Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 8/07 tsamba 5
  • Musamawalekerere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musamawalekerere
  • Galamukani!—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kulemekeza Ulamuliro N’chifukwa Chiyani Kuli Kofunika?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Onani Zambiri
Galamukani!—2007
g 8/07 tsamba 5

Mfundo 3

Musamawalekerere

N’chifukwa Chiyani? Magazini ina (Parents) inanena kuti ofufuza anapeza kuti “pali makolo ena achikondi koma osalekerera, amene amasamalira bwinobwino ana awo komanso amawapatsa malamulo osasinthasintha. Motero anawo amachita bwino kusukulu, amakhala anthu olongosoka, sadzikayikira, ndiponso amasangalala ndi moyo wawo. Koma ana amene makolo awo ali olekerera kwambiri kapena ovuta kwambiri sakhala otere ayi.”

Kuvuta kwake: Kuyambira ali aang’ono mpaka kufika pokula, ana amachita zinthu zosamvera ulamuliro wanu. M’buku lina lonena za ulamuliro wa makolo (Parent Power!) John Rosemond anati: “Makolo akakhala olekerera ndiponso akamagonjera ana awo, anawo amadziwa msanga zimenezi.” Iye anatinso: “Makolo akapanda kuonetsa ana awo kuti wamkulu ndani panyumbapo anawo amayamba kuchita zinthu ngati kuti iwowo ndiye aakulu.”

Mmene mungakwanitsire: Musamaganize kuti ana anu asiya kukukondani kapena akhumudwa kwambiri chifukwa choti mukusonyeza mphamvu zanu panyumbapo. Yehova Mulungu, yemwe anayambitsa banja, safuna kuti ana azikhala ndi mphamvu zofanana ndi makolo awo pa za kayendetsedwe ka banjalo. M’malo mwake iye anapatsa makolo udindo wolamulira banjalo ndipo analamula ana kuti: “Muzimvera makolo anu.”—Aefeso 3:14, 15; 6:1-4.

N’zotheka kugwiritsira ntchito mphamvu zanu popanda kupondereza anawo. Mungachite zimenezi motani? Mungatero potsanzira Yehova. Iye ali ndi mphamvu zoti atafuna angathe kumakakamiza ana ake tonsefe kuchita zimene iyeyo akufuna, komano satero ayi. M’malo mwake iye amatilimbikitsa kuti tikhale ndi makhalidwe abwino. Mawu ake amati: “Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.” (Yesaya 48:18) Yehova amafuna kuti tizimumvera, osati chifukwa chomuopa ngati kuti iyeyo ndi chinthu choopsa, koma chifukwa choti timamukonda. (1 Yohane 5:3) Iye satilamula kuchita zinthu zimene sitingathe, ndipo amadziwa kuti timapindula tikamachita zinthu motsatira mfundo zake za makhalidwe abwino.—Salmo 19:7-11.

Kodi mungatani kuti mulimbe mtima n’kuyamba kugwiritsa ntchito mphamvu zanu m’njira yoyenerera? Choyamba, muyenera kusakayika ngakhale pang’ono kuti zimenezi n’zimene Mulungu amafuna kuti muzichita. Chachiwiri, musakayikenso kuti kutsatira makhalidwe abwino a Mulungu pa moyo wanu kungakuthandizeni kwambiri inuyo komanso ana anu.—Aroma 12:2.

Komano kodi ndi zinthu zotani kwenikweni zimene mungachite kuti musakhale olekerera?

[Mawu Otsindika patsamba 5]

‘Langizani ana anu, ndipo adzasangalatsa moyo wanu.’—Miyambo 29:17

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena