Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 4/8 tsamba 8-11
  • Kodi Ndani Adzateteza Ana Athu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Adzateteza Ana Athu?
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Makolo Angachite Zambiri
  • Njira Yeniyeni Yothetsera Vutoli
  • Mmene Mungatetezere Ana Anu
    Galamukani!—2007
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Makolo, Tetezani Cholowa Chanu Chamtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Vutolo N’lapadziko Lonse
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 4/8 tsamba 8-11

Kodi Ndani Adzateteza Ana Athu?

ZILI BWINO kuti anthu akudziŵa kuti kusautsa ana ndi vuto lapadziko lonse. Mabungwe oteteza ana kumalonda auhule, monga lotchedwa Stockholm Congress Against Commercial Sexual Exploitation of Children, lokhala ndi nthumwi zoimira mayiko 130, ayamba kulimbana ndi vuto limeneli.

Ndiponso, mayiko ena akupanga malamulo oletsa maulendo oyendera chisembwere ndi oletsa kuuza ana kapena kuwasonyeza zolaula. Mpaka ena akulemba m’buku mayina a amuna okonda kugona ana, ndi kuwaletsa kukhala pafupi ndi ana.

Ndiyeno pali aja amene amafuna kuti ana azikhala ndi moyo wabwino, mwakupanga malamulo owateteza. Ndipo mayiko ena angapo limodzi ndi anthu enanso amakana kugula zinthu zopangidwa ndi ana.

Mosakayikira tonsefe timayamikira anthu akamachita khama kuti athetse zakugona ana, koma tisaiwale kuti vuto lakugona ana linayamba kale kwambiri mwa anthu. Kungakhale kupusa kuganiza kuti njira yapafupi monga yakupanga malamulo, idzateteza ana athu. Anthu apanga kale malamulo ambiri ndithu, komabe vutolo lilipobe. Pali mfundo imodzi yomvetsa chisoni imene imasonyeza kuti anthu achikulire n’ngopulupudza, yakuti amafuna kuikiridwa malamulo ambirimbiri owaletsa kupondereza ufulu wachibadwidwe wa ana.

Malamulo si chinthu chotsirizira choteteza ana ayi. Tangoonani mmene lachitira lamulo lamphamvu la UN la Pangano la Ufulu wa Mwana, lomwe maboma ambiri analisainira. Pali umboni wokwanira wakuti ngakhale ambiri mwa maboma ameneŵa, chifukwa chosoŵa ndalama, akulephera kuletsa anthu kusautsa ana awo. Kugona ana kudakali vuto lalikulu m’mayiko ambiri.

Makolo Angachite Zambiri

Kulera bwino ana ndi ntchito yaikulu. Kholo limafunikira kuvutika. Ndipo makolo osamala ana awo amafunikira kumaona kuti iwowo ndiwo akuvutika, osati anawo. Magazini ya Maclean’s inati nthaŵi zambiri “makolo amaona ntchito yolera ana ngati kantchito wamba.” Chidole mukhoza kuchitaya kapena ntchito wamba mukhoza kuisiya, koma kulera ana kuli udindo umene Mulungu anakupatsani.

Kukhala kwanu kholo labwino ndiyo mphatso yabwino imene mungapatse mwana wanu, chifukwa mum’thandiza kukhala ndi moyo wachimwemwe, wosungika. Koma si kuti kukhala ndi ndalama zambiri ndiko kudzathandiza anawo kukhala osungika ayi. Mwana wanu amafuna inuyo​—⁠chikondi chanu, amafuna kuti muzim’limbikitsa pamene ali ndi nkhaŵa, ndipo amafunanso nthaŵi yanu. Mwana wanu amafuna kumva mawu anu mukumuuza nkhani, amafuna kumakuonani monga chitsanzo chake, ndipo amafuna kuti muzimulangiza mwachikondi.

Pankhani zokhudza kugonana​—⁠makolo, chitani ndi ana anu modzichepetsa ndipo lemekezani maganizo ndi matupi a ana anu. Ana amaphunzira msanga kukaniza munthu wina kuwagwira paliponse, monga mmene makolo awaphunzitsira. Afunikira kuphunzitsidwa mmene ayenera kuyendera ngati ali panyumba kapena kwina. Ngati inuyo simuwaphunzitsa, munthu wina adzakuphunzitsirani, ndipo mwina simudzakondwera ndi zotsatirapo zake. Phunzitsani ana zimene ayenera kuchita ngati wina akulankhula nawo mosayenera. Auzeni ntchito ya ziwalo zawo zobisika, ndipo aphunzitseni kuti munthu wina asazigwire. Auzeni mmene ayenera kuchitira ngati munthu wina akufuna kuwavutitsa.

Nthaŵi zonse ndi bwino kudziŵa kumene kuli mwana wanu ndi kudziŵanso kuti ali ndi yani. Nanga mwana wanuyo mabwenzi ake ndani? Kodi ndani amene amasamala mwana wanu ngati inuyo mwachokapo? Kodi ndi anthu odalirika? Komabe zimenezo sizikutanthauza kuti kholo liyenera kukayikira aliyense. Adziŵeni bwino anthu achikulire amene amacheza ndi mwana wanu, osati kungowadziŵa pamaso basi.

Ganizirani za chisoni chimene makolo amakhala nacho pamene amva zothaitha kuti ana awo anali atagonedwapo ndi akuluakulu atchalitchi, aphunzitsi, kapenanso achibale omwe ankawadalira. Mungachite bwino kudzifunsa monga kholo, kuti, ‘Kodi tchalitchi changa chimalolera zogona ana kapena chimabisa milandu yakugona ana? Kodi chipembedzo changa chimaphunzitsa makhalidwe abwino?’ Mayankho a mafunso ameneŵa angakuthandizeni kusankha mwanzeru zimene muyenera kuchita pakuteteza ana anu.

Koma kuposa zonse, athandizeni kudziŵa Mlengi ndi kukonda malamulo ake, chifukwa amenewo adzawateteza. Ana akaona kuti makolo awo ali ndi makhalidwe abwino kwambiri, nawonso amatsanzira mwamsanga chitsanzo chabwinocho.

Njira Yeniyeni Yothetsera Vutoli

Zoona, malamulo ngakhale kuika anthu osautsa ana m’ndende kwanthaŵi yaitali sikungateteze ana athu. Mlengi mwiniyo, kupyolera m’Mawu ake ouziridwa, Baibulo, ndiye angathe kuphunzitsa bwino anthu kukhala ndi khalidwe labwino, mwa kusintha maganizo onga a zilombo n’kukhala anthu achikondi ndipo akhalidwe lokoma.

Zaoneka kale kuti zimenezo n’zotheka. Pali ambiri amene anasiya moyo wawo wakale wokonda akazi. Tsopano akusonyeza umboni wakuti Mawu a Mulungu n’ngamphamvu. Ngakhale kuti enawo anachita bwino kusintha, anthu ena ambiri akhalidwe loipitsitsa sadzasintha. N’chifukwa chake Yehova Mulungu walonjeza kuti posachedwapa adzachotsa onse amene amasautsa ana athu padziko lapansi​—⁠limodzi ndi maganizo awo oipa, zikhumbo zawo, ndi umbombo wawo.⁠—​1 Yohane 2:​15-17.

Ndiyeno, m’dziko latsopano la Mulungu, pamene umphaŵi udzakhala utatha, ana onse adzakhala ndi moyo wabwino osavutidwa ndi aliyense, poti umenewo ndiwo ufulu umene Mulungu anawapatsa. Si kuti zimenezi zidzatanthauza chabe kutha kwa anthu osautsa ana komanso zidzatanthauza kutheratu kwa zinthu zonse zopweteketsa maganizo a anthu lerolino: “Zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima.”​—⁠Yesaya 65:17.

Choncho, m’dziko latsopano la Mulungu, mawu a Yesu Kristu adzamveka bwino tanthauzo lake, akuti: “Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba [wolamulira padziko lapansi, mudzi wa anthu wa Paradaiso] uli wa totere.”​—⁠Mateyu 19:⁠14.

[Chithunzi patsamba 9]

Phunzitsani mwana wanu mwanzeru zimene ayenera kuchita ngati wina akufuna kumugona

[Chithunzi patsamba 9]

Kukhala kwanu kholo labwino ndiyo mphatso yamtengo wapatali kwa ana anu

[Chithunzi patsamba 9]

Thandizani ana anu kudziŵa zolinga za Mlengi ndi malamulo ake

[Zithunzi patsamba 10]

M’dziko latsopano la Mulungu, ana onse adzakondwera kwambiri ndi ubwana wawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena