Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/10 tsamba 14-31
  • Zoti Banja Likambirane

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zoti Banja Likambirane
  • Galamukani!—2010
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Anaganiza Bwino?
  • KODI MUKUDZIWA CHIYANI ZOKHUDZA MFUMU SAULI?
  • ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE
  • KUCHOKERA M’MAGAZINI INO
  • MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2008
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 1/10 tsamba 14-31

Zoti Banja Likambirane

Kodi Anaganiza Bwino?

Werengani Genesis 39:1-23. Ndiyeno yang’anani pachithunzipa. Lembani mayankho anu pa mizere ili m’munsiyi.

1. Kodi mkazi amene ali pachithunzipa ndi ndani?

․․․․․

2. Nanga mwamunayo ndi ndani?

․․․․․

3. Kodi mwamunayo anaganiza zochita chiyani?

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi n’chifukwa chiyani mwamunayo anaganiza zochita zimenezi? Kodi zimene anachita zinamubweretsera mavuto otani? Kodi mukuona kuti iye anaganiza bwino? Ngati anaganiza bwino, n’chifukwa chiyani mukuyankha choncho? Kodi ndi pazochitika ziti pamene mungakumane ndi mavuto chifukwa chosankha kuchita zinthu zabwino?

KODI MUKUDZIWA CHIYANI ZOKHUDZA MFUMU SAULI?

4. Kodi Sauli anali ndi maonekedwe otani omwe anthu ankachita nawo chidwi?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Samueli 9:1, 2.

․․․․․

5. Kodi Yehova anakana Sauli chifukwa chiyani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Samueli 13:13, 14.

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi chofunika kwambiri kwa Mulungu n’chiyani kuposa maonekedwe?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Samueli 16:6, 7.

Kodi kudziwa mfundo imeneyi kungakuthandizeni bwanji kuti muzidzikongoletsa moyenerera?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Timoteyo 4:8.

ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE

Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowa.

TSAMBA 4 Pankhani ya ntchito, kodi Baibulo limatilangiza chiyani? Mlaliki 3:․․․

TSAMBA 7 Kodi tiyenera kugwirira ntchito chiyani? Yohane 6:․․․

TSAMBA 10 Kodi Mulungu wakhazikitsa tsiku lodzachita chiyani? Machitidwe 17:․․․

TSAMBA  28 Kodi mwamuna ndi mkazi akakwatirana amakhala chiyani? Genesis 2:․․․

● Mayankho ali patsamba 14

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Mkazi wa Potifara.

2. Yosefe.

3. Kusagona ndi mkazi wa Potifara.

4. Sauli anali wamtali ndiponso wokongola.

5. Sauli sanamvere Mulungu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena