Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 9/8 tsamba 21
  • Kutengekatengeka ndi Zilengezo za Malonda Zochuluka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutengekatengeka ndi Zilengezo za Malonda Zochuluka
  • Galamukani!—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Luso la Kukopa
    Galamukani!—1998
  • Mphamvu ya Osatsa Malonda
    Galamukani!—1998
  • Fodya ndi Kusanthula
    Galamukani!—1989
  • Gawo 6: Kukhupuka ndi Kugwa kwa Dongosolo Lamalonda
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 9/8 tsamba 21

Kutengekatengeka ndi Zilengezo za Malonda Zochuluka

“ATATE, kodi mwezi umalengeza chiyani?” Funso lachilendo limeneli, limene mwana anafunsa, linali m’ndakatulo imene Carl Sandburg analemba zaka pafupifupi 50 zapitazo. Mtsogolomu, mwina funso lotero silikhalanso lachilendo ayi. Malinga ndi magazini ya New Scientist, akuluakulu aŵiri a makampani osatsa malonda ku London akukonza kuti azilunjikitsa kuŵala kwa dzuŵa pamwezi kuti mawu osatsira malonda azionekera pamwezipo.

Taganizani zogwiritsa ntchito mwezi ngati chikwangwani! Taganizani zolengeza uthenga wa malonda kwa anthu onse padziko lapansi, uthenga umene oonera ake sangauzimitse, kuudula, kuutaya kudzala, kapena kutseka mawu ake. Mwina ganizo limenelo silikukusangalatsani, koma ena angaone kuti likukwaniritsa zolinga zawo.

Pamene kusatsa malonda sikunafikebe ku mwezi, iko kwaphimba dziko lapansi. Magazini ambiri a ku America ndi manyuzipepala amasunga 60 peresenti ya masamba awo kuikapo zilengezo za malonda. The New York Times ya Lamlungu yokha nthaŵi zina imakhala ndi masamba 350 osatsa malonda. Nyumba zina za wailesi zimawononga mphindi 40 pa ola lililonse zikusatsa malonda.

Kenako pali wailesi yakanema. Malinga ndi kunena kwina, achinyamata a ku America amaonera zilengezo za malonda pawailesi ya kanema mlungu uliwonse kwa maola pafupifupi atatu. Pofika nthaŵi imene amaliza maphunziro asekondale, amakhala ataonera zilengezo za malonda 360,000 pa TV. Mawailesi a kanema amasatsa malonda m’mabwalo a ndege, m’zipinda zoyembekezeramo kuchipatala, ndi m’masukulu.

Maseŵero aakulu tsopano akhala malo aakulu osatsirapo malonda. Galimoto zampikisano zimakhala zikwangwani zolengeza malonda. Ndalama zambiri zimene amalandira ochita maseŵero zimachokera kwa osatsa malonda. Munthu wina wotchuka pa kuseŵera mpira wa basketball anapeza ndalama zokwanira $3,900,000 mwa kungoseŵera mpira basi. Osatsa malonda anampatsa ndalama kuŵirikiza zimenezo kasanu ndi kanayi kuti awalengezere katundu.

Sungawathaŵe osatsa malonda. Zilengezo za malonda zimaonetsedwa pamakoma, m’mabasi, ndi m’malole. Zimapezeka mkati mwa mateksi ndi m’sitima za pansi pa nthaka—ngakhalenso pazitseko za zimbudzi za anthu onse. Timamva mauthenga olengezedwa m’masupamaliketi, m’masitolo, m’zikepe—pamene tikuyembekezera wina patelefoni. M’maiko ena anthu amalandira zilengezo zochuluka za malonda m’makalata moti ambiri amangoti akatenga makalata m’bokosi lolandiriramo amakataya makalata osafunikirawo m’bini.

Malinga ndi Insider’s Report, yofalitsidwa ndi McCann-Erickson, bungwe la padziko lonse losatsa malonda, ndalama zomwe anawonongera pa kusatsa malonda kuzungulira dziko lonse lapansi mu 1990 zinakwana pafupifupi $275,500,000,000. Kuchokera panthaŵiyo, ndalamazo zawonjezeka mpaka $411,600,000,000 mu 1997 ndipo akuti mu 1998 zifika pafupifupi $434,400,000,000. Ndalama zake kuchuluka!

Zotsatira zake? Wina wopenda zimenezo anati: “Ngati pali zinthu zimene zili ndi mphamvu koposa yosonkhezera munthu kutengera chikhalidwe cha ena, kusatsa malonda nchimodzi cha zinthuzo. . . . Zilengezo za malonda sizimangosonkhezera anthu kugula katunduyo basi. Zimasonkhezera munthu kutengera malingaliro ofala, kaonedwe ka zimene zili zofunika, zolinga, zikhulupiriro za amene ife tili ndi amene tiyenera kukhala . . . Zimaumba kaganizidwe kathu, kaganizidwe kathunso kamaumba khalidwe lathu.”

Popeza zilengezo za malonda sizitheka kuzipeŵa, bwanji osayesa kudziŵa mmene zimagwirira ntchito ndi mmenenso zingakukhudzireni?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena