Chiyembekezo Chimathandizadi?
DANIEL anali ndi zaka teni basi, koma anali atatha chaka chathunthu akuvutika ndi matenda a kansa. Madokotala ndiponso achinansi ake anali atataya kale mtima. Koma Daniel sanataye mtima ayi. Iye ankakhulupirira kuti akadzakula adzakhala wofufuza ndipo adzathandiza kupeza mankhwala ochiritsa matenda a kansa. Chinamulimbitsanso mtima makamaka chinali chakuti ankayembekezera kubwera kwa dokotala wodziŵa bwino za kansa yakeyo. Komano tsiku lake litakwana, dokotalayo analephera kubwera chifukwa kunja sikunache bwino. Zimenezi Daniel zinamulefula. Kwa nthaŵi yoyamba, iye anatayiratu mtima. Kenaka patangotha masiku angapo anamwalira.
Amene anasimba nkhani ya Daniel ndi munthu wina wa zaumoyo yemwe anafufuza mmene chiyembekezo ndi kutaya mtima zimakhudzira thanzi lathu. N’kutheka kuti nkhani zoterezi munazimvapo. Mwachitsanzo, mwina munamvapo za agogo enaake amene ankadwala mwakayakaya komano ankafunitsitsa ataona chinthu chinachake chomwe achidikirira kwa nthaŵi yaitali; chinthu monga kufika kwa wokondedwa wawo winawake kapena chabe chikondwerero chinachake cha pachaka. Ndiye chinthucho chitangochitika, basi agogowo anafa. Kodi n’chiyani chimachititsa zoterezi? Kodi kukhala n’chiyembekezo n’kothandizadi kwambiri monga mmene anthu ena amaganizira?
Anthu ambiri ofufuza za matenda amati kusataya mtima, kukhala n’chiyembekezo, komanso maganizo ena otere, kumathandizadi pa moyo ndiponso thanzi la munthu. Komano si onse amagwirizana ndi mfundoyi. Ofufuza ena amati zimenezi n’zikhulupiriro chabe ndipo zilibe umboni wasayansi. Iwoŵa amaona kuti matenda amayambitsidwa ndi zinthu zenizeni osati za m’maganizo chabe ayi.
Inde, kuyambira kale anthu akhala asakukhulupirira kuti chiyembekezo n’chothandizadi. Zaka masauzande zapitazo, Aristotle, yemwe anali wafilosofi wa ku Greece anafunsidwapo kuti anene tanthauzo la chiyembekezo, ndiyeno iye anayankha kuti chiyembekezo “n’kulota uli maso.” Ndipo osati kale kwenikweni, mtsogoleri wa dziko la America, Benjamin Franklin ananena monyoza kuti: “Wodalira chiyembekezo amangotaya nthaŵi pachabe.”
Motero kodi zoona zake zenizeni za chiyembekezo n’zotani? Kodi nthaŵi zonse munthu akakhala n’chiyembekezo amakhala akungodzinamiza yekha kuti akwanitsa kuchita zinthu zomwe kwenikweni zili zosatheka? Kapena kodi pali zifukwa zomveka zoganizira kuti chiyembekezo n’chinthu chofunikiradi kwa tonsefe kuti tikhale athanzi ndi osangalala, komanso kuti chiyembekezo n’chinthu chotsimikizika ndiponso chopindulitsadi?