Zimene Baibulo Limanena
Kodi Ngati Anthu Akukondana Ndiye Kuti Palibe Cholakwika Atagonana Asanakwatirane?
PA KAFUKUFUKU winawake, pafupifupi anthu 90 pa anthu 100 amene anafunsidwa mafunso anati kugonana anthu asanakwatirane si kulakwa ngati akukondana. Maganizo amenewa amasonyezedwa ndi kuvomerezedwa m’mabuku, pa TV, m’mawailesi, ndi m’manyuzipepala. Ma TV ndi mafilimu nthawi zambiri amasonyeza kuti kugonana ndi chinthu chimene anthu amachita mwachibadwa akayamba kukondana.
Komabe, anthu amene akufuna kusangalatsa Mulungu sayembekezera kuti dzikoli liwapatse malangizo, ndipo amadziwa kuti limangotsatira maganizo a wolamulira wake, Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Amasamalanso kuti asamangotsatira zimene akumva mumtima mwawo, chifukwa akudziwa kuti “mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.” (Yeremiya 17:9) M’malo mwake, anthu amene alidi anzeru amayembekezera kuti Mlengi ndiponso Mawu ake ouziridwa awatsogolere.—Miyambo 3:5, 6; 2 Timoteyo 3:16.
Kugonana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu
“Mphatso iliyonse yabwino ndi mtulo uliwonse wangwiro zimachokera kumwamba, pakuti zimatsika kuchokera kwa Atate wa zounika zonse zakuthambo,” limatero lemba la Yakobu 1:17. Kugonana mu ukwati ndi imodzi ya mphatso za mtengo wapatali zimenezo. (Rute 1:9; 1 Akorinto 7:2, 7) Kumathandiza anthu kuberekana, ndiponso kumagwirizanitsa mwamuna ndi mkazi wake m’thupi ndi m’maganizo m’njira yachikondi ndi yosangalatsa kwambiri. “Ukondwere ndi mkazi wokula nayo,” inalemba choncho Mfumu Solomo yakale. “Maere ake akukwanire nthawi zonse.”—Miyambo 5:18, 19.
Mwachibadwa, Yehova amafuna kuti tipindule ndi kusangalala ndi mphatso zake. Kuti zimenezi zitheke, watipatsanso malamulo ndi mfundo zabwino kwambiri zoti tizitsatira. (Salmo 19:7, 8) Yehova ndi ‘amene amatiphunzitsa kupindula, amene amatitsogolera m’njira yoyenera ife kupitamo.’ (Yesaya 48:17) Kodi Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi chikondi, angatimane chinthu chimene chilidi chosangalatsa?—Salmo 34:10; 37:4; 84:11; 1 Yohane 4:8.
Kugonana Musanakwatirane N’kupanda Chikondi
Mwamuna ndi mkazi akakwatirana, amakhala ngati “thupi limodzi.” Anthu awiri osakwatirana akagonana, limene limatchedwanso dama, nawonso amakhala “thupi limodzi,” koma lodetsedwa pamaso pa Mulungu.a Komanso, kugonana koteroko n’kupanda chikondi. N’chifukwa chiyani tikutero?—Maliko 10:7-9; 1 Akorinto 6:9, 10, 16.
Chifukwa chimodzi n’choti kuchita dama ndiko kugonana ndi munthu wina popanda kudzipereka kwenikweni kwa munthuyo. Ndipo kuwonjezera pa kumuchotsera munthu ulemu, dama likhoza kubweretsa matenda, mimba zosafunidwa, ndi kupwetekedwa maganizo. Koposa zonse, kumaphwanya miyezo yolungama ya Mulungu. Choncho, dama limasonyeza kusaganizira za moyo ndi chimwemwe cha panopa ndi cha m’tsogolo cha munthu winayo.
Kwa Mkhristu, dama limatanthauzanso kuphwanya ufulu wa mbale kapena mlongo wake wauzimu. (1 Atesalonika 4:3-6) Mwachitsanzo, anthu amene amati ndi atumiki a Mulungu amene amagonana asanakwatirane amabweretsa chidetso mu mpingo wachikhristu. (Aheberi 12:15, 16) Ndiponso amamulanda munthu amene achita naye damayo mwayi woonedwa monga munthu wa makhalidwe abwino, ndipo ngati munthu winayo ali wosakwatira, amamulepheretsa kudzalowa m’banja ali woyera. Amaipitsanso mbiri yabwino ya banja lawo, komanso amalakwira banja la munthu amene agona nayeyo. Pomaliza, amasonyeza kuti samvera Mulungu, yemwe am’pweteka maganizo pophwanya malamulo ndi mfundo zake zolungama. (Salmo 78:40, 41) Ndipo Yehova ‘adzapereka chilango’ kwa anthu osalapa ochita zoipa zonse zoterozo. (1 Atesalonika 4:6) Choncho kodi n’zodabwitsa kuti Baibulo limatiuza kuti, ‘tithawe dama’?—1 Akorinto 6:18.
Kodi pali winawake amene mukumukonda ndipo mukufuna kumanga naye banja? Ndiyeno bwanji osagwiritsa ntchito nthawi ya chibwenzi chanu kuti mumange maziko olimba a kukhulupirirana ndi kulemekezana? Taganizirani izi: Kodi mkazi angamukhulupirire bwanji ndi mtima wonse mwamuna amene wasonyeza kuti ndi wosadziletsa? Ndipo kodi mwamuna angathe bwanji kuchengeta ndi kulemekeza mosavuta mkazi amene waphwanya malamulo a Mulungu kuti akhutiritse zilakolako zake kapena kuti asangalatse mwamunayo?
Kumbukiraninso kuti anthu amene amaphwanya mfundo zachikondi za Mulungu amakolola zomwe afesa. (Agalatiya 6:7) Baibulo limati, “amene amachita dama amachimwira thupi lake la iye mwini.” (1 Akorinto 6:18; Miyambo 7:5-27) N’zoona kuti ngati mwamuna ndi mkazi amene anagonana asanakwatirane alapadi, kuchita khama kuti abwezeretse ubwenzi wawo ndi Mulungu, ndi kulimbikitsa kukhulupirirana kwawo, maganizo oipa akhoza kutha pamapeto pake. Komabe, zimene anachita m’mbuyomu nthawi zambiri zimawasiyira chipsera. Mwamuna ndi mkazi wina amene tsopano anakwatirana amamva chisoni kwambiri kuti anachita dama. Mwamunayo nthawi zina amadzifunsa kuti, ‘kodi kukangana kwa m’banja mwathuku mwina n’chifukwa cha maziko odetsedwa amenewa?’
Chikondi Chenicheni N’chopanda Dyera
Ngakhale kuti munthu amene ali ndi chikondi chenicheni akhozanso kukopeka ndi munthu winayo, chikondicho “sichichita zosayenera” ndiponso “sichisamala zofuna zake zokha.” (1 Akorinto 13:4, 5) M’malo mwake, chimayesetsa kusamala ndi kusangalatsa munthu winayo. Chikondi choterocho chimalimbikitsa mwamuna ndi mkazi kulemekezana ndi kuika kugonana pamalo ake oyenera oikidwa ndi Mulungu, omwe ndi kama wa ukwati.—Aheberi 13:4.
Kukhulupirirana ndi kukhala wotetezeka kumene kumachititsa banja kukhala ndi chimwemwe chenicheni n’kofunika kwambiri m’banjamo mukabadwa ana, chifukwa Mulungu anafuna kuti ana azikulira pamalo achikondi, okhazikika, ndi otetezeka. (Aefeso 6:1-4) Ndi mu ukwati mokha mmene anthu awiri amakhaladi odzipereka kwa wina ndi mnzake. Mu mtima mwawo, ndiponso nthawi zambiri ndi mawu, amalumbira kuti adzasamalirana ndi kuthandizana pa nthawi zabwino ndi zovuta kwa moyo wawo wonse.—Aroma 7:2, 3.
Kugonana kwa mwamuna ndi mkazi wake kukhoza kulimbitsa unansi wawo. Ndiponso mu ukwati wachimwemwe, mwamuna ndi mkazi amaona kuti kugonana kumakhala kosangalatsa ndi kwatanthauzo, popanda kunyazitsa ukwatiwo, kuvutitsa chikumbumtima, kapena kusamvera Mlengi.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “dama” akuphatikizapo zachiwerewere zilizonse zomwe munthu wachita ndi munthu yemwe sanakwatirane naye zimene zimaphatikizapo kugwiritsa ntchito maliseche, monga kugonana m’kamwa.—Onani Galamukani! ya August 8, 2004, tsamba 12, ndi Nsanja ya Olonda ya February 15, 2004, tsamba 13, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
◼ Kodi Mulungu amakuona bwanji kugonana kwa anthu amene sanakwatirane?—1 Akorinto 6:9, 10.
◼ N’chifukwa chiyani dama limapweteketsa?—1 Akorinto 6:18.
◼ Kodi anthu awiri amene ali pachibwenzi angasonyezane bwanji chikondi chenicheni?—1 Akorinto 13:4, 5.