Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/10 tsamba 25
  • Fupa Ndi Lolimba Modabwitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Fupa Ndi Lolimba Modabwitsa
  • Galamukani!—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Matenda Ofooketsa Mafupa Amayamba Mosaonekera
    Galamukani!—2010
  • Tsopano Ndife Thupi Limodzi
    Imbirani Yehova
  • Tsopano Ndife Thupi Limodzi
    Imbirani Yehova Mosangalala
  • Kuwadziŵa bwino Matenda a Nyamakazi
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 1/10 tsamba 25

Panagona Luso!

Fupa Ndi Lolimba Modabwitsa

● Fupa ndi lolimba kwambiri ndipo akatswiri ena amayerekezera kulimba kwake ndi “chitsulo, konkire, komanso chingwe champhamvu chomwe chimatanuka.” Chifukwa chiyani?

Taganizirani izi: Thupi la munthu lili ndi mafupa pafupifupi 206 ndipo mafupa amenewa analumikizana m’malo osiyanasiyana okwana 68. Fupa lalitali kwambiri ndi la pantchafu ndipo lalifupi kwambiri limapezeka mkatikati mwa khutu. Mafupa amenewa amathandiza munthu kuyenda komanso kudzipinda mochititsa chidwi monga mmene amachitira akatswiri a masewera. Lipoti la bungwe lina lochita kafukufuku linati: “Chala chathu chamanthu pachokha chimasonyeza kuti mmisiri amene anapanga thupi lathu (kaya inu mumati ndi ndani) ndi wanzeru kwambiri!”—National Space Biomedical Research Institute.

Fupa silisweka wamba, ngakhale mutalimenya mwamphamvu ndi chinthu china cholimba kwambiri. Lipoti la bungwe lija linanenanso kuti: “[Fupa] linapangidwa mofanana ndi konkire yolimba kwambiri yokhala ndi zitsulo mkati mwake. Zitsulozi zimathandiza kuti konkireyo ikhale yolimba, pamene simenti, mchenga ndi miyala zimathandiza kuti konkireyo igwirane bwinobwino. Koma fupa ndi logwirana kwambiri kuposa konkire iliyonse yolimba kwambiri.” Pulofesa Robert O. Ritchie wa pa yunivesite ya Berkeley, ku U.S.A, anati: “Timafuna titabera nzeru za mmene fupa linapangidwira.”

Mosiyana ndi konkire, fupa ndi mbali yofunika kwambiri ya zinthu zambiri zamoyo. Likasweka limatha kudzilumikiza lokha, limakula ndiponso limathandiza kwambiri popanga magazi m’thupi. Komanso, mofanana ndi minofu ya m’thupi, fupa limalimba kwambiri likamagwiritsidwa ntchito kunyamula zinthu zolemera. Ichi n’chifukwa chake anthu ochita masewera amakhala ndi mafupa olimba kusiyana ndi anthu amene amangokhala.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi fupa linangokhalako mwangozi kapena linachita kupangidwa ndi Mlengi?

[Chithunzi patsamba 25]

Fupa (lakulitsidwa)

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Leg bone: © MedicalRF.com/age fotostock; close-up: © Alfred Pasieka/Photo Researchers, Inc.; gymnast: Cultura RF/​Punchstock

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena