Kodi Ndege n’Zodalirika Motani?
PACHAKA chimodzi anthu ngati theka la miliyoni amafera pamsewu. Koma anthu ofa pangozi yandege mu 1996 anali 1,945. Mu 1997 chiŵerengero chake chinatsika mpaka pa 1,226. Malinga ndi mmene ananenera a kampani yokonza ndege za Boeing, “pamaulendo 1 miliyoni ndege zonyamula anthu zimagwa nthaŵi zosakwana ziŵiri.”
Komabe, ngozi zandege zimaulutsidwa kwambiri panyuzi, pomwe ngozi zatsiku ndi tsiku zapamsewu zimangoonedwa ngati zozoloŵereka. Ku United States, maulendo a pabasi ndiwo okha amene amaonedwa ngati abwino kuposa apandege.
Kodi n’chifukwa chiyani ndege ili bwino kuposa galimoto? Chifukwa china chodziŵikiratu n’chakuti ndege n’zosiyana ndi magalimoto, izo zimaulukira kutali ndi zinzake. China n’chakuti oyendetsa ndege ambiri n’ngophunzitsidwa zedi ndipo amasamala ntchito yawo monga mwa udindo wawo. Woyendetsa ndege ya Boeing 747 amayenera kukhala wazaka 50 ndipo ayenera kukhala ndi luso loyendetsa ndege kwa zaka 30. Onse oyendetsa ndege amakumbukira mfundo imodzi yofunika yakusamala ngozi. Poti nawonso moyo wawo umakhala pachiswe.
Kukhala Osamala mu Deck
Mutati muime muyang’ane mkati mwa deck (kachipinda mokhala oyendetsa ndege), mudzaona kuti ziŵiya zonse zofunika n’ziŵiriziŵiri—zina zili kulamanzere za woyendetsa ndipo zina zili kulamanja za woyendetsa ndege wachiŵiri.a Choncho, malinga ndi buku lakuti The Air Traveler’s Handbook, “zitangochitika kuti mwina wina wakomoka, mnzakeyo ndiye adzagwirizira nthaŵi yomweyo mpaka akafike popanda vuto. Pouluka, woyendetsa ndege aliyense angamaone ziŵiya za mnzake, ndi kutsimikizira kuti zonse zikusonyeza zizindikiro zofanana.”
Chinthu china chothandizira kusamala ngozi mu deck n’chakuti woyendetsa limodzi ndi wachiŵiri wake nthaŵi zonse amadya zakudya zosiyana. Chifukwa? Kuchitira kuti mwina winayo atadwala m’mimba, angokhala mmodzi yemweyo, osati onsewo.
“Ndege zimakhala ndi mitundu iŵiri kapena ingapo ya zoimitsira, zina zoiteretsa bwino pansi, kuchitira kuti zina zikalephera, zina zigwire ntchito.” Masiku ano ndege zambiri zimafunikira kukhala ndi mitundu iŵiri kapena itatu ya mabuleki kuchitira kuteteza ngozi.
Kodi Mungatani?
Nawa machenjezo angapo, omwe onse oyenda pandege angawagwiritse ntchito: Ŵerengani khadi la malangizo ofotokoza zimene muyenera kuchita pangozi, ndipo mvetserani ogwira ntchito m’ndege pofotokoza njira zopeŵera ngozi pamene ndege iliyonse ikunyamuka. Pamene mukukhala pansi, onani pamene pali khomo lotulukira lapafupi kwambiri. Ndiye ngati ngozi ili pafupi kuchitika, mvetserani zimene ogwira ntchito m’ndegewo akulangiza. Onse anaphunzitsidwa bwino kwambiri kudziŵa zochita ngati zinthu zavuta. Pamene malangizo aperekedwa, apaulendo afunikira kuchita mwamsanga ndi kuiŵala za katundu wawo. Moyo n’ngwofunika kwambiri kuposa katundu.
Ndege zamakono kaŵirikaŵiri zimauluka pamwamba pamitambo, choncho ndege zoyenda maulendo ataliatali zimayenda mosagwederagwedera. N’chifukwa chake anthu ambiri sachita chizungulire akatsikamo. Ngati woyendetsa ndege akuganiza kuti mwina ndege idzagwederagwedera, kaŵirikaŵiri amauziratu apaulendo kuti adzimangirire malamba.
Kodi ulendo wapandege n’ngwabwinopo? Yankho n’lakuti inde. Koma apaulendo ambiri amaona kuti zimawavuta kusintha zimene anazoloŵera. Ndizo ziti? Kuti akhale choyang’ana kumbuyo m’malo mokhala choyang’ana kutsogolo! Ubwino wakukhala choncho ungakhale uti? Ngati ndegeyo yachepetsa liŵiro mwadzidzidzi, apaulendowo amachirikizika mwa kutsamira mpando womwewo umene akhalapo, m’malo mongodzimangirira ndi lamba pamimba, lamba lapamimba si lokwanira poyerekezera ndi lamba la m’galimoto lomwe limadzeranso pachifuŵa. Komabe, anthu amakonda kuyang’ana kumene akupita osati kumene akuchokera!
Kodi Mumaopa Kukwera Ndege?
Akuti mwa anthu aakulu asanu ndi mmodzi a ku America, mmodzi mwa iwo amaopa kukwera ndege. Ena mantha awo n’ngopambanitsa—mantha ake aja om’pundula munthu. N’chiyani chimene chingawathandize?
Kudziŵa zambiri kungam’thandize wapaulendo kutha mantha. Chaka chilichonse padziko lonse, ndege ngati 15,000 zimene zimatera pamabwalo andege pafupifupi 10,000 zimanyamula anthu oposa 1.2 biliyoni popanda ngozi zambiri kapena zochitika zina zachilendo. “Malinga ndi zimene ananena a [kampani ya inshuwalansi], ya Lloyd ku London, kuyenda pandege kuli bwino kwambiri nthaŵi 25 kusiyana ndi kuyenda pagalimoto.”
Ngati mumachita mantha kuyenda ulendo wapandege, ŵerengani mabuku onena za ulendo wapandege, ndi onenanso za mmene oyendetsa ndege amawaphunzitsira. Ŵerengani za miyezo yabwino kwambiri imene oyendetsa ndege amaphunzitsidwa ndi malamulo owauza kuti ayenera kugona maola okwanira, ndi malamulo owaletsa kumwa kwambiri moŵa atatsala pang’ono kuyendetsa ndege, limodzi ndi kuwapima kuti aone ngati ena asuta kapena kumwa zogodomalitsa ubongo. Ndiponso oyendetsa ndege amayesedwa mayeso kaŵiri pachaka kuti aone mmene amachitira ngozi itayamba kuchitika. Mayeso amenewo amakhaladi ngati zenizeni moti oyendetsa ndege ena amatuluka “akunjenjemera ndipo atanyowa ndi thukuta.” Ngati wina woyendetsa ndege walephera mayeso amenewo, amamulanda chilolezo choyendetsera ndege yonyamula anthu.
Miyezo imeneyo n’njapamwamba kwambiri kuposa yonse imene oyendetsa galimoto amafunikira kukwanitsa. Choncho, mutadziŵa zambiri ponena za ndege ndi oyendetsa ake, mudzalimbanso mtima kwambiri.
Mwinanso mutakaona bwalo landege mungathandizike. Yang’anitsitsani zimene apaulendo akuchita, ndiponso onani mmene anthu ena akuchitira. Mudzaona kuti anthu ambiri potsika m’ndege amangotsika ngati kuti akutsika m’basi. Kwa iwowo, ulendo wapandege wangokhala chinthu cha masiku onse. Onaninso mmene ndege zimanyamukira ndi kutera kwake. Zindikirani mmene ndege inapangidwira mwanjira yoti ikhoza kuuluka popanda vuto ndipo chitani nazo chidwi.
Potsiriza ngati mutadzafuna kuyenda pandege, muuzeni wogwira ntchito m’ndege kuti inuyo mukuyamba kumene kuyenda pandege ndi kutinso mwina mungachite mantha pang’ono. Anthuwo n’ngoidziŵa bwino ntchito yawo kwambiri moti amadziŵa mmene angakuthandizireni kukhazika mtima pansi. Yesani kukhazika mtima pansi. Pamene woyendetsa ndege wanena kuti tsopano mungathe kumayendayenda m’ndegemo, nyamukani muyendeyende cha kuno ndi uko. Mmene mukuteromo mwina mudzakhala mutatsala pang’ono kutaya mantha okwera ndege!
[Mawu a M’munsi]
a M’ndege zambiri woyendetsa angakuloleni kuyang’ana mkati mwa deck pamene ndegeyo idakali chiimire. Angakuyankheninso mafunso anu.
[Mawu Otsindika patsamba 19]
“Malinga ndi zimene ananena a [kampani ya inshuwalansi] ya Lloyd ku London kuyenda pandege kuli bwino kwambiri nthaŵi 25 kusiyana ndi kuyenda pagalimoto”
[Zithunzi patsamba 20]
Kuphunzira kukhazika mtima pansi kungapangitse ulendo wanu wapandege kusangalatsa
[Mawu a Chithunzi patsamba 18]
Photograph courtesy of Boeing Aircraft Company