Miyoyo Yowonongeka, Miyoyo Yotayika
“MANKHWALA osokoneza bongo ali ngati nyundo zazikulu,” anatero Dr. Eric Nestler. N’zoonadi kumwa mankhwala amphamvu ngati nyundo zazikulu ameneŵa kamodzi kokha kungakhaledi koopsa. “Mwachitsanzo Cocaine opangidwa mwatsopano akuti wakhala akupha anthu nthaŵi yoyamba kumulawa,” likulongosola choncho buku lotchedwa Drugs in America.
Mankhwala enanso opangidwa mwatsopano angakhale oopsa chimodzimodzi. “Achinyamata poti ndi osavuta kunamizidwa sangadziŵe ngakhale pang’ono kuti msanganizo wa mankhwala amene akufuna kumwa pa dansi ya ‘rave’ awononga ubongo wawo,” likuchenjeza motero buku la bungwe la United Nations lotchedwa World Drug Report. Komabe, achinyamata ambiri amagwera m’mphompho la chizoloŵezi cha kumwa mankhwalawa mwapang’onopang’ono, monga mmene zitsanzo zotsatirazi zikusonyezera.
“Kuthaŵa Moyo Weniweni”
Pedro, a m’modzi wa ana asanu ndi anayi, anabadwira m’dera lovuta mumzinda wa Córdoba, ku Spain. Ubwana wake unali wovuta kwambiri chifukwa cha uchidakwa wa atate wake. Pamene Pedro anafika zaka 14, msuweni wake anamuphunzitsa kusuta chamba. Patangotha mwezi umodzi, chinasanduka chizoloŵezi chake.
“Kumwa mankhwala osokoneza bongo kunali kungotayirako nthaŵi, kuthawa moyo weniweni, ndiponso njira yodziloŵetsa nawo m’gulu,” analongosola motero Pedro. Ndili ndi zaka 15 ndinayamba kusakaniza chamba ndi mankhwala a LSD komanso a mtundu wa amphetamine. Ndinkakonda kwambiri LSD, ndipo kuti ndipeze ndalama zowagulira ndinayamba kugulitsa mankhwala osokoneza bongo. Kwenikweni ndinkagulitsa chamba. Nthaŵi ina ndinamwa mankhwala a LSD mopitirira, ndipo sindinagone usiku wonse, ndinkangomva ngati ndachita misala. Zimenezi zinandiopsa. Ndinaona kuti ndikapitiriza kumwa mankhwala osokoneza bongo, mapeto ake ndidzamangidwa apo ayi ndidzafa. Koma chilakolako cha mankhwala osokoneza bongo chinandichititsa kunyalanyaza mantha ameneŵa. Ndinazoloŵera kwambiri kumwa LSD ndipo kuti ndiledzere ndimayenera kumwa ambiri. Ngakhale kuti anali ndi zoopsa zake ndikamwa, ndinalephera kusiya. Sindinali kudziŵa mmene ndikanasiyira.
“LSD sanali wotsika mtengo, choncho ndinaphunzira kuba m’masitolo a mikanda yamtengo wapatali, kuba tizikwama ta alendo odzacheza m’dziko, ndi kuba mawotchi ndi zikwama zandalama za anthu amene akudutsa. Ndili ndi zaka 17 ndinali nditakhazikika m’malonda ogulitsa mankhwala osokoneza bongo kwathuko, ndipo nthaŵi zina ndinali kuchita nawo umbava woba moopseza ndi mfuti. Chifukwa chakuti ndimadziŵika monga chigaŵenga anthu akwathuko anandipatsa dzina lakuti el torcido limene limatanthauza kuti ‘mambala’.
“Ukamamwa mankhwala osokoneza bongo mosakaniza ndi mowa, umunthu wako umasintha, nthaŵi zambiri umakhala wachiwawa. Ndipo chikhumbo chofuna kumwa mankhwala osokoneza bongo mopitirira chimakhala champhamvu kwambiri mwakuti chimagonjetseratu chikumbumtima chako. Moyo umakhala ndi mikwingwirima yambiri, ndipo umangokhala chiledzerere ndi mankhwalawa.
“Kuzingidwa M’dziko la Mankhwala Osokoneza Bongo”
Ana, mkazi wa Pedro anakulira ku Spain, m’banja lina lolongosoka. Pamene anali ndi zaka 14, Ana anakumana ndi anyamata angapo osuta chamba ochokera kusukulu imene anayandikana nayo. Poyamba iye anali kudana nalo khalidwe lawo loipalo. Koma Rosa mnzake wapamtima wa Ana, anali kufuna mmodzi wa anyamatawo. Mnyamatayo anam’kopa Rosa pomuuza kuti kusuta chamba si koipa ndipo kuti iye akayesa kusuta achikonda. Choncho Rosa anasuta molawa ndipo anam’patsira Ana nduduyo
“Nditasuta ndinamva bwino, ndipo pakutha pa milungu ingapo, ndinali kusuta chamba tsiku lililonse,” Ana anatero. “Patatha mwezi kapena kuposerapo, chamba chinasiya kundikhutiritsa motero ndinayamba kuchisuta pamodzi ndi mankhwala a amphetamine.
“Posachedwa ine ndi anzanga tinaloŵerera kotheratu m’gulu la anthu ogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Tinkakambirana zoti tizipikisana kuti tione amene angathe kumwa ambiri koma osavutika nawo, ndiponso amene angaledzere kwambiri. Pang’onopang’ono ndinayamba kudzipatula ku moyo weniweni, ndipo nthaŵi zambiri ndinkajomba kusukulu. Chamba ndi amphetamine sizinali kundikwananso, choncho ndinayamba kudzibaya jakisoni wa mankhwala a morphine amene ndinali kugula ku masitolo ogulitsirako mankhwala osiyanasiyana. M’nyengo ya chilimwe tinali kupita ku madansi apabwalo a nyimbo za rock, kumene nthaŵi zonse kunali kosavuta kupezako mankhwala monga LSD.
“Tsiku lina amayi anga anandipezerera ndikusuta chamba. Makolo angawa anayesetsa kunditeteza. Anandiuza za kuopsa kwa mankhwala osokoneza bongo ndipo ananditsimikizira kuti amandikonda ndipo amandifunira zabwino. Koma ndinali kuona zoyesayesa zawo monga kuti akuloŵerera m’moyo wanga. Pamene ndinali ndi zaka 16 ndinaganiza zochoka kunyumba. Ndinaloŵa nawo m’kagulu ka achinyamata amene anali kungozungulirazungulira m’dziko lonse la Spain kumagulitsa mikanda yopangidwa pamanja komanso kumamwa mankhwala osokoneza bongo. Patatha miyezi iŵiri ndinagwidwa ndi apolisi ku Málaga.
“Pamene apolisi anakandipereka kwa makolo anga, anandilandira ndi manja aŵiri ndipo ndinachita manyazi chifukwa cha zimene ndinachitazi. Bambo wanga anali kulira; zimene sindinawaonepo akuchita n’kale lonse. Ndinadandaula poona kuti ndawakhumudwitsa, koma sizinandikhudze kwambiri koti n’kadasiya kumwa mankhwala osokoneza bongo. Ndinapitiriza kumwa mankhwalawa tsiku lililonse. Nthaŵi zina ndikapanda kumwa ndinali kuganiza za kuopsa kwake, koma sindinkakuganizira kwa nthaŵi yaitali.”
Womanga Nyumba Asanduka Wogulitsa Mankhwala Osokoneza Bongo
José, mwamuna wokwatira ndiponso wansangala anakhala zaka zisanu akugulitsa chamba kuchokera ku Morocco kupita ku Spain. Kodi anayamba bwanji? José analongosola kuti, “Pamene ndinali womanga nyumba, mnzanga anayamba kugulitsa mankhwala osokoneza bongo. Chifukwa chofuna ndalamazo, ndinadzifunsa ndekha kuti, ‘Bwanji inenso osangochita chimodzimodzi?’
“Ku Morocco zinali zosavuta kugula chamba chochuluka mmene ndikanathera. Ndinali ndi bwato lothamanga kwambiri limene ndimatha kuthaŵira nalo apolisi mosavuta. Ndinkati ndikafika nacho chambacho ku Spain, ndinali kuchigulitsa m’miyulu ikuluikulu, pafupifupi makilogilamu 600 panthaŵi imodzi. Ndinali ndi anthu ondigula atatu ngati si anayi okha, ndipo anali kutenga chamba chonse chimene ndinali kuwapititsira. Ngakhale kuti apolisi anali kuyendera, chambacho chinkadutsabe osagwidwa. Akatangalefe tinali ndi zida zamphamvu kwambiri kuposa zimene apolisi anali nazo.
“Ndinapeza ndalama zambiri mosavuta. Ulendo umodzi chabe wochokera ku Spain kukafika ku North Africa umabweretsa ndalama zokwana madola 25,000 kapena mpaka 30,000. Posachedwa, ndinalemba ntchito anthu 30. Sankandigwira chifukwa chakuti ndinalemba ntchito kazitape kuti azindiuza ngati a boma atulukira za ntchito yanga.
“Nthaŵi zina ndinali kuganiza za zimene mankhwalawa akuchita kwa amene akuwamwa, koma ndinadzilimbitsa mtima pomalingalira kuti chamba si mankhwala amphamvu kwambiri ndipo sangaphe munthu. Chifukwa chakuti ndinali kupanga ndalama zambiri, zimenezi sindinkaziganizira kwenikweni. Ine mwini sindinali kumwa mankhwala osokoneza bongo.”
Ndalama Zanu Pamodzi ndi Moyo Wanu!
Monga mmene zitsanzo zimenezi zikusonyezera, mankhwala osokoneza bongo amalamulira miyoyo ya anthu. Munthu akangowazoloŵera, amavutika kwambiri kuti asiye. Monga mmene buku lotchedwa Drugs in America linanenera, akuti “Kale ku America, achifwamba anali kulozetsa mfuti kumaso kwa amene akufuna kuwabera n’kuwauza kuti, ‘Sankha pakati pa ndalama zako kapena moyo wako.’ Mankhwala oletsedwa ndi oipa kuposa achifwamba akale ameneŵa, chifukwa amatenga zonse ziŵiri.”
Kodi pali njira iliyonse yothetsera vuto la dzaoneni la mankhwalawa? Nkhani yotsatirayi idzalongosola njira zina.
[Mawu a M’munsi]
a Mayina ena asinthidwa m’nkhani zino.
[Mawu Otsindika patsamba 8]
“Kale ku America, achifwamba anali kulozetsa mfuti kumaso kwa amene akufuna kuwabera n’kuwauza kuti, ‘Sankha pakati pa ndalama zako kapena moyo wako.’ Mankhwala oletsedwa ndi oipa kuposa achifwamba akale ameneŵa, chifukwa AMATENGA ZONSE ZIŴIRI.”
[Bokosi/Chithunzi patsamba 10]
KODI MWANA WANU ANGADZAKANE KUGWIRITSA NTCHITO MANKHWALA OSOKONEZA BONGO?
KODI NDI ACHINYAMATA ATI AMENE KWENIKWENI ALI PANGOZI?
a. Amene amafuna kuonetsa kuti ndi odzidalira ndiponso saopa chilichonse.
b. Amene alibe chidwi ndi tsogolo lawo pamaphunziro kapena pa zauzimu.
c. Amene amaona kuti zochita zawo sizigwirizana ndi zochita za anthu anzawo.
d. Amene satha kusiyanitsa bwinobwino pakati pa chabwino ndi choipa.
e. Amene amaona kuti makolo awo samawachirikiza ndipo anzawo amawalimbikitsa kuti azigwiritsa ntchito mankhwalawa. Ofufuza apeza kuti “ubwenzi wabwino pakati pa wachinyamata wongosinkhuka kumene ndi makolo ake ukuoneka kuti ndi wothandiza kwambiri pothetsa mchitidwe wogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.”—tapendeketsa mawu ndife.
KODI MUNGATETEZE BWANJI ANA ANU?
a. Pokhala nawo pa ubwenzi wathithithi komanso kucheza nawo.
b. Pokhomereza m’maganizo mwawo chidziŵitso cha zimene zili zabwino ndi zimene zili zoipa.
c. Powathandiza kukhala ndi zolinga zotsimikizika.
d. Powaonetsa kuti ali m’banja lowakonda ndiponso kuti ali pakati pa anthu abwino.
e. Powaphunzitsa za kuopsa kwa kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ana ayenera kumvetsetsa chifukwa chimene ayenera kukanira mankhwalawa.
[Mawu a Chithunzi]
Gwero: United Nations World Drug Report
[Chithunzi patsamba 9]
Mankhwala osokoneza bongo ogwidwa ku Gibraltar
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy of Gibraltar Police
[Chithunzi patsamba 10]
Ndinali ndi bwato lothamanga kwambiri longa limeneli, ndipo ndinkatha kuthawira nalo apolisi mosavuta
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy of Gibraltar Police
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Godo-Foto