Zochitika Padzikoli
◼ “Mosakayikira [chaka cha 2006] chikhala nambala 6 pa mndandanda wa zaka zofunda kwambiri.” Pamndandandawo zaka 10 zofunda kwambiri zinali m’kati mwa zaka 12 zapitazi.—WORLD METEOROLOGICAL ORGANIZATION.
◼ Dipatimenti yoona zachitetezo ku Beijing inalamula kuti khomo lililonse lizikhala ndi “galu mmodzi” basi, n’cholinga chochepetsa kufala kwa matenda a chiwewe. Ku China, anthu pafupifupi 2,660 anafa ndi matendawa mu 2004.—XINHUA ONLINE, CHINA.
◼ Alendo ambiri omwe amagona ku hotela ndipo amagwiritsira ntchito zigwiriro za zitseko, nyale, telefoni, ndi zipangizo zoyatsira ma TV za m’hotelamo, amatenga tizilombo toyambitsa chimfine.—MACLEAN’S, CANADA.
Kuwerengetsera Tizilombo ku Amazon
Akatswiri a maphunziro a tizilombo apeza mitundu pafupifupi 60,000 ya tizilombo tosiyanasiyana m’nkhalango ya Amazon. Malinga ndi nyuzipepala ina ya pa Intaneti, ya Folha Online, mitunduyi ikhoza kufika 180,000. Panopa, pali akatswiri 20 amene akugwira ntchitoyi. Malipoti aposachedwapa akusonyeza kuti chaka chilichonse, tinganene kuti akatswiriwa akutulukira ndi kufotokoza pafupifupi mitundu itatu ya tizilomboti. Ngati ntchitoyi ipitiriza kuyenda motere, kuti ithe pangafunike mibadwo 90 ya akatswiriwa, ndipo mbadwo uliwonse uyenera kugwira ntchitoyi zaka 35, kapena kuti ntchito yonseyi ingatenge zaka pafupifupi 3,300.
Umphawi wa Magetsi
Magazini ya Our Planet, yofalitsidwa ndi bungwe loona za chilengedwe la United Nations Environment Programme inati: “Anthu oposa biliyoni imodzi ndi theka, kutanthauza pafupifupi munthu mmodzi pa anayi alionse, sagwiritsira ntchito magetsi ndipo pafupifupi mabiliyoni awiri ndi theka amaphikira ndi kuwotha makala, ndowe kapena nkhuni.” Magaziniyi inapitiriza kuti: “Chaka chilichonse, utsi wa zinthu zimenezi umapha amayi ndi ana pafupifupi mamiliyoni awiri ndi theka.”
Vuto la Kucheza pa Intaneti
Pa Intaneti anthu amatha kucheza ndi anthu ambiri osawadziwa ndipo akatero amadzimva kuti ndi otchuka. Amenewanso ndi “malo abwino kwambiri kwa anthu abodza,” atsankho, ndiponso amiseche, inatero nyuzipepala ya pa Intaneti ya Folha Online. Anthu ena akamacheza ndi anzawo sanena zoona za moyo wawo. Ena amanyoza anthu onenepa kwambiri, aafupi, atsitsi lanzindo ndi enanso, moti onyozedwawo amavutika maganizo kwambiri. Malinga ndi zimene katswiri wina wa za maganizo wa ku Brazil, Ivelise Fortim ananena, izi zimachitika chifukwa chakuti “anthu onyozedwawo amaona kuti zimene zimachitika pa [Intaneti] ndi zofunika kwambiri kuposa zinthu zochitika pamoyo wa tsiku ndi tsiku.”
Chipangizo Chakale Chodziwira Zinthu Zakuthambo
Mu 1901, anthu ofufuza zamoyo zina m’nyanja anapeza chipangizo chinachake chadzimbiri m’sitima ya Aroma yomwe inamira kufupi ndi chilumba cha Antikýthēra ku Greece. Anthu akuona kuti chipangizochi n’chimene ankadziwira zakuthambo m’zaka za m’ma 100 B.C.E., ndipo chinapangidwa mwaluso kwambiri. Posachedwapa asayansi ataphunzira za chipangizochi pogwiritsira ntchito makamera amphamvu kwambiri, apeza kuti chili ndi mawiro amkuwa 30 amanomano ndipo poyamba ankachisunga m’bokosi lamatabwa. Pogwiritsira ntchito chipangizochi ankatha kudziwa malo omwe pali dzuwa ndi mwezi komanso nthawi yomwe kudzachitika kadamsana kapena yomwe mwezi udzada. Malinga ndi zimene magazini ya Nature inanena “chipangizochi chinapangidwa mwaluso kwambiri kuposa chipangizo china chilichonse chimene anthu akuchidziwa chopangidwa m’zaka 1,000 kuchokera m’nthawi imene chinapangidwa.”
[Mawu a Chithunzi patsamba 21]
AP Photo/Thanassis Stavrakis