tinatengazo zimaphatikizapo chikhoterero chofuna kuchita uchimo, chimene chimaonekera mwa kudzikonda ndiponso chiwerewere. Kugonana, nkwabwino kutachitika moyenera. Mulungu analamula banja loyambiriraro kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Ndipo monga Mlengi wachikondi, anapangitsa kuti kutsatira lamulolo kukhale kosangalatsa kwa mwamuna ndi mkazi wake. (Miyambo 5:18) Koma kupanda ungwiro kwa munthu kwapangitsa kuti azigonana m’njira yolakwika. Ndipotu, kupanda ungwiro kumakhudza mbali zonse za moyo wathu, kuphatikizapo kagwiridwe ka ntchito ka maganizo ndi matupi athu, monga mmene tonsefe tikudziŵira.

Koma kupanda ungwiro sikunachotse mphamvu yathu yozindikira makhalidwe abwino. Ngati tikufunadi, tikhoza “kuwongolera” ndi kupewa ngozi zomwe tingakhale nazo m’moyo mwa kulimbana ndi kuchita uchimo chifukwa cha chilakolako chathu. Komatu, palibe munthu wopanda ungwiro amene angalimbane ndi uchimo bwino, ndipo mwachifundo Mulungu amadziwa zimenezi.—Salmo 103:14; Aroma 7:21-23.

Chifukwa Chake Sitifuna Kufa

Baibulo limanenanso chinthu china chodabwitsa chimene nkhani ya chisinthiko siilongosola bwino: chibadwa cha munthu chosafuna kufa, ngakhale kuti imfa imaoneka kuti ndi yachibadwa ndipo njosapeweka.

Malinga ndi mmene Baibulo limanenera, imfa inayambika ndi uchimo, mwa kusamvera Mulungu. Ngati makolo athu oyambawo akanapitiriza kumvera, akanakhalabe ndi moyo kosatha, pamodzi ndi ana awo. Poyamba pomwe Mulungu anaika m’maganizo a munthu chilakolako chofuna kukhala ndi moyo kosatha. “Waika zamuyaya m’mitima yawo,” pamatero pa Mlaliki 3:11. Motero kuweruzidwa kwawo kuti azifa, kunapangitsa chisokonezo m’maganizo mwawo, kusagwirizana kwa zinthu komwe sikutha.

Kuti athetse kusamvetsetsa zinthu kumene ali nako mwa iwo okha ndi kuti akhutiritse chilakolako cha kupitirizabe kumakhala ndi moyo, anthu adzipangira zikhulupiriro zosiyanasiyana, kuyambira chikhulupiriro chakuti mzimu sufa mpaka chakuti munthu amabadwanso kwina. Asayansi nawonso amafufuza chinthu chodabwitsachi chakuti timakalamba chifukwa nawonso amafuna kuchotsa imfa kapena kuipangitsa kuti isabwere tsopano. Asayansi yachisinthiko omwe amati kulibe Mulungu amatsutsa chilakolako chofuna kukhala ndi moyo wosatha akumati ndi maloto, kapena chinyengo, chifukwa zimawombana ndi malingaliro awo akuti munthu ndi nyama yapamwamba chabe. Kwinaku, nkhani ya m’Baibulo yakuti imfa ndi mdani imagwirizana ndi chilakolako chathu chachibadwa chofuna kukhala ndi moyo.—1 Akorinto 15:26.

Chabwino, kodi matupi athuwa amasonyeza kuti tinayenera kumakhala ndi moyo kosatha? Yankho nlakuti inde! Ubongo wa munthu wokha umatipatsa umboni wochuluka wakuti tinapangidwa kuti tizikhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali kuposa mmene zilili.

Tinapangidwa Kukhala ndi Moyo Kosatha

Ubongo umalemera makilogalamu 1.4, ndipo uli ndi mitsempha yonyamula mauthenga pakati pa mabiliyoni 10 ndi mabiliyoni 100, ndipo kumanenedwa kuti kulibe iŵiri ya imeneyi yofanana ndendende. Uliwonse wa mitsempha imeneyi umatha kumapatsirana mauthenga ndi mitsempha ina 200,000, ikumapangitsa njira zoyendamo mauthenga zosiyanasiyana zochuluka kwambiri. Ndiponso pawokha, “mtsempha uliwonse uli ngati kompyuta yopangidwa mwaluntha kwambiri,” inatero Scientific American.

Ubongo uli m’madzi okhala ndi makemikolo, omwe amathandiza kuti mitsempha yonyamula mauthenga izigwira bwino ntchito. Ndipo ubongo ndi wovuta kwambiri kuumvetsa kuposeratu kompyuta yamphamvu kwambiri yomwe ilipo. “M’mutu uliwonse,” analemba motero Tony Buzan ndi Terence Dixon, “muli mphamvu yozizwitsa, chiwalo chaching’ono koma chogwira bwino ntchito chomwe mphamvu yake imachita ngati ikukulirakulira kukhala yosatha pamene tiphunzira zambiri ponena za icho.” Pogwira mawu Profesa Pyotr Anokhin, iwo anati: “Padakali pano palibe munthu amene angathe kugwiritsira ntchito mphamvu zonse zomwe ubongo wake uli nazo. Ichi ndicho chifukwa chake sitivomereza kuyerekezera kulikonse ponena za mmene ubongo wa munthu angagwirire ntchito. Ulibe malire.”

Mfundo zodabwitsa zimenezi zimawombana ndi nkhani ya chisinthiko. Nchifukwa ninji chisinthiko “chingalengere” munthu wokhala m’mapanga, kapena ngakhale munthu wamakono wophunzira kwambiri, chiwalo chimene akhoza kuchigwiritsira ntchito kwa nthaŵi yomwe munthu amakhala ndi moyo kuŵirikiza miliyoni kapena mamiliyoni chikwi? Ndithu, ndi nkhani yamoyo wosatha yokha yomwe ingamveke! Koma nanga bwanji za thupi lathu?

Buku lotchedwa kuti Repair and Renewal—Journey Through the Mind and Body linati: “Mmene mafupa, minofu, ndi ziwalo zina zimadzichiritsira zikawonongeka ndi chinthu chodabwitsa zedi. Ndipo titakhala chete kulingalira zimenezi, tikanaona kuti kudzibwezeretsa kwa khungu ndi tsitsi ndi zikhadabo—ndiponso ziwalo zina zathupi—nzodabwitsa ndithu: zimachitika maola 24 tsiku lililonse, mlungu ndi mlungu, kwenikweni kumakhala kutipanganso, kuti tinene mwausayansi ya makemikolo, ndiye kuti kumakhala kutipanganso nthaŵi zambiri panthaŵi ya moyo wathu.”

Panthaŵi yake Mulungu, silidzakhala vuto kwa iye kupangitsa kudzibwezeretsa kwa thupi kodabwitsa kumeneku kuchitika kosatha. Ndiye, pomaliza, ‘imfa idzathetsedwa.’ (1 Akorinto 15:26) Koma kuti tikhaledi ndi chimwemwe, tifunikira zambiri koposa kungokhala ndi moyo wosatha. Timafunikira mtendere—mtendere ndi Mulungu ndiponso ndi anthu anzathu. Mtendere umenewu ungatheke ngati anthu akukondanadi wina ndi mnzake.

Dziko Latsopano Lomwe Maziko Ake Nchikondi

“Mulungu ndiye chikondi,” amatero 1 Yohane 4:8. Chikondi nchamphamvu kwambiri—makamaka chikondi cha Yehova Mulungu—moti ndicho chifukwa chenicheni chimene tingakhulupirire kuti tidzakhala ndi moyo kosatha. Yohane 3:16 amati, “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”

Moyo wosatha! Nchiyembekezo chodabwitsa chotani nanga! Koma popeza tinalandira uchimo, sitiyenera kukhala ndi moyo. “Mphotho yake ya uchimo ndi imfa,” limatero Baibulo. (Aroma 6:23) Komabe mosangalatsa, chikondi chinapangitsa mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, kutifera ife. Mtumwi Yohane analemba motere za Yesu: “Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife.” (1 Yohane 3:16) Inde, anapereka moyo wake wangwiro monga munthu “dipo la anthu ambiri” kuti ife amene timamkhulupirira machimo athu akhululukidwe ndi kuti tikasangalale ndi moyo wosatha. (Mateyu 20:28) Baibulo limalongosola kuti: “Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha, alowe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye.”—1 Yohane 4:9.

Nanga ife tichite bwanji pa chikondi chimene Mulungu ndi Mwana wake wachisonyeza kwa ife? Baibulo limapitiriza kuti: “Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.” (1 Yohane 4:11) Tiyenera kuphunzira kukonda, chifukwa limenelo ndilo lidzakhala khalidwe lofunika kwambiri m’dziko latsopano la Mulungu. Lerolino ambiri amazindikira kufunika kwa chikondi, monga momwe Yehova Mulungu amachigogomezera m’Mawu ake Baibulo.

Buku lakuti Love and Its Place in Nature linati ngati palibe chikondi “ana amangofa.” Komabe, kufunika kwa chikondi kumeneko sikutha anthu akakula. Katswiri wa sayansi ya anthropology anati chikondi “chili pakati pa zinthu zonse zimene anthu amafunikira monga momwe lakhalira dzuŵa pa mapulaneti . . . Mwana amene sakondedwa, makemikolo a thupi lake, thupi lake lomwe, ndi maganizo zimasiyana kwambiri ndi za mwana amene amakondedwa. Mwana wokondedwayo amakula mosiyana kwambiri ndi amene sakondedwa.”

Kodi mungalingalire mmene moyo udzakhalira padziko ngati anthu onse adzakhala okondanadi? Taonani, palibenso aliyense amene adzada mnzake chifukwa chakuti ndi wadziko lina, kaya wafuko lina, kapena ali ndi khungu losiyana ndi lake! Pansi pa ulamuliro wa Mfumu yoikidwa ndi Mulungu, Yesu Kristu, dziko lapansi lidzadzala ndi mtendere ndi chikondi, pokwaniritsa salmo louziridwa la m’Baibulo:

“Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu . . . Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphaŵi, nadzaphwanya wosautsa. . . . Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi. Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi. Pakuti adzapulumutsa waumphaŵi wopfuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.”—Salmo 72:1, 4, 7, 8, 12, 13.

Woipa sadzaloledwa kukhala m’dziko latsopano la Mulungu, monga momwe limalonjezera salmo lina m’Baibulo: “Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi. Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:9-11.

Ndiye, kenaka malingaliro ndi matupi a anthu onse omvera, kuphatikizapo amene adzaukitsidwa kwa akufa mwa chiukiriro, adzakhala atachiritsidwa. Pomaliza, aliyense amene adzakhala ndi moyo adzasonyeza mwangwiro chifanizo cha Mulungu. Potsirizira pake nkhondo yaikulu yofuna kuchita chabwino idzatha. Kusagwirizana pakati pa chilakolako chathu chofuna kukhala ndi moyo ndi imfa yomwe ilipoyi kudzakhalanso kutatha! Inde, ili ndi lonjezo loona la Mulungu wathu wachikondi: “Sipadzakhalanso imfa.”—Chivumbulutso 21:4; Machitidwe 24:15.

Choncho inu, musaleke kumenyera nkhondo kuchita chabwino. Mverani chenjezo la Mulungu: “Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha.” Moyo umenewo m’dziko latsopano la Mulungu ndiwo umene Baibulo limatcha kuti “moyo weniweniwo.”—1 Timoteo 6:12, 19.

Muyenera kuyamikira choonadi chonenedwa m’Baibulo chakuti: “Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga.” Kuyamikira choonadi chimenecho ndi chinthu chofunika kwambiri kuti mukalandire moyo m’dziko lapansi latsopano la Yehova la chikondi ndi chilungamo.—Salmo 100:3; 2 Petro 3:13.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Moyo m’dziko latsopano la Mulungu ndiwo umene Baibulo limautcha kuti ‘moyo weniweni’.—1 Timoteyo 6:19

[Chithunzi patsamba 25]

Anthu adawomba zitsulo zotetezera m’mphepete mwa msewu wa malamulo a Mulungu, zotsatirapo zake ndi zoŵaŵa

[Chithunzi patsamba 26]

Anthu pansi pa ulamuliro wa Mulungu, adzasangalala ndi dziko latsopano la mtendere

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena