Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 9/8 tsamba 18-20
  • Ndingatani Kuti Ndizipeza Ndalama?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndingatani Kuti Ndizipeza Ndalama?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchitapo Kanthu
  • Kufunsira Ntchito
  • Kudzilemba Ntchito Nokha
  • Pangani Zomwe Mungathe!
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizipeza Ndalama?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Ndiyenera Kupeza Ntchito Yogwira Pambuyo Poŵeruka Kusukulu?
    Galamukani!—1990
  • Kodi Nkulakwa Kupeza Ndalama?
    Galamukani!—1997
  • Mfundo Zisanu Zomwe Zingakuthandizeni Kupeza Ntchito
    Galamukani!—2005
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 9/8 tsamba 18-20

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Ndingatani Kuti Ndizipeza Ndalama?

“Ndikufuna ntchito imene ndingamapeze nayo ndalama zochulukirapo.”—Tanya.

ACHINYAMATA ambiri amalingalira ngati Tanya. “Ndikufuna ndalama kuti ndigule galimoto ndiponso kugula zovala,” anatero wachinyamata wotchedwa Sergio. “Sindifuna kuti pachilichonse ndizidalira makolo anga.” Nayenso Laurie-Ann amagwira ntchito nchifukwa chimodzimodzicho. “Ndine mtsikana, ndipo ndimakonda kugula zinthu,” iye anatero.

Motero nzosadabwitsa kuti, malinga ndi magazini ya U.S.News & World Report, “ana atatu mwa anayi alionse a ku sekondale ku United States tsopano amapita kukagwira ntchito ataŵeruka kusukulu ndiponso kumapeto kwa mlungu.” Kumbali ina, zimenezi zimasonyeza ‘kukonda ndalama’ kumene kuli kofala m’dziko la makono lokonda chuma. (1 Timoteo 6:10) Komabe sikuti achinyamata onse amene amafuna ndalama ndi okonda chuma.

Baibulo limati, “Ndalama zichinjiriza.” (Mlaliki 7:12) Ndipo pakhoza kukhala zifukwa zambiri zofunika zimene monga Mkristu wachinyamata mungafunire kumapeza ndalama.a Mwachitsanzo, wachinyamata wotchedwa kuti Avian analongosola chifukwa chake amagwira ntchito masiku aŵiri pamlungu: “Zimandithandiza kuti ndizidzithandiza pantchito yanga monga mpainiya wokhazikika [mlaliki wanthaŵi zonse].”

Mwina mungakhale ndi zifukwa zofananazo zomwe mungafunire kuti muzichita ganyu. Mwina muli ncholinga chakuti mudzapite ku msonkhano wachikristu. Mwina cholinga chanu nchakuti mugule zovala zoti muzivala pamisonkhano yampingo. Mulimonse mmene zilili, zinthu zimenezi zimafuna ndalama. Nzoona kuti Yesu analonjeza kuti Mulungu adzasamalira amene ‘amafuna Ufumu ndi chilungamo chake.’ (Mateyu 6:33) Izi sizitanthauza kuti muyenera kumangokhala. (Yerekezerani ndi Machitidwe 18:1-3.) Choncho, kodi nchiyani chimene mungachite kuti muzipeza ndalama zowonjezereka?

Kuchitapo Kanthu

Yerekezerani kuti makolo anu avomereza zakuti muzigwira ntchito ina, choyamba muyenera kufikira anthu a m’dera lanu, aphunzitsi, ndi achibale kuti adziŵe kuti mukufuna ntchito. Ngati mukuchita manyazi kuŵafunsa pamaso, mukhoza kungoŵafunsa kuti nchiyani chimene anachita kuti apeze ntchito ali achinyamata. Akhoza kukupatsani nzeru. Pamene anthu ambiri adziwa kuti mukufuna ntchito, mpamenenso ambiri amakuuzani kumene mungaipeze ndiponso amakuimirani mukaipeza.

Kenaka yeserani kuona m’manyuzipepala ndiponso malo ena amene mungapezeko chilengezo chakuti akufuna antchito, kusukulu kwanu, ndiponso malo ena amene kumakhala anthu ambiri. “Ndimo mmene ndinapezera ntchito,” anatero wachinyamata wotchedwa Dave. “Ndinkaŵerenga m’manyuzipepala, nkumawatumizira zikalata zanga za ntchito, ndiye nkupitako.” Koma kodi mumazindikira kuti ntchito zambiri sazilengeza? Malinga ndi magazini ya Seventeen, ena amayerekezera kuti “ntchito zitatu mwa khumi sizizindikiridwa nkomwe kuti zilipo kufikira patafika munthu woyenerera kuzigwira.” Mwinamwake zingakhale bwino ngati mutamtsimikizira wolemba ntchitoyo kuti ayenera kukupezerani ntchito ndi kukulembani!

Koma motani? ‘Sindinagwirepo ntchito ina iliyonse,’ mukhoza kulingalira motero. Chabwino, talingaliraninso bwino. Kodi munayamba mwalerapo mwana makolo anu atachokapo kapena kulera mwana wa anthu ena? Izi zimasonyeza kuti mungathe kuigwira ntchitoyo. Kodi munathandizapo abambo anu kukonza galimoto? Izi zimasonyeza kuti inu mumakonda umakaniko. Kodi mumatha kutayipa kapena kugwiritsira ntchito kompyuta? Kapena kodi munakhoza bwino kusukulu? Izi ndizo mfundo zabwino zimene munganene kwa olemba ntchito.

Komanso musanyalanyaze zimene mumakonda. Mwachitsanzo, ngati mumatha kuimba ndi chida choimbira nyimbo, yang’anani ngati akufuna munthu kusitolo ya zoimbaimba. Nzodziŵikiratu kuti inu mumasangalatsidwa ndi katundu amene amagulitsidwa m’sitoloyi choncho mungathe kuyankha mafunso a ofuna kugula.

Kufunsira Ntchito

Tiyerekezere kuti mwaitanidwa kuti mukaonane ndi akuluakulu antchito kuti akakufunseni mafunso. Samalani mmene muvalire ndi mmene mupesere chifukwa maonekedwe anu amalankhula. Zovala zanu zingamuuze munthu kuti ndinu “woyenera, waukhondo, ndi wotha kulinganiza zinthu”—kapena ayi. Baibulo limanena nkhani yothandiza pamene limalimbikitsa akazi achikristu kuti “adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso.” (1 Timoteo 2:9) Zimenezi zimakhudzanso amuna. Osavala zovala za mafashoni achinyamata kapena kuvala mwauve, mosasamala kanthu kuti ntchitoyo ndi yotani.

Makhalidwe anu nawonso amanena zambiri za inu. Gwiritsirani ntchito Lamulo la Chikhalidwe ili: Chitirani ena monga mmene inu mumafunira ena kukuchitirani. (Mateyu 7:12) Fikani panthaŵi yeniyeni imene mwaitanidwayo. Sonyezani kukhala woifunadi ntchito ndi wochenjera. Sonyezani makhalidwe abwino. Mosadzitama kapena kukulitsa zinthu ndi mkamwa, nenani chifukwa chake mukuona kuti ndinu woyenera kugwira ntchitoyo. Nenani zofunika zokha.

Akatswiri ena odziŵa za nkhaniyi amati muzipita ndi (kapena kutumiziratu) ndandanda yooneka bwino yonena za ntchito imene mumagwira ndi maphunziro anu. Muyenera kuphatikizapo dzina lanu, adiresi, nambala ya telefoni, chifukwa chake mukufuna ntchitoyo, maphunziro anu (kuphatikizapo maphunziro ena apadera amene mungakhale mutaphunzira), ntchito yomwe munagwirapo kale (zonse ziŵiri ntchito yolipidwa kapena yongothandiza chabe), maluso apadera amene muli nawo, zinthu zomwe mumakonda ndi zomwe mumachita panthaŵi yomwe mukungopumula (izi zingasonyeze ngati mungaithedi ntchitoyo) ndiponso kakalata konena kuti pali anthu amene angakuchitireni umboni ngati atawafuna. Mungathenso kulemba pepala lina losonyeza maina, maadiresi, ndi manambala a telefoni a anthu ena amene angathe kukuyamikirani kuti mutha kugwira ntchitoyo. Koma, onetsetsani kuti mwauziratu anthuwo musanachite zimenezo. Anthu ameneŵa angathe kukhala omwe anakulembanipo ntchito kale, mphunzitsi, mlangizi wapasukulu, mnzanu koma wachikulire—amene angathe kuchitira umboni za maluso anu, kunena zinthu zomwe mungathe kuchita, ndiponso umunthu wanu.

Kudzilemba Ntchito Nokha

Koma nanga bwanji ngati mosasamala kanthu za kuyesayesa kwanu simukupezabe ntchito? Izi nzofala m’maiko ambiri. Koma musataye mtima. Yankho likhoza kukhala kuyamba bizinesi. Ubwino wake nchiyani? Mungathe kumadzipangira nokha ndandanda ya mmene mugwirire ntchito, kaya kugwira kwambiri kapena pang’ono monga mmene mufunira. Komabe kudzilemba ntchito nokha kumafuna kuti mukhale akhama, odziletsa, ndiponso ofunitsitsa kuchita ntchitoyo.

Koma nanga, ndi ntchito yanji imene mungayambe? Lingalirani za kumene mumakhalako. Kodi kukufunika zinthu zina kapena kuti mugwire kantchito kena kamene palibe wina aliyense amene akukachita? Mwachitsanzo, mwinamwake mumakonda ziŵeto. Mungayambe kumasambitsa kapena kumeta ubweya wa ziŵeto za anansi anu a komweko nkumalandira malipiro. Mwinamwake mumaimba chida chinachake choimbira. Kodi simungamaphunzitse ena kuimba? Mwinamwake mukhoza kumagwira ntchito imene ena saikonda, monga kutsuka mawindo kapena kuchapa. Mkristu sachita manyazi kugwira ntchito ndi manja ake. (Aefeso 4:28) Mwinanso mungayesere kuphunzira ntchito ina. Kayang’aneni mu laibulale mabuku ophunzitsa ntchito zosiyanasiyana kapena funsirani munthu wina kuti akuphunzitseni. Mwachitsanzo, wachinyamata wotchedwa Joshua anakaphunzira zolembalemba. Ndiye anayamba kabizinesi kake komalemba makadi oitanira anthu ku ukwati.—Onani bokosi lakuti “Ntchito Zimene Mungayambe.”

Chenjezo: Osayamba ntchito iliyonse musanayambe mwadziŵa kuti imafuna ndalama zingati zoyambira ndiponso zinthu zonse zomwe zidzakhudzidwapo. (Luka 14:28-30) Choyamba kambitsiranani nkhaniyo ndi makolo anu. China, kambitsiranani ndi ena amene anayamba achitapo bizinesi yotero. Kodi mudzafunikira kulipira msonkho? Kodi mudzafunikira kuti mukhale ndi layisensi kapena chilolezo? Fufuzani kwa oona za ntchito yoteroyo kuti mumve zambiri.—Aroma 13:1-7.

Pangani Zomwe Mungathe!

Komabe pali vuto la kukhala ndi zochuluka zomwe sungathe kuchita. Laurie-Ann ananena zotsatirazi za achinyamata omwe ali pantchito: “Salemba homuweki ndiponso amakhala otopa kwambiri mwakuti samvetsera m’kalasi.” Nzoona kuti mbali zina za dziko lapansi, achinyamata sangachitire mwina koma kugwira ntchito kwa maola ambiri kuti athandize panyumba pawo. Koma ngati inu mulibe vuto limenelo, nkuchitiranji zimenezo? Malinga nkunena kwa akatswiri ambiri, kugwira ntchito kwa maola oposa 20 pamlungu kwinaku mukumapita kusukulu nkoposa mlingo ndipo sikupindula. Ena amaona kuti ndibwino kugwira ntchito maola asanu ndi aŵiri kufika khumi pamlungu.

Ngati muthera nthaŵi yanu yambiri, mphamvu, ndi chidwi chanu pazinthu zomwe mumachita mutaŵeruka kusukulu, ndiye kuti thanzi lanu, kakhozedwe kanu m’kalasi, makamaka uzimu wanu ungabwerere mmbuyo. Ndithudi, sikuti ndi akuluakulu okha amene amapusitsidwa ndi “chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina.” (Marko 4:19) Motero chitani zokhazo zomwe mungathe. Solomo anachenjeza za kugwira ntchito mopambanitsa, anati: “Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja aŵiri oti tho pali vuto ndi kungosautsa mtima.”—Mlaliki 4:6.

Kupeza ndalama kungakhale kofunika. Ndipo ngati cholinga chanu nchabwino pakuchita zimenezo ndipo chaumulungu, monga wachinyamatayo Avian amene anatchulidwa poyamba paja, mungatsimikizire kuti Yehova adzadalitsa zoyesayesa zanu. Komabe tsimikizirani kuti musakhale otangwanika kwambiri kwakuti nkuiŵala “zinthu zofunika kwambiri,” ndizo zinthu zauzimu. (Afilipi 1:10, NW) Ngakhale kuti ndalama ‘zimachinjiriza,’ ndi ubwenzi wanu ndi Mulungu umene ungapangitse kuti zinthu zikuyenderenidi bwino.—Mlaliki 7:12; Salmo 91:14.

[Mawu a M’munsi]

a Nkhani za “Achinyamata Akufunsa Kuti . . .  ” zomwe zinali m’magazini a December 8, 1990; January 8, 1991 ndi October 8, 1997, mu Galamukani! zinalongosola ubwino ndi kuipa kwa ntchito yomwe mungamagwire mutaŵeruka kusukulu.

[Bokosi patsamba 20]

Ntchito Zimene Mungayambe

• Kutsuka mawindo

• Kunyamula kapena kugulitsa manyuzipepala

• Kufoshola (chipale chofewa) snow

• Kulima kapena kuthirira maluŵa

• Kulera mwana

• Kudyetsa, kukusa, kapena kusambitsa ziŵeto

• Kupukuta nsapato

• Kusoka ndi kusita zovala

• Kulima mbewu zakudimba nkumagulitsa

• Kuŵeta nkhuku kapena kumagulitsa mazira

• Kutaipa kapena kulemba ndi kompyuta

• Kutumikira pamalo ena alionse

• Kunyamula ndi kukatula katundu

• Kuphunzitsa kuimba kapena maphunziro ena

[Chithunzi patsamba 19]

Kugwira ntchito kwambiri kungathe kupangitsa kuti muyambe kumalakwa m’kalasi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena