Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g01 2/8 tsamba 3
  • Mukadwala Kwambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mukadwala Kwambiri
  • Galamukani!—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Matenda Aakulu Ndi Nkhani ya Banja Lonse
    Galamukani!—2000
  • Kusokonezeka Maganizo
    Galamukani!—2001
  • Mmene Mabanja Amapiririra Matenda Aakulu
    Galamukani!—2000
  • Kodi Baibulo Lingandithandize Kupirira Matenda?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Galamukani!—2001
g01 2/8 tsamba 3

Mukadwala Kwambiri

“Zinandisokoneza maganizo kwabasi.”Anatero John atadziŵa kuti ali ndi matenda oopsa.

“Ndinagwidwa nthumanzi.”Anatero Beth atazindikira kuti matenda ake afika podetsa nkhaŵa.

KUDZIŴA kuti muli ndi matenda aakulu ndiponso owononga thupi kapena kudziŵa kuti mupunduka chifukwa cha zilonda zimene munavulala pangozi ndi china cha zinthu zoŵaŵa kwambiri m’moyo. Kaya matendawo mwawadziŵira mu ofesi ya dokotala kuli zii kapena ngati mwazindikira kukula kwa vuto lanulo m’chipinda cha kungozi poona madokotala ali yakaliyakali, mungalephere kumvetsa. Si zinthu zambiri m’moyo zimene zimakukonzekeretsani kudzathana ndi chisoni chimene mumakhala nacho matenda oopsa akakusokonezani.

Pofuna kudziŵa zimene zingathandize anthu amene adwala kwambiri posachedwapa, atolankhani a Galamukani! analankhula ndi anthu ambiri m’mayiko osiyanasiyana amene kwa zaka zambiri athana nawo matenda aakulu owononga thupi. Anawafunsa kuti anenepo maganizo awo pamafunso onga akuti: Kodi zinakukhudzani bwanji? Kodi n’chiyani chinakuthandizani kupirira ndiponso kulimba mtima? Kodi munachita zinthu zotani kuti mukhaleko ndi mphamvu yochitanso zinthu bwino? Zimene anapeza pa kufufuzaku komanso mfundo zina zimene ofufuza zotsatira za matenda anthaŵi yaitali apeza tazilemba kuti zithandize anthu amene akusauka ndi matenda pakali pano.a

[Mawu a M’munsi]

a Nkhani ino talembera makamaka anthu odwala kapena olumala, koma nkhani zamutu wakuti “Nthenda Yaikulu” (Galamukani! ya June 8, 2000) zinali ndi chidziŵitso chokhudza makamaka anthu amene akusamalira odwalawo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena