Lingaliro la Baibulo
Mmene Mungasankhire Wokwatirana Naye
MKAZI WINA WOSAKWATIWA ANAFUNSIDWA KUTI, “KODI MUMAGANIZAKO ZODZAKWATIWA?” “KUGANIZA?” IYE ANAYANKHA MWAMSANGA. “NDIMADA NKHAŴA.”
YANKHO losapsatira la mkaziyu likulongosola zambiri za chikhumbo chofuna kukondedwa komanso kukhala paubwenzi chimene anthu ena ali nacho. Anthu ambiri amaona kuti kupeza munthu wokwatirana naye n’chimodzi mwa zinthu zofunikira kwambiri m’moyo. Motero padziko lonse ntchito zofuna kuthandiza anthu kupeza okwatirana nawo zachuluka kwambiri. Komabe, m’mbali zambiri za dziko, chiŵerengero cha mabanja amene akutha chikuposa cha amene akupitirira.
M’mayiko a Kumadzulo, kusankha yekha munthu amene wina akufuna kum’kwatira n’kofala. Komabe, mosiyana ndi zimenezi, kumbali zina za ku Asia ndi ku Africa, maukwati ochita kupezeredwa mkazi kapena mwamuna akuchitidwabe monga mwambo. Mulimonsemo ntchito imeneyi siyenera kuonedwa mopepuka. Pali zinthu zina zochepa chabe zimene munthu angasankhe kuchita m’moyo zimene zingabweretse chimwemwe kapena chisoni. Banja lokhala ndi chikondi lingakhale losangalatsa komanso lokhutiritsa. Komatu, ukwati womangokangana ungakhale woŵaŵa komanso wosoŵetsa mtendere.—Miyambo 21:19; 26:21.
Monganso anthu ena onse, Akristu oona, amafuna banja lawo kukhala lachimwemwe ndi lokhutiritsa. Koma amafunanso kukondweretsa Mulungu ndi kumulemekeza. (Akolose 3:23) Pakuti iye ndi Mlengi ndiponso Woyambitsa wa ukwati, Mulungu amadziŵa bwino lomwe zimene tikufunadi ndiponso zinthu zimene zili zabwino kwambiri kwa ife. (Genesis 2:22-24; Yesaya 48:17-19) Ndiponsotu, iye waona mamiliyoni ambiri a mabanja, abwino ndi oipa, kwa zaka zikwi zambiri zimene anthu akhalako. Iye akudziŵa njira zothandiza ndi zosathandiza. (Salmo 32:8) Kudzera m’Mawu ake Baibulo, iye amasonyeza mapulinsipulo omveka bwino ndiponso atchutchutchu, amene angathandize Mkristu aliyense kusankha modziŵa zimene akuchita. Kodi ena mwa mapulinsipulo ameneŵa ndi ati?
Musayang’ane Maonekedwe Okha
Kumene anthu amasankha okha yemwe akufuna kukwatirana naye, angapeze munthuyo mopanda dongosolo kapena angamudziŵe kudzera mwa anzawo kapena am’banja lawo. Nthaŵi zambiri, kukonda munthu moti uchite naye chibwenzi kumayamba chifukwa cha kumuona kukongola. Ngakhale kuti kutero n’kwachibadwa komanso n’kosonkhezera mwamphamvu, Baibulo limatilimbikitsa kuti tikaganiza zokhala pabanja tiziyang’ana zambiri osati maonekedwe okha.
“Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; Koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa,” imatero Miyambo 31:30. Mtumwi Petro ananenapo za “chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.” (1 Petro 3:4) Inde, mikhalidwe yauzimu ya wofuna kukwatirana naye, kudzipereka kwake kwa Mulungu ndi kukonda kwake Mulungu ndiponso umunthu wake wachikristu, ndi zinthu zofunika kwambiri kuposa kukongola kwakuthupi. N’kofunika kwambiri kufatsa kuti musankhe munthu amene mwamupenda bwinobwino, munthu amene ali ndi zolinga zauzimu zofanana ndi zanu ndi amenenso akuyesayesa kuonetsa zipatso za mzimu wa Mulungu. Zimenezi zidzakuthandizani kuti patsogolo mudzamange naye banja losangalatsa.—Miyambo 19:2; Agalatiya 5:22, 23.
‘Kwatirani Kokha Mwa Ambuye’
Kukhala ndi zolinga komanso zikhulupiriro zofanana ndi munthu amene mukufuna kukwatirana naye n’kofunika kwambiri. Banja n’lovutadi, ndipo limafunika kuti nonse aŵiri musinthe khalidwe ndiponso mmene mumaonera zinthu. N’zachidziŵikire kuti ngati inuyo ndi mnzanuyo muli ogwirizana kale m’zinthu zambiri, kusinthaku sikudzavuta kwambiri.
Zimenezi zikutithandiza kuona chifukwa chimene mtumwi Paulo analimbikitsira Akristu kuti ‘asakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana.’ (2 Akorinto 6:14) Paulo anadziŵa kuti kukwatirana ndi munthu amene alibe chikhulupiriro chonga chanu komanso amene samva mapulinsipulo a Baibulo monga inu kungachititse mkangano ndi kusagwirizana. Langizo la kukwatira ‘kokha mwa Ambuye’ ndi lomvekadi. (1 Akorinto 7:39) Limasonyeza maganizo a Mulungu. Anthu amene mwanzeru amalitsatira amapeŵa zosautsa ndi mavuto ambiri.—Miyambo 2:1, 9.
Mabanja Ochita Kupezeredwa
Kodi nanga kumadera amene kudakali mwambo wopezerana mabanja angatani? Mwachitsanzo, kummwera kwa dziko la India, ena anena kuti 80 peresenti ya mabanja onse amapezeredwa ndi makolo. Makolo achikristu angasankhe kutsatira kapena kusatsatira mwambo umenewu. Mulimonsemo, kupezerana mabanja kumeneku kumakhala bwino ngati chofunika kwambiri chili makhalidwe auzimu.
Anthu amene amafuna mabanja opezeredwa amaona kuti zimenezi zimaika ntchito yosankha m’manja mwa anthu odziŵa bwino ndiponso achikulire. “Makolo ena amaona kuti chifukwa cha msinkhu wa ana awo komanso kusadziŵa bwino zinthu, sangathe kuwadalira kuti angathe kuona molondola kukula kwa uzimu kwa munthu amene akufuna kukwatirana naye,” anatero mkulu wachikristu wina ku Africa. “Ana sakudziŵa moyo bwino ndipo angasankhe kuchita zinthu mongotengeka maganizo,” anawonjeza choncho mtumiki woyendayenda wina ku India. Chifukwa chakuti makolo amadziŵa bwino makhalidwe a ana awo koposa mmene amawadziŵira wina aliyense, amaona kuti iwo okha ndi amene angathe kuwasankhira mwanzeru. Angachitenso mwanzeru ngati atayamba afunsa kaye mmene mwana wawoyo akulingalilira.
Komabe, makolo akanyalanyaza mapulinsipulo a Baibulo, angadzavutike pambuyo pake ngati banjalo litadzayamba kupeza zovuta zina. Chifukwa chakuti nthaŵi zambiri pamakhala mwayi wochepa kwambiri woti wofuna kukwatiranawo adziŵane bwino, mavuto angabuke. Ndipo pamene abukadi, bambo wina wa ku India yemwe ndi Mkristu analongosola kuti, “chizoloŵezi chimene chimakhalapo ndicho choloza chala makolo.”
Makolo achikristu amene akupezera banja mwana, ayenera kuona cholinga chawo pa kusankhako. Ngati mukusankha munthu wodzakwatirana ndi mwana wanu n’cholinga chofuna chuma kapena kukhumba kukhala wapamwamba, pamadzakhala mavuto. (1 Timoteo 6:9) Choncho, amene akupezera ena mabanja ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi n’zotsimikizika kuti amene ndasankha akakhazikana mosangalala komanso mwathanzi lauzimu? Kapena, kodi ndatero pongofuna kutchukitsa banja lathu kapena kulilemeretsa kapena kupindulapo ndalama?’—Miyambo 20:21.
Uphungu wa Baibulo ndi watchutchutchu ndiponso n’ngothandiza. Pamene tikufuna munthu wokwatirana naye, khalidwe labwino komanso uzimu wa amene tikufunayo nthaŵi zonse ziyenera kukhala chinthu choyamba kuchiganizira, zilibe kanthu kuti akusankhayo ndani. Zimenezi zikachitidwa, Yehova Mulungu, Woyambitsa ukwati, amalemekezeka ndipo okwatiranawo amayamba banjalo pa maziko olimba auzimu. (Mateyu 7:24, 25) Zimenezi zidzathandiza kwambiri kuti mumange banja lachimwemwe, ndi losangalatsa.