Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g01 1/8 tsamba 15-17
  • Inali Yoyamba Zaka 100 Zapitazo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Inali Yoyamba Zaka 100 Zapitazo
  • Galamukani!—2001
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Nthambi Zoyamba Zinkakulira
  • Nthambi Zina Zazikulu Zosindikiza Mabuku
  • Kodi Kuofesi ya Mboni za Yehova Kumachitika Zotani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Chionetsero Chokhala ndi Cholinga
    Nsanja ya Olonda—2008
Galamukani!—2001
g01 1/8 tsamba 15-17

Inali Yoyamba Zaka 100 Zapitazo

Mfundo zovomereza bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society zinalembedwa mwalamulo ku Pennsylvania, U.S.A., pa December 15, 1884.a Bungweli linakhazikitsa likulu lake kumeneko. Kenako, pa April 23, 1900, bungweli linapeza malo mumzinda wa London, ku England omangapo ofesi yanthambi yoyamba. Nthambiyo inali pamalo otchedwa 131 Gipsy Lane, m’dera la Forest Gate, kum’maŵa kwa mzinda wa London, monga mukuonera panopo.

PAMENE nthambi yoyambayo inkakhazikitsidwa zaka 100 zapitazo n’kuti ku England kuli Ophunzira Baibulo (dzina lomwe Mboni za Yehova zinkatchedwa panthaŵiyo) okwana 138. Patatha zaka ziŵiri, mu 1902, nthambi yachiŵiri inatsegulidwa ku Germany ndipo pomwe inkakwana 1904, maofesi ena anthambi anali atamangidwa ku Australia ndiponso ku Switzerland.

Mu 1918, chaka chomwe nkhondo yoyamba ya padziko lonse inatha, panali Ophunzira Baibulo okwana 3,868 omwe ankapereka lipoti la ntchito yolalikira padziko lonse. M’chaka chotsatira, nthambi yachisanu ya Watch Tower Society inakhazikitsidwa ku Canada. Kenako, kulalikira uthenga wa m’Baibulo kutayamba kuyenda bwino, nthambi zatsopano zinatsegulidwa m’mayiko ambiri osiyanasiyana ndipo zisanu ndi imodzi zinatsegulidwa m’chaka cha 1921 chokha.

Pofika 1931 pomwe Ophunzira Baibulo anatenga dzina la m’Baibulo lakuti Mboni za Yehova, n’kuti padziko lonse pali maofesi anthambi okwana 40. (Yesaya 43:10-12) M’zaka zitatu zotsatira, chiŵerengerochi chinakwera n’kufika pa 49! Pofika 1938 n’kuti pali chiŵerengero chachikulu koposa cha Mboni zokwana 59,047 zomwe zinali kulalikira m’mayiko 52. Komabe, panthaŵiyo n’kuti ntchito yawo yachikristu ikutsutsidwa kwadzaoneni m’madera ambiri.

Ulamuliro wandale wopondereza ndiponso wankhanza utafalikira m’mayiko ambiri komanso nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itayamba mu September 1939, maofesi anthambi a Mboni za Yehova m’mayiko ambiri anatsekedwa. Pomwe chinkakwana chaka cha 1942, maofesi anthambi 25 okha ndiwo ankagwira ntchito. Komabe, zodabwitsa n’zakuti panthaŵi ya nkhondo yosakaza kwambiriyo m’mbiri ya anthu, Mboni za Yehova zinkagwirabe ntchito mwachangu padziko lonse ndipo zinawonjezeka pamlingo winanso waukulu koposa m’mbiri yamakono.

Ngakhale pamene nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inali kutha mu 1945, ndiponso kuti madera ambiri a dziko lapansi anali atawonongedwa kukhala mabwinja, maofesi anthambi a Mboni anatsegulidwanso ndipo ena atsopano anakhazikitsidwa. Pomwe chinkafika chaka cha 1946 n’kuti pali maofesi anthambi 57 padziko lonse. Kodi nanga Mboni zachangu zinalipo zingati? Zinalipotu 176,456! Chiŵerengerochi n’chachikulu kuŵirikiza katatu chiŵerengero cha mu 1938!

Mmene Nthambi Zoyamba Zinkakulira

Mu 1911 nthambi yoyamba ya Watch Tower Society mu mzinda wa London, ku England, inasamutsidwa kupita ku malo otchedwa 34 Craven Terrace komwe malo a maofesi ndiponso a nyumba zokhalamo analiko ambiri. Kenako pa April 26, 1959, nthambi yatsopano ku Mill Hill, mu mzinda womwewu wa London anaipatulira. Kenako nyumba zogona zinakuzidwa, ndipo m’kupita kwanthaŵi (mu 1993) malo ena chapafupi pomwepo aakulu mamita 18,500 osindikizirako mabuku ndiponso maofesi oyendetsa ntchito anawapatulira. Kumeneko, makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! okwana 90 miliyoni amapangidwa chaka n’chaka m’zinenero 23.

Kukula kwa ofesi ya nthambi yachiŵiri ya Sosaite kunali kochititsa chidwi kuposa apa. Mu 1923 nthambi ya ku Germany inasamutsidwa kupita ku Magdeburg. Nsanja ya Olonda ya July 15, 1923, ndiyo inali yoyamba kusindikizidwa pa makina osindikizira a Sosaite kumeneko. M’zaka zingapo zotsatira, malo ena apafupi pomwepo anagulidwa, nyumba zina zowonjezera zinamangidwa, ndipo makina okonzera mabuku komanso makina ena osindikizira mabuku anagulidwa. Mu 1933, achipani cha Nazi analanda nthambiyo ndipo a Mboni analetsedwa kugwira ntchito yawo ndiponso m’kupita kwanthaŵi ena mwa iwo okwanira zikwi ziŵiri anatumizidwa ku misasa yachibalo.

Itatha nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse mu 1945, malo amene anali ku Magdeburg omwe panthaŵiyo anali m’dera la East Germany, anabwezedwa ndipo nthambi inakhazikitsidwanso. Koma pa August 30, 1950 apolisi achikomyunizimu anadzasokoneza pa nthambiyo ndipo anamanga ogwirapo ntchito, ndipo Mboni za ku East Germany zinaletsedwa kugwira ntchito yawo. Apa n’kuti mu 1947 malo ena atagulidwa mumzinda wa Wiesbaden, West Germany. M’zaka makumi angapo zotsatira, nyumba za ofesi yanthambi zomwe anamanga kumeneko zinkakuzidwa nthaŵi ndi nthaŵi malinga ndi kuchuluka kwa mabuku omwe ankafunika.

Popeza kuti malo omangapo maofesi ena owonjezera anali atatha ku Wiesbaden, malo ena okwana mahekitala 30 anagulidwa pafupi ndi Selters mu 1979. Atamanga kwa zaka pafupifupi zisanu, nthambi yaikuluyo anaipatulira pa April 21, 1984. Pakali pano inakuzidwa kuti ithe kusunga antchito oposa chikwi chimodzi. Mwezi uliwonse magazini opitirira 16 miliyoni, m’zinenero zoposa 30, amasindikizidwa pa makina aakulu kwambiri a ku Selters ndipo chaka chathachi, mabuku oposa 18 miliyoni kuphatikizapo mabaibulo, anapangidwa pa makina opangira mabuku.

Nthambi Zina Zazikulu Zosindikiza Mabuku

Nthambi ina inakhazikitsidwa koyamba mumzinda wa Kobe, ku Japan mu 1927, koma ntchito ya Mboni inachepa chifukwa chakuti Mboni zinali kuzunzidwa koopsa panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse. Komabe, nkhondoyo itangotha, nthambi inakhazikitsidwa mu mzinda wa Tokyo. Ataona kuti pamalowo palibe malo oti n’kuwonjezera kumanga, anamanga nthambi ina yatsopano ku Namazu. Nthambiyo anaipatulira mu 1973. Mwamsanga maofesi anthambi ameneŵa anayamba kuchepa, ndipo maofesi ena atsopano aakulu anamangidwa ku Ebina ndipo anawapatulira mu 1982. Nyumba zina zowonjezera zomwe zingasunge antchito okwana 900 zatha kumangidwa pamalopa posachedwapa. Mu 1999 makope opitirira 94 miliyoni a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndiponso mabuku oposa mamiliyoni ambiri anasindikizidwa m’chinenero cha chijapanizi chokha.

Kukula kwa maofesi anthambi kwakhala kofanana m’mayiko ambiri. Nthambi ina inakhazikitsidwa mu mzinda wa Mexico City, ku Mexico mu 1929. Kenako, Mboni zitawonjezeka kufika pa 60,000, nthambi ina yatsopano yaikulu inamangidwa kunja kwa mzindawo. Nthambiyo inapatulidwa mu 1974 ndipo maofesi ena owonjezera anamalizidwa mu 1985 ndi 1989. Padakali pano, nyumba yatsopano yaikulu yosindikiziramo mabuku ndiponso nyumba zogona zowonjezera zili pafupi kutha. Choncho, posachedwapa nthambi ya ku Mexico izidzasunga antchito okwana 1,200. Panopo nthambiyo ikupereka mabuku ndiponso magazini kwa Mboni zopitirira 500,000 ndiponso kwa anthu ena miyandamiyanda a ku Mexico komanso okhala m’mayiko ena oyandikana ndi dzikolo.

Mu 1923 analinganiza ofesi yanthambi mu mzinda wa Rio de Janeiro, ku Brazil ndipo kenako anamanga nthambi yatsopano yokongola kwambiri kumeneko. Koma popeza kuti mzinda wa São Paulo ndiwo chimake cha ntchito zamalonda ndi za mtengatenga ku Brazil, mu 1968 anamanga nthambi yatsopano mu mzinda umenewo. Pofika chapakatikati m’ma 1970, ku Brazil kunali Mboni pafupifupi 100,000. Komabe, kunali kosatheka kuti maofesi ena owonjezera amangidwe ku São Paulo, motero malo ena okwana mahekitala 115 anagulidwa ku Cesário Lange, mtunda wa makilomita 150 kunja kwa mzinda wa São Paulo. Pa March 21, 1981, nthambi ya kumalo atsopanowo anaipatulira. Chifukwa cha kuwonjezedwa kwa nyumba pamalowo, nthambiyo itha kusunga anthu pafupifupi 1,200. Ku Brazil kumapangidwa magazini ndiponso mabuku opita m’madera ambiri a ku South America ndi m’madera enanso a padziko lapansi.

Nthambi inanso yaikulu yosindikiza mabuku anaimaliza kumayambiriro kwa m’ma 1990, pafupi ndi mzinda wa Bogotá, ku Colombia. Kumeneko magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amapangidwa kuti afalitsidwe m’chigawo chonse cha kumpoto chakumadzulo kwa South America.

Nthambi zina zomwe zimasindikiza magazini miyandamiyanda chaka n’chaka zili ku Argentina, Australia, Canada, Finland, Italy, Korea, Nigeria, Philippines, South Africa, ndi Spain. Nthambi ya ku Italy imapanganso mabuku komanso mabaibulo m’zinenero zambiri chaka chilichonse. N’zoona kuti, pachaka, mabuku opitirira 40 miliyoni ndiponso magazini opitirira biliyoni imodzi omwe amapangidwa amawapangirabe ku likulu la Watch Tower Bible and Tract Society ku Brooklyn, New York, komanso ku malo ake osindikizirako mabuku omwe ali kumpoto kwa New York.

Ndithudi, n’zochititsadi chidwi kwambiri kuti chiŵerengero cha maofesi anthambi omwe akusamalira zofunika za Mboni za Yehova m’mayiko 234 chawonjezeka kuchoka pa imodzi zaka 100 zapitazo kufika pa 109 lerolino. Komanso, n’zochititsatu chidwi kwabasi kuti nthambizi zili ndi antchito odzipatulira achikristu odzifunira opitirira 13,000! Ndithudi, ntchito yawo pamodzi ndi ya antchito odzifunira anzawo opitirira 5,500 omwe ali ku likulu la Sosaite, yakhala yofunika kwambiri pa kukwaniritsa ulosi wa Yesu Kristu wakuti ‘uthenga uwu wabwino wa Ufumu wa Mulungu udzalalikidwa padziko lonse lapansi chimaliziro chisanafike.’—Mateyu 24:14.

[Mawu a M’munsi]

a Panthaŵiyo inkatchedwa Zion’s Watch Tower Tract Society.

[Chithunzi patsamba 15]

Tom Hart, ndiye akuti mwina anali Wophunzira Baibulo woyamba ku England

[Chithunzi patsamba 16]

Nthambi ya mumzinda wa London pamalo otchedwa 34 Craven Terrace (pachithunzi chomwe chili kumanja)

[Chithunzi patsamba 16]

Malo omwe panopa akugwiritsidwa ntchito mumzinda wa London

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena