Ana Akuvutika ndi Uchigawenga
Dzuwa likangolowa kumene kumpoto kwa Uganda, mumaona ana ambirimbiri osavala nsapato akuyenda m’misewu. Amachoka kumidzi kwawo kunja kusanade ndipo amapita ku mizinda ikuluikulu, monga ku Gulu, ku Kitgum, ndi ku Lira. Akafika kumeneko, amamwazikana. Ena amapita ku nyumba zochitira mabizinesi, kokwerera mabasi, ku mapaki, ndi kumabwalo a nyumba zikuluzikulu. Dzuwa likatuluka, mumawaonanso ali pamsewu akubwerera kwawo. N’chifukwa chiyani amachita zinthu zachilendozi?
ANTHU ena amati anawa ndi ogwira ntchito shifiti cha usiku. Koma ana amenewa sakhala akupita kuntchito. Amachoka kunyumba dzuwa likangolowa kumene chifukwa kunja kukada, kumidzi kumene amakhala kumakhala koopsa kwambiri.
Kwa zaka pafupifupi 20, asilikali okhala kutchire akhala akupita ku midzi ya anthu n’kumakaba ana. Chaka chilichonse amaba anyamata ndi atsikana ambirimbiri n’kulowera nawo m’nkhalango yowirira. Anawo amabedwa makamaka usiku, ndipo zigawengazo zikawaba, zimawasandutsa asilikali, zimawanyamulitsa katundu, ndiponso zimagona nawo. Ana obedwawo akapanda kumvera, zigawengazo zimatha kuwadula mphuno kapena milomo. Zikagwira ana amene akufuna kuthawa, zimawapha mwankhanza zosaneneka.
Palinso ana ena amene akuvutika ndi uchigawenga. Ku Sierra Leone kuli achinyamata opunduka amene anawadula manja ndi mapazi adakali ana aang’ono. Ku Afghanistan kuli anyamata ndi atsikana amene amaduka zala ndi kuchoka maso chifukwa choseweretsa mabomba apansi ooneka ngati zidole za agulugufe.
Ana ena uchigawenga umawakhudza m’njira ina. Mwachitsanzo, mu 1995 pamene zigawenga zinaukira mzinda wa Oklahoma City, ku United States, pa anthu 168 amene anaphedwa, 19 anali ana. Ena a iwo anali makanda. Bombalo litaphulika, moyo wa tianato unatha mwadzidzidzi, monga momwe kandulo imazimira ndi mphepo. Chifukwa cha uchigawengawo, anawo analandidwa ufulu wokhala ndi moyo, wosewera, kuseka, ndi kukupatiridwa m’manja mwa mayi awo ndi bambo awo.
Zinthu tatchulazi n’zaposachedwapa, koma uchigawenga wakhala ukuvutitsa anthu kwa zaka zambiri, monga momwe tionere.
[Bokosi patsamba 3]
AMAKONZEKERA IMFA YA MWANA
“Lero m’mawa, pamene ndimadzutsa mwana wanga wamwamuna wa zaka 11, anandifunsa kuti, ‘Kodi lero zigawenga zaphulitsa kale?’” Analemba choncho David Grossman pofotokoza za chiwawa chomwe chafala m’dziko lawo. Iye anapitiriza kuti: “Mwana wanga ali ndi mantha.”
Pa zaka zaposachedwapa, ana ambiri aphedwa pa ziwawa za zigawenga moti makolo ena amakonzekera zoti ana awo adzaphedwa pa ziwawa. Grossman analemba kuti: “Sindidzaiwala zimene mnyamata ndi mtsikana wina anandiuza za momwe anali kukonzekerera tsogolo lawo. Iwo anati adzakwatirana n’kubereka ana atatu. Osati awiri ayi, koma atatu, kuti mmodzi atafa, padzatsale awiri.”
Sananene zomwe angachite ngati awiri mwa anawo atafa, kapena onse atatu.a
[Mawu a M’munsi]
a Mawu amene alembedwa mu nkhani ino achokera m’buku lakuti Death as a Way of Life, lolembedwa ndi David Grossman.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
© Sven Torfinn/Panos Pictures