Galamukani! Inathandiza Mayi Wina Kuti Asachotse Mimba
● Mayi wina wa ku Mexico dzina lake Anita anali ndi ana atatu ndipo anapezekanso kuti ndi woyembekezera.a Iye anauza mwamuna wake kuti sakufuna mwana wina ndipo achita chilichonse chimene angathe kuti achotse mimbayo. Iye ananena kuti atha kufika mpaka podzipha. Panthawiyi n’kuti Anita akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova koma samalimbikira kwenikweni. Iye anati: “Panthawiyi ndinali munthu wamakani.”
Munthu wa Mboni amene ankaphunzira ndi Anita anamufotokozera mfundo za m’Baibulo zokhudzana ndi nkhaniyi. Mwachitsanzo, iye anauza Anita kuti Mulungu amaona kuti moyo wa mwana wosabadwa ndi wopatulika. Kale ku Isiraeli, ngati munthu wavulaza mayi wapakati mpaka mayiyo kapena mwanayo kufa, Chilamulo cha Mulungu chinkanena kuti munthuyo ayenera kuweruzidwa kuti wapha munthu. (Eksodo 21:22, 23)b Koma Anita sankamva zonsezi. Iye anali atasankha kale kuti achotse mimba.
Anita anati: “Winawake anandiuza kuti ngati nditadzibaya mankhwala enaake, mimbayo ikhoza kuchoka nthawi yomweyo. Ndinaguladi mankhwalawo ndipo ndinapempha mnzanga kuti andibaye. Anandibayadi, koma palibe chimene chinachitika. Kenako ndinazindikira kuti mnzangayo sanafune kuti andithandize kuchotsa mimba ndipo m’malo mwa mankhwalawo anagwiritsa ntchito madzi.”
Koma Anita ankafunitsitsabe kuchotsa mimba. Atafika mwezi wachinayi ali ndi pakati, anapeza dokotala amene analola kuchotsa mimba. Patangotsala masiku 6 kuti akachotse mimba, munthu wa Mboni uja anapatsa Anita nkhani yakuti “Nkhani ya Mwana Wosabadwa” (Diary of an Unborn Child), yomwe inali mu Galamukani! ya Chingelezi ya May 22, 1980. Nkhaniyo inamaliza ndi mawu akuti: “Lero ndaphedwa ndi mayi anga.” Mawu amenewa anamukhudza kwambiri Anita ndipo analira kwa maola angapo. Anita anati: “Nkhani imeneyi inanditsegula m’maso.”
Anita anabereka mwana wamkazi wathanzi. Iye anati: “Panopa ndimadziwa Yehova amene ndimam’konda ndi mtima wanga wonse.” Iye akuphunzitsanso mwana wake Mawu a Mulungu n’cholinga choti nayenso ayambe kukonda Yehova. Ndipo mwana wakeyo amanena kuti ali ndi moyo chifukwa cha Mulungu, yemwe ndi chitsime cha moyo, komanso chifukwa chakuti mfundo za m’Mawu a Mulungu zomwe zinali mu Galamukani! zinathandiza mayi ake kuti asachotse mimba.
[Mawu a M’munsi]
a Tasintha dzina la mayiyu
b Mawu a lembali m’chinenero choyambirira, amanena za imfa ya mayiyo kapena mwanayo.