Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingapange Bwanji Choonadi Kukhala Changachanga?
“Ndinaleredwa monga wa Mboni za Yehova, ndipo nthaŵi zonse ndinkalingalira kuti ngati waleredwa choncho, ndiye kuti umamdziŵadi Yehova. Koma ndinkalingalira molakwa kwambiri!”—Antoinette.
“CHOONADI nchiyani?” Pontiyo Pilato, munthu amene anapereka Yesu kuti apachikidwe ndiye anafunsa funso limenelo. (Yohane 18:38) Komabe, zimaoneka kuti Pilato anafunsa funso lakelo mwaukali kuti athetse—osati kuyambitsa—kukambitsirana koona mtima. Sikuti iye ankafunadi kudziŵa “choonadi.” Koma nanga bwanji za inu? Kodi mukufuna kudziŵadi choonadi?
Afilosofi akhala akulingalira za chimene choonadi chili kwa zaka mazana ambiri, komabe mokhumudwitsa sanapeze chimene amafuna pa kuyesayesa kwawo. Koma inu mukhoza kupeza yankho la funso la Pilato. Yesu Kristu anaphunzitsa kuti Mawu a Mulungu ndi choonadi. Ndiponso ananena za iye mwini kuti “ndi choonadi.” Ndipo mtumwi Yohane analemba kuti: ‘Choonadi chinadza mwa Yesu.’ (Yohane 1:17; 14:6; 17:17) Chiphunzitso chonse chachikristu, chimene pambuyo pake chinakhala mbali ya Baibulo, chimatchedwa kuti “choonadi” kapena “choonadi cha Uthenga Wabwino.” (Tito 1:14; Agalatiya 2:14; 2 Yohane 1, 2) Chiphunzitso chachikristu chimenechi chimanena zinthu monga dzina la Mulungu, kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu, chiukiriro, ndi dipo la Yesu.—Salmo 83:18; Mateyu 6:9, 10; 20:28; Yohane 5:28, 29.
Achinyamata zikwizikwi aphunzitsidwa choonadi cha Baibulo ndi makolo awo achikristu. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti amenewo “alikuyenda m’choonadi”? (3 Yohane 3, 4) Si choncho. Mwachitsanzo, Jennifer wazaka 20 analeredwa monga wa Mboni za Yehova. Iye amakumbukira kuti: “Amayi anga ankanditenga kupita kumisonkhano ya Mboni ndipo ankanena kuti ndiyenera kumalingalira za ubatizo. Koma ine ndekha ndinkalingalira kuti, ‘Sindifuna kudzakhala wa Mboni mpaka kalekale. Ndimangofuna zinthu zondisangalatsa!’”
Achinyamata ena amakhulupirira zimene amaphunzitsidwa, koma amalephera kudzithandiza kudziŵa zinthu zozama zimene Baibulo kwenikweni limaphunzitsa. Kodi pangakhale zoipa zanji? Yesu anachenjeza kuti ena “alibe mizu mwa iwo okha.” Otero ‘amakhala kanthaŵi, pakudza masautso kapena mazunzo chifukwa cha mawu, pomwepo amakhumudwa.’ (Marko 4:17) Ena angathe kulongosola zambiri ndithu za chikhulupiriro chawo chokhala ndi maziko m’Baibulo, koma sanadziŵe Mulungu monga wawo wa iwo eni. Mtsikana wina wotchedwa Aneesa anati: “Sindiganiza kuti ndinali paubwenzi ndi Yehova pamene ndinali wamng’ono . . . Ndimaona kuti zinkangodalira chabe ubwenzi umene makolo anga anali nawo ndi iye.”
Nanga zili bwanji kwa inu? Kodi Yehova ndi Mulungu wa makolo anu chabe? Kapena mungathe kunena monga wamasalmo kuti: “Ndakhulupirira inu, Yehova: Ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga.”? (Salmo 31:14) Kuti mudziŵedi kaimidwe kanu pamafunikira kulimba mtima. Wachinyamata wina wotchedwa Alexander ananena kuti: “Kwa ine, chinthu choyamba kuchita chinali kudzifufuza moona mtima.” Mutafufuza bwino moyo wanu, mwina mudzazindikira kuti simunayambe mwafufuzapo choonadi (Chiphunzitso chonse cha chikristu) inu mwini. Mungakhale muli wosatsimikizira kwenikweni, motero mungakhale mulibe cholinga chenicheni m’moyo wanu, popanda kwenikweni komwe mukuloŵera.
Pamisonkhano yawo yachikristu, Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri zimaimba nyimbo yakuti “Pangani Chowonadi Kukhala Chanu.”a Malangizo amenewo angakhale oyenerera kwa inu. Koma nanga mungazichite bwanji zimenezo? Kodi nkuyambira pati?
Zindikirani Vutolo Inu Mwini
Pa Aroma 12:2, timapeza uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: “Mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” Kodi zimenezo mungachite motani? Mwa kukhala ndi “chidziŵitso cholongosoka cha choonadi.” (Tito 1:1, NW) Anthu a mu mzinda wa Bereya sankavomereza popanda kufunsa za zimene azimva. M’malo mwake, iwo [‘ankasanthula] m‘malembo masiku onse, ngati zinthu [zimene anali kuphunzira] zinali zotero.’—Machitidwe 17:11.
Wachinyamata wina wachikristu wotchedwa Erin anaona kuti nkofunika kuti nayenso achite zomwezo. Iye akukumbukira kuti: “Ndinkafufuza. Ndinkadzifunsa ndekha kuti, ‘Kodi ndingadziŵe bwanji kuti chimenechi nchipembedzo choona? Kodi ndingadziŵe bwanji kuti kuli Mulungu wotchedwa Yehova?’” Bwanji osayamba phunziro laumwini nanunso? Mukhoza kuyamba ndi buku lonena za m’Baibulo la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.b Liŵerengeni bwino. Ŵerengani Malemba onse omwe ali m’nkhaniyo ndipo onani mmene akugwirizanirana ndi nkhani. Mudzadabwa kuona mmene mukumvera ponena za choonadi pamene mukhala “wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.”—2 Timoteo 2:15.
Mtumwi Petro ananena kuti muli zinthu zina m’Baibulo “zovuta kuzizindikira,” ndipo mudzapeza kuti zimenezi nzoona. (2 Petro 3:16) Koma mzimu wa Mulungu udzakuthandizani kuti mumvetse ngakhale nkhani zovuta. (1 Akorinto 2:11, 12) Pemphani kuti Mulungu akuthandizeni pamene zikukuvutani kumvetsa kanthu kena. (Salmo 119:10, 11, 27) Yesani kufufuza zina zambiri m’mabuku ofalitsidwa ndi Watch Tower Society. Ngati simukudziŵa mmene muchitire zimenezo, pemphani wina kuti akuthandizeni. Makolo anu kapena ena achikulire mwauzimu mumpingo wachikristu angathe kukuthandizani.
Kumbukirani kuti simukuphunzira ncholinga choti ena akutameni chifukwa cha chidziŵitso chanu. Wachinyamata wotchedwa Collin anati: “Umakhala ukufuna kudziŵa kuti Yehova ndi munthu wotani.” Khalani chete kanthaŵi kulingalira zimene mukuŵerenga kuti zikhazikike mumtima mwanu.—Salmo 1:2, 3.
Zikhozanso kukuthandizani ngati mumagwirizana ndi mpingo pamisonkhano yachikristu. Ndiponso, monga mmene mtumwi Paulo analembera, mpingo ndi “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Timoteo 3:15) Achinyamata ena amadandaula kuti misonkhano yachikristu imakhala yosasangalatsa ndi yotopetsa. Collin anati, “Ngati sukonzekera popita kumisonkhano ndiye kuti sukamvapo zambiri.” Choncho musanapite muyenera kukonzekereratu maphunzirowo. Misonkhano imasangalatsa ngati ukutengamo mbali—osati kumangoonerera.
Kodi Ndinu Wotangwanika Mpaka Kulephera Kukonzekera?
Kunena zoona, chifukwa cha ntchito ya kusukulu, ntchito ya panyumba, kuti mupeze nthaŵi yokonzekera kungakhaledi kovuta. Mtsikana wina wotchedwa Susan analemba kuti: “Kwa zaka zambiri malingaliro akhala akundivuta pozindikira kuti ndimayenera kukonzekera misonkhano ndi kuphunzira pandekha, koma sindinkatha kuchita zimenezo.”
Susan anaphunzira “kusawononga nthaŵi” pazinthu zosafunika kwenikweni. (Aefeso 5:15, 16, NW) Choyamba anapanga ndandanda ya zinthu zimene afunika kuŵerenga. Ndiye kenaka anagaŵa nthaŵi yoti aŵerenge. Komanso anawonjezerapo nthaŵi yoseŵera. Iye ananena kuti: “Osaika pandandanda nthaŵi iliyonse imene mukhale opanda chochita. Tonsefe timafuna nthaŵi yopumula.” Nanunso zinthu zidzakuyenderani bwino ngati muli ndi ndandanda.
Uzankoni Ena Zimene Mukuphunzira
Kugwiritsira ntchito zimene mukuphunzira nkothandiza kwambiri kuti zikhazikike mumtima mwanu. Yeserani kuphunzitsako wina. Wamasalmo anati: “Pakamwa panga padzanena zanzeru; ndipo chilingiriro cha mtima wanga chidzakhala cha chidziŵitso.”—Salmo 49:3.
Ngati simuchita manyazi ndi uthenga wabwino, simudzakayikira kuuzako anzanu kusukulu ndiponso ena amene mungakumane nawo. (Aroma 1:16) Ngati mugwiritsira ntchito mpata umenewu kulankhula za choonadi ndi ena, mudzakhala mukugwiritsira ntchito zimene mwaphunzira; motero mudzakhomereza choonadi m’malingaliro ndi m’mtima mwanu.
Samalani ndi Mabwenzi Anu
M’zaka za zana loyamba Akristu ena anapita patsogolo bwino mwauzimu. Koma posapita nthaŵi mtumwi Paulo anaŵalembera kuti: “Anakuletsani ndani kuti musamvere choonadi?” (Agalatiya 5:7) Zotero zinamchitikiranso mnyamata wina wotchedwa Alex. Iye anavomereza kuti kuyesayesa kwake kuti aphunzire Mawu a Mulungu sikunkaphula kanthu chifukwa cha “kucheza ndi mabwenzi oipa.” Kuti mupite patsogolo mwauzimu, muyenera kusintha pankhani imeneyinso.
Koma kukhala ndi mabwenzi abwino kudzakuthandizani kupita patsogolo. Miyambo 27:17 imati: “Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.” Pezani anthu oti mukhoza kuŵatsanzira—anthu amene amagwiritsira ntchito choonadi m’miyoyo yawo. Nthaŵi zina sipafunikiranso kuti mukafune kunja kusiya m’banja mwanu momwemo. Mtsikanayo Jennifer akukumbukira kuti: “Chitsanzo chabwino kwa ine chinali agogo anga amuna. Nthaŵi zonse Lamlungu ankathera maola atatu kukonzekera phunziro la Baibulo la mpingo. Ankayang’ana lemba lililonse la m’phunzirolo m’mabaibulo osiyanasiyana ndi kufufuza mawu m’dikishonale yawo. Iwo ankadziŵa zinthu za m’Baibulo zomwe sizimvekamveka. Chilichonse chomwe mungaŵafunse, iwo yankho ankalipeza.”
Ngati mupanga choonadi kukhala chanuchanu, mumakhala mutapeza chinthu chamtengo wapatali—chinthu chimene simungalole kuchitaya zivutezitani. Choncho osamatcha choonadi kuti “chipembedzo cha makolo anga.” Muyenera kukhala otsimikiza mtima monga wamasalmo amene anati: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) Mwakuzindikira zimene Baibulo limaphunzitsa, kuzikhulupirira, kuuzako ena chikhulupiriro chanu, ndiponso koposa zonse, kumakhala mogwirizana ndi zikhulupiriro zimenezi, mudzasonyeza kuti mwapanga choonadi kukhala chanu.
[Mawu a M’munsi]
a Yochokera m’buku la nyimbo la Imbirani Yehova Zitamando, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 21]
Pangani choonadi kukhala chanuchanu mwa kufufuza ndi kuphunzira panokha