Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/09 tsamba 3
  • Ophunzira Ambiri Amapanikizika ndi Sukulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ophunzira Ambiri Amapanikizika ndi Sukulu
  • Galamukani!—2009
  • Nkhani Yofanana
  • “Zikomo Kwambiri Chifukwa cha Nkhani Zimenezi”
    Galamukani!—2011
  • Achinyamatanu—Yehova Sadzaiŵala Ntchto Yanu!
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Ngati Mwana Wanu Wamkazi Akuvutika Maganizo
    Galamukani!—2014
  • Kodi Makolo Mungathandize Bwanji Ana Anu?
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Galamukani!—2009
g 4/09 tsamba 3

Ophunzira Ambiri Amapanikizika ndi Sukulu

MTSIKANA wina wazaka 17, dzina lake Jennifer, ankakhoza bwino m’kalasi. Ankachitanso nawo masewera osiyanasiyana ndipo aphunzitsi ankamukonda kwambiri. Koma atatsala pang’ono kumaliza sukulu, anayamba kudwala mutu ndipo nthawi zambiri ankachita nseru. Iye akuganiza kuti anayamba kudwala chifukwa chodzipanikiza kwambiri ndi kuwerenga komanso chifukwa chosagona mokwanira.

Pali ophunzira ambiri amene ali ndi vuto ngati la Jennifer. Vutoli limayamba chifukwa chopanikizika ndi sukulu, ndipo chiwerengero cha ophunzira amene ali ndi vutoli chikuwonjezereka chaka chilichonse. Ena afika pokaonana ndi madokotala odziwa za vutoli. Ichi n’chifukwa chake aphunzitsi ena a ku America ayambitsa pulogalamu yothandiza ana a sukulu kuti azikhoza bwino komanso kuti asamapanikizike.

Ngati ndinu mwana wasukulu, mwina nanunso muli ndi vuto lofanana ndi la Jennifer. Koma ngati ndinu kholo, mwina mukuona kuti mwana wanu akupanikizika kwambiri ndi sukulu. Kodi n’chiyani chingathandize ana a sukulu komanso makolo kuthetsa vutoli?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena