Kuchita Chidwi ndi Angelo
“Ife ‘tonse’ tili ndi angelo amene amatitsogolera, ndi kutiteteza . . . Tikapanda kuwavutitsa, kudzipereka kwa iwo, monga ana, mokhulupirika kotheratu ndiponso mwachikondi ndi kuyamikira kodzichepetsa, iwo adzatidalitsa moolowa manja. Amaseŵera nafe. Amatisamalira. Amatichiritsa, kutisisita, kutitonthoza mwachikondi ndi manja awo osaoneka, ndipo nthaŵi zonse iwo amayesetsa kutipatsa zimene timafuna.”—Zachokera m’buku lotchedwa “Angel Letters” (Makalata a Angelo).
MUYENERA kuvomereza kuti njirayi imene anthu ambiri amaonera angelo ndi yokopa. Malingana ndi lingaliro limene ena akulitcha kuti “uzimu watsopano,” aliyense ali ndi angelo ngakhale atakhala mmodzi chabe, mngelo amene ntchito yake ndiyo kutitonthoza ndi kutiteteza kuzoipa. Akuti mngelo wanuyo amakhala wamphamvu komanso wachikondi. Safunikira kuti muzimumvera kapena kumulambira, ndipo samakuweruzani kapena kukukalipirani. Nthaŵi zonse amakhala pambali panu, amadzipereka kuchita zotheka kuti mukhale bwino ndipo amakhala wokonzeka kukwaniritsa zofuna zanu zonse. Anthu ambiri lero amakhulupirira zinthu zimenezi ndi mtima wonse.
Inde, kukhulupirira angelo si kwachilendo. Kwakhala mbali yaikulu ya zikhulupiriro za anthu zachipembedzo kuyambira makedzana. Zojambula, zosemasema komanso nyimbo zimaonetsa choncho. Zifanifani za akerubi, mtundu wa angelo, zinali zokongoletsera chihema komanso kachisi wakale wachiyuda. Zifanifani za angelo zimakongoletsa matchalitchi ndi maparishi kulikonse m’mayiko achikristu. Nyumba zoonetseramo zinthu zamakedzana n’zodzaza ndi zojambula ndi zosemasema zosonyeza angelo.
Kutchuka kwa Angelo
Angelo atchuka kwambiri m’mayiko ena posachedwapa. Makanema nthaŵi zambiri amaonetsa angelo monga anthu amene anamwalira ndipo abweranso kudziko lapansi kuti adzachite zinthu zabwino. M’filimu ina, angelo anathandiza timu yolephera ya mpira wa baseball kuti ipambane. M’filimu inanso, mngelo womuteteza anathandiza mnyamata wina kuti abwezere imfa ya chibwenzi chake. Nkhani yothandizidwa ndi angeloyi ndiyo mutu wa pologalamu ina yotchuka yoonetsedwa pa wailesi yakanema ya ku America.
Nyimbo zonena za angelo zangoti mbwee! Ku United States, pa zaka khumi zapitazo nyimbo imodzi mwa nyimbo 10 zilizonse zotchuka inatchulapo mngelo. Mmene timafika mkati mwa zaka za m’ma 1990, “masitolo oposa 120 ogulitsa zinthu zokhala ndi angelo” anatsegulidwa ku America. Masitolo ameneŵa amagulitsa zidole, zokoloŵeka zokongoletsa ndi zolembera kapena zolembapo, ngakhale zoseŵeretsa ana zokhala ndi zithunzi za angelo. Misonkhano ngakhale manyuzi akuti amaphunzitsa anthu mmene angapezerane ndi zamoyo zauzimu zimenezi. Magazini, manyuzipepala, ndi mapologalamu a pawailesi kapena pa TV ocheza ndi anthu otchuka amasimba za nkhani za anthu akukumana ndi angelo.
Mabuku Mazanamazana
Ndiyenso pali mabuku. Sitolo ina yaikulu yogulitsa mabuku mumzinda wa New York imagulitsa mabuku osiyanasiyana opitirira 500 amene amanena za angelo, makamaka angelo oteteza. Mabuku ameneŵa amalonjeza kuonetsa omwe awaŵerenge mmene angapezerane ndi angelo owateteza, mmene angadziŵire mayina awo, mmene angalankhulirane nawo, ndi mmene angapemphere thandizo lawo. Mabuku ameneŵa ali ndi tinkhani tambiri tonena za mmene angelo akhala akuchitira pakakhala mavuto, kumachotsa anthu pamsewu kuti asagundidwe ndi galimoto, kuchiritsa matenda oopsa, kutonthoza othodwa, komanso kuteteza asilikali kunkhondo. Angelo ameneŵa amachita zimenezi “popanda kufuna kuti musonyeze kaye kulapa, kutembenuka mtima, kapena kuvomereza kuti muzitsatira malamulo ena ake.” Koma kaŵirikaŵiri “kukumana” ndi angelo kwa masiku anoku sikuchititsa anthu kusintha moyo wawo. Nthaŵi zambiri anthu amene amati anakumanapo ndi zoterezi chimene amapindulapo chimangokhala kumva bwino chabe basi.
M’nyengo yathu ino ya kupsinjika maganizo ndiponso ya mavuto aakulu, nkhani zimenezi zingaoneke ngati zabwino kwabasi. Koma kodi n’zoti n’kuzikhulupirira? Kodi pali chovuta chilichonse mutazikukhulupirira kapena ayi?
[Mawu Otsindika patsamba 24]
Anthu ambiri amaganiza kuti anakumanapo ndi angelo